Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 6 tsamba 20-tsamba 21 ndime 8
  • Mwana Amene Mulungu Analonjeza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwana Amene Mulungu Analonjeza
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Mwana wa Lonjezo
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • ‘Anaganizira Tanthauzo la Mawu Onsewo Mumtima Mwake’
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • ‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 6 tsamba 20-tsamba 21 ndime 8
Simiyoni wanyamula Yesu ali wakhanda ndipo Yosefe, Mariya ndiponso Ana, yemwe anali mneneri, akuyang’ana mwanayo

MUTU 6

Mwana Amene Mulungu Analonjeza

LUKA 2:21-39

  • YESU ANADULIDWA KENAKO ANAPITA NAYE KU KACHISI

Yosefe ndi Mariya anakhalabe ku Betelehemu m’malo mobwerera kwawo ku Nazareti. Atatha masiku 8, Yesu anadulidwa potsatira zimene Chilamulo cha Mulungu chinkanena. (Levitiko 12:2, 3) Pa nthawiyo unali mwambo kuti mwana wamwamuna azipatsidwanso dzina pa tsiku limeneli. Choncho, anapatsa mwana wawo dzina lakuti Yesu potsatira zimene mngelo uja anawauza.

Kenako patatha masiku 40, Yosefe ndi Mariya anapita ndi Yesu kukachisi ku Yerusalemu. Kuchokera ku Betelehemu kupita kukachisiko unali ulendo wa makilomita ochepa. Iwo anapita kukachisiko chifukwa chakuti Chilamulo chinkanena kuti pakadutsa masiku 40 kuchokera pamene mkazi wabereka mwana wamwamuna, mkaziyo azikapereka nsembe kukachisi n’cholinga choti ayeretsedwe.—Levitiko 12:4-8.

Pokapereka nsembeyo, Mariya anatenga timbalame tiwiri. Zimenezi zikutithandiza kudziwa mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Chilamulo chinkanena kuti munthu azipereka mwana wa nkhosa ndi mbalame ngati nsembe yoyeretsa. Koma ngati mkaziyo sakwanitsa kupereka mwana wa nkhosayo, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda. Ndipo izi n’zimene Mariya anachita chifukwa anali wosauka.

‘MASIKU AKUTI AYERETSEDWE ANAKWANIRA’

Yosefe ndi Mariya apita kukachisi ndi Yesu ali wakhanda kukapereka nsembe yakudziyeretsa

Akazi achiisiraeli ankati akabereka mwana, ankaonedwa kuti ndi odetsedwa kwa masiku angapo. Masikuwo akatha, ankafunika kupereka nsembe yopsereza kuti ayeretsedwe. Zimenezi zinkawakumbutsa kuti iwowo ndi ochimwa komanso kuti mwana amene aberekayo ndi wochimwa. Koma Yesu anabadwa ali woyera komanso analibe uchimo. (Luka 1:35) Ngakhale zinali choncho, Yosefe ndi Mariya “anapita naye” kukachisi kuti ‘iwo akayeretsedwe’ potsatira zimene Chilamulo chinkanena.—Luka 2:22.

Ali kukachisiko munthu wina wachikulire dzina lake Simiyoni, anafika pamene panali Yosefe ndi Mariya. Mulungu anali atamuululira kuti asanamwalire adzaona Khristu, yemwe ndi Wodzozedwa wa Yehova kapena kuti Mesiya. Pa tsiku limeneli mzimu woyera unatsogolera Simiyoni kuti apite kukachisi kumene anakapeza Yosefe ndi Mariya komanso Yesu ali wakhanda. Kenako Simiyoni ananyamula mwanayo.

Atamunyamula, Simiyoni anathokoza Mulungu kuti: “Tsopano, Ambuye Wamkulu Koposa, mukulola kapolo wanu kupita mu mtendere malinga ndi zimene inu munanena. Chifukwa maso anga aona njira yanu yopulumutsira imene mwakonzeratu pamaso pa mitundu yonse ya anthu. Maso anga aona kuwala kochotsa nsalu yophimba mitundu ya anthu ndi ulemerero wa anthu anu Aisiraeli.”—Luka 2:29-32.

Atamva zimenezi, Yosefe ndi Mariya anadabwa kwambiri. Simiyoni anawadalitsa ndipo anauza Mariya kuti mwana wakeyo “waikidwa kuti ambiri agwe, ndiponso kuti ambiri adzukenso mu Isiraeli.” Anamuuzanso kuti chisoni chachikulu ngati lupanga lalitali chidzalasa moyo wake.—Luka 2:34.

Munthu wina amene analinso kukachisiko ndi Anna, mneneri wamkazi wazaka 84. Iye ankapezeka pakachisi nthawi zonse. Nayenso anapita pamene panali Yosefe ndi Mariya n’kuyamba kuthokoza Mulungu komanso kulankhula zokhudza Yesu kwa anthu ena omwe analipo.

Yosefe ndi Mariya ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi zimene zinachitikazi ndipo zinawatsimikizira kuti mwana wawo analidi amene Mulungu analonjeza kuti adzabadwa.

  • Kodi mwana wamwamuna wachiisiraeli ankapatsidwa dzina pa nthawi iti?

  • Kodi mzimayi ankayenera kuchita chiyani mwana wake wamwamuna akatha masiku 40? Kodi nsembe zimene Mariya anapereka zinasonyeza kuti zinthu zinali bwanji pa moyo wawo?

  • Yosefe ndi Mariya atapita kukachisi, kodi ndani amene anazindikira Yesu, nanga anachita chiyani posonyeza kuti amuzindikira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena