Kuphunzitsidwa Kuchita Chifuniro cha Yehova
“Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu, pakuti ndinu Mulungu wanga.”—SALMO 143:10, NW.
1, 2. (a) Kodi ndi liti pamene tiyenera kuphunzitsidwa, ndipo tiyenera kukumbukira choonadi chotani? (b) Kodi nchifukwa ninji kuphunzitsidwa ndi Yehova kuli kofunika kwambiri?
TSIKU lililonse limene munthu ali moyo ndi kugwira ntchito, angathe kuphunzitsidwa kanthu kena ka phindu. Zimenezo zili choncho kwa inu, ndiponso kwa anthu enanso. Koma kodi chimachitika nchiyani pa imfa? Sikuli kotheka kuphunzitsidwa kapena kuphunzira kanthu kalikonse mumkhalidwe umenewo. Baibulo limanena momveka bwino kuti akufa “sadziŵa kanthu bi.” Kulibe chidziŵitso ku Sheol, manda a anthu onse. (Mlaliki 9:5, 10) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kuphunzitsidwa kwathu, kupeza kwathu chidziŵitso, kuli chabe? Zimenezi zimadalira pa zimene timaphunzitsidwa ndi mmene timagwiritsirira ntchito chidziŵitsocho.
2 Ngati tingophunzitsidwa za dziko, tilibe mtsogolo mokhalitsa. Komabe, ubwino wake ngwakuti alipo anthu mamiliyoni m’mitundu yonse omwe akuphunzitsidwa chifuniro cha Mulungu namakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Maziko a chiyembekezo chimenechi ali m’kuphunzitsidwa ndi Yehova, Magwero a chidziŵitso chopatsa moyo.—Salmo 94:9-12.
3. (a) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yesu anali wophunzira woyamba wa Mulungu? (b) Kodi tili ndi chitsimikizo chotani chakuti anthu anali kudzaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo pakumakhala chotulukapo chotani?
3 Mwana woyamba wa Mulungu, monga wophunzira Wake woyamba, anaphunzitsidwa kuchita chifuniro cha Atate wake. (Miyambo 8:22-30; Yohane 8:28) Yesunso anasonyeza kuti anthu miyandamiyanda adzaphunzitsidwa ndi Atate wake. Kodi ife amene tikuphunzitsidwa ndi Mulungu tikuyembekezeranji mtsogolo? Yesu anati: “Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine. . . . Indetu, indetu, ndinena ndi inu, iye wokhulupira ali nawo moyo wosatha.”—Yohane 6:45-47.
4. Kodi anthu mamiliyoni ambiri ayambukiridwa motani ndi chiphunzitso cha Mulungu, ndipo ali ndi chiyembekezo chotani?
4 Yesu anali kugwira mawu pa Yesaya 54:13, amene ananenedwa kwa mkazi wa Mulungu wophiphiritsa, Ziyoni wakumwamba. Ulosi umenewo umakwaniritsidwa mwapadera kwa ana ake, ophunzira a Yesu Kristu obadwa ndi mzimu a 144,000. Otsalira a ana auzimu amenewo akugwira ntchito lerolino, akumapititsa patsogolo programu yakuphunzitsa ya padziko lonse. Chotulukapo nchakuti, mamiliyoni a anthu ena amene akupanga “khamu lalikulu,” nawonso akupindula mwa kuphunzitsidwa ndi Yehova. Iwo ali ndi chiyembekezo chapadera cha kupitiriza kuphunzira popanda imfa kuwadodometsa. Motani? Eya, iwo ali pamzere wokapulumuka “chisautso chachikulu” chomwe chikufika mofulumiracho ndi kudzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso.—Chivumbulutso 7:9, 10, 13-17.
Chigogomezero Chokulirapo pa Kuchita Chifuniro cha Mulungu
5. (a) Kodi lemba la chaka cha 1997 ndi liti? (b) Kodi tiyenera kukuona motani kupezeka pamisonkhano yachikristu?
5 M’chaka cha 1997, Mboni za Yehova, m’mipingo yoposa 80,000 kuzungulira dziko lonse, zidzakumbukira nthaŵi zonse mawu oyamba a Salmo 143:10, NW, akuti: “Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu.” Limeneli lidzakhala lemba la chaka cha 1997. Mawuwo, omwe adzalembedwa moonekera bwino m’Nyumba za Ufumu, adzakhala chikumbutso chakuti malo apadera olandirirako chiphunzitso cha Mulungu ndiwo pamisonkhano yampingo, pamene tingakhale ndi phande m’programu yakulangizidwa kopitiriza. Pamene tigwirizana ndi abale athu pamisonkhano kuti tiphunzitsidwe ndi Mlangizi Wamkulu, tingalingalire mmene wamasalmo anachitira, amene analemba kuti: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”—Salmo 122:1; Yesaya 30:20.
6. Kodi nchiyani chimene ifenso tikuzindikira mogwirizana ndi mawu a Davide?
6 Inde, timafuna kuphunzitsidwa kuchita chifuniro cha Mulungu m’malo mwa chifuniro cha mdani wathu Mdyerekezi kapena chifuno cha anthu opanda ungwiro. Choncho, mofanana ndi Davide, timazindikira Mulungu amene timamlambira ndi kumtumikira: “Pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu uli wokoma; unditsogoleretu m’dziko la chilungamo.” (Salmo 143:10, NW) Chifukwa chosafuna kuyanjana ndi anthu opanda choonadi, Davide anakonda kukhala kumalo olambirirako Yehova. (Salmo 26:4-6) Popeza kuti mzimu wa Mulungu unatsogolera mapazi ake, Davide anakhoza kuyenda m’mabande a chilungamo.—Salmo 17:5; 23:3.
7. Kodi ndi motani mmene mzimu wa Mulungu wagwirira ntchito pampingo wachikristu?
7 Davide wamkulu, Yesu Kristu, analonjeza atumwiwo kuti mzimu woyera udzawaphunzitsa zinthu zonse ndi kuwakumbutsa zinthu zonse zimene anali atawaphunzitsa. (Yohane 14:26) Kuyambira pa Pentekoste kumkabe mtsogolo, Yehova wakhala akuvumbula pang’onopang’ono “zakuya za Mulungu” zopezeka m’Mawu ake olembedwa. (1 Akorinto 2:10-13) Iye wachita zimenezi kudzera m’njira yooneka imene Yesu anaitcha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Iye amagaŵira chakudya chauzimu chimene chimaphunziridwa m’programu yophunzitsa m’mipingo ya anthu a Mulungu padziko lonse lapansi.—Mateyu 24:45-47.
Kuphunzitsidwa Chifuniro cha Yehova pa Misonkhano Yathu
8. Kodi nchifukwa ninji kukhala ndi phande pa Phunziro la Nsanja ya Olonda kuli kofunika kwambiri?
8 Nkhani za m’Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu ndi mlungu kaŵirikaŵiri zimaphunzitsa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo. Zimenezi zimatithandizadi kulimbana ndi nkhaŵa za moyo. Pa maphunziro ena, pamakhala kuphunzira mfundo zauzimu za choonadi kapena maulosi a Baibulo. Ha, nzochuluka chotani nanga zimene timaphunzitsidwa pamaphunziro ameneŵa! M’maiko ambiri Nyumba za Ufumu zimadzaza pha, pamisonkhano imeneyi. Komabe m’maiko angapo, chiŵerengero cha ofika pamisonkhano chatsika. Muganiza nchifukwa ninji? Kodi mwina ena akulola ntchito yakuthupi kudodometsa kusonkhana kwawo pamodzi mokhazikika “kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino”? Kapena mwina amatayira maola ochuluka m’machitachita akucheza kapena kuonerera wailesi yakanema, akumachulukidwa ndi zochita moti nkumalephera kufika pamisonkhano yonse? Kumbukirani chilangizo chouziridwa pa Ahebri 10:23-25. Kodi kusonkhana pamodzi kuti tiphunzitsidwe ndi Mulungu sikuli kofunika kwenikweni tsopano pamene ‘tsiku lilinkuyandikira’?
9. (a) Kodi Msonkhano Wautumiki ungatikonzekeretse motani kuchita utumiki? (b) Kodi kuchitira umboni tiyenera kukuona motani?
9 Limodzi la mathayo athu ofunika koposa ndilo kutumikira monga atumiki a Mulungu. Msonkhano Wautumiki wakonzedwa kuti utiphunzitse mmene tingachitire zimenezi bwino lomwe. Timaphunzira mmene tingafikire anthu, zimene tiyenera kunena, mmene tingachitire pamene anthu avomereza, ngakhalenso zimene tingachite pamene anthu akana uthenga wathu. (Luka 10:1-11) Pamene njira zogwira ntchito zikulongosoledwa ndi kusonyezedwa pamsonkhano wa mlungu ndi mlungu umenewu, timakhala okonzekeretsedwa bwino kufikira anthu osati kokha popita kukhomo ndi khomo komanso polalikira m’makwalala, m’malo oimikamo magalimoto, m’zoyendera za onse, pamabwalo andege, pamalonda, kapena m’masukulu. Mogwirizana ndi pempho lathu lakuti, “Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu,” tiyenera kugwiritsira ntchito mwaŵi uliwonse kuchita zimene Mbuye wathu analimbikitsa kuti: “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti . . . alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.”—Mateyu 5:16.
10. Kodi ndi motani mmene tingawathandizire kwenikweni ‘oyenera’?
10 Pamisonkhano yampingo imeneyo, timaphunzitsidwanso kupanga anthu ena kukhala ophunzira. Titapeza okondwerera kapena titagaŵira buku, cholinga chathu popanga ulendo wobwereza ndicho kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. M’lingaliro lina, zimenezi zikufanana ndi ‘kukhala ndi oyenera’ kumene ophunzira anakuchita kotero kuti awaphunzitse zinthu zimene Yesu anawalamulira. (Mateyu 10:11; 28:19, 20) Pokhala ndi zipangizo zabwino koposa, monga buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, tilidi okonzekeretsedwa bwino kukwaniritsa utumiki wathu bwino lomwe. (2 Timoteo 4:5) Mlungu uliwonse pamene muli pa Msonkhano Wautumiki ndi Sukulu Yautumiki Wateokrase, yesetsani kumvetsetsa ndi kugwiritsira ntchito mfundo zothandiza zimene zidzasonyeza kuti muli mtumiki woyenera wa Mulungu, wochita chifuniro chake.—2 Akorinto 3:3, 5; 4:1, 2.
11. Kodi ena asonyeza motani chikhulupiriro m’mawu a pa Mateyu 6:33?
11 Chili chifuniro cha Mulungu kuti tipitirize ‘kuthanga tafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.’ (Mateyu 6:33) Dzifunseni nokha kuti, ‘Kodi ndingagwiritsire ntchito motani pulinsipulo limeneli ngati ntchito yanga yakuthupi [kapena ya mnzanga wa muukwati] ikudodometsa kusonkhana?’ Anthu okhwima mwauzimu ambiri amachitapo kanthu mwa kulankhula kwa owalemba ntchito za nkhaniyo. Mtumiki wina wanthaŵi zonse anadziŵitsa womlemba ntchito kuti anafunikira kupeza nthaŵi mlungu uliwonse ya kupezeka kumisonkhano yampingo. Womlemba ntchitoyo anavomereza pempholo. Koma pofunitsitsa kudziŵa zimene zinali kuchitika kumisonkhanoyo, anapempha kuti iyenso akapezekeko. Kumeneko anamva chilengezo cha msonkhano wachigawo womwe unalinkudza. Chotulukapo nchakuti, wolemba ntchitoyo anakonzekera kukapezeka pamsonkhanowo tsiku lonse lathunthu. Kodi mukutengapo phunziro lanji pa chitsanzochi?
Kuphunzitsidwa Chifuniro cha Yehova ndi Makolo Aumulungu
12. Kuti ana aphunzitsidwe chifuniro cha Yehova, kodi makolo achikristu ayenera kuchitanji moleza mtima komanso mokhwima?
12 Koma misonkhano yampingo ndi misonkhano yaikulu sindiyo makonzedwe okha omwe alipo otiphunzitsira kuchita chifuniro cha Mulungu. Makolo opembedza Mulungu akulamulidwa kuphunzitsa, kulanga, ndi kulera bwino ana awo kuti atamande Yehova ndi kuchita chifuniro chake. (Salmo 148:12, 13; Miyambo 22:6, 15) Kuchita zimenezo kumafuna kupita ndi “ana aang’ono” kumisonkhano kumene ‘angamve ndi kuphunzira,’ koma bwanji za kuwaphunzitsa za m’malemba oyera kunyumba? (Deuteronomo 31:12; 2 Timoteo 3:15) Mabanja ambiri mwa chikumbumtima chabwino ayamba programu ya phunziro la Baibulo lokhazikika la banja, komano posapita nthaŵi alilolanso kuzilala kapena kunyalanyazika. Kodi zimenezo zachitika kwa inunso? Kodi mudzangoganiza kuti chilangizocho cha kukhala ndi phunziro lokhazikika lotero chili chosayenera kapena kuti banja lanu nlosiyana kwambiri kwakuti zimenezo sizingagwire ntchito kwa inu? Mulimonse mmene zingakhalire, chonde inu makolo, ŵerenganinso nkhani zabwinozo, zakuti “Choloŵa Chathu Chauzimu Chaulemerero” ndi “Mfupo za Kulimbikira” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1995.
13. Kodi mabanja angapindule motani mwa kukambitsirana lemba la tsiku?
13 Mabanja akulimbikitsidwa kukhala ndi chizoloŵezi cha kukambitsirana lemba la tsiku m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Kungoŵerenga lembalo ndi ndime yake kuli bwino, koma kukambitsirana lembalo ndi kuona mmene lingagwirire ntchito kuli kopindulitsa koposa. Mwa chitsanzo, ngati mukukambitsirana Aefeso 5:15-17, NW, a m’banjawo angalingalire mmene ‘angawombolere nthaŵi’ kaamba ka phunziro laumwini, kukhala ndi phande mumtundu uliwonse wa utumiki wa nthaŵi zonse, ndi kusamalira magawo ena ateokrase. Inde, kukambitsirana lemba la tsiku kwa banja kungachititse wina kapena ambiri ‘kupitiriza kudziŵa [mokwanira] chimene chili chifuniro cha Yehova.’
14. Kodi Deuteronomo 6:6, 7 amasonyeza kuti makolo ayenera kukhala aphunzitsi a mtundu wanji, ndipo zimenezo zimafunanji?
14 Makolo ayenera kukhala aphunzitsi akhama kwa ana awo. (Deuteronomo 6:6, 7) Koma safunikira kumangodzudzula kapena kulamulira ana awo. Tate ndi mayi afunikiranso kumvetsera, mwakutero adzadziŵa bwino chimene ayenera kulongosola, kumveketsa bwino, kupereka chitsanzo, kapena kubwereza. M’banja lina lachikristu, makolo amayambitsa kulankhulana komasuka mwa kulimbikitsa ana awo kufunsa mafunso onena za zinthu zimene sakuzimvetsetsa kapena zowadetsa nkhaŵa. Mwakutero iwo anazindikira kuti mnyamata wawo anali ndi vuto la kusamvetsetsa nkhani yakuti Yehova alibe chiyambi. Makolowo anali okhoza kugwiritsira ntchito chidziŵitso cha m’zofalitsa za Watch Tower Society kusonyeza kuti anthu amakhulupirira kuti nthaŵi ndi thambo zilibe malire. Zimenezo zinathandiza kumveketsa mfundoyo, ndipo inakhutiritsa mwana wawoyo. Chotero dekhani kuti muyankhe mafunso a ana anu momvekera bwino ndi mwa Malemba, mukumawathandiza kuona kuti kuphunzira kuchita chifuniro cha Mulungu kungakhale kokhutiritsa kwambiri. Kodi ndi ziti zina zimene anthu a Mulungu—achichepere ndi achikulire omwe—amaphunzitsidwa lerolino?
Kuphunzitsidwa Kukonda ndi Kumenya Nkhondo
15. Kodi ndi liti pamene chikondi chathu chaubale chingayesedwe kaya chili chenicheni?
15 Mogwirizana ndi lamulo la Yesu latsopano, ‘tikuphunzitsidwa ndi Mulungu kuti tikondane wina ndi mnzake.’ (1 Atesalonika 4:9) Pamene pali bata ndipo zinthu zikuyenda bwino, tinganene kuti timawakondadi abale athu onse. Komano chimachitika nchiyani pamene pabuka kusemphana kapena pamene tikhumudwa ndi zimene Mkristu wina wanena kapena kuchita? Pamenepo chikondi chathu chingayesedwe kaya ngati chili chenicheni kapena ayi. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:8.) Kodi Baibulo limatiphunzitsa kuchitanji m’mikhalidwe yotero? Choyamba tiyenera kuyesayesa kusonyeza chikondi m’lingaliro lenileni. (1 Peter 4:8) M’malo mongoyang’ana pa zabwino za ife tokha, ndi kumakhumudwa pa zophophonya za ena zazing’ono, kapena kusunga chakukhosi, tiyenera kuyesayesa kulola chikondi kukwirira machimo ambiri. (1 Akorinto 13:5) Tikudziŵa kuti chimenechi ndi chifuniro cha Mulungu, pakuti nchimene Mawu ake amaphunzitsa.
16. (a) Kodi Akristu akuphunzitsidwa kumenya nkhondo yotani? (b) Kodi tili okonzekeretsedwa motani?
16 Ngakhale kuti ambiri sangagwirizanitse chikondi ndi nkhondo, timaphunzitsidwanso nkhondo, koma yamtundu wapadera. Davide anazindikira kudalira kwake pa Yehova kuti amphunzitse kumenya nkhondo, ngakhale kuti m’nthaŵi yake zimenezo zinaphatikizapo nkhondo yeniyeni yolimbana ndi adani a Israyeli. (1 Samueli 17:45-51; 19:8; 1 Mafumu 5:3; Salmo 144:1) Bwanji za nkhondo yathu lerolino? Zida zathu sizili zakuthupi. (2 Akorinto 10:4) Nkhondo yathu ili yauzimu, imene tiyenera kuikonzekera ndi zida zauzimu. (Aefeso 6:10-13) Kupyolera m’Mawu ake ndi mpingo wa anthu ake, Yehova akutiphunzitsa kumenya nkhondo yauzimu yachilakiko.
17. (a) Kodi ndi machenjera otani amene Mdyerekezi amagwiritsira ntchito kuti atipambutse? (b) Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchipeŵa mwanzeru?
17 Mwa njira zachinyengo ndi zamachenjera, Mdyerekezi kaŵirikaŵiri amagwiritsira ntchito zonyengerera za dziko, ampatuko, ndi ena otsutsa choonadi poyesayesa kutipambutsira ku zinthu zina zopanda pake. (1 Timoteo 6:3-5, 11; Tito 3:9-11) Kuchita ngati akuona kuti alibe mwaŵi weniweni wakutigonjetsa mwa njira yachindunji ndi yoonekeratu, choncho amayesa kutitchera msampha mwa kutisonkhezera kumadandaula pa zinthu zazing’ono ndi kufunsa mafunso opanda pake, amene alibemo phindu lauzimu lililonse. Monga asilikali atcheru, tiyenera kukhala maso pa ngozi zoterozo monga momwe timakhalira pa njira zoukira zachindunji.—1 Timoteo 1:3, 4.
18. Kodi kusakhalanso ndi moyo kaamba ka ife eni kumaphatikizaponji kwenikweni?
18 Sitimachirikiza zikhumbo za anthu kapena chifuniro cha mitundu. Yehova watiphunzitsa kupyolera mwa chitsanzo cha Yesu kuti tiyenera kukhala ndi moyo osati kaamba ka ife eni; m’malo mwake, tiyenera kukhala ndi maganizo omwe Kristu Yesu anali nawo ndipo tikhale ndi moyo kaamba ka chifuniro cha Mulungu. (2 Akorinto 5:14, 15) Mwina kale tinali ndi moyo wosadzisungira ndi womwerekera, tikumawawanya nthaŵi yamtengo wapatali. Madyerero, mamwaimwa, ndi chisembwere ndiyo mikhalidwe ya dzikoli. Tsopano pokhala kuti tikuphuzitsidwa kuchita chifuniro cha Mulungu, kodi sitili oyamikira kukhala olekanitsidwa ndi dziko lovundali? Chotero, tiyeni timenye zolimba nkhondo yauzimu kuti tisagwere m’machitachita odetsa a dzikoli.—1 Petro 4:1-3.
Kutiphunzitsa Kudzipindulitsa Ife Eni
19. Kodi kuphunzitsidwa chifuniro cha Yehova ndi kuchichita kumadzetsa mapindu otani?
19 Kuli kofunika kwambiri kudziŵa kuti kuphunzitsidwa kuchita chifuniro cha Yehova kumatipindulitsa kwambiri. Ndithudi, tiyenera kuchita mbali yathu mwa kutchera khutu kotero kuti tiphunzire ndiyeno kutsatira malangizo amene amadza kwa ife kupyolera mwa Mwana wake ndiponso mwa Mawu ake ndi mpingo wa anthu ake. (Yesaya 48:17, 18; Ahebri 2:1) Mwa kuchita zimenezo, tidzalimbitsidwa kuima nji m’nthaŵi zino zamasoka ndi kukhala okhoza kulimbana ndi zamtsogolo. (Mateyu 7:24:27) Ngakhale tsopano, tidzakondweretsa Mulungu mwa kuchita chifuniro chake ndipo tidzakhala ndi chitsimikizo chakuti mapemphero athu akuyankhidwa. (Yohane 9:31; 1 Yohane 3:22) Ndipo tidzapeza chimwemwe chenicheni.—Yohane 13:17.
20. Kodi mungachite bwino kusinkhasinkha pa chiyani pamene muona lemba la chaka m’chaka chonse cha 1997?
20 M’chaka chonse cha 1997, kaŵirikaŵiri tidzakhala ndi mpata wa kuŵerenga ndi kukambitsirana lemba la chaka, Salmo 143:10 lakuti: “Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu.” Pamene tikuchita zimenezi, tiyeni tigwiritsire ntchito ina ya mipatayo kusinkhasinkha za makonzedwe omwe talongosolapo kale, amene Mulungu wapereka kwa ife kuti tiphunzitsidwe. Ndipo tiyeni tigwiritsire ntchito kusinkhasinkha pa mawu koteroko monga chotisonkhezera kuchita mogwirizana ndi pempholo, tikumadziŵa kuti “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndani lerolino omwe akuphunzitsidwa kuchita chifuniro cha Yehova?
◻ Kodi Salmo 143:10 liyenera kutikhudza motani m’chaka cha 1997?
◻ Kodi timaphunzitsidwa motani kuchita chifuniro cha Yehova?
◻ Kodi chofunika nchiyani kwa makolo achikristu pophunzitsa ana awo?