Kodi Nchiyani Chikuletsani Kubatizidwa?
“Tawonani! Madzi; chindiletsa ine nchiyani ndisabatizidwe?”—MACHITIDWE 8:36.
1. Nchiyani chimene chinali kuchitika pa njira pakati pa Yerusalemu ndi Gaza?
MNGELO wa Yehova anali atalankhula, ndipo chinachake chofunikira kwambiri chinkachitika pa njira ya m’chipululu pakati pa Yerusalemu ndi Gaza. Yemwe analikhale pa gareta yomayenda anali munthu wa ku Aitiopiya akumaŵerenga Malemba. Mwamsanga munthu wina ankathamanga cha kumbali kwa garetalo. “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” iye anafunsa tero. “Ndithudi,” anayankha tero munthu wa ku Aitiopiyayo, “ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?” Chitsogozo chimenecho chinaperekedwa ndi wolengeza Filipo, yemwe anatumizidwa ndi mngelo. Mwamsanga atakwera pa garetalo, Filipo anayamba ndi ulosi wolembedwa ndi Yesaya ndi kulengeza “mbiri yabwino yonena za Yesu.”
2, 3. (a) Ndimotani mmene munthu wa ku Aitiopiya anayankhira ku mbiri yabwino? (b) Ndi mafunso otani amene chochitikachi chikudzutsa?
2 Pa malo amodzi m’mbali mwa msewuwo, munthu wa ku Aitiopiyayo anafuula kuti: “Tawonani! Madzi; chindiletsa ine nchiyani ndisabatizidwe?” Pa chimenecho, iye analamulira garetalo kuima. Amuna aŵiriwo analowa m’madzi ndipo Filipo anambatiza iye. Kenaka mzimu wa Yehova unatsogoza wolengezayo kwinakwake, ndipo munthu wa ku Aitiopiyayo anapita m’njira yake akumasangalala.—Machitidwe 8:26-39.
3 Ngati inu mukuyanjana ndi Mboni za Yehova koma simunabatizidwe, zochitika zimenezi zingakufulumizeni inu kufunsa kuti: Nchifukwa ninji munthu wa ku Aitiopiya anabatizidwa mwamsanga chotero? Ndimotani mmene ubatizo uyenera kuchitidwira? Kodi iwo uli chizindikiro cha chiyani? Ndipo kodi chindiletsa ine nchiyani kuti ndisabatizidwe?
Sanabatizidwe Mofulumira Kwambiri
4. Ndani yemwe anali munthu wa ku Aitiopiya ameneyu?
4 Popeza kuti munthu wa ku Aitiopiyayo “anapita ku Yerusalemu kukalambira,” iye anali wotembenuziridwa ku Chiyuda wodulidwa. Iye anali “mdindo” koma osati mu lingaliro la kuthupi, chifukwa chakuti amuna ovulazika ziwalo zogonanira anapatulidwa ku mpingo wa Chiisrayeli. (Deuteronomo 23:1) M’nkhani yake, “mdindo” anatanthauza nduna, popeza kuti iye anali ‘wamphamvu wa Kandake Mfumu Yaikazi ya anthu aku Aitiopiya ndi wosunga chuma chake chonse.’—Machitidwe 8:27.
5. Nchifukwa ninji mdindo wa ku Aitiopiya akanabatizidwira mofulumira chotero?
5 Munthu wa ku Aitiopiyayo anali munthu wa amitundu. Popeza kuti anali atatembenuzidwira ku chipembedzo cha Chiyuda, ngakhale kuli tero, iye akanabatizidwa monga wophunzira wa Kristu uthenga wa Ufumu usanapite kwa Akunja osadulidwa onga ngati Korneliyo mu 36 C.E. Monga munthu wotembenuzidwira ku Chiyuda, munthu wa ku Aitiopiyayo anadziŵa ponena za Mulungu ndi Mawu Ake, ngakhale kuti anafunikira thandizo lauzimu. Chotero Filipo anatsogozedwa kukalalikira kwa munthu ameneyu ndipo akanakhoza kumbatiza iye mbiri yabwino isanapite kwa Akunja.
Ubatizo Wachikristu Woyambirira
6. Ndimotani mmene munthu wa ku Aitiopiyayu anabatizidwira, ndipo nchifukwa ninji mwayankha tero?
6 Kodi ndimotani mmene munthu wa ku Aitiopiyayo anabatizidwira? Liwu lakuti “kubatiza” limachokera ku liwu la Chigriki lakuti ba·ptiʹzo, kutanthauza “kumiza, kuviika.” Mtundu wa liwu lofananalo wagwiritsiridwa ntchito kaamba ka “kumiza” pa 2 Mafumu 5:14 mu Septuagint ya Chigriki. Ndipo chiri chodziŵika bwino kuti munthu wa ku Aitiopiyayo anafunsira ubatizo pamene iye ndi Filipo anadza ku “madzi.” Kaamba ka ubatizo, iwo “anatsikira m’madzi,” pambuyo pake ndi “kutuluka” mmenemo. (Machitidwe 8:36-39) Chotero, mdindo wa ku Aitiopiyayo anabatizidwa mwa kumizidwa m’madzi.
7. Ndi chowonerako chotani chimene chinalipo kaamba ka ubatizo mwa kumizidwa m’madzi?
7 Yesu iyemwini anabatizidwa mwa njira ya kumizidwa m’madzi. Chotero, pambuyo pa ubatizo wake mu Mtsinje wa Yordano, kwanenedwa kuti iye “anatuluka m’madzi.” (Mateyu 3:13, 16) M’chenicheni, monga malo oyenerera kuchitirapo ubatizo, Yohane Mbatizi anasankha malo mu Chigwa cha Yordano pafupi ndi Salemu. Chifukwa ninji? “Chifukwa panali madzi ambiri pamenepo.” (Yohane 3:23) Chotero Malemba amavomereza ubatizo kuchitidwira m’madzi.
8. Ponena za ubatizo, nchiyani chomwe tingamalize kuchokera ku kachitidwe ka Afarisi ndi Ayuda ena?
8 Tingatenge kumaliza kwabwino ponena za ubatizo ngati tilingalira miyambo ya Afarisi ndi Ayuda ena. Mlembi wa Uthenga Wabwino Marko ananena kuti: “Pakuchoka kumsika, iwo sakudya kusiyako kokha atadziyeretsa iwoeni mwa kuwaza madzi [Chigriki, ran·tiʹzo]; ndipo pali miyambo ina yambiri imene anailandira kuisunga, ndiyo kubatiza [ba·pti·smousʹ] kwa zikho ndi miphika ndi zotengera zamkuwa.” (Marko 7:3, 4, NW) Amuna amenewa anadziyeretsa mwa kudziwaza madzi iwo eni asanadye pamene anabwera kuchokera kumsika. Koma anabatiza, kapena kumiza m’madzi, ziwiya zosiyanasiyana zomwe anagwiritsira ntchito pakudya.
9. Nchiyani chomwe Tertullian ananena ponena za ubatizo?
9 Ngakhale pambuyo pa kulowerera kwa mpatuko, bambo wa tchalitchi Tertullian (c. 160-230 C.E.) ananena ponena za ubatizo kuti: “Palibe kwenikweni chirichonse chimene chimapangitsa maganizo a anthu kukhala olimba kwambiri kuposa kupepuka kwa ntchito zaumulungu zomwe ziri zowonekera m’kachitidweko, zitayerekezedwa ndi kulemekezeka kumene kwalonjezedwa mmenemo m’chotulukapo; kotero kuti kuchokera ku chenichenicho, kuti ndi kupeputsa kokulira koteroko, popanda zochitika zamwambo, popanda kukonzekera kulikonse kolingaliridwa kukhala kwatsopano, potsirizira pake, popanda zotaika, munthu amamizidwa m’madzi, ndipo pakati pa kukambidwa kwa mawu ena ochepa, amawazidwa madzi, ndipo kenaka amatulukanso, osati woyera kwambiri (kapena mpang’ono ponse), kufikira umuyaya wolingaliridwa umawonedwa kukhala wozizwitsa koposa.” Dziŵani kuti Tertullian ananena kuti, “munthu amizidwa m’madzi . . . ndipo kenaka kutulukanso.”
10. Nchiyani chimene ophunzira amanena ponena za mtundu wa ubatizo Wachikristu woyambiria?
10 Ophunzira amasonyezanso kuti Akristu poyambirirapo anabatiza anthu mwa kuwamiza kotheratu m’madzi. Encyclopedia yodziŵika ya chiFrench ikunena kuti: “Akristu oyambirira analandira ubatizo mwa kumizidwa kulikonse kumene madzi anapezedwa.” Ndipo The Catholic Encyclopedia ikulongosola kuti: “Mkhalidwe wakale kwambiri wogwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri mosakaikira unali kumiza.”—Volyumu II, tsamba 261 (chofalitsidwa cha mu 1907).
Kuphunzitsa ndi Kubatiza
11. Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yotani?
11 Munthu asanabatizidwe, ayenera kupeza ndi kugwirira ntchito pa chidziŵitso cholongosoka. Ichi chinamveketsedwa bwino pamene Kristu anauza atsatiri ake kuti: “Chifukwa chake mukani phunzitsani anthu amitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo, onani! Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mateyu 28:19, 20.
12. Kodi nchiyani chomwe chimatanthauza kubatizidwa “m’dzina la Atate”?
12 Kubatizidwa “m’dzina la Atate” kumatanthauza kuti munthu wopita ku ubatizo amazindikira malo a Mulungu ndi ulamuliro. Yehova amadziŵidwa monga “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,” Mlengi ndi Mfumu ya Chilengedwe Chonse. (Salmo 36:9; 83:18; 2 Mafumu 19:15) Munthu woteroyo amalandiranso Yehova monga Woŵeruza wake, Mpatsi wa Malamulo, ndi Mfumu.—Yesaya 33:22; Salmo 119:102; Chibvumbulutso 15:3, 4.
13. Kubatizidwa ‘m’dzina la Mwana’ kumatanthauza chiyani?
13 Kubatizidwa ‘m’dzina la Mwana’ kumatanthauza kuvomereza malo a Kristu ndi ulamuliro ndi kumuzindikira iye monga mmodzi kupyolera mwa amene Mulungu wapereka “dipo lolingana nalo.” (1 Timoteo 2:5, 6, NW) Pambuyo pa imfa ya Yesu monga wosunga umphumphu, “Mulungu anamkweza iye ku malo apamwamba,” ndipo awo okhumba ubatizo ayenera kuvomereza Kristu monga “Ambuye ku ulemerero wa Mulungu Atate.” (Afilipi 2:9-11) Iwo ayeneranso kulandira Yesu monga “Mboni Yokhulupirika” ya Yehova ndipo monga “Mfumu ya mafumu.”—Chibvumbulutso 1:5; 19:16.
14. Ubatizo ‘m’dzina la mzimu woyera’ umafunikira chiyani?
14 Munthu afunikiranso kubatizidwa ‘m’dzina la mzimu woyera.’ Afunikira kuzindikira kuti mzimu woyera suli munthu koma uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, yogwiritsiridwa ntchito m’chilengedwe, kuwuzira olemba Baibulo, ndi zina zotero. (Genesis 1:2; 2 Samueli 23:1, 2; 2 Petro 1:21) Mzimu wa Yehova uyenera kuzindikiridwa kukhala wofunika koposa ngati titi tizindikire “zinthu zakuya za Mulungu” ndi kusonyeza chipatso chaumulungu cha “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (1 Akorinto 2:10; Agalatiya 5:22, 23) Chiyeneranso kuvomerezedwa kuti mzimu wa Mulungu umafunikira kuti tipitirizebe ntchito yolalikira Ufumu.—Yoweli 2:28, 29.
Chimene Ubatizo Umaimira
15. Nchifukwa ninji kuli kwakuti ubatizo Wachikristu sumasambitsa machimo?
15 Chinali ndi kuchirikizidwa kwa mzimu woyera kuti Yohane Mbatizi anamiza anthu. (Machitidwe 13:24) Iye anawabatiza iwo, osati kusamba machimo awo, koma m’chizindikiro cha kulapa kwawo. (Machitidwe 19:4) Yohane anabatizanso Yesu, yemwe “sanachimwe.” (1 Petro 2:22) Ndipo Hananiya analimbikitsa Saulo wa ku Tariso: “Tawuka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako nuitane pa dzina lake [Yesu].” (Machitidwe 22:12-16) Chotero, kumizidwa m’madzi kwa Chikristu sikumasambitsa machimo. Si ubatizo koma kutsanulidwa kwa mwazi wa Yesu ndi “kuitanira pa dzina lake” ndi kumene kumapangitsa chikhululukiro kukhala chothekera.—Ahebri 9:22; 1 Yohane 1:7.
16. (a) Popeza kuti ubatizo sumasambitsa machimo, kodi iwo umaimira chiyani? (b) Mophiphiritsira, nchiyani chimene chimachitika pamene munthu wabatizidwa?
16 Ngakhale kuti ubatizo Wachikristu sumasambitsa machimo, iwo uli chizindikiro chosonyeza kuti munthu womizidwa m’madziyo wapanga kudzipereka kwapadera kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu. (Yerekezani ndi Mateyu 16:24.) Kudzipereka kumatanthauza “kulengeza, kutsimikizira, kudziikako.” Kudzipereka kwa Mulungu kumalozera ku kachitidwe mu kamene munthu waikidwa pambali kotheratu ndi chipangano cha kuchita chifuniro cha Mulungu kupyolera mwa Kristu. Mophiphiritsira, pamene wopita ku ubatizo “wamizidwa” kwa kanthaŵi m’madzi ndipo kenaka kutulutsidwa mu iwo, iye amafa ku njira yake yakale ndipo amadzutsidwa ku njira yatsopano ya moyo, kuchita chifuno cha Yehova kotheratu.—Yerekezani ndi Aroma 6:4-6.
17. Nchifukwa ninji kubatiza makanda kuli kosalondola?
17 Mowonekera bwino, ubatizo uli sitepi losamalitsa. Kubatiza mwana kuli kolakwa chifukwa chakuti khanda silingamvetsetse, kupanga chosankha, ndi kukhala wophunzira. (Mateyu 28:19, 20) Awo obatizidwa mkati mwa utumiki wa Filipo mu Samariya anali “amuna ndi akazi,” osati makanda. (Machitidwe 8:4-8, 12) Ubatizo uli kaamba ka awo achikulire mokwanira kukhoza kuphunzira, kukhulupirira, ndi kusonyeza chikhulupiriro. (Yohane 17:3; Machitidwe 5:14; 18:8; Ahebri 11:6) M’chiyang’aniro cha ichi, katswiri wa mbiri yakale Augustus Neander analemba kuti: “Chikhulupiriro ndi ubatizo zinali nthaŵi zonse zogwirizana china ndi chinzake; ndipo chotero chiri pa mlingo wokulira koposa wothekera . . . kuti kachitidwe ka kubatiza makanda kanali kosadziŵika [m’zana loyamba C.E.]. . . . Kuti iko kanazindikiridwa choyamba monga mwambo wa utumwi mkati mwa zana lachitatu, chiri umboni wolimbana kuposa kukhala wochirikiza kulandiridwa kwa chiyambi chake cha utumwi.”—History of the Planting and Training of the Christian Church by the Apostles (New York, 1864), tsamba 162.
18. (a) Mwa Malemba, nchiyani chimene chimafunikira kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova? (b) Ndi umboni wotani wa chikhulupiriro womwe ungasonyeze kuti munthu angabatizidwe? (c) Ndimotani mmene chikhulupiriro m’dipo chimagogomezedwera kaamba ka anthu opita ku ubatizo?
18 Malemba mobwerezabwereza amatchula ubatizo wa okhulupirira. (Machitidwe 4:4; 5:14; 8:13; 16:27-34; 18:8; 19:1-7) Kuti akhale mmodzi wa Mboni za Yehova, chotero, munthu afunikira kukhala wokhulupirira—mmodzi yemwe amasonyeza chikhulupiriro ndi kubatizidwa. Ngakhale asanabatizidwe, chikhulupiriro choterocho chimadziwonetsera icho chokha mu mkhalidwe waumulungu, kukhulupirira mwa Yehova, kugawanamo mu ntchito yolalikira Ufumu, ndi kulandira kwa nsembe ya dipo ya Yesu. Chikhulupiriro m’dipo chimagogomezeredwa kaamba ka opita ku ubatizo, popeza kuti funso loyamba la aŵiri omwe mlankhuli amawafunsa liri lakuti: “Pa maziko a nsembe ya Yesu Kristu, kodi mwalapa machimo anu ndi kudzipereka inu eni kwa Yehova kuchita chifuniro chake?” Kokha ngati munthuyo ayankha m’kuvomereza ndiponso kumvetsetsa kuti kudzipereka kwake ndi ubatizo kumamuzindikiritsa iye monga mmodzi wa Mboni za Yehova m’chigwirizano ndi gulu lotsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu ndi pamene iye molandirika angalowe mu kumizidwa m’madzi.
Kudzipereka m’Pemphero
19. Nchifukwa ninji kupanga kudzipereka kwa Yehova m’pemphero?
19 Awo olowa ubatizo afunikira kukhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Kristu. Koma kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimanena kuti kudzipereka kwa Mulungu kuyenera kupangidwa m’pemphero? Chifukwa chakuti chiri choyenera kulongosola kwa Yehova m’pemphero chigamulo chathu cha kumpatsa iye kudzipereka kotheratu kumene iye amayenerera. (Deuteronomo 5:8, 9; 1 Mbiri 29:10-13) Chinali mwachiwonekere m’pemphero kuti Yesu anapangitsa chikhumbo chake kudziŵika cha kupereka utumiki wopatulika kotheratu kwa Atate wake wa kumwamba. (Ahebri 10:7-9) N’kulekeranji, popeza Yesu “anali kupemphera” ngakhale pamene analikubatizidwa! (Luka 3:21, 22) Chotero chiri chachiwonekera kuti kudzipereka kwa Mulungu kuyenera kupangidwa m’pemphero.
20. Nchifukwa ninji chiri chachidziŵikire kuti Akristu oyambirira analimbikitsa ophunzira atsopano kupanga kudzipereka kwa Mulungu m’pemphero?
20 Akristu oyambirira mwachiwonekere analimbikitsa ophunzira achatsopano kupanga kudzipereka m’pemphero, popeza kuti ngakhale Tertullian pambuyo pake ananena kuti: “Awo omwe ali pafupi kulowa ubatizo afunikira kupemphera ndi mapemphero obwerezabwereza, kusala kudya, ndi kugwada pa mawondo awo.” Kumayambiriro, Justin Martyr (c. 100-165 C.E.) analemba kuti: “Ndidzasimbanso mkhalidwe mu umene tinadzipereka ife eni kwa Mulungu pamene tinapangidwa atsopano kupyolera mwa Kristu . . . Pamene ochulukira akokedwa ndi kukhulupirira kuti zimene timaphunzitsa ndi kunena ziri zowona, ndi kukhoza kukhala ndi moyo mogwirizana ndi izo, amalangizidwa kupemphera ndi kufikira Mulungu ndi kusala kudya, kaamba ka kukhululukidwa kwa machimo awo omwe ali a kumbuyo, timapemphera ndi kusala kudya ndi iwo.”
21. Nchiyani chimene chiri chothekera, ngakhale ngati kupanga kudzipereka m’pemphero sikunagogomezeredwe pamene tinabatizidwa zaka zingapo zapitazo?
21 Ngati kupanga kudzipereka m’pemphero sikunagogomezeredwe pamene tinabatizidwa zaka zingapo zapitazo, chimenecho sichimachepetsa kwenikweni ubatizo wanu. Ngakhale m’masiku amenewo, mosakaikira ambiri anali monga munthu mmodzi yemwe amakumbukira mowonekera bwino kugwada ndi kupanga kudzipereka kwake kwa Yehova m’pemphero lofunitsitsa pamene anali kokha wachichepere zoposa zaka 40 zapitazo. Ndipo pa nthaŵi imeneyo, ngakhale ngati munthu sanapange kudzipereka m’pemphero lochitidwa poyambiriralo, iye anachipanga icho kukhala nkhani ya pemphero monga wopita ku ubatizo ndipo ena anapempherera pamodzi pamene nkhani ya ubatizo inaperekedwa pa tsiku la kumizidwa kwake.
Chifukwa Chimene Ena Amasinkhasinkhira
22. Nchifukwa ninji ena amasinkhasinkha kubatizidwa?
22 Popeza kuti kukhala mboni yodzipereka ya Yehova kuli mwaŵi wodalitsika chotero, nchifukwa ninji ena amasinkhasinkha kubatizidwa? Kusoweka kwa chikondi chowona kuli chifukwa chimodzi chimene ena samamverera Mawu a Mulungu, kutsatira chitsogozo cha Yesu, ndi kubatizidwa. (1 Yohane 5:3) Ndithudi, anthu osabatizidwa kaŵirikaŵiri samanena kuti sadzatsatira chitsanzo cha Yesu kapena kumvera Mulungu. M’malomwake, iwo amakhala odzilowetsa kwambiri m’machitachita a kudziko kotero kuti amakhala ndi nthaŵi yochepera kaamba ka zotsatira zauzimu. Ngati iri lingakhale vuto lanu, kodi sichikakhala chanzeru kusintha zokonda zanu, zikondwerero, ndi zotsatira? Awo omwe mowonadi amakonda Mulungu sangakondenso dziko lino. (1 Yohane 2:15-17) Ndipo musadzilole inu eni kugwidwa ndi lingaliro lonyenga la chisungiko kupyolera mu “chinyengo cha chuma.” (Mateyu 13:22) Chisungiko chowona chimapezedwa kokha mu unansi wodzipereka ndi Yehova Mulungu.—Salmo 4:8.
23. Nchifukwa ninji ena amapewa kudzipereka kwa Yehova ndi kuzindikiritsa iko mwa kumizidwa m’madzi?
23 Ena amadzinenera kukhala okonda Mulungu koma amasinkhasinkha kupanga kudzipereka chifukwa chakuti amadzimva kuti iwo mwakutero amapewa thayo ndipo sadzakhala a mlandu. Iwo angakonde kukhala m’Paradaiso, koma pakali pano akuchita zochepera kapena osati chirichonse ponena za icho. (Miyambo 13:4) Anthu oterowo sangapewe kuŵerengera chifukwa chakuti thayo linadza pa iwo pamene anamva mawu a Yehova. (Ezekieli 33:7-9) Ngati anati apange kudzipereka, iwo akasonyeza kuti amvetsetsa chifuniro cha Mulungu ndipo ali ofunitsitsa kuchichita icho. M’malo moika katundu wolemetsa pa iwo, chimvero choterocho chikaitanira dalitso la Yehova ndipo chikatulukamo mu chisangalalo chifukwa chakuti akakhalira ndi moyo ku kudzinenera kwawo kwakuti amamukonda iye.
24. Ndi kaamba ka chifukwa chotani chimene ena amasinkhasinkhirabe kubatizidwa?
24 Kudzimva kwakuti sakudziŵa zokwanira kulongosola Malemba kumapangitsabe ena kupewa ubatizo. Koma mdindo wa ku Aitiopiya anali wokonzekera kusonyeza kudzipereka kwake kwa Mulungu pambuyo pa kukambitsirana ndi Filipo mkati mwa ulendo wa pa gareta. Motsimikizirika, munthu wa ku Aitiopiyayo sakanakhoza kuyankha mafunso onse a awo amene analankhulako chowonadi. Koma mtima wake unasefukira ndi chiyamikiro kaamba ka zimene anamva, ndipo sanasinkhesinkhe m’mantha. “Mulibe mantha mu chikondi, koma chikondi chitulutsa mantha kunja.” (1 Yohane 4:18) Osati mutu wodzaza ndi mayankho koma mtima wodzaza ndi chikondi ndi umene umasonkhezera munthu kupanga kudzipereka kwa Mulungu ndi kubatizidwa.—Luka 10:25-28.
25. Nchiyani chimene Yehova Mulungu amayembekezera kwa awo odzinenera kumkonda iye?
25 Ngati simunabatizidwebe, dzifunseni inu eni: Nchiyani chimene Mulungu amayembekezera kwa awo omwe amanena kuti amamkonda? Iye amafuna kudzipereka kotheratu ndipo akufunafuna kaamba ka awo omwe angamulambire iye “mu mzimu ndi m’chowonadi.” (Yohane 4:23, 24; Eksodo 20:4, 5; Luka 4:8) Mdindo wa ku Aitiopiyayo anapereka mtundu umenewo wa kulambira, ndipo sanachedwe pamene anapatsidwa mwaŵi wa kulowa ubatizo. Kodi simufunikira kupanga kudzipereka kwa Yehova kukhala nkhani ya pemphero lofunitsitsa tsopano lino ndi kudzifunsa inu eni kuti: “Chindiletsa ine kubatizidwa nchiyani?”
Mafunso kaamba ka Kubwereramo
◻ Nchifukwa ninji mdindo wa ku Aitiopiya anabatizidwa mofulumira chotero?
◻ Ndi njira yotani ya kubatiza yomwe inali pakati pa Akristu oyambirira?
◻ Kubatizidwa ‘m’dzina la Atate, la Mwana, ndi la mzimu woyera’ kumatanthauzanji?
◻ Nchiyani chimene ubatizo Wachikristu umaimira?
◻ Nchifukwa ninji kupanga kudzipereka kwa Yehova m’pemphero?
◻ Ndi kaamba ka zifukwa zotani zimene ena amasinkhasinkhira kudzipereka ndi ubatizo?