Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 2/1 tsamba 8-9
  • Nkhani ya Mwana Wotaika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani ya Mwana Wotaika
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Fanizo la Mwana Woloŵerera
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mwana Wotayika Anabwerera
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Pamene Mwana Wotayika Apezeka
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Yehova, Mulungu Wachifundo ndi Wachisomo”
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 2/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Nkhani ya Mwana Wotaika

AFARISI asuliza Yesu chifukwa cha kukhala ndi ochimwa odziŵika, ndipo  m’kuyankha iye wangotha kumene kulongosola mafanizo onena za kupeza nkhosa yotaika ndi kobiri lotaika. Iye akupitiriza tsopano ndi fanizo lina, ilo lonena za atate wachikondi ndi kuchita kwake kwa ana ake aŵiri, aliyense wa amene ali ndi zophophonya zazikulu.

Choyamba, pali mwana wam’ng’ono, wotengamo mbali wokulira wa fanizolo. Iye asonkhanitsa chuma chake, chomwe chapatsidwa kwa iye mosasinkhasinkha ndi atate wake. Iye kenaka achoka panyumba ndi kukhala woloŵetsedwa m’njira ya moyo ya makhalidwe oipa kwambiri. Koma mvetserani pamene Yesu akulongosola nkhaniyo, ndi kuwona ngati mungagamulepo amene anthuwo akutanthauza kuimira.

“Munthu wina,” Yesu akuyamba tero, “anali ndi ana amuna aŵiri. Ndipo wam’ng’onoyo anati kwa atate wake, ‘Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu.’ Ndipo [atateyo] anagawira za moyo wake.” Kodi nchiyani chimene wam’ng’onoyo akuchita ndi zimene walandira?

“Ndipo,” Yesu akulongosola tero, “pakupita masiku oŵerengeka, mwana wam’ng’onoyo anasonkhanitsa zonse napita ulendo wake ku dziko lakutali, ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitaiko.” Chenicheni chiri chakuti, iye akutsiriza ndalama zake mwa kukhala ndi achigololo. Pambuyo pake nthaŵi zovuta zibwera, monga mmene Yesu akupitiriza kusimba kuti:

“Ndipo pamene atatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m’dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa. Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija, ndipo uyu anamutumiza kubusa kwake kukaweta nkhumba. Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.”

Kunali kuchepetsedwa kotani nanga kukakamizidwa kutenga ntchito yoweta nkhumba, popeza kuti nyama zimenezi zinali zodetsedwa mogwirizana ndi Chilamulo! Koma chimene chinawawitsa mwana wamwamunayo mokulira chinali njala yowawitsa imene inakhoza ngakhale kumpangitsa kulakalaka zakudya zomwe zinadyetsedwa kwa nkhumba. Chifukwa cha tsoka lake loipitsitsa, Yesu ananena kuti, “anakumbukira mu mtima.”

Akumapitiriza nkhani yake, Yesu akulongosola kuti: “Anati [kwa iyemwini], ‘Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndiwonongeke kuno ndi njala! Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga ndipo ndidzanena naye: “Atate, ndinachimwira kumwamba ndi pamaso panu. Sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu. Mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu.”’ Ndipo iye ananyamuka nadza kwa atate wake.”

Pano pali chinachake choyenera kulingalira: Ngati atate wake anamtembenukira iye ndi kufuula mwaukali pa iye pamene iye anachoka panyumba, mwana wamwamunayo mwachidziŵikire sakanakhoza kukhala wa malingaliro amodzi chotero ponena za chimene iye akachita. Iye akanagamulapo kubwerera ndi kuyesera kupeza ntchito kwinakwake m’dziko la kumudzi kwawo kotero kuti sakanakhoza kuyang’anizana ndi atate wake. Ngakhale kuli tero, palibe ganizo lirilonse loterolo linaloŵa m’malingaliro ake. Kumudzi ndi kumene iye anafuna kukhala!

Mwachiwonekere, atate m’fanizo la Yesu amaimira Atate wathu wakumwamba wachikondi, wachifundo, Yehova Mulungu. Ndipo inu mwinamwake mumazindikiranso kuti mwana wotaika, kapena wolowerera, amaimira ochimwa odziŵika. Afarisi, kwa amene Yesu akulankhula, anali atasuliza Yesu papitapo chifukwa cha kudya ndi amenewa.

Koma kodi ndani yemwe mwana wamkulu amaimira? Ndipo kodi ndi kugwiritsiridwa ntchito kotani kumene fanizo la Yesu liri nako m’zana lathu la 20? Kope lathu lotsatira la magazini iyi lidzayankha mafunso amenewa pamene lilingalira yotsalira ya nkhani ya Yesu yonena za mwana wamwamuna wotaika yemwe anapezeka. Luka 15:11-20, 30; Levitiko 11:7, 8.

◆ Kodi ndi kwayani kumene Yesu akuwuza fanizo limeneli, kapena nkhani, ndipo nchifukwa ninji?

◆ Kodi ndani yemwe ali wotengamo mbali wokulira m’nkhaniyi, ndipo nchiyani chomwe chikuchitika kwa iye?

◆ Kodi ndani yemwe atate ndi mwana wam’ng’ono akuimira?

◆ Kodi ndi chidziŵitso chotani chomwe tingayembekezere m’kope lotsatira la magazini ino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena