Mafunso Ochokera kwa Owerenga
◼ Pamene anali pa mtengo, Yesu analira: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” Kodi iye analibe chikhulupiriro, kukhulupirira kuti Mulungu anamusiya iye?
Pamene tiwerenga mawu awa pa Mateyu 27:46 kapena Marko 15:34, ena amamaliza kuti pamene Yesu anayang’anizana ndi imfa yopweteka, chidaliro chake mwa Mulungu chinagwedezeka. Ena ananena kuti iri linali kokha yankho la umunthu la Yesu, kulira komvekera kwa kusowa chochita kwa munthu wa nyama ndi mwazi wovutika. Pali chifukwa chabwino, ngakhale kuli tero, kuyang’ana kupyola kawonedwe ka umunthu kameneka kozikidwa pa kuwonekera kwa kunja. Pamene palibe aliyense wa ife lerolino amene angadziwe motsimikizirika zonse zimene zinaphatikizidwamo mu kulira kwaYesu monga mmene anachitira, tingazindikire malingaliro awiri oyenerera.
Yesu anadziwa bwino kuti anayenera “kupita ku Yerusalemu ndi kuvutika ndi zinthu zambiri . . . , ndipo ndi kuphedwa, ndipo pa tsiku lachitatu kuukitsidwa.” (Mateyu 16:21) Ali kumwamba Mwana wa Mulungu anawona ngakhale anthu opanda ungwiro akukumana ndi imfa zoipa pamene anali kusunga umphumphu wawo. (Ahebri 11:36-38) Chotero palibe chifukwa cha kukhulupirira kuti Yesu—munthu wangwiro—angagwidwe ndi mantha pa zomwe anayenera kuyang’anizana nazo; imfa ya pamtengo sikanamupatsanso ganizo lakuti Atate wake anamukana iye. Yesu anadziwa pasadakhale “mtundu wa imfa imene iye akafa,“ kunena kuti, imfa mwa kupachikidwa. (Yohane 12:32, 33) lye anali wotsimikizira, ndiponso, kuti pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa. Ndimotani, ndiyeno, mmene Yesu akananenera kuti Mulungu anamutaya iye?
Choyamba, iye akanatanthauza mu lingaliro loyenerera kuti Yehova anachotsa chinjirizo kuchokera kwa Mwana wake kotero kuti umphumphu wa Yesu uyesedwe kumlingo, imfa yowawa ndi yochititsa manyazi. Koma kupulumutsidwa kwa Yesu ndi Mulungu ku mkwiyo wa adani otsogozedwa ndi Satana sikunasonyeze kumukana kotheratu. Yehova anapitiriza kusonyeza chikondi kwa Yesu, monga mmene chinatsimikizidwira pa tsiku lachitatu pamene lye anaukitsa Mwana wake, chimene Yesu anadziwa kuti chikachitika.—Machitidwe 2:31-36; 10:40; 17:31.
Chogwirizana ku zokambidwazi chiri chifukwa chachiwiri choyenerera kaamba ka mawu a Yesu pamene anali pamtengo, kuti mwakugwiritsira ntchito mawu amenewa iye akakwaniritse chisonyezero cha ulosi wonena za Mesiya. Maora ambiri pasadakhale Yesu anauza atumwi kuti zinthu zikachitika “monga mmene kwalembedwera ponena za iye.” (Mateyu 26:24; Marko 14:21) Inde, iye anafuna kuchita zinthu zomwe zinalambedwa, kuphatikizapo zinthu za mu Masalmo 22. Mungachipeze icho kukhala chovumbulutsa kuyerekeza Masalmo 22:7, 8—Mateyu 27:39, 43; Masalmo 22:15—Yohane 19:28, 29; Masalmo 22:16—Marko 15:25 ndi Yohane 20:27; Masalmo 22:18—Mateyu 27:35. Masalmo 22, yomwe inapereka zisonyezero zambiri zaulosi za zokumana nazo za Mesiya limayamba: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?“ Chotero, pamene Yesu analira monga mmene anachitira, iye anali kuwonjezera ku mbiri ya maulosi omwe iye anakwaniritsa.—Luka 24:44.
Wa masalmo sanakhulupirire kuti Mulungu wake anangomuleka kokha kapena kumukana iye, popeza Davide anapitiriza kunena kuti iye ’adzalalikira dzina la Mulungu kwa abale ake,’ ndi kufulumiza ena kulemekeza Yehova. (Masalmo 22:22, 23) Mofananamo, Yesu, yemwe anadziwa Masalmo 22 bwino lomwe, analinso ndi chifukwa kaamba ka chidaliro kuti Atate wake anamuvomerezabe ndi kumukonda iye, mosasamala kanthu za zimene Mulungu anamulola iye kukumana nazo pa mtengo.