-
Dziko Lopanda MatendaGalamukani!—2004 | June 8
-
-
Kodi tingayembekezere kuti Ufumu wa Mulungu udzabwera liti? Poyankha funso limenelo, Yesu ananeneratu kuti anthu a padziko lapansi adzaona zinthu zofunika kwambiri zikuchitika zimene zidzakhale chizindikiro chosonyeza kuti Ufumuwo watsala pang’ono kuchitapo kanthu. Iye anati chimodzi mwa zizindikiro zimenezi chidzakhala kugwa kwa “miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:10, 11; Mateyu 24:3, 7) Liwu lachigiriki limene analimasulira kuti “miliri” limatanthauza “nthenda iliyonse yakupha yopatsirana.” M’zaka za m’ma 1900 miliri yoipa kwambiri inagwadi m’madera ambiri, ngakhale kuti sayansi ya zamankhwala yapita patsogolo.—Onani bokosi lakuti “Anthu Omwalira ndi Miliri Chiyambire 1914.”
Ulosi umene uli m’buku la Chivumbulutso, umene umafanana ndi mawu a Yesu opezeka m’Mauthenga Abwino, umasonyeza anthu angapo okwera akavalo ali ndi Yesu Kristu pamene akuyamba kulamulira kumwamba. Munthu wachinayi anakwera “kavalo wotumbuluka,” ndipo anasiya “imfa” m’mbuyo mwake. (Chivumbulutso 6:2, 4, 5, 8) Tikaona anthu amene afa ndi matenda ena akuluakulu opatsirana chiyambire 1914 tingatsimikizedi kuti wokwera pakavalo wophiphiritsira ameneyu wakweradi kavaloyo. Kuvutika ndi “imfa” padziko lonse ndi umboni winanso wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi kubwera.b—Marko 13:29.
-
-
Dziko Lopanda MatendaGalamukani!—2004 | June 8
-
-
[Bokosi patsamba 28]
Anthu Omwalira ndi Miliri Chiyambire 1914
Ziŵerengero zili m’munsizi n’zongoyerekezera. Komabe, zikusonyeza mmene miliri yavutitsira anthu chiyambire 1914.
◼ Nthomba (pakati pa 300 miliyoni ndi 500 miliyoni) Palibe mankhwala ochiza nthomba amene anakonzedwapo. Katemera wapadziko lonse ndi amene pomalizira pake anathetsa nthendayi pofika mu 1980.
◼ TB (pakati pa 100 miliyoni ndi 150 miliyoni) TB tsopano imapha anthu pafupifupi 2 miliyoni chaka chilichonse, ndipo pafupifupi munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse ali ndi kachilombo koyambitsa TB m’thupi mwake.
◼ Malungo (pakati pa 80 miliyoni ndi 120 miliyoni) M’zaka zoyambirira za m’ma 1900, anthu ofa ndi malungo anali pakati pa 2 miliyoni chaka chilichonse. Kum’mwera kwa Sahara ku Africa kuno n’kumene anthu amafa kwambiri ndi malungo, ndipo kudera limeneli malungo akuphabe anthu opitirira wani miliyoni chaka chilichonse.
◼ Fuluwenza ya ku Spain (pakati pa 20 miliyoni ndi 30 miliyoni) Olemba mbiri ena akuganiza kuti anthu amene anafa ndi ambiri kuposa pamenepa. Mliri wakupha umenewu unavutitsa anthu padziko lonse mu 1918 ndi 1919, nkhondo yoyamba yapadziko lonse itangotha kumene. Buku lakuti Man and Microbes linati: “Ngakhale mliri wa makoswe sunaphe anthu ambiri choncho m’kanthaŵi kochepa kotero.”
◼ Nthenda yofanana ndi tayifodi (pafupifupi 20 miliyoni) Miliri ya nthenda imeneyi nthaŵi zambiri inkagwa panthaŵi yankhondo, ndipo panthaŵi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse mliri wa nthenda imeneyi unavutitsa anthu m’mayiko a kum’maŵa kwa Ulaya.
◼ Edzi (kupitirira 20 miliyoni) Mliri wamakonowu tsopano ukupha anthu 3 miliyoni chaka chilichonse. Ziwerengero zoyerekezera za bungwe la United Nations loona za Edzi zikusonyeza kuti “ngati sipakhala kuyesetsa kwakukulu kofuna kupeŵa ndi kuchiza nthendayi, anthu 68 miliyoni adzafa . . . m’zaka za pakati pa 2000 ndi 2020.”
-