Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2020 | Na. 2
    • Yesu ananena kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala m’malo osiyanasiyana.” (Luka 21:10, 11) Zinthu zimenezi ndi zomwe Yesu ananena kuti zikadzachitika pa nthawi yofanana, zidzakhala chizindikiro choti “ufumu wa Mulungu wayandikira.” Kodi pali umboni wakuti zinthu zimenezi zikuchitika pa nthawi imodzi komanso padziko lonse? Taganizirani izi.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2020 | Na. 2
    • 2. ZIVOMEZI

      Chivomezi chikuwononga nyumba.

      Buku lina limanena kuti chaka chilichonse kumachitika zivomezi zamphamvu pafupifupi 100 “zowononga kwambiri.” (Britannica Academic) Ndipotu lipoti la bungwe lina lofufuza za nthaka ndi miyala linanena kuti “tikatengera mmene zivomezi zakhala zikuchitikira kuyambira m’ma 1900, tikuyembekezera kuti kutsogoloku kuzichitikanso zivomezi zina zamphamvu kwambiri pafupifupi 16 chaka chilichonse.” (United States Geological Survey) Anthu ena akhoza kuganiza kuti zivomezi zikuoneka kuti zikuwonjezereka chifukwa choti akatswiri apeza njira zapamwamba zochitira kafukufuku. Ngakhale zili choncho, zoona n‘zakuti panopa zivomezi zamphamvu zikubweretsa mavuto komanso kuphetsa anthu ambiri padziko lonse.

      3. KUSOWA KWA CHAKUDYA

      Mzere wosonyeza kuti chakudya chimene anthu akukolola chikucheperachepera.

      Padziko lonse lapansi, chakudya chimasowa chifukwa cha nkhondo, chinyengo, mavuto aakulu azachuma, kusachita bwino kwa zaulimi kapenanso kusakonzekera bwino mavuto azanyengo. Lipoti la 2018 la nthambi ya UN yoona za chakudya padziko lonse linanena kuti: “Padziko lonse, anthu 821 miliyoni alibe chakudya chokwanira ndipo pa anthu amenewa 124 miliyoni alibiretu chakudya.” Matenda osowa zakudya m’thupi achititsa kuti ana pafupifupi 3.1 miliyoni azimwalira chaka chilichonse. Mu 2011, ana pafupifupi 45 pa 100 alionse, anamwalira chifukwa cha matendawa.

      4. MATENDA KOMANSO MILIRI

      Zizindikiro zosonyeza mankhwala odwalitsa anthu komanso mabakiteriya.

      Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena kuti: “Zaka za m’ma 2000, kwakhala kukuchitika miliri yoopsa. Matenda akale monga kolera ndi chikasu ayambiranso kuvutitsa anthu ndipo pabweranso ena atsopano monga SARS, chimfine choopsa, matenda obanika a MERS, Ebola ndi Zika.” Posachedwapa kwabwera mliri wa COVID-19. Ngakhale kuti madokotala ndi asayansi aphunzira zambiri zokhudza matenda, akulephera kuthana ndi matenda onse.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena