Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bt mutu 15 tsamba 117-123
  • “Ankalimbikitsa Mipingo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ankalimbikitsa Mipingo”
  • ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Tiyeni Tibwerere . . . Kuti Tikachezere Abale” (Machitidwe 15:36)
  • “Anakangana Koopsa” (Machitidwe 15:37-41)
  • “Anapereka Umboni Wabwino Wonena za Iyeyo” (Machitidwe 16:1-3)
  • Mipingo ‘Inapitiriza kukhala ndi Chikhulupiriro Cholimba’ (Machitidwe 16:4, 5)
  • “Mwana Wanga Wokondedwa Ndi Wokhulupirika Mwa Ambuye”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timoteyo Anali Wokonzeka Komanso Wofunitsitsa Kutumikira
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Maliko ‘Anali Wofunika Potumikira’
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Timoteo—‘Mwana Weniweni m’Chikhulupiriro’
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
bt mutu 15 tsamba 117-123

MUTU 15

“Ankalimbikitsa Mipingo”

Atumiki oyendayenda anathandiza mipingo kuti ikhalebe yolimba m’chikhulupiriro

Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 15:36–16:5

1-3. (a) Kodi Paulo anayamba kuyenda ndi ndani, nanga mnzakeyo anali wotani? (b) Kodi tiphunzira chiyani m’mutuwu?

MTUMWI Paulo ankachita chidwi ndi mnyamata amene anali naye, pamene ankayenda ulendo wapansi kudutsa mumsewu wa m’mapiri wolumikiza matauni awiri. Mnyamatayu dzina lake linali Timoteyo. Timoteyo anali mnyamata wamphamvu amene mwina pa nthawiyi anali atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20 kapena atangopitirira pang’ono. Iwo anayenda mtunda wautali kuchoka kwawo kwa Timoteyo ndipo pofika madzulo, anali ali kutali kwambiri ndi mizinda ya Lusitara ndi Ikoniyo. Kodi ankayembekezera kukumana ndi zotani? Paulo ankadziwa zimene angakumane nazo chifukwa umenewu unali ulendo wake wachiwiri waumishonale. Iye ankadziwa kuti angakumane ndi mavuto komanso zinthu zambiri zoopsa. Koma kodi mnyamata amene ankayenda nayeyo akanakwanitsa kupirira mavuto amenewo?

2 Paulo ankakhulupirira kuti Timoteyo, yemwe anali wodzichepetsa, akwanitsa kugwira ntchito imeneyo mwinanso kuposa mmene Timoteyoyo ankadzionera. Zimene Paulo anakumana nazo masiku angapo m’mbuyomo zinam’chititsa kuganiza kuti ayenera kupeza munthu woyenda naye woyenerera. Paulo ankadziwa kuti iyeyo limodzi ndi munthu amene akuyenda naye, ayenera kukhala olimba mtima ndiponso ogwirizana kwambiri kuti akwanitse kugwira ntchito yawo yoyendera mipingo ndi kuilimbikitsa. N’chifukwa chiyani Paulo ankaganiza zimenezi? Mwina chifukwa chimodzi chimene chinam’chititsa kuganiza zimenezi ndi choti m’mbuyomu anasemphana maganizo ndi Baranaba ndipo zimenezi zinachititsa kuti asiyane.

3 M’mutuwu, tiphunzira njira zabwino za mmene tingathetsere kusamvana. Tionanso chifukwa chake Paulo anasankha Timoteyo kuti akhale mnzake woyenda naye, ndipo tidziwa ntchito yofunika imene oyang’anira madera amagwira masiku ano.

“Tiyeni Tibwerere . . . Kuti Tikachezere Abale” (Machitidwe 15:36)

4. Kodi Paulo anali ndi zolinga zotani pa ulendo wake wachiwiri waumishonale?

4 M’mutu wapitawu, tinaona kuti abale 4 omwe anali Paulo, Baranaba, Yudasi ndi Sila, amene anatumizidwa kuchokera ku Yerusalemu, analimbikitsa mpingo wa ku Antiokeya ndi mfundo imene bungwe lolamulira linagwirizana pa nkhani ya mdulidwe. Kodi tsopano Paulo anachita chiyani? Iye anauza Baranaba kuti: “Tiyeni tibwerere kumizinda yonse kumene tinalalikira mawu a Yehova kuti tikachezere abale ndiponso tikawaone kuti ali bwanji.” (Mac. 15:36) Apa Paulo sankanena za ulendo wokangocheza basi ndi Akhristu atsopanowo. Buku la Machitidwe limasonyeza zolinga zenizeni za ulendo wachiwiri waumishonale wa Paulo. Choyamba, iye ankafuna kupitiriza kupereka malamulo ochokera ku bungwe lolamulira m’mipingo. (Mac. 16:4) Chachiwiri, popeza Paulo anali woyang’anira woyendayenda, iye ankafunitsitsa kukalimbikitsa mipingo mwauzimu ndi kuithandiza kuti ilimbe m’chikhulupiriro. (Aroma 1:11, 12) Kodi gulu la Mboni za Yehova masiku ano limatsanzira bwanji chitsanzo cha atumwi chimenechi?

5. Kodi Bungwe Lolamulira masiku ano limatsogolera ndiponso kulimbikitsa bwanji mipingo?

5 Masiku ano, Khristu amagwiritsa ntchito Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova potsogolera mpingo wake. Amuna okhulupirika odzozedwa amenewa, amatsogolera ndiponso kulimbikitsa mipingo yonse padziko lapansi, ndipo amachita zimenezi kudzera m’makalata, mabuku apazipangizo zamakono komanso osindikizidwa, misonkhano ndi njira zina. Bungwe Lolamulira limayesetsanso kuti lizilankhula ndi mpingo uliwonse. Kuti zimenezi zitheke, bungweli limagwiritsa ntchito oyang’anira madera. Bungwe Lolamulira linasankha akulu oyenerera padziko lonse kuti akhale oyang’anira madera.

6, 7. Kodi oyang’anira madera amagwira ntchito ziti?

6 Masiku ano, oyang’anira madera amayesetsa kuthandiza komanso kulimbikitsa mwauzimu munthu aliyense payekha m’mipingo yonse imene amaiyendera. Kodi amachita bwanji zimenezi? Amatsanzira chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi monga Paulo. Iye analimbikitsa woyang’anira mnzake kuti: “Lalikira mawu. Uzilalikira modzipereka, pa nthawi yabwino ndi pa nthawi yovuta. Dzudzula, tsutsa, dandaulira, ndipo uzichita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri. . . . Uzigwira ntchito ya mlaliki.”​—2 Tim. 4:2, 5.

7 Mogwirizana ndi mawu amenewa, woyang’anira dera limodzi ndi mkazi wake, ngati ali wokwatira, amalalikira limodzi ndi ofalitsa amumpingo umene akuchezera. Alaliki oyendayenda amenewa amachita utumiki wawo mwakhama komanso mwaluso ndipo zimenezi zimalimbikitsa nkhosa. (Aroma 12:11; 2 Tim. 2:15) Oyang’anira madera amadziwika kuti ndi anthu achikondi komanso odzimana. Iwo amatumikira ena mosanyinyirika ndipo amayenda ngakhale m’madera oopsa kapena pa nthawi imene nyengo sili bwino. (Afil. 2:3, 4) Komanso, iwo amalimbikitsa, kuphunzitsa ndi kupereka malangizo ku mpingo uliwonse pogwiritsa ntchito nkhani za m’Baibulo. Anthu onse mumpingo amapindula akamaganizira khalidwe la oyang’anira madera amenewa komanso akamatsanzira chikhulupiriro chawo.​—Aheb. 13:7.

“Anakangana Koopsa” (Machitidwe 15:37-41)

8. Kodi Baranaba anatani Paulo atamupempha kuti ayendere limodzi?

8 Baranaba anagwirizana ndi maganizo a Paulo akuti ‘akachezere abale.’ (Mac. 15:36) M’mbuyomu, atumiki awiriwa anagwira ntchito limodzi yoyendera mipingo ndipo onsewa ankadziwa bwino madera komanso anthu amene ankafuna kuwachezerawo. (Mac. 13:2–14:28) Choncho, mwina iwo anaona kuti ndi bwino kuti ayenderenso limodzi pokachita utumikiwu. Koma panachitika vuto linalake. Lemba la Machitidwe 15:37 limatiuza kuti: “Baranaba ankafunitsitsa kuti atenge Yohane, wotchedwanso Maliko.” Apa sikuti Baranaba ankangonena maganizo ake, koma “ankafunitsitsa” kutenga msuweni wake Maliko kuti ayende naye pa ulendo waumishonalewu.

9. N’chifukwa chiyani Paulo anasemphana maganizo ndi Baranaba?

9 Koma Paulo sanagwirizane nazo. Chifukwa chiyani? Nkhaniyi imati: “Paulo anaona kuti si bwino kumutenga chifukwa ulendo wina Yohane anawasiya ku Pamfuliya ndipo sanapite nawo ku ntchitoyi.” (Mac. 15:38) Maliko anayenda ndi Paulo ndi Baranaba pa ulendo wawo woyamba waumishonale koma anabwerera panjira. (Mac. 12:25; 13:13) Chakumayambiriro kwa ulendowo asanachoke ku Pamfuliya, Maliko anasiya utumiki wake n’kubwerera kwawo ku Yerusalemu. Baibulo silinena chifukwa chake Maliko anabwerera, koma zikuoneka kuti mtumwi Paulo anaona kuti zimene anachitazo zinali zachibwana. Choncho, Paulo ayenera kuti ankakayikira zoti Maliko angakhale wodalirika.

10. Kodi chinachitika n’chiyani Paulo ndi Baranaba atasemphana maganizo, nanga zotsatira zake zinali zotani?

10 Koma Baranaba anaumirirabe kuti Maliko apite nawo. Nayenso Paulo sanalolere kuti Maliko ayende nawo pa ulendowu. “Zitatero anakangana koopsa mpaka anasiyana.” (Mac. 15:39) Kenako Baranaba anatenga Maliko ndipo anayamba ulendo wa pamadzi wopita kuchilumba cha Kupuro, komwe kunali kwawo. Koma Paulo sanasinthe cholinga chake chofuna kukachezera abale. Nkhaniyi imati: “Paulo anasankha Sila, ndipo abale atamupempherera Pauloyo kuti Yehova amusonyeze kukoma mtima kwakukulu, ananyamuka.” (Mac. 15:40) Paulo ndi Sila anayamba ulendo wawo ndipo “anadzera ku Siriya ndi ku Kilikiya ndipo ankalimbikitsa mipingo.”​—Mac. 15:41.

11. Kodi ndi makhalidwe ati ofunika kwambiri amene tiyenera kukhala nawo kuti tipewe kudana ndi anthu amene atilakwira?

11 Nkhaniyi imatikumbutsa mfundo yakuti anthufe si angwiro. Paulo ndi Baranaba anasankhidwa kuti akhale atumiki apadera oimira bungwe lolamulira. Ndipo n’kutheka kuti patapita nthawi, Paulo anakhala mmodzi wa abale a m’bungwe lolamulira. Komabe pa nthawiyi, Paulo ndi Baranaba anachita zinthu zosayenera chifukwa chakuti sanali angwiro. Kodi iwo analolera kuti adane chifukwa cha zimene zinachitikazi? Ngakhale kuti sanali angwiro, Paulo ndi Baranaba anali anthu odzichepetsa ndipo anali ndi maganizo a Khristu. Choncho n’zosakayikitsa kuti iwo anachita zimene abale a Chikhristu amayenera kuchita ndipo anakhululukirana. (Aef. 4:1-3) Patapita nthawi, Paulo ndi Maliko anagwira ntchito limodzi potumikira Mulungu.a​—Akol. 4:10.

12. Kodi oyang’anira masiku ano ayenera kukhala ndi makhalidwe otani potsanzira Paulo ndi Baranaba?

12 Mkangano woopsa umene unabuka pakati pa Baranaba ndi Paulo sukusonyeza kuti anthuwa anali okonda mikangano. Baranaba ankadziwika kuti anali munthu wachikondi komanso wopatsa moti atumwi sankamuitana ndi dzina lake lakuti Yosefe, koma anam’patsa dzina lakuti Baranaba, lomwe limatanthauza kuti “Mwana Wotonthoza.” (Mac. 4:36) Nayenso Paulo ankadziwika kuti anali munthu wachifundo komanso woganizira ena. (1 Ates. 2:7, 8) Potsanzira Paulo ndi Baranaba, oyang’anira onse a Chikhristu masiku ano limodzi ndi oyang’anira madera, ayenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa komanso achifundo kwa akulu anzawo ndi kwa gulu lonse la nkhosa.​—1 Pet. 5:2, 3.

“Anapereka Umboni Wabwino Wonena za Iyeyo” (Machitidwe 16:1-3)

13, 14. (a) Kodi Timoteyo anali ndani ndipo ayenera kuti anakumana bwanji ndi Paulo? (b) N’chifukwa chiyani Paulo anachita chidwi ndi Timoteyo? (c) Kodi Timoteyo anapatsidwa utumiki wotani?

13 Pa ulendo wake wachiwiri waumishonale, Paulo anafika kuchigawo cha Galatiya chomwe chinkalamulidwa ndi Aroma ndipo kumeneko kunali mipingo ingapo. Kenako “Paulo anafika ku Debe ndiponso ku Lusitara.” Nkhaniyi imapitiriza kuti: “Kumeneko kunali wophunzira wina dzina lake Timoteyo, mwana wa mayi wa Chiyuda wokhulupirira, koma bambo ake anali Mgiriki.”​—Mac. 16:1.b

14 Zikuoneka kuti Paulo anadziwana ndi anthu a m’banja la Timoteyo pa ulendo wake woyamba cha m’ma 47 C.E. Tsopano Paulo ali pa ulendo wake wachiwiri, patapita zaka ziwiri kapena zitatu, anachita chidwi kwambiri ndi Timoteyo, yemwe pa nthawiyi anali wachinyamata. N’chifukwa chiyani anachita naye chidwi? Chifukwa chakuti abale “anapereka umboni wabwino wonena za iyeyo.” Iye sankangokondedwa ndi abale a m’tauni yakwawo yokha koma mbiri yake yabwino inamvekanso m’mipingo ina ya m’madera akutali. Nkhaniyi imati abale a ku Lusitara komanso ku Ikoniyo, womwe unali mtunda wa makilomita pafupifupi 30, ankanena zabwino zokhudza Timoteyo. (Mac. 16:2) Motsogoleredwa ndi mzimu woyera, akulu anam’patsa Timoteyo, yemwe anali wachinyamata, udindo waukulu kuti azithandiza Paulo ndi Sila pa utumiki wawo woyendayenda.​—Mac. 16:3.

15, 16. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Timoteyo akhale ndi mbiri yabwino?

15 Kodi zinatheka bwanji kuti Timoteyo akhale ndi mbiri yabwino chonchi ali wachinyamata? Kodi chinali chifukwa chakuti anali wanzeru, mmene ankaonekera, kapenanso anali ndi maluso achibadwa? Kawirikawiri anthu amakopeka ndi zinthu ngati zimenezi. Ngakhale mneneri Samueli nthawi ina anakopeka ndi maonekedwe a anthu. Komabe, Yehova anamukumbutsa kuti: “Mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera. Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mumtima.” (1 Sam. 16:7) Akhristu ankanena zinthu zabwino zokhudza Timoteyo chifukwa chakuti iye anali ndi makhalidwe abwino, osati chifukwa chakuti anali wooneka bwino, wanzeru komanso wodziwa kuchita bwino zinthu.

16 Patapita zaka zingapo, mtumwi Paulo anatchula ena mwa makhalidwe a Chikhristu amene Timoteyo anali nawo. Paulo anafotokoza kuti Timoteyo anali ndi mtima wabwino, anali wachikondi, wodzimana komanso anali wakhama potumikira Mulungu. (Afil. 2:20-22) Timoteyo ankadziwikanso kuti anali ndi ‘chikhulupiriro chopanda chinyengo.’​—2 Tim. 1:5.

17. Kodi achinyamata masiku ano angatsanzire bwanji Timoteyo?

17 Masiku ano, achinyamata ambiri amatsanzira Timoteyo poyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu. Choncho amakhala ndi mbiri yabwino pamaso pa Yehova ndi anthu ake ngakhale ali ana. (Miy. 22:1; 1 Tim. 4:15) Iwo amasonyeza chikhulupiriro chopanda chinyengo popewa kukhala achiphamaso. (Sal. 26:4) Choncho, achinyamata ambiri mofanana ndi Timoteyo, angakhale odalirika potumikira mumpingo. Iwo amalimbikitsa kwambiri anthu onse okonda Yehova akayenerera kukhala ofalitsa uthenga wabwino, akadzipereka kwa Yehova kenako n’kubatizidwa.

Mipingo ‘Inapitiriza kukhala ndi Chikhulupiriro Cholimba’ (Machitidwe 16:4, 5)

18. (a) Kodi Paulo ndi Timoteyo anali ndi mwayi wapadera wotani monga atumiki oyendayenda? (b) Nanga mipingo inapindula bwanji?

18 Paulo ndi Timoteyo anatumikira Mulungu limodzi kwa zaka zambiri. Popeza iwo anali atumiki oyendayenda, anagwira ntchito zosiyanasiyana poimira bungwe lolamulira. Nkhani ya m’Baibulo imeneyi imati: “M’mizinda yonse imene ankadutsa, ankapatsa okhulupirira akumeneko malamulo oyenera kuwatsatira, mogwirizana ndi zimene atumwi ndiponso akulu ku Yerusalemu anagamula.” (Mac. 16:4) N’zodziwikiratu kuti mipingo inatsatira malangizo ochokera kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu. Chifukwa chakuti iwo anamvera, “anthu m’mipingo anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo chiwerengero chinkawonjezeka tsiku ndi tsiku.”​—Mac. 16:5.

19, 20. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kumvera ‘amene akuwatsogolera’ pakati pawo?

19 Masiku anonso, a Mboni za Yehova amadalitsidwa chifukwa chomvera malangizo ochokera kwa ‘amene akuwatsogolera’ pakati pawo. (Aheb. 13:17) Popeza kuti zochitika za m’dzikoli zikusintha nthawi ndi nthawi, m’pofunika kuti Akhristu azimvera malangizo ochokera kwa “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru.” (Mat. 24:45; 1 Akor. 7:29-31) Kuchita zimenezi kungatiteteze kuti tisasiye choonadi ndiponso kungatithandize kuti tisatengere makhalidwe oipa a dzikoli.​—Yak. 1:27.

20 N’zoona kuti oyang’anira a Chikhristu masiku ano, ngakhalenso abale a m’Bungwe Lolamulira, si angwiro mofanana ndi mmene analili Paulo, Baranaba, Maliko ndi akulu ena odzozedwa a m’nthawi yawo. (Aroma 5:12; Yak. 3:2) Komabe Bungwe Lolamulira ndi lodalirika kwambiri chifukwa chakuti nthawi zonse limagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu komanso limatsatira chitsanzo cha atumwi. (2 Tim. 1:13, 14) Chifukwa cha zimenezi, mipingo imalimbikitsidwa ndipo imakhala ndi chikhulupiriro cholimba.

TIMOTEYO ANATUMIKIRA NGATI KAPOLO “POFALITSA UTHENGA WABWINO”

Mtumwi Paulo ankakonda kwambiri Timoteyo chifukwa ankamuthandiza pa utumiki wake. Anthu awiriwa atatumikira Mulungu limodzi kwa zaka pafupifupi 11, Paulo analemba zokhudza Timoteyo kuti: “Ndilibe wina amene ali ndi mtima ngati wake, amene angasamaliredi moona mtima zosowa zanu. . . . Inu mukudziwa chitsanzo chabwino chimene Timoteyo anasonyeza, kuti monga mwana ndi bambo ake, watumikira ngati kapolo limodzi ndi ine pofalitsa uthenga wabwino.” (Afil. 2:20, 22) Timoteyo anadzipereka kwambiri pa ntchito yolalikira, ndipo zimenezi zinachititsa kuti Paulo azimukonda kwambiri. Komanso Timoteyo ndi chitsanzo chabwino kwa ife masiku ano.

Timoteyo.

Zikuoneka kuti Timoteyo anakulira ku Lusitara. Bambo ake anali Mgiriki koma mayi ake anali Myuda. Kuyambira ali wakhanda, Timoteyo anaphunzitsidwa Malemba ndi amayi ake a Yunike komanso agogo ake a Loisi. (Mac. 16:1, 3; 2 Tim. 1:5; 3:14, 15) N’kutheka kuti Timoteyo, mayi ake komanso agogo akewa anakhala Akhristu nthawi yoyamba imene Paulo anafika m’tauni yakwawo.

Paulo anapitanso m’tauniyo patapita zaka zingapo, ndipo pa nthawiyi, “abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo” anali atayamba kale ‘kupereka umboni wabwino’ wonena za Timoteyo, amene mwina pa nthawiyi anali atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20 kapena atangopitirira pang’ono. (Mac. 16:2) Mzimu wa Mulungu unali utaneneratu “maulosi” onena za mnyamatayu, ndipo mogwirizana ndi maulosi amenewo, Paulo ndi akulu a mumpingo wakumeneko anavomereza kuti Timoteyo ayambe utumiki wapadera. (1 Tim. 1:18; 4:14; 2 Tim. 1:6) Utumiki wake unali woti aziyenda ndi Paulo pochita utumiki waumishonale. Timoteyo anafunika kusiya achibale ake komanso analolera kudulidwa kuti asakhumudwitse Ayuda amene akanawayendera.​—Mac. 16:3.

Timoteyo anayenda m’madera ambiri. Iye analalikira ndi Paulo komanso Sila ku Filipi, analalikiranso ndi Sila ku Bereya ndipo kenako analalikira yekha ku Tesalonika. Atakumananso ndi Paulo ku Korinto, Timoteyo anamuuza nkhani yabwino yoti abale a ku Tesalonika anali okhulupirika ndiponso achikondi ngakhale kuti ankakumana ndi masautso. (Mac. 16:6–17:14; 1 Ates. 3:2-6) Atamva za vuto limene linali mumpingo wa ku Korinto, Paulo, amene pa nthawiyo anali ku Efeso, anaganiza zotumizako Timoteyo. (1 Akor. 4:17) Ali ku Efeso komweko, Paulo anatumiza Timoteyo ndi Erasito ku Makedoniya. Koma pamene Paulo ankalembera kalata Aroma, anali limodzi ndi Timoteyo ku Korinto. (Mac. 19:22; Aroma 16:21) Awa ndi ena mwa maulendo amene Timoteyo anayenda polalikira uthenga wabwino.

Zikuoneka kuti Timoteyo ankaopa kuchita zinthu zimene zinali udindo wake pa utumikiwo, koma Paulo anamulimbikitsa kuti: “Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamng’ono.” (1 Tim. 4:12) Paulo anatumiza Timoteyo kumpingo umene unali ndi mavuto ndipo anamulangiza kuti: “Uletse anthu ena ake kuti asamaphunzitse zosiyana ndi zimene timaphunzitsa.” (1 Tim. 1:3) Paulo anam’patsanso Timoteyo udindo woika akulu ndi atumiki othandiza m’mipingo.​—1 Tim. 5:22.

Paulo ankakonda kwambiri Timoteyo chifukwa cha makhalidwe ake abwino. Malemba amasonyeza kuti mnyamatayu anali mnzake wapamtima wa Paulo ndipo ankamukonda ngati mwana wake. Iye analemba kuti ankakumbukira misozi ya Timoteyo, ankalakalaka kumuona ndiponso ankamupempherera. Paulo ankamudera nkhawa Timoteyo monga mwana wake ndipo anamulangiza zimene angachite ndi vuto lake la “kudwaladwala,” mwina matenda a m’mimba.​—1 Tim. 5:23; 2 Tim. 1:3, 4.

Pamene Paulo anamangidwa koyamba ku Roma, Timoteyo anali komweko ndipo ankamudikirira. Kwa kanthawi ndithu, nayenso Timoteyo anamangidwa. (Filim. 1; Aheb. 13:23) Tingadziwe zoti anthu awiriwa ankakondana kwambiri tikaona zimene Paulo analemba ataona kuti watsala pang’ono kuphedwa. Iye anamulembera Timoteyo kuti: “Yesetsa kuti ubwere posachedwapa.” (2 Tim. 4:6-9) Malemba safotokoza ngati Timoteyo anafika mlangizi wake wokondedwayu asanaphedwe kapena ayi.

MALIKO ANACHITA MAUTUMIKI OSIYANASIYANA

Buku la Uthenga Wabwino limene Maliko analemba limanena kuti anthu amene anagwira Yesu ankafunanso kugwira “mnyamata wina” koma ‘anathawa ali maliseche.’ (Maliko 14:51, 52) Popeza kuti Maliko, amenenso amadziwika ndi dzina lakuti Yohane Maliko, ndiye yekha amene analemba nkhani imeneyi, n’kutheka kuti mnyamata amene anathawa ali malisecheyo anali iyeyo. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti nthawi ina Maliko ankakumana ndi Yesu.

Maliko akumvetsera ndipo akulemba manotsi pamene munthu wachikulire akulankhula.

Patapita zaka pafupifupi 11, pa nthawi imene Herode Agiripa ankazunza Akhristu, “anthu ambiri” a mumpingo wa ku Yerusalemu anasonkhana m’nyumba ya Mariya, mayi ake a Maliko kumene ankapemphera. Ndipo mtumwi Petulo atatulutsidwa m’ndende mozizwitsa, anapita kunyumba imeneyi. (Mac. 12:12) Choncho Maliko ayenera kuti anakulira m’nyumba imene Akhristu anayamba kuchitiramo misonkhano. Zikuoneka kuti iye ankadziwa bwino ophunzira oyambirira a Yesu, ndipo ophunzirawo anamulimbikitsa mwauzimu.

Maliko anatumikira limodzi ndi oyang’anira angapo a m’mipingo yoyambirira ya Chikhristu. Mmene tikudziwira, iye anachita utumiki wake woyamba wapadera ndi msuweni wake Baranaba komanso mtumwi Paulo pamene anali ku Antiokeya wa ku Siriya. (Mac. 12:25) Baranaba ndi Paulo atayamba ulendo wawo woyamba waumishonale, Maliko anayenda nawo limodzi ndipo choyamba anapita ku Kupuro, ndipo kenako ku Asia Minor. Koma pa zifukwa zimene sizinatchulidwe m’Baibulo, Maliko anawasiya n’kubwerera ku Yerusalemu. (Mac. 13:4, 13) Monga mmene chaputala 15 cha buku la Machitidwe chimafotokozera, Baranaba ndi Paulo anasemphana maganizo chifukwa cha zimene Maliko anachitazi. Zitatero, Maliko ndi Baranaba anapita ku Kupuro kukapitiriza utumiki wawo waumishonale.​—Mac. 15:36-39.

Paulo, Baranaba ndi Maliko ayenera kuti sanasungirane chakukhosi chifukwa Maliko anatumikiranso ndi Paulo ku Roma cha m’ma 60 kapena 61 C.E. Paulo amene anali atamangidwa mumzindawu, analembera mpingo wa ku Kolose kuti: “Arisitako mkaidi mnzanga akuti moni nonse. Komanso Maliko msuweni wa Baranaba, (amene ndinakulangizani kuti mumulandire nthawi iliyonse akadzafika kwa inu).” (Akol. 4:10) Choncho Paulo ankaganiza zotumiza Yohane Maliko kuchokera ku Roma kupita ku Kolose kuti akamuimire.

Nthawi ina, mwina cha m’ma 62 mpaka 64 C.E., Maliko anatumikira limodzi ndi mtumwi Petulo ku Babulo. Monga mmene taonera m’Mutu 10 wa bukuli, abalewa anayamba kukondana kwambiri moti Petulo ankamutchula Maliko kuti “mwana wanga.”​—1 Pet. 5:13.

Kenako cha m’ma 65 C.E., pamene mtumwi Paulo anamangidwa kachiwiri ku Roma, analembera mtumiki mnzake Timoteyo amene anali ku Efeso kuti: “Ubwerenso ndi Maliko chifukwa amandithandiza pa utumiki wanga.” (2 Tim. 4:11) N’zosakayikitsa kuti atangomva zimenezi, nthawi yomweyo Maliko anayamba ulendo wobwerera ku Roma kuchokera ku Efeso. N’zosadabwitsa kuti Baranaba, Paulo ndi Petulo ankamuona Maliko kuti ndi wofunika kwambiri.

Utumiki wapadera kwambiri umene Maliko anachita unali wolemba nkhani za m’buku lake la Uthenga Wabwino mouziridwa ndi Yehova. Anthu amakhulupirira kuti nkhani zambiri zimene Maliko analemba anauzidwa ndi mtumwi Petulo. Zimenezi zikuoneka kuti ndi zoona chifukwa Maliko analemba Uthenga Wabwino umenewu m’njira yosonyeza kuti anauzidwa ndi munthu ngati Petulo, amene anaona kapena amene ankadziwa mmene zinthuzo zinachitikira. Komabe, zikuoneka kuti Maliko analemba buku la Uthenga Wabwino limeneli ali ku Roma, osati ku Babulo kumene ankatumikira ndi Petulo. Zikuonekanso kuti uthenga wa Maliko unkapita kwa anthu a mitundu ina chifukwa iye anagwiritsa ntchito mawu ambiri a Chilatini komanso anamasulira mawu a Chiheberi amene anthu omwe sanali Ayuda akanavutika kuwamva.

a Onani bokosi lakuti “Maliko Anachita Mautumiki Osiyanasiyana.”

b Onani bokosi lakuti “Timoteyo Anatumikira Ngati Kapolo ‘Pofalitsa Uthenga Wabwino.’”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena