-
Buku la Nzeru Lokhala ndi Uthenga Wothandiza LerolinoNsanja ya Olonda—1999 | April 1
-
-
Ataona kuti mwamuna wake akusintha, Mihoko nayenso anayamba kutsatira zimene anali kuphunzira. Lamulo lina limene linamuthandiza kwambiri linali lakuti: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa.”e Chotero Mihoko ndi mwamuna wake anati azikambirana za zinthu zabwino zimene amachita ndi mmene angawongolere zinthu m’malo moimbana mlandu. Chotsatirapo chake? Mihoko akukumbukira kuti: “Zandipatsa chimwemwe chachikulu. Takhala tikuchita zimenezi pachakudya chamadzulo masiku onse. Ngakhale mwana wathu wa zaka zitatu zakubadwa amayankhulapo. Zimatitsitsimula zedi!”
-