-
“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
-
-
11 Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azidalira Yehova. Iye anawauza kuti: “Musatenge golide, siliva kapena kopa m’zikwama zanu za ndalama. Musatenge thumba la chakudya cha pa ulendo kapena malaya awiri kapena nsapato kapenanso ndodo chifukwa wantchito ayenera kulandira chakudya chake.” (Mateyu 10:9, 10) Pa nthawiyo anthu apaulendo ankakonda kutenga zikwama za ndalama ndi matumba a zakudya komanso nsapato zapadera. Polangiza ophunzira akewo kuti asamade nkhawa ndi zinthu zimenezi, iye kwenikweni ankatanthauza kuti: “Muzidalira Yehova ndi mtima wonse chifukwa iye adzakupatsani zosowa zanu.” Yehova akanawasamalira pochititsa kuti anthu amene angamvetsere uthenga wabwino achereze ophunzirawo, ndipotu anthu a ku Isiraeli ankakonda kuchereza alendo.—Luka 22:35.