Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu Aphunzitsa ku Yeriko
MWAMSANGA Yesu ndi makamu oyenda limodzi naye akufika ku Yeriko, umene uli mzinda chifupifupi ulendo wa tsiku limodzi kuchokera ku Yerusalemu. Mwachiwonekere Yeriko uli mzinda wambali ziŵiri, mzinda wakale Wachiyuda wokhala chifupifupi kilomita imodzi ndi theka kuchokera ku mzinda Wachiroma watsopanowo. Pamene makamuwo akutuluka mu mzinda wakalewo ndi kuyandikira watsopanowo, akhungu aŵiri opemphapempha akumva mkupitiwo. Mmodzi wa iwo akutchedwa Bartimeyu.
Atamva kuti ali Yesu amene akupita, Bartimeyu ndi mnzake akuyamba kufuula kuti: “Mutichitire ife chifundo, inu Mwana wa Davide.” Pamene khamulo liwawuza iwo mwaukali kukhala chete, iwo akufuuladi mowonjezereka mwamawu apamwamba kuti: “Ambuye, mutichitire chifundo, inu Mwana wa Davide.”
Atamva phokosolo, Yesu akuima. Napempha amene ali naye kuitana ofuulawo. Amenewa akupita kwa akhungu opemphapemphawo nati kwa mmodzi wa iwo: “Limba mtima; nyamuka, akuitana.” Monyanyuka kwambiri, munthu wakhunguyo akutaya chofunda chake, kulumpha ndi mapazi ake, ndi kumka kwa Yesu.
“Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” (NW) Yesu akuwafunsa amuna aŵiriwo.
“Kuti maso athu apenye.” Iwo akuchonderera.
Pogwidwa ndi chifundo, Yesu akugwira maso awo. Mogwirizana ndi cholembera cha Marko, Yesu akunena kwa mmodzi wa iwo kuti: “Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.” Pomwepo akhungu opemphapemphawo ayambanso kuwona, ndipo mosakaikira aŵiriwo ayamba kulemekeza Mulungu. Pamene anthu onse awona chimene chachitika, nawonso alemekeza Mulungu. Mosazengereza, Bartimeyu ndi mnzake ayamba kutsatira Yesu.
Pamene Yesu adutsa m’Yeriko, makamuwo akuchulukitsitsa. Aliyense akufuna kuwona amene wachiritsa amuna akhunguwo. Anthu akukankhanakankhana kumka kwa Yesu kuchokera ku mbali zonse, ndipo monga chotulukapo, ena sakhoza ngakhale kuwona chideru chake. Pakati pa amenewa pali Zakeyu, mkulu wa osonkhetsa msonkho mkati ndi kuzungulira Yeriko. Iye ngwamfupi kwambiri kotero kuti sakuwona zimene zikuchitika.
Chotero Zakeyu athamangira kutsogolo ndi kukwera mtengo wa mkuyu pa njira imene Yesu akudzera. Kuchokera pa malo apamwamba amenewa, iye angathe kuwona zonse bwino lomwe. Pamene makamuwo ayandikira, Yesu akuitana pamwamba mu mtengo kuti: “Zakeyu, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m’nyumba mwako.”
Zakeyu akutsikira pansi mwachisangalalo ndi kufulumira kupita kunyumba kukakonzekera zinthu kaamba ka mlendo wake wapadera. Koma pamene anthu awona zimene zikuchitika, iwo onse akuyamba kung’ung’udza. Akulingalira kuti kuli kosayenera kuti Yesu akhale mlendo wa munthu wotero. Mwawona nanga, Zakeyu anakhala wachuma mwa kuba ndalama mosawona mtima pa ntchito yake yokhometsa msonkho.
Anthu ambiri akutsatira, ndipo pamene Yesu akuloŵa m’nyumba ya Zakeyu, iwo akudandaula: “Analoŵa amchezere munthu ali wochimwa.” Komabe Yesu akuwona kuthekera kwa kulapa mwa Zakeyu. Ndipo Yesu sakutaya mtima, popeza kuti Zakeyu akuimirira nalengeza kuti: “Tawonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga ndimbwezera kanayi.”
Zakeyu akutsimikizira kuti kulapa kwake kuli kuwona mtima mwa kupatsa theka la zinthu zake kwa osauka ndi kugwiritsira ntchito theka lina kubwezera amene iye anawanyenga. Mwachiwonekere iye akhoza kuŵerengera kuchokera pa zolembapo zake za misonkho kuti kwenikweni ndi zingati zimene iye ali nazo monga mangawa kwa anthu amenewa. Chotero iye akulumbira kubwezera kuwirikiza kanayi, mogwirizana ndi lamulo la Mulungu limene limanena kuti: ‘Ngati munthu waba nkhosa, iye ayenera kulipira nkhosa zinayi kaamba ka nkhosayo.’
Yesu akusangalatsidwa ndi njira imene Zakeyu akulonjeza kugawa chuma chake, popeza Iye akuti: “Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu. Pakuti Mwana wa munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”
Osati kale kwambiri, Yesu anali atayerekezera mkhalidwe wa ‘otayika’ ndi fanizo lake la mwana woloŵerera. Tsopano tiri ndi chitsanzo chenicheni cha munthu wotayika amene wapezedwa. Ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo ndi otsatira awo akung’ung’udza ndi kudandaula ponena za chisamaliro cha Yesu kwa anthu onga Zakeyu, Yesu akupitirizabe kufunafuna ndi kubwezeretsa ana otayika a Abrahamu amenewa. Mateyu 20:29-34; Marko 10:46-52; Luka 18:35–19:10; Eksodo 22:1.
◆ Kodi nkuti kumene, Yesu mwachiwonekere akutsagana ndi akhungu opemphapemphawo, ndipo kodi akuwachitiranji?
◆ Kodi Zakeyu ndani, ndipo kodi nchifukwa ninji iye akwera mtengo?
◆ Kodi Zakeyu akutsimikizira motani kulapa kwake?
◆ Kodi ndi phunziro lotani limene tingaphunzire kuchokera ku kachitidwe ka Yesu kwa Zakeyu?