‘Nditsateni’ Kosalekeza
1 Anthu ambiri amakonda kudzikondweretsa, koma nthawi zambiri amapezekanso kuti alibe chimwemwe. Mosiyana ndi moyo wodzikonda umenewu, Yesu ananena kuti kupatsa kopanda dyera n’kumene kumabweretsa chimwemwe chenicheni. (Mac. 20:35) Iye anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, . . . nanditsate Ine [kosalekeza, NW.]” (Marko 8:34) Zimenezo zimafuna zambiri koposa kungodzimana chabe zinthu zosangalatsa nthawi ndi nthawi. Zimafuna kuti tizichita zinthu zosangalatsa Yehova tsiku lililonse, m’malo modzisangalatsa tokha.—Aroma 14:8; 15:3.
2 Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Chifukwa cha “mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu,” anasiya kulondola zokhumba zake ndipo anadzipereka kuti apititse patsogolo zofunika za Ufumu. (Afil. 3:7, 8) Kenako ananena kuti: “Ndipo ndidzadzipereka ndi kuperekedwa konse” potumikira ena. (2 Akor. 12:15) Tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndi kugwiritsa ntchito motani nthawi yanga, mphamvu zanga, ndi luso langa? Kodi cholinga changa chachikulu ndicho kukwaniritsa zofuna zanga, kapena ndikufuna kukondweretsa Yehova?’
3 Zimene Tingachite: Chaka chilichonse, anthu a Mulungu amathera maola opitirira biliyoni imodzi mu ntchito yolalikira za Ufumu, ntchito imene cholinga chake ndicho kupulumutsa anthu. Mumpingo, ana ndi achikulire omwe amagwira ntchito zosiyanasiyana zomwe zimapindulitsa anthu ambiri. Pali ntchito zinanso zambiri zokhudzana ndi misonkhano yachigawo ndi yadera, komanso ntchito yomanga ndi kukonzanso nyumba zomwe zimagwiritsidwa ntchito popititsa patsogolo kulambira koona. Taganiziraninso za thandizo lachikondi limene abale amene akutumikira m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala ndi a m’Magulu Ozonda Odwala akuchita. Kudzipereka kotere kuli dalitso ku ubale wathu wachikristu.—Sal. 110:3.
4 Kukachitika tsoka kapena ngozi, tingafunikire kukhala opatsa m’njira zambiri. Komano, nthawi zambiri timangofunikira kuzindikira zimene zikuchitikira abale athu kuti tidziwe ngati akufunikira thandizo kapena kulimbikitsidwa. (Miy. 17:17) Pamene tikudzipereka kutumikira ena ndi kupititsa patsogolo zofunika za Ufumu, timakhala tikutsatira chitsanzo cha Yesu. (Afil. 2:5-8) Tiyeni tiyesetse kuchita zimenezi kosalekeza.