Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 May tsamba 8
  • “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi ...”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi ...”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Chisudzulo—Kodi Nchiyani Chimene Baibulo Limanena Kwenikweni?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Tizilemekeza “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Chisudzulo Chiridi ndi Minkhole
    Galamukani!—1991
  • Chisudzulo—Zotulukapo Zake Zoŵaŵa
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 May tsamba 8
Mwamuna ndi mkazi atagwirana dzanja

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi . . . ”

Chilamulo cha Mose chinkanena kuti mwamuna akafuna kusiya mkazi wake ankafunika kukhala ndi kalata yothetsera ukwati. Zimenezi zinkathandiza kuti anthu asamangothetsa ukwati mwachisawawa. Komabe m’nthawi ya Yesu, atsogoleri achipembedzo ankachititsa kuti kuthetsa maukwati kuzikhala kosavuta. Amuna ankasiya akazi awo pazifukwa zosamveka. (“kalata yothetsa ukwati” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 10:4, nwtsty, “wosiya mkazi wake” “wachita chigololo molakwira mkaziyo” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 10:11, nwtsty) Yesu anasonyeza kuti Yehova ndi amene anayambitsa ukwati. (Maliko 10:2-12) Mwamuna ndi mkazi wake ankafunika kukhala “thupi limodzi” ndipo sankayenera kusiyana. Malinga ndi zimene Mateyu analemba pa nkhaniyi, chifukwa chimodzi chokha cha m’Malemba, chomwe chingachititse kuti ukwati uthe ndi “chigololo.”​—Mat. 19:9.

Masiku ano, anthu ambiri samaona ukwati ngati mmene Yesu ankauonera. Iwo amaona ngati mmene Afarisi ankauonera moti mavuto akabuka, amathamangira kuthetsa banja. Mosiyana ndi zimenezi, mabanja achikhristu amalemekeza zimene analonjeza patsiku la ukwati wawo ndipo amayesetsa kuthana ndi mavuto potsatira mfundo za m’Baibulo. Pambuyo poonera vidiyo yakuti, Chikondi ndi Ulemu Zimachititsa Banja Kukhala Logwirizana, yankhani mafunso otsatirawa:

  • Akuwerenga Baibulo; mwamuna akumvetsera pamene mkazi wake akuyankhula; chithunzi chaukwati chong’ambika

    Kodi mungatsatire bwanji mfundo ya pa Miyambo 15:1 m’banja lanu ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

  • Kodi kugwiritsa ntchito mfundo ya pa Miyambo 19:11 kungakuthandizeni bwanji kupewa mavuto m’banja?

  • Ngati banja lanu likuvutavuta, m’malo moganiza kuti ‘Mwinatu ndingolithetsa,’ kodi ndi mafunso ati amene muyenera kuwaganizira?

  • Kodi mfundo ya pa Mateyu 7:12, ingakuthandizeni bwanji kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena