Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/15 tsamba 30-31
  • Ngale Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Marko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngale Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Marko
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Unalembedwera Yani?
  • Mwana wa Mulungu Wochita Zozizwitsa
  • Uminisitala mu Dekapoli
  • Yesu ndi Mwambo
  • Uminisitala Wapoyera Womalizira wa Yesu
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliko
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Maliko ‘Anali Wofunika Potumikira’
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Pontiyo Pilato Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Maliko Sanafooke
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/15 tsamba 30-31

Ngale Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Marko

MZIMU wa Yehova unawuzira Marko kulemba cholembedwa chodzala ndi zochitika za moyo ndi uminisitala za Yesu za pa dziko lapansi. Ngakhale kuti Uthenga Wabwino umenewu sumanena kuti unalembedwa ndi Marko, pali umboni wa zimenezi m’mabukhu a Papias, Justin Martyr, Tertullian, Origen, Eusebius, Jerome, ndi ena amene mabukhu awo akufola zochitika za zaka mazana anayi oyambirira za Nyengo Yathu.

Mwambo umanena kuti, mtumwi Petro anapereka mbali yaikulu ya mawu a Uthenga Wabwino umenewu. Mwachitsanzo, Origen adanena kuti Marko anaulemba “mogwirizana ndi malangizo a Petro.” Komabe mwachiwonekere Marko anali wokhozanso kufika ku magwero ena, chifukwa chakuti ophunzira ankasonkhana m’nyumba ya amake. Kwenikweni, popeza kuti mwinamwake Marko anali “mnyamata wina” amene anathaŵa anthu omanga Yesu, angakhale anali ndi kukambitsirana kwaumwini ndi Kristu.​—Marko 14:51, 52; Machitidwe 12:12.

Kodi Unalembedwera Yani?

Mwachiwonekere Marko analembera kwakukulukulu oŵerenga Amitundu. Mwachitsanzo, kalembedwe kake kachidule kanayenerera mpangidwe wa Aroma. Iye analongosola “kobani” kukhala “mtulo woperekedwa kwa Mulungu” (7:11) ndipo anasonyeza kuti kachisi anali wokhoza kuwoneka kuchokera pa Phiri la Azitona. (13:3) Marko analongosolanso kuti Afarisi ‘anali ndi chizoloŵezi cha kusala kudya’ ndipo Asaduki “amanena kuti palibe kuuka kwa akufa.” (2:18; 12:18) Mawu otere akakhala osafunikira kwa oŵerenga Achiyuda.

Ndithudi, kuŵerenga Uthenga Wabwino wa Marko kungapindulitse munthu aliyense. Koma kodi ndi zochitika zozungulira zotani zimene zingatithandize kuyamikira zina za ngale zake?

Mwana wa Mulungu Wochita Zozizwitsa

Marko akusimba zozizwitsa zimene Kristu anachita mwa mphamvu ya Mulungu. Machitsanzo, pa nthaŵi imodzi m’nyumba ina munali khamu lalikulu kotero kuti munthu wamanjenje achiritsidwe, anafunikira kutsitsidwira pafupi ndi Yesu kudzera pa chiboo chopangidwa pa tsindwi. (2:4) Chifukwa chakuti nyumbayo inali yodzala anthu, munthuyo angakhale anakwezedwa pamakwerero kapena makwerero a kunja kwa nyumba. Koma kodi nchifukwa ninji anafunikira kupasula tsindwiro? Chabwino, matsindwi ambiri anali athyathyathya ndipo anayedzamira pa nsanamira zopingasa kuchokera ku chipupa mpaka ku chipupa. Modutsa nsanamirazo panali mphaso zofoleredwa ndi nthambi, mabango, ndi zina zotero. Pamwamba pake panali muyalo wochindikala wa dothi lomatidwa ndi pulasitala ya dongo kapena dongo ndi laimu. Chifukwa chake, kuti afikitse munthu wamanjenjeyo kwa Yesu, amunawo anafunikira kupasula kuti apange chiboo pa tsindwi la dothilo. Koma ndi dalitso lalikulu chotani nanga kuti iwo anachita motero! Kristu anachiritsa mwamunayo, ndipo onse amene analipo analemekeza Mulungu. (2:1-12) Ndi chitsimikiziro chotani nanga chakuti Mwana wa Yehova adzachita machiritso ozizwitsa m’dziko latsopano!

Yesu anachita chimodzi cha zozizwitsa zimenezi m’bwato pamene anatontholetsa mkuntho pa Nyanja ya Galileya pambuyo pa kudzutsidwa atagona pa “mtsamiro.” (4:35-41) Mwachiwonekere mtsamirowo sunali wofewa monga wogwiritsidwa ntchito masiku ano wotsamizapo mutu pa bedi. Uwo ungakhale unali chokhalira wamba chimene opalasa ngalawa anakhalapo kapena kushoni yokhalira poyendetsa choyendera. Mulimonse mmene zinaliri, pamene Yesu anauza nyanja kuti, “Tonthola, khala bata” amene anali naye anachitira umboni chikhulupiriro chogwira ntchito, chifukwa chakuti “mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu.”

Uminisitala mu Dekapoli

Atawoloka Nyanja ya Galileya, Yesu analoŵa m’Dekapoli, kapena chigawo cha mizinda khumi. Ngakhale kuti mosakaikira mizinda imeneyi inali ndi chiŵerengero chachikulu cha Ayuda, iyo inali malo apakati ozolowereka a Agriki kapena Ahelene. Konko, kudziko la Agerasa, Yesu anawonjola munthu wina wogwidwa ndi chiwanda amene “anayesa nyumba yake kumanda.”​—5:1-20.

Nthaŵi zina, manda osemedwa a m’thanthwe anali malo okhala anthu openga, malo obisala apandu, kapena malo okhala anthu osauka. (Yerekezani ndi Yesaya 22:16; 65:2-4.) Mogwirizana ndi bukhu la m’zaka za zana la 19, mlendo wina amene anakacheza ku chigawo chimene Yesu anakumanako ndi munthu wogwidwa ndi chiwandayo anati ponena za nyumba yotero: “Mandawo anali pafupifupi mapazi asanu ndi atatu kutalika cha mkatimo, popeza panali potsika kuchokera pa mwala wopanga chiwundawo kufika pansi penipeni. Ukulu wake unali pafupifupi ndawala khumi ndi ziŵiri monsemonse; koma, popeza panalibe malo ena olowera kuwunika kusiyapo khomo, sitikanawona kuti kaya munali chipinda cha mkati monga momwe ena aliri. Munali chikhalirebe bokosi la maliro lenileni mkatimo, ndipo tsopano limeneli linali kugwiritsidwa ntchito ndi banjalo monga mtanga wosungiramo chimanga ndi zakudya zina, kotero kuti mwanjirayi zimenezi zinasanduliza malo a mandawo kukhala otetezereka, achete, ndi owopedwa ndi anthu amoyo.”

Yesu ndi Mwambo

Pa nthaŵi ina, Afarisi ndi alembi anadandaula kuti ophunzira a Yesu anadya ndi manja osasamba. Kaamba ka phindu la oŵerenga Amitundu, Marko analongosola kuti Afarisi ndi Ayuda ena ‘sanadye kusiyapo ngati anasamba manja awo kufikira pa chikongono.’ Atabwerera kuchoka ku msika, anadya kokha pambuyo pa kusamba mwa kuwaza madzi, ndipo miyambo yawo inaphatikizapo ‘kuviika zikho ndi mitsuko ndi zotengera za mkuwa.’​—7:1-4.

Kuwonjezera pa dzoma lodziwaza madzi asanadye, Ayuda amenewa anamiza, kapena kuviika m’madzi, zikho, miphika, ndi zotengera za mkuwa zimene anagwiritsira ntchito pa nthaŵi ya zakudya. Kuti iwo anali okonda mwambo kwambiri kunalongosoledwa mwa fanizo ndi katswiri wina John Lightfoot. Akumagwira mawu mabukhu a arabi, anasonyeza kuti chisamaliro chachikulu chinaperekedwa ku maumboni monga kuchuluka kwa madzi, dongosolo, ndi nthaŵi yoyenerera ya kusamba. Lightfoot anagwira mawu bukhu lina kusonyeza kuti Ayuda ena anasamba mosamalitsa asanadye kotero kuti apewe kuvulazidwa ndi Shibta, “mzimu woipa umene umakhala pamanja a amuna usiku: ndipo ngati aliyense akhudza chakudya chake ndi manja osasamba, mzimu umenewo umakhala pa chakudya chimenecho, ndipo pamakhala upandu kuchokera ku uwo.” Nchosadabwitsa kuti Yesu anatsutsa alembi ndi Afarisi chifukwa cha ‘kusiya lamulo la Mulungu pamene akunonomera mwambo wa anthu’!​—7:5-8.

Uminisitala Wapoyera Womalizira wa Yesu

Atasimba uminisitala wa pambuyo pake wa Yesu m’Galileya ndi ntchito Yake m’Pereya, Marko akusumika chisamaliro pa zochitika m’Yerusalemu ndi malo ozungulira. Mwachitsanzo, iye anasimba za nthaŵi pamene Kristu anali kuwona anthu akuponya ndalama m’mabokosi osungira ndalama m’kachisi. Yesu anawona kuti mkazi wamasiye waumphawi anapereka kokha ‘tindalama tiŵiri tating’ono ta mtengo wochepetsetsa.’ Komabe, iye adanena kuti mkaziyu anapereka zambiri kuposa ena onse, chifukwa chakuti iwo anapereka kuchokera pa zowonjezereka zawo, pamene kuli kwakuti mkaziyo ‘anapereka mwa kusowa kwake, zonse anali nazo.’ (12:41-44) Mogwirizana ndi lemba Lachigriki, iye anapereka malepta aŵiri. Lepton inali ndalama Yachiyuda yochepetsetsa ya mkuwa kapena ya chitsulo, ndipo mtengo wa ndalama imeneyi uli pafupifupi wosanunkha kanthu lerolino. Komatu ntchemberembaya yosauka imeneyi inachita zimene inali yokhoza, ikumapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kupanda dyera pochirikiza kulambira kowona.​—2 Akorinto 9:6, 7.

Pamene uminisitala wa Yesu unafika kumapeto, iye anafunsidwa ndi Pontiyo Pilato, amene dzina lake lenileni ndi laulemu lakuti “kazembe” limawonekera pa zilembo zozokotedwa zimene zinapezeka ku Kaisareya mu 1961. M’zigawo zozungulirazo monga Yudeya, bwanamkubwa (kazembe) anali ndi ulamuliro pa ankhondo, anali ndi thayo la kuyendetsa nkhani za chuma, ndipo anatumikira monga woweruza milandu. Pilato anali ndi ulamuliro wa kumasula Kristu, koma anagonjera kwa adani a Yesu nafunafuna kukhutiritsa khamulo mwa kumpereka kwa iwo kukampachika ndi kumasula wochita mbanda wachiŵembu Baraba.​—15:1-15.

Pali manenanena osiyanasiyana okhudza moyo ndi imfa ya Pilato pambuyo pake. Mwachitsanzo, wolemba mbiri Eusebius analemba kuti: “Pilato mwiniyo, mbwanamkubwa wa mu nthaŵi ya Mpulumutsi wathu, anaphatikizidwa m’zochitika za tsoka zotero kotero kuti anakakamizika kudziweruza ndi kudzilanga iyemwini ndi dzanja lake: kukuwonekera kuti, chiweruzo cholungama cha Mulungu, sichinachedwe kumkantha.” Komabe, mosasamala kanthu za zothekera zotero, imfa yokhala ndi tanthauzo lalikulu ndiyo ya Yesu. Kazembe wankhondo wa Roma (kentuliyo) amene anawona imfa ya Kristu ndi zochitika zachilendo pa nthaŵi ya imfayo analankhuladi zowona pamene anati: “Zowonadi koma munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.”​—15:33-39.

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Israel Department of Antiquities and Museums; photograph from Israel Museum, Jerusalem

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena