Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 48 tsamba 120-tsamba 121 ndime 8
  • Yesu Anachita Zozizwitsa Koma Anakanidwa Ngakhale Kwawo ku Nazareti

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anachita Zozizwitsa Koma Anakanidwa Ngakhale Kwawo ku Nazareti
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchoka Panyumba ya Yairo ndi Kukachezanso ku Nazarete
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kuchoka ku Nyumba ya Yairo ndi Kuchezeranso ku Nazarete
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Yesu Ankazitenga Kuti Mphamvu Zochitira Zozizwitsa?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 48 tsamba 120-tsamba 121 ndime 8
Anthu ambirimbiri akutsatira Yesu pamene akuchoka kunyumba ya Yairo

MUTU 48

Yesu Anachita Zozizwitsa Koma Anakanidwa Ngakhale Kwawo ku Nazareti

MATEYU 9:27-34; 13:54-58 MALIKO 6:1-6

  • YESU ANACHIRITSA ANTHU OSAONA NDI WINA WOSALANKHULA

  • ANTHU A KU NAZARETI ANAKANA YESU

Yesu atachoka m’dera la Dekapole, anapita ku Kaperenao komwe anachiritsa mzimayi amene ankadwala matenda otaya magazi komanso anaukitsa mwana wamkazi wa Yairo. Yesu anachita zinthu zonsezi tsiku limodzi. Komabe pamene ankachoka kunyumba kwa Yairo, anthu awiri osaona anayamba kumutsatira n’kumakuwa kuti: “Mutichitire chifundo, Mwana wa Davide.”—Mateyu 9:27.

Chifukwa choti anthuwo anatchula Yesu kuti “Mwana wa Davide,” anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Yesu ndiye woyenera kulowa Ufumu wa Davide ndiponso kuti anali Mesiya. Poyamba Yesu anaoneka ngati sanamve zimene anthuwo ankanena koma n’kutheka kuti anachita dala zimenezi kuti aone ngati anthuwo ankafunitsitsa kuti Yesuyo awathandize. Ndipo anthuwo anachitadi zimenezo. Yesu atalowa m’nyumba, anthu awiri aja anamutsatira. Kenako anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chikhulupiriro kuti ndingachite zimenezi?” Iwo anamuyankha motsimikiza kuti: “Inde, Ambuye.” Pamenepo Yesu anawagwira m’maso n’kuwauza kuti: “Malinga ndi chikhulupiriro chanu zichitike momwemo kwa inu.”—Mateyu 9:28, 29.

Nthawi yomweyo anthu aja anayamba kuona. Yesu anauzanso anthuwa ngati mmene anachitira ndi anthu oyambirira aja kuti asauze aliyense zimene anawachitira. Koma chifukwa chakuti anali osangalala, patapita nthawi anayamba kufotokozera anthu a m’madera apafupi komanso akutali zimene Yesu anawachitira.

Pa nthawi imene anthu awiriwa ankachoka, anthu anabweretsa munthu wina amene sankalankhula chifukwa chakuti anali wogwidwa ndi chiwanda. Yesu atangotulutsa chiwandacho, munthuyo anayamba kulankhula. Anthu ambiri ataona zimenezi anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Zinthu zoterezi sizinaonekepo n’kale lonse mu Isiraeli.” Pamene zimenezi zinkachitika panalinso Afarisi. Afarisi sakanatha kutsutsa zozizwitsa zimene Yesu anachitazi, koma anayambanso kunena kuti Yesu “amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”—Mateyu 9:33, 34.

Kenako pasanapite nthawi yaitali, Yesu anabwerera ku tauni ya kwawo ku Nazareti ali ndi ophunzira ake. Pa nthawiyi n’kuti patadutsa pafupifupi chaka kuchokera pamene anaphunzitsa m’sunagoge wa ku Nazaretiko. Ngakhale kuti pa nthawi imeneyo anthu anagoma ndi uthenga wake, koma anakwiya kwambiri ndipo ankafuna kumupha. Komabe Yesu anapanganso ulendowu ndi cholinga choti akathandize anthu akwawo.

Pa tsiku la Sabata Yesu analowa m’kachisi kukaphunzitsa. Anthu ambiri anadabwa ndi mmene ankaphunzitsira ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru ndi ntchito zamphamvu zoterezi anazitenga kuti? Kodi si mwana wa mmisiri wamatabwa uyu? Kodi mayi ake si Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? Alongo ake onse sitili nawo konkuno? Nanga iyeyu zinthu zonsezi anazitenga kuti?”—Mateyu 13:54-56.

Anthuwo ankaona Yesu ngati munthu wamba, moti ankaganiza kuti: ‘Tamuona akukula uyu ndiye angakhale bwanji Mesiya?’ Choncho ngakhale kuti panali umboni wokwanira wosonyeza kuti Yesu anali Mesiya komanso anamuona akuchita zinthu zamphamvu ndiponso zosonyeza kuti anali wanzeru kwambiri, anthuwo anamukana. Anachita zimenezi chifukwa ankamudziwa bwino ndipo ngakhale achibale ake anakhumudwa naye. Zimenezi zinachititsa Yesu kunena kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo kapena m’nyumba mwake, koma kwina.”—Mateyu 13:57.

Mosakayikira Yesu anadabwa ndi kupanda chikhulupiriro kwa anthuwa. Choncho sanachite zozizwitsa zilizonse kumeneko kupatulako ‘kungoika manja pa odwala owerengeka ndi kuwachiritsa.’—Maliko 6:5, 6.

  • Potchula Yesu kuti “Mwana wa Davide,” kodi anthu osaona aja anasonyeza kuti ankakhulupirira chiyani?

  • Kodi Afarisi ananenanso chiyani ataona kuti Yesu akuchita zozizwitsa?

  • Kodi Yesu analandiridwa bwanji ku Nazareti, ndipo n’chifukwa chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena