Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 2/15 tsamba 19-22
  • Mmene Mungapezere Chimwemwe Popanga Ophunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungapezere Chimwemwe Popanga Ophunzira
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziŵa Omwe Angakhale “Nkhosa”
  • Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo
  • Kusunga Chikondwerero Chili Chamoyo
  • Kukulitsa Chikondi cha pa Yehova
  • Perekani Chithandizo Chogwira Ntchito
  • Alimbitseni Kuti Apirire
  • Chifukwa Chake Kupanga Ophunzira Nkofunikadi
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Aliyense Mumpingo Angathandize Ophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Kodi Mungagwire Nawo Ntchito Yothandiza Anthu Kukhala Ophunzira a Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 2/15 tsamba 19-22

Mmene Mungapezere Chimwemwe Popanga Ophunzira

CHIMODZI cha zinthu zopatsa chimwemwe chachikulu chimene munthu angakhale nacho ndicho kukhala wantchito mnzake wa Mulungu. Lerolino, ntchito ya Mulungu imaphatikizapo kusonkhanitsira anthu okonda chilungamo kumpingo wachikristu ndi kuwaphunzitsa kwa moyo wonse monga Akristu tsopano ndi kuti akapulumuke kuloŵa m’dziko latsopano.​—Mika 4:1-4; Mateyu 28:19, 20; 2 Petro 3:13.

Kwakhala kodzetsa chimwemwe chachikulu kwa Mboni za Yehova ku Latin America kuona anthu miliyoni imodzi akukhala ophunzira a Yesu Kristu kuyambira 1980. M’munda umenewu wobala zipatso, mmene anthu ambiri amalemekeza Baibulo ndi kulikhulupirira, atumiki ena a nthaŵi yonse atha kuthandiza anthu ochuluka kupatulira moyo wawo kwa Yehova. Pokhala ndi chidziŵitso chochuluka, mwinamwake angatiuze zinazake ponena za chimwemwe cha kupanga ophunzira. Zina za njira zawo zingakuthandizeni kupeza chimwemwe popanga ophunzira kwanuko.

Kudziŵa Omwe Angakhale “Nkhosa”

“Ndipo m’mzinda uliwonse, kapena m’mudzi mukaloŵamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo,” anatero Yesu pamene anatumiza atumwi ake kukalalikira. (Mateyu 10:11) Pamene mupita kukachezera anthu, kodi ndi motani mmene mungadziŵire awo amene angathandizidwe mwauzimu? Edward, mtumiki wanthaŵi yonse kwa zaka zoposa 50, akunena kuti: “Iwo amaonekera m’mafunso awo oona mtima ndi kukhutira kwawo pamene apatsidwa mayankho ochokera m’Malemba.” Carol akuwonjezera kuti: “Ngati munthu andiululira vuto laumwini kapena nkhaŵa, kumeneko kulidi kuchonderera thandizo. Ndimayesa kupeza chidziŵitso chimene chingamthandize mu zofalitsa za Watch Tower Society. Kufunitsitsa kwanga kumthandiza kumatsogolera ku phunziro la Baibulo.” Komabe, sikumakhala kwapafupi nthaŵi zonse kudziŵa oona mtima. Luis akusimba kuti: “Ena amene anaoneka kukhala okondwerera anadzakhala osakondwerera konse, koma ena amene poyamba anaoneka kukhala osakondwerera anasintha pamene anamva zimene Baibulo limanenadi.” Popeza anthu ambiri a ku Latin America amalemekeza Baibulo, iye akuwonjezera kuti, “Ndimadziŵa awo amene angathandizidwe mwauzimu pamene amalandira zimene Baibulo limaphunzitsa nditawasonyeza zimenezo.” Kuthandiza “oyenera” otero kupita patsogolo mwauzimu kumadzetsa chimwemwe chenicheni ndi chikhutiro. Kodi ndi motani mmene mungachitire zimenezi?

Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo

Nthaŵi zambiri njira yabwino koposa yothandizira anthu kumvetsa choonadi cha Baibulo ndiyo ya kugwiritsira ntchito zothandizira kuphunzira Baibulo zofalitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Kodi ndi motani mmene mungathandizire wina kukulitsa chiyamikiro cha zothandizira kuphunzira Baibulo zimenezi? Edward akuti: “Popeza kuti mikhalidwe ya anthu, umunthu wawo, ndi malingaliro zimasiyana kwambiri, ndimayesetsa kusaumirira panjira imodzi yoyambitsira maphunziro.” Simungagwiritsire ntchito njira imodzi kwa aliyense.

Kwa ena, makambitsirano a m’Malemba angapo ongocheza angafunikire musanawasonyeze buku lothandizira kuphunzira Baibulo. Komabe, amishonale aŵiri okwatirana akuti: “Nthaŵi zambiri timapempha kuyambitsa phunziro paulendo woyamba.” Mofananamo, Mboni ina imene yathandizira anthu 55 kufika pa kudzipatulira ikuti: “Njira yanga yaikulu yoyambitsira maphunziro a Baibulo yakhala yoyamba pamenepo kuphunzira buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.” Ngakhale kuti ena samakonda lingaliro la kuphunzira zilizonse, ena ngofunitsitsa kuphunzira zilizonse zimene amakhulupirira kuti zidzaŵathandiza m’moyo. Kugaŵira maphunziro a Baibulo aulere panyumba kaŵirikaŵiri kumamveka kukhala chinthu chabwino kwa ameneŵa. Amishonale ena akufotokoza kugaŵira kumeneku, ndipo akuti: “Ndikufuna kukusonyezani mmene timachitira. Ngati mudzalikonda, mudzapitiriza. Ngati simudzalikonda, kumeneko ndi kufuna kwanu.” Ngati ligaŵiridwa motero, anthu samamva mantha kulivomereza.

Mboni, ina imene yathandiza anthu ambiri ovutikira ndi osaphunzira kwenikweni, ikuti: “Matrakiti ndawaona kukhala othandiza makamaka poyambitsa maphunziro a Baibulo.” Kaya agwiritsire ntchito chofalitsa chotani, aphunzitsi anthaŵi yonse amayesetsa kugogomezera kwenikweni pa Baibulo. Carola akuti: “Paphunziro loyamba, ndimagwiritsira ntchito zithunzithunzi zokha ndi malemba ngati asanu, kotero kuti nsonga zenizeni zidziŵike ndi kuti Baibulo lisaoneke kukhala lolimba.”

Kusunga Chikondwerero Chili Chamoyo

Anthu amakondwera akamaona kuti akupita patsogolo, motero Jennifer akunena kuti: “Chititsani phunziro kukhala lokondweretsa. Pangani kupita patsogolo.” Kuchititsa phunziro mokhazikika mosaphonya milungu ina kumawathandizanso kuona kuti akupita patsogolo. Mpainiya amene anakulira kumidzi akufotokoza kufunika kwa kupeputsa mafotokozedwe ndi kusumika maganizo pa mfundo zazikulu, kotero kuti ngakhale awo a maphunziro ochepa angapite patsogolo mwamsanga. Iye akunena kuti: “M’mudzi mwathu tinafunikira kuwaza madzi panthaka titabzala mbewu. Ngati tinathira madzi ambiri m’mindayo, nthaka inkauma kwambiri kwakuti mbewu zomamera zinkalephera kutuluka, ndipo zinkafa. Mofananamo, ngati mudzaza okondwerera chatsopano ndi mfundo zambiri, zingaoneke kukhala zovuta kwambiri ndipo angabwevuke.” Ngakhale anthu ofuna kudziŵa zinthu zambiri ayenera kuphunzira kusumika maganizo pankhani imodzi panthaŵi imodzi kuti apite patsogolo m’kumvetsetsa. Yesu anati kwa atumwi ake: “Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.”​—Yohane 16:12.

Njira ina yosungira chikondwerero chili chamoyo ndiyo ya kulimbikitsa awo amene mumachezera kupitirizabe kulingalira za Mawu a Mulungu pamene inu muchoka. Yolanda anena kuti: “Siyani funso losayankha. Apatseni zochita, monga kuŵerenga mbali ina ya Baibulo kapena kufufuza nkhani ina yowakhudza.”

Kukulitsa Chikondi cha pa Yehova

Chikondwerero chanu chidzakula pamene muthandizira ophunzira anu kukhala “akuchita mawu, osati akumva okha.” (Yakobo 1:22) Kodi ndi motani mmene mungachitire zimenezo? Akristu oona amasonkhezeredwa ndi chikondi cha pa Yehova. Pedro, wa ku Mexico, akufotokoza kuti: “Anthu sangakonde munthu amene samadziŵa, chotero kuyambira kuchiyambi kwa phunziro, ndimawaphunzitsa dzina la Mulungu kuchokera m’Baibulo, ndipo ndimafunafuna mipata yogogomezera mikhalidwe ya Yehova.” M’makambitsirano, mungakulitse chiyamikiro cha Yehova mwa kusonyeza malingaliro anu ponena za iye. Elizabeth akuti: “Nthaŵi zonse ndimayesa kutchula ukoma wa Yehova. Pamaphunziro anga, ngati ndaona duŵa lokongola, mbalame yokongola, kapena mwana wa mphaka womaseŵera, ndimatchula nthaŵi zonse kuti imeneyo ndi ntchito ya Yehova.” “Lankhulani za dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu kuti ndi lenileni monga mmene mumalidziŵira,” akutero Jennifer. “Afunseni zimene adzafuna kuchita m’dziko latsopanolo.”

Pamene munthu asinkhasinkha moyamikira pa zimene akuphunzira ponena za Yehova, zimam’loŵa mumtima ndi kumsonkhezera kuchitapo kanthu. Koma sangasinkhesinkhe ngati sakukumbukira. Kubwereramo kwachidule kwa mfundo zazikulu zitatu kapena zinayi pambuyo pa phunziro lililonse kumathandiza kukumbukira. Aphunzitsi a Baibulo ambiri amauza achatsopano kulemba malemba ofunika kwambiri pamodzi ndi ndemanga yake kumbuyo kwa Baibulo lawo. Mmishonale wina wochokera ku England akufotokoza phindu lina la kubwereramo kuti: “Ndimafunsa mmene chidziŵitsocho chawapindulira. Zimenezi zimawachititsa kusinkhasinkha moyamikira pa njira za Yehova ndi malamulo ake.”

Mboni yokhulupirika imene inamaliza maphunziro ake m’kalasi yachitatu ya Gileadi ikuti: “Tiyenera kukhala otentha. Ophunzira athu ayenera kuzindikira kuti timakhulupirira zimene timaphunzitsa.” Chikhulupiriro chimene chinakuchititsani kukhala “wakuchita ntchito” wachimwemwe chingakhale choyambukira ngati timachisonyeza.​—Yakobo 1:25.

“Ndimaona kuti anthu amamva kukhala oyandikira kwa Mulungu ngati ndiwathandiza kuzindikira mayankho a mapemphero awo,” ikutero Mboni imene yathandiza ambiri kulambira Yehova. “Ndimawapatsa zitsanzo za zokumana nazo zanga, zonga ichi: Pamene ineyo ndi mnzanga tinafika ku gawo lathu latsopano monga apainiya, tinali chabe ndi ndiwo zamasamba zochepa, pakete imodzi ya majarini, ndipo tinalibe ndalama. Tinamaliza chakudya chathu pachakudya chamadzulo ndi kunena kuti, ‘Tsopano tilibe kalikonse ka maŵa.’ Tinapemphera za zimenezi, ndipo tinapita kukagona. Mmaŵa mwake mmamaŵa Mboni ina ya kumeneko inafika ndi kudzidziŵikitsa, ikumati, ‘Ndinali kupemphera kwa Yehova kuti atumize apainiya. Tsopano ndikhoza kutsagana nanu kwa pafupifupi tsiku lonse, koma popeza ndimakhala kutali, ndidzayenera kudya nanu chakudya chamasana, chotero ndabweretsa chakudyachi kaamba ka tonsefe.’ Inali nyama yang’ombe yambiri ndi ndiwo zamasamba zambiri. Nthaŵi zonse ndimauza ophunzira anga kuti Yehova samatisiya konse ngati tifunafuna Ufumu wake choyamba.”​—Mateyu 6:33.

Perekani Chithandizo Chogwira Ntchito

Pali zambiri zofunika pa kupanga ophunzira a Kristu kuposa kungochititsa phunziro la Baibulo. Mmishonale amene anatumikira kwa zaka zambiri monga woyang’anira woyendayenda akuti: “Apatseni nthaŵi. Osangotuluka m’phunziro litangotha. Ngati nkotheka, khalani ndi kucheza kwa kanthaŵi.” Elizabeth akuti: “Ndili wokhudzidwa ndi iwo chifukwa moyo ukuloŵetsedwamo. Nthaŵi zambiri ndimawadera nkhaŵa monga ngati ali ana anga.” Mboni zina zinapereka njira izi: “Achezereni pamene akudwala.” “Pamene muli pafupi ndi nyumba yawo, mwachitsanzo mu utumiki wakumunda, achezereni mwachidule kuwasonyeza Mboni zina.” Eva akuti: “Tcherani khutu mosamala kuti mudziŵe za banja lake ndi mkhalidwe wake m’moyo. Zimenezi zimayambukira mmene anthu amachitira ndi choonadi ndipo zingachedwetse kupita kwawo patsogolo. Khalani bwenzi lawo, kotero kuti akhale ndi chidaliro cha kulankhula za mavuto awo.” Carol akuwonjezera kuti: “Chikondwerero chenicheni mwa munthu nchofunika popeza kusintha kumene choonadi chidzabweretsa m’moyo wake nthaŵi zina kudzatanthauza kutaya banja lake ndi mabwenzi. Mwachisawawa nkwabwino kuti wophunzira adziŵe kumene timakhala ndipo ali ndi chidaliro cha kudza kwa ife nthaŵi ina iliyonse.” Mthandizeni kuona mpingo monga banja lake latsopano.​—Mateyu 10:35; Marko 10:29, 30.

“Khalani atcheru kuti mupereke chithandizo chogwira ntchito. Khalani nawo pamodzi pamisonkhano, ndipo athandizeni ndi ana awo,” akutero Yolanda. Kusonyeza achatsopano mmene angaphunzitsire ana awo, kuwongolera ukhondo wawo, kukonzekera ndemanga za pamisonkhano, ndi kupereka nkhani mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki konseko kuli mbali ya ntchito yopanga ophunzira. Mlongo wina akuwonjezera kuti: “Nkofunika kwambiri kuphunzitsa achatsopano utumiki. Pamene mbali imeneyi yakuphunzitsa inyalanyazidwa, ena amangowopabe ntchito yolalikira, kutaya chimwemwe chawo cha kutumikira Yehova, ndi kulephera kupirira.” Motero aphunzitseni mosamala ntchito ya kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza, ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Chimwemwe chanu chidzakhala chachikulu kwambiri pamene muona wophunzira wanu akupita patsogolo chifukwa cha chithandizo chanu ndi chitsogozo.

Alimbitseni Kuti Apirire

“Pali chikhoterero cha kuleka kuphunzira wophunzirayo atangobatizidwa,” akuchenjeza motero wopanga ophunzira wina wachidziŵitso. Mphunzitsi ndi wophunzira yemwe ayenera kukumbukira kuti Mkristu wobatizidwa chatsopano akali kutali ndi kukhala wokhwima mwauzimu. Afunikira kukula kwambiri m’chikhulupiriro chake, chidziŵitso chake pa malamulo a Mulungu, ndi chikondi chake pa Yehova. Nkofunika kwambiri kumlimbikitsa kukulitsa njira zabwino za phunziro laumwini kotero kuti apitirizebe kupita patsogolo.​—1 Timoteo 4:15.

Wachatsopano angafunikire kuthandizidwa kuti apite patsogolo ndi kukhala womasuka pakati pa gulu la abale. Angafunikire chitsogozo pochita ndi zophophonya za abale pamene ayandikana nawo. (Mateyu 18:15-35) Angafunikire chithandizo kuti akhale mphunzitsi waluso, wokhoza kuchita kufufuza payekha. Mmishonale wina akusimba kuti: “Wophunzira wina pambuyo pa ubatizo anafuna kukulitsa luso lake monga mphunzitsi, motero anandiuza kuti, ‘Ndidzafunikira kutsogoza phunziro latsopano mlungu wamaŵa, koma ndiyenera kukumbukira zinthu za m’machaputala oyambirira amene ndinaphunzira. Kodi tingapendenso machaputala ameneŵa, imodziimodzi, kotero kuti ndilembe mafotokozedwe ena a malemba ndi mafanizo, kotero kuti ndikazigwiritsire ntchito pamene ndipita kukachititsa phunziro langa?’ Iye wakhala mphunzitsi wabwino kwambiri, anayi a ophuzira ake anabatizidwa pamsokhano umodzi.”

Chifukwa Chake Kupanga Ophunzira Nkofunikadi

“Kupanga ophunzira kumawonjezera atamandi a Yehova. Ndiko moyo kwa aja amene amalandira choonadi,” akutero Pamela. “Ndimakondadi kuphunzitsa ena choonadi​—nchinthu chabwino kwambiri! Munthu amaona ophunzira ake akumakula pang’onopang’ono, akumapanga kusintha m’moyo wawo ndi kugonjetsa zopinga zimene zikanaoneka ngati zosagonjetseka popanda mzimu wa Yehova. Ambiri amene akhala okonda Yehova ndiwo amene akhala mabwenzi anga okondedwa.”

“Pamene ndilingalira za awo amene ndathandizira kukhala ophunzira,” akusimba motero mmishonale wochokera ku Germany, “ndimaona anthu opandadi chidaliro amene apita patsogolo kwambiri monga atumiki a Mulungu kwakuti sinditha kukhulupirira. Ndimaona anthu amene amagwetsa zopinga zolimba, mosakayikira ndi thandizo la Yehova. Ndimaona mabanja amene kale anali osweka koma tsopano ali ogwirizana​—ana achimwemwe okhala ndi makolo osamala. Ndimaona anthu amene akusangalala ndi moyo watanthauzo, akumatamanda Yehova. Chimenechi ndicho chimwemwe cha kupanga ophunzira.”

Inde, kukhala wantchito mnzake wa Yehova Mulungu m’ntchito yopanga ophunzira ali magwero a chimwemwe chosayerekezereka. Zokumana nazo za amishonale ndi za apainiya zatsimikiza zimenezo. Mungapeze chimwemwe chofananacho ndi chikhutiro ngati mudzagwiritsira ntchito njirazi ndi kulimbikira kuchita zimenezo ndi mtima wonse. Ndi dalitso la Yehova, chimwemwe chanu chidzakhala chodzala.​—Miyambo 10:22; 1 Akorinto 15:58.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena