Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Anaona Ulemelero wa Khristu Atasandulika
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Pamene Yesu ankaphunzitsa anthu m’dera la Kaisareya wa Filipi ananena zinthu zomwe zinadabwitsa kwambiri atumwi ake. Derali linali pamtunda wa makilomita 25 kuchokera ku phiri la Herimoni. Iye anauza atumwiwo kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe kufikira choyamba ataona Mwana wa munthu akubwera monga mfumu.”—Mateyu 16:28.

      Ophunzirawo ayenera kuti anadabwa kuti Yesu ankatanthauza chiyani. Patatha mlungu umodzi, Yesu anatenga atumwi ake atatu omwe mayina awo anali Petulo, Yakobo ndi Yohane ndipo anakwera nawo m’phiri lalitali. Zikuoneka kuti anakwera m’phirili usiku. Tikutero chifukwa pa nthawiyi ophunzira atatuwo anali ndi tulo. Pamene Yesu ankapemphera, anasandulika iwo akuona. Atumwiwo anaona nkhope ya Yesu ikuwala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinali zoyera kwambiri komanso zinkanyezimira.

  • Anaona Ulemelero wa Khristu Atasandulika
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Masomphenya amenewa analimbikitsa kwambiri Yesu komanso atumwiwo. Anasonyeza ulemelero umene Khristu adzakhale nawo mu Ufumu wake. Choncho ophunzirawo anaona “Mwana wa munthu akubwera monga mfumu” ngati mmene Yesu anawalonjezera. (Mateyu 16:28) Pa nthawi imene atumwiwo anali m’phiri muja ‘anaona ndi maso awo ulemerero wake.’ Ngakhale kuti Afarisi ankafuna kuti Yesu awaonetse chizindikiro chosonyeza kuti iye ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, Yesu sanawaonetse chizindikiro chilichonse. Koma ophunzira a Yesu anapatsidwa mwayi woona Yesu akusandulika, zomwe zinawathandiza kutsimikizira kuti malonjezo onena za Ufumu adzakwaniritsidwa. Moti patapita nthawi Petulo analemba kuti: “Mawu aulosiwa ndi odalirika kwambiri.”—2 Petulo 1:16-19.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena