Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Pamene Mwana Wotayika Apezeka
    Nsanja ya Olonda—1989 | February 15
    • Pa nthaŵiyo, “mwana wamkulu wa [atateyo] anali kumunda.” Onani ngati mungazindikire amene iye akuimira mwa kumvetsera ku yotsalira ya nkhaniyo. Yesu akunena za mwana wamkuluyo: “Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba anamva kuyimba ndi kuvina. Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata namfunsa zinthu izi nzotani. Ndipo uyu anati kwa iye, ‘M’ng’ono wako wafika, ndipo atate wako anapha mwana wa ng’ombe wonenepa, chifukwa anamulandira iye wamoyo.’ Koma anakwiya ndipo sanafuna kuloŵamo.

      “Ndipo atate wake anatuluka namudandaulira. Koma anayankha nati kwa atate wake, ‘Onani ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthaŵi iriyonse, ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wambuzi kuti ndisekere ndi abwenzi anga. Koma pamene anadza mwana wanu uyu wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munaphera iye mwana wa ng’ombe wonenepa.’”

      Ndani, mofanana ndi mwana wamkulu, wakhala wosuliza za chifundo ndi chisamaliro choperekedwa kwa ochimwa? Kodi si alembi ndi Afarisi? Popeza chiri chisulizo chawo cha Yesu chifukwa iye akulandira ochimwa chomwe chadzutsa fanizo limeneli, iwo mwachimvekere ayenera kukhala amene akuimiridwa ndi mwana wamkuluyo.

  • Pamene Mwana Wotayika Apezeka
    Nsanja ya Olonda—1989 | February 15
    • Koma ndani mu nthaŵi zamakono amene akuimira ana aŵiri amenewo? Chiyenera kukhala awo omwe adziŵa mokwanira ponena za zifuno za Yehova kukhala ndi maziko kaamba ka kulowa kwawo mu unansi ndi iye. Mwana wamkulu amaimira ziwalo zina za “kagulu ka nkhosa,” kapena “mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m’mwamba.” Awa anatengera mkhalidwe wofanana ndi uja wa mwana wamkulu. Iwo analibe chikhumbo cha kulandira gulu la pa dziko lapansi, “nkhosa zina,” omwe anawalingalira kukhala anali kuba chidziŵitso.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena