Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kupsyinjika Mtima m’Munda
    Nsanja ya Olonda—1990 | October 1
    • Akumasiya atumwi asanu ndi atatu​—mwinamwake pafupi ndi poloŵera pa mundawo​—iye akuwalangiza kuti: “Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.” Pamenepo iye anatenga atatu enawo​—Petro, Yakobo, ndi Yohane​—napita mkati mwa mundawo. Yesu akhala wachisoni navutitsidwa kwakukulu. ‘Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa,’ iye akuwauza tero. ‘Khalani pano muchezere pamodzi ndi ine.’

  • Kupsyinjika Mtima m’Munda
    Nsanja ya Olonda—1990 | October 1
    • Kutalitali! Yesu sakupembedzera kuti apulumutsidwe ku imfa. Ngakhale lingaliro lopeŵa imfa yansembe, limene panthaŵi ina linaperekedwa ndi Petro, nlonyansa kwa iye. M’malo mwake, iye ngwopsyinjika mtima chifukwa akuwopa kuti njira imene adzaferamo posachedwapa​—monga mpandu woipitsitsa​—idzabweretsa chitonzo pa dzina la Atate wake. Iye akuzindikira tsopano kuti m’maola oŵerengeka adzapachikidwa pamtengo monga munthu woipitsitsa​—wochitira Mulungu mwano! Ichi ndicho chimene chikumvutitsa kwambiri.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena