Kodi Mukuthamanga Motani m’Makani a Moyo?
“Kodi simudzi ŵa kuti iwo akuchita makani a liŵiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.”—1 AKORINTO 9:24.
1. Kodi Baibulo limayerekezera njira yathu Yachikristu ndi chiyani?
BAIBULO limayerekezera kufunafuna kwathu moyo wosatha ndi makani a liŵiro. Chakumapeto kwa moyo wake, mtumwi Paulo ananena za iye mwini kuti: “Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhupiriro.” Iye anafulumiza Akristu anzake kuchita chimodzimodzi pamene anati: “Titaye cholemetsa chirichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.”—2 Timoteo 4:7; Ahebri 12:1.
2. Kodi ndichiyambi cholimbikitsa chotani chimene timawona m’makani a moyo?
2 Kuyerekezerako nkolondola chifukwa chakuti makani a liŵiro amakhala ndi poyambira, malo enieni othamanga, ndi potsirizira, kapena chonulirapo. Chomwechonso mchitidwe wauzimu wa kupita kwathu patsogolo kuti tipeze moyo. Monga momwe tawonera, chaka chirichonse zikwi mazana ambiri za anthu zimayamba bwino lomwe m’makani a liŵiro a moyo. Mwachitsanzo, m’zaka zisanu zapitazo, anthu 1,336,429 anayamba mwalamulo makaniwo mwa kudzipatulira ndi ubatizo wa mmadzi. Kuyamba kwamphamvu kotero nkolimbikitsa koposa. Komabe, chinthu chofunika ndicho, kukhalabe m’makaniwo mpaka chonulirapo chitafikiridwa. Kodi mukuchita zimenezo?
Makani a Moyo
3, 4. (a) Kodi Paulo anasonyeza motani kufunika kwa kukhalabe oyendera limodzi m’makani? (b) Kodi ena alephera motani kulabadira uphungu wa Paulo?
3 Kugogomezera kufunika kwa kukhalabe m’makaniwo, Paulo analangiza kuti: “Kodi simudziŵa kuti iwo akuchita makani a liŵiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.”—1 Akorinto 9:24.
4 Zowonadi, m’maseŵera akale, mmodzi yekha ankalandira mfupo. Komabe, m’makani a moyo, aliyense angayenerere mphotho. Kuli kofunikadi kukhalabe m’njirayo kufikira mapeto! Mwachimwemwe, ambiri athamanga mokhulupirika m’njirayo kufikira mapeto a moyo wawo, monga momwe anachitira mtumwi Paulo. Ndipo mamiliyoni ambiri akupitirizabe kuthamanga. Komabe, ena, alephera kuchirimika kapena kupanga kupita patsogolo kumka kumapeto. Mmalo mwake, analola zinthu zina kuwalepheretsa kotero kuti mwina anagwa nachoka m’makaniwo kapena kusayeneretsedwa mwanjira ina. (Agalatiya 5:7) Zimenezi ziyenera kupatsa tonsefe chifukwa chopendera mmene tikuthamangira m’makani a moyo.
5. Kodi Paulo anali kuyerekezera makani a moyo ndi maseŵera a mpikisano weniweni wa othamanga? Fotokozani.
5 Funso lingafunsidwe: Kodi Paulo anali kulingaliranji pamene anati “mmodzi alandira mfupo”? Monga momwe kwawonedwera poyambapo, iye sanatanthuze kuti pakati pa onse amene anayamba makani a moyo, mmodzi yekha adzalandira mphotho ya moyo wosatha. Mwachiwonekere zimenezo sizikanakhala choncho, pakuti mobwerezabwereza, iye anamveketsa bwino lomwe kuti chiri chifuniro cha Mulungu kuti anthu amtundu uliwonse ayenera kupulumutsidwa. (Aroma 5:18; 1 Timoteo 2:3, 4; 4:10; Tito 2:11) Ayi, iye sanali kunena kuti makani a moyo ndiwo mpikisano mwa umene wotenga nawo mbali aliyense amayesayesa kugonjetsa ena onse. Akorinto anadziŵanso bwino kwambiri kuti mtundu wotero wa mzimu wa mpikisano unali pakati pa otenga mbali mumpikisano pa Maseŵera awo a Isthmus, wonenedwa kukhala wotchuka kwambiri panthaŵiyo koposa Maseŵera a Olympic. Pamenepo, kodi nchiyani chimene Paulo anali kulingalira?
6. Kodi mawu apatsogolo ndi pambuyo m’nkhaniyo amavumbulanji ponena za makambitsirano a Paulo a wothamanga ndi makani a liŵiro?
6 Potchula fanizo la wothamanga, kwakukulukulu Paulo anali kunena za ziyembekezo za iye mwini za chipulumutso. M’mavesi oyambirira, anafotokoza mmene anagwirira ntchito zolimba ndi kudzigwiritsira ntchito mwamphamvu m’njira zambiri. (1 Akorinto 9:19-22) Ndiyeno, m’vesi 23, iye anati: “Koma ndichita zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.” Iye anazindikira kuti chipulumutso chake sichinali chotsimikiziridwa kokha chifukwa chakuti anali wosankhidwa kukhala mtumwi kapena chifukwa chakuti anali atathera zaka zambiri akumalalikira kwa ena. Kuti akakhale ndi phande m’madalitso a mbiri yabwino, ayenera kupitirizabe kuchita zonse zomwe angathe kaamba ka mbiri yabwino. Ayenera kuthamanga ali ndi cholinga chonse cha kupambana, akumayesetsa mwamphamvu monga ngati kuti anali kuthamanga m’makani enieni othamanga liŵiro m’Maseŵera a Isthmus, kumene ‘mmodzi yekha analandira mfupo.’—1 Akorinto 9:24a.
7. Kodi nchiyani chimene chimafunika ‘pothamanga kuti mukalandire’?
7 Pali zambiri zimene tingaphunzire m’zimenezi. Ngakhale kuti aliyense amene amagwirizana nawo m’makaniwo amafuna kupambana, ali awo okha otsimikizira kotheratu kupambana amene ali ndi chiyembekezo chirichonse cha kutero. Chifukwa chake, sitiyenera kulingalira kukhala okhutira kokha chifukwa chakuti tagwirizana nawo m’makaniwo. Sitiyenera kulingalira kuti zinthu zonse zidzakhala bwino chifukwa chakuti ‘tiri m’chowonadi.’ Tingaitanidwe ndi dzina lakuti Mkristu, koma kodi tiri ndi umboni wotitsimikiziritsa kuti ndife Akristu? Mwachitsanzo, kodi timachita zinthu zimene timadziŵa kuti Mkristu ayenera kuchita—kufika pamisonkhano Yachikristu, kukhala ndi phande muuminisitala wakumunda, ndi zina zotero? Ngati ziri choncho, zimenezo nzoyamikirika, ndipo tiyenera kuyesayesa kupitirizabe kuchita khama m’zizoloŵezi zabwino kwambiri zotero. Komabe, kodi nkotheka, kuti tingapindule kwambiri ndi zimene timachita? Mwachitsanzo, kodi ife nthaŵi zonse timakhala okonzekera kukhala ndi phande pamisonkhano? Kodi timayesayesa kugwiritsira ntchito zimene tikuphunzira m’moyo wathu? Kodi timapereka chisamaliro pakuwongolera maluso athu kotero kuti tingathe kupereka umboni mosamalitsa mosasamala kanthu za zopinga zimene timapeza mmunda? Kodi tiri ofunitsitsa kuyang’anizana ndi chitokoso cha kubwereranso kwa okondwerera ndi kuchititsa maphunziro Abaibulo apanyumba? “Thamangani, kuti mukalandire,” anafulumiza motero Paulo.—1 Akorinto 9:24b.
Sonyezani Kudziletsa m’Zinthu Zonse
8. Kodi nchiyani chimene chingakhale chitasonkhezera Paulo kufulumiza Akristu anzake ‘kusonyeza kudziletsa m’zonse’?
8 M’nthaŵi ya moyo wake, Paulo anawona ambiri amene anali atayamba kufooka, kutengeka, kapena amene analekeratu makani a moyo. (1 Timoteo 1:19, 20; Ahebri 2:1) Ndicho chifukwa chake anakumbutsa Akristu anzake mobwerezabwereza kuti iwo ali mumpikisano wamphamvu ndi wopitirizabe. (Aefeso 6:12; 1 Timoteo 6:12) Anawonjezera pang’ono chitsanzo cha munthu wothamanga ndipo anati: “Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse.” (1 Akorinto 9:25a) M’kunena zimenezi, Paulo anali kusonyeza kanthu kena kamene Akristu a ku Akorinto anali atazoloŵerana nako bwino lomwe, ndiko kuti, kulimbitsa thupi kwamphamvu kochitidwa ndi ochita mpikisano ku Maseŵera a Isthmus.
9, 10. (a) Kodi bukhu lina limafotokoza motani ochita mpikisano m’Maseŵera a ku Isthmus? (b) Kodi nchiyani chimene chiri choyenerera mwapadera kudziŵa ponena za mafotokozedwewo?
9 Nawa mafotokozedwe omvekera bwino a wochita mpikisano poyeseza:
“Amadzigonjetsera kumalamulo ndi ziletso mokhutira ndi mosang’ung’udza pakuyeseza kwake kwa miyezi khumi imene, ngati sachita motero sayenera kuloŵa mumpikisano. . . . Ngwonyada ndi kuvutika kwake kochepako, kutopa, ndi kudzimana, ndipo amauyesa mwaŵi kusala kudya chirichonse mwankhokera chimene chingachepetse ngakhale pamlingo wochepetsetsa mwaŵi wake wa kupeza chipambano. Amawona anthu ena akugonjera kukukhumba kudya, akumapuma pamene iye akuwefumuka, akumasangalala ndi kusamba, ndi moyo wabwino; koma iye samasirira konse, chifukwa chakuti mtima wake uli pamphotho, ndipo kudzizoloŵezetsa kwambiri nkofunika kotheratu. Amadziŵa kuti mwaŵi wake umatha ngati panthaŵi iriyonse kapena pamphindi iriyonse asiya kudzilanga kwamphamvuko.”—The Expositor’s Bible, Volyumu V, tsamba 674.
10 Chokondweretsa mwapadera ndicho lingaliro limene munthu wophunzitsidwayo amakhala nalo ‘lakuuyesa mwaŵi’ kutsatira njira ya kudzilanga yodzimana yotero. Kwenikweni, iye “samasirira” ufulu ndi kupeza bwino zimene amawona ena akusangalala nazo. Kodi tingaphunzire kanthu kena m’zimenezi? Inde, ndithu.
11. Kodi ndilingaliro losayenera lotani limene tiyenera kupeŵa pamene tiri m’makani a moyo?
11 Kumbukirani mawu a Yesu akuti “chipata chiri chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Pamene mukuyesayesa kuyenda pa ‘njira yopapatiza,’ kodi mumasirira ufulu ndi kupeza bwino zimene awo amene akuyenda pamsewu winawo akuwonekera kukhala nazo? Kodi mumalingalira kuti mukutayikiridwa zinthu zina zimene ena akuchita, zimene sizingawonekere kukhala zoipa mwa izo zokha? Kuli kosavuta kwa ife kulingalira mwa njira imeneyi ngati tilephera kukumbukira chifukwa chake tasankhira njira imeneyi. “Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda,” anatero Paulo.—1 Akorinto 9:25b.
12. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti ulemerero ndi thamo zimene anthu anafunafuna ziri zofanana ndi korona wovunda wofupidwa pa Maseŵera a Isthmus?
12 Wopambana pa Maseŵera a Isthmus analandira korona wa kanjedza wa ku Isthmus kapena zitsamba zina za mtundu umenewo, amene mwinamwake anafota m’masiku oŵerengeka kapena masabata. Zowonadi, othamangawo sanalimbanire korona wokhoza kuwonongekayo koma kaamba ka ulemerero, ulemu, ndi thamo zimene anadzetsa. Bukhu lina limati pamene wopambanayo anabwerera kwawo, analandiridwa monga ngwazi yogonjetsa. Kaŵirikaŵiri malinga a mizinda ankagwetsedwa kuti oguba pomlandira adzere, ndipo ankaumba mafano omlemekezera. Komabe, mosasamala kanthu za zonsezi, ulemerero wake unali wodzavunda. Lerolino, ndianthu oŵerengeka chabe amene amadziŵa za ngwazi zimenezo, ndipo kwenikweni ochuluka samasamala. Awo amene amalepa nthaŵi yawo, nyonga, thanzi, ndipo ngakhale chimwemwe chabanja kuti apeze ulamuliro, kutchuka, ndi chuma m’dziko, koma amene sali olemera kwa Mulungu, adzapeza kuti “korona” wawo wa kukondetsa zinthu zakuthupiyo, monga moyo wawo, ngwakanthaŵi chabe.—Mateyu 6:19, 20; Luka 12:16-21.
13. Kodi njira ya moyo wa munthu wokhala m’makani a moyo iri yosiyana motani ndi ya wothamanga?
13 Ochita mpikisano m’maseŵera othamanga angakhale ofunitsitsa kuvomereza zofunika zovuta pa kuzoloŵeza thupi, zonga zimene zafotokozedwa pamwambapa, komatu amatero kwa nthaŵi yaifupi chabe. Pamene maseŵerawo atha, amabwerera kumoyo wozoloŵereka. Iwo angapitirizebe kuzoloŵeza thupi panthaŵi ndi nthaŵi kuti asatayikiridwe ndi maluso awo, koma iwo samatsatiranso njira ya kudzimana kwambiri yofananayo, pafupifupi kufikira mpikisano wina wotsatira utayandikira. Sikuli motero ndi awo amene ali m’makani a moyo. Kwa iwo, kuyeseza ndi kudzimana kuyenera kukhala njira ya moyo.—1 Timoteo 6:6-8.
14, 15. Kodi nchifukwa ninji wotenga mbali m’makani a moyo ayenera kusonyeza kudziletsa mosalekeza?
14 “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga,” anatero Yesu Kristu kwa ophunzira osonkhana ndi ena, “adzikane [kapena, “iye ayenera kunena kuti, ‘Toto’ kwa iye mwini,” Charles B. Williams] nadzitengere mtengo wozunzirapo nanditsate mosalekeza.” (Marko 8:34, NW) Pamene tilandira chiitano chimenechi, tiyenera kukhala okonzekera kutero “mosalekeza,” osati chifukwa chakuti pali kanthu kena kapadera koyenerera m’kudzimana, koma chifukwa chakuti kusazindikira kwamphindi imodzi, kuphonyetsa kumodzi chiweruzo chabwino, kungawononge zonse zimene zakhala zikuchitidwa, ngakhale kuika pachiswe ubwino wathu wamuyaya. Kaŵirikaŵiri kupita patsogolo kwauzimu kumapangidwa pamlingo wapang’onopang’ono, koma kungafafanizidwe mofulumira chotani nanga ngati sitisamala mosalekeza!
15 Ndiponso, Paulo anafulumiza kuti tiyenera kugwiritsira ntchito kudziletsa mu “zonse,” ndiko kuti, tiyenera kutero mosalekeza m’mbali zonse za moyo. Zimenezi zikumvekera kukhala zanzeru chifukwa chakuti ngati wophunzitsidwa adzikhutiritsa mopambanitsa kapena akhala ndi moyo wosadzisungira, kodi nchiyani chimene chidzakhala phindu la kudzimvetsa ululu ndi kutopa zimene amapirira? Mofananamo m’makani athu a moyo, tiyenera kugwiritsira ntchito kudziletsa m’zinthu zonse. Munthu angadziletse m’zinthu zonga kuledzera ndi dama, koma phindu la zimenezi limazimiririka ngati ali wodzitukumula ndi wandewu. Kapena bwanji ngati ali woleza mtima ndi wokoma mtima kwa ena, koma nachita uchimo wobisika m’moyo wake wamtseri? Kuti kudziletsa kukhale kopindulitsa mokwanira, kuyenera kugwiritsiridwa ntchito mu “zonse.”—Yerekezerani ndi Yakobo 2:10, 11.
Thamangani ‘Osati Mosatsimikizira’
16. Kodi kuthamanga ‘osati mosatsimikizira’ kumatanthauzanji?
16 Powona zoyesayesa zamphamvu zofunikazo kuti munthu apambane m’makani a moyo, Paulo anapitirizabe kunena kuti: “Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, simonga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, simonga ngati kupanda mlengalenga.” (1 Akorinto 9:26) Liwulo “chosinkhasinkha” kwenikweni limatanthauza “popanda chifukwa chake” (Kingdom Interlinear), “mosawonedwa, mosazindikiridwa” (Lange’s Commentary). Chifukwa cha chimenecho, kuthamanga ‘osati mosatsimikizira’ kumatanthauza kuti kwa wowonerera aliyense ayenera kuwona bwino lomwe kumene wothamangayo akumka. The Anchor Bible limati “osati panjira yokhotakhota.” Ngati munawona midindo ya mapazi imene imakwera nitsika mokhotakhota kumka mmbali mwa gombe, ikumazungulira mobwerezabwereza, ndipo panthaŵi zina ibwerera kumbuyo, simungathe kuganiza konse kuti munthuyo anali kuthamanga kapena ayi, osanena kanthu zakuti amadziŵa nkomwe kumene amapita. Koma ngati inu munawona midindo ya mapazi imene ikupanga mzera wautali, woongoka, phazi lina likutsatira linzake ndipo onsewo ali ndi madanga ofanana, mukatsimikizira kuti mapaziwo ngamunthu amene akudziŵa bwino lomwe kumene akupita.
17. (a) Kodi Paulo anasonyeza motani kuti anali kuthamanga ‘osati mosatsimikizira’? (b) Kodi tingatsanzire Paulo motani pamfundoyi?
17 Moyo wa Paulo umasonyeza bwino kwambiri kuti iye anali kuthamanga ‘osati mosatsimikizira.’ Anali ndi umboni wokwanira wotsimikizira kuti anali minisitala Wachikristu ndi mtumwi. Anali ndi cholinga chimodzi chokha, ndipo anayesetsa mwamphamvu m’moyo wake wonse kuti achipeze. Sanapatutsidwe konse ndi kutchuka, ulamuliro, chuma, kapena zosangalatsa, ngakhale kuti mwinamwake akanapeza chirichonse cha zimenezi. (Machitidwe 20:24; 1 Akorinto 9:2; 2 Akorinto 3:2, 3; Afilipi 3:8, 13, 14) Pamene muyang’ana m’mbuyo panjira yanu yamoyo, kodi ndimtundu wanji wa njira imene mumawona? Mzera wowongoka wosonyeza njira yowoneka bwino kumene mukupita kapena wokhotakhota wosalunjika? Kodi pali umboni wakuti mukulimbana nawo m’makani a moyo? Kumbukirani, tiri m’makani ameneŵa, osati kokha kuti zitichoke, kunena kwake titero, koma kufikira kuchonulirapo.
18. (a) Kodi nchiyani chimene chikayerekezeredwa ndi “kupanda mlengalenga” kwa ife? (b) Kodi nchifukwa ninji imeneyo iri njira yaupandu kuitsatira?
18 Poyerekezera ndi chochitika china cha wothamanga, Paulo akupitiriza kuti: “Ndilimbana chotero, simonga ngati kupanda mlengalenga.” (1 Akorinto 9:26b) M’makani athu a moyo, tiri ndi adani ambiri, kuphatikizapo Satana, dziko, ndi kupanda ungwiro kwathu. Mofanana ndi woseŵera nkhonya wakale, tiyenera kukhala wokhoza kuwagonjetsa ndi nkhonya zolunjikitsidwa bwino lomwe. Mwachimwemwe, Yehova Mulungu amatiphunzitsa ndi kutithandiza m’kumenyanako. Amapereka malangizo m’Mawu ake, mabukhu ofotokoza Baibulo, ndi pamisonkhano Yachikristu. Komabe, ngati tiŵerenga Baibulo ndi mabukhuwo ndi kufika pamisonkhano koma osagwiritsira ntchito zimene timaphunzira, kodi sitikungowononga zoyesayesa zathu, “kupanda mlengalenga”? Kuchita motero kumatiika mumkhalidwe waupandu kwambiri. Timaganiza kuti tikumenya nkhonya ndipo motero kukhala ndi lingaliro lonyenga la chisungiko, komatu sitikugonjetsa adani athu. Ndicho chifukwa chake wophunzirayo Yakobo analangiza kuti: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.” Monga momwe “kupanda mlengalenga” sikudzagonjetsa adani athu, choteronso kukhala “akumva okha” sikudzatsimikira kuti tikuchita chifuniro cha Mulungu.—Yakobo 1:22; 1 Samueli 15:22; Mateyu 7:24, 25.
19. Kodi tingatsimikizire motani kuti ife eni tisakhale osavomerezedwa?
19 Pomalizira, Paulo anatiuza za chinsinsi chake cha chipambano: “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.” (1 Akorinto 9:27) Mofanana ndi Paulo, nafenso tiyenera kukhala ndi ulamuliro pazikhoterero za matupi athu opanda ungwiroŵa mmalo mwa kuwalola kutilamulira. Tifunikira kuzula zikhoterero zakuthupi, zolakalaka, ndi zikhumbo. (Aroma 8:5-8; Yakobo 1:14, 15) Kuchita motero kungakhale komvetsa ululu, popeza kuti liwu lotembenuzidwalo “pumphuntha” kwenikweni limatanthauza ‘kukantha nkhonya padiso’ (Kingdom Interlinear). Komabe, kodi sikuli bwino kwambiri kuvulala padiso, kunena kwake titero, ndi kukhalabe ndi moyo, koposa kulolera molakwa kuzikhumbo za thupi lakugwa ndi kufa?—Yerekezerani ndi Mateyu 5:28, 29; 18:9; 1 Yohane 2:15-17.
20. Kodi nchifukwa ninji makamaka tsopano kuli kofulumira kupenda mmene tikuthamangira m’makani a moyo?
20 Tsopano, tikuyandikira mapeto a makaniwo. Nthaŵi yakuti mphotho ziperekedwe yayandikira. Kwa Akristu odzozedwa, ndiyo ‘mfupo ya maitanidwe akumwamba a Mulungu mwa Kristu Yesu.’ (Afilipi 3:14) Kwa a khamu lalikulu, ndiyo moyo wosatha m’paradaiso wa padziko lapansi. Popeza kuti mphothoyo njaikulu motero, tikhaletu otsimikiza, monga momwe analiri Paulo, kuti ‘mwina tingakhale otayika.’ Aliyense wa ife alabadiretu chilimbikitso chakuti: “Thamangani, kuti mukalandire.”—1 Akorinto 9:24, 27.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kolondola kuyerekezera moyo Wachikristu ndi makani a liŵiro?
◻ Kodi ndimotani mmene makani a moyo aliri osiyana ndi mpikisano weniweni wa kuthamanga?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusonyeza kudziletsa mosalekeza ndipo mu “zonse”?
◻ Kodi ndimotani mmene munthu amathamangira ‘osati mosatsimikizira’?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kwaupandu kukhala ‘ukupanda mlengalenga’?
[Chithunzi patsamba 16]
Korona wa ngwazi, ndiponso ulemerero ndi ulemu, zimafwifwa