-
Anazindikira Chikhumbo cha Mtima WakeNsanja ya Olonda—1994 | March 15
-
-
Mulungu waika mzimu wake woyera pa Simeoni ndipo wamfupa ndi vumbulutso. Simeoni sadzafa kufikira ataona Amene adzakhala Mesiya. Koma pakupita masiku ndi miyezi. Simeoni akukalamba ndipo sangayembekezere konse kukhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali. Kodi lonjezo la Mulungu kwa iye lidzakwaniritsidwa?
-
-
Anazindikira Chikhumbo cha Mtima WakeNsanja ya Olonda—1994 | March 15
-
-
Simeoni ali ndi chikondwerero chotani nanga pamene akutenga mwanayo Yesu m’manja mwake! Ameneyu adzakhala Mesiya wolonjezedwayo—“Kristu wa Yehova.” (NW) Pausinkhu waukalamba umenewo, Simeoni sangayembekezere kuona Yesu akukwaniritsa ntchito Yake yapadziko lapansi. Komabe, nkokondweretsa kumuona monga khanda. Maulosi Aumesiya akuyamba kukwaniritsidwa. Simeoni ngwachimwemwe chotani nanga! Adzakhala wokhutira tsopano kugona tulo ta imfa kufikira chiukiriro.—Luka 2:25-28.
-