Njala Inanenedweratu
M’ZAKA zaposachedwapa vuto la njala lakhala lofala movutitsa maganizo m’malipoti a nkhani za padziko lonse. Kuchokera ku Ethiopia ndi malo ena kwadza nkhani zosaiŵalika za kuvutika kwa anthu. Mu 1992 dziko linasumika maganizo pa anthu ovutika ndi kufa ndi njala mu Somalia, imene inakhalapo chifukwa cha chilala ndi nkhondo. International Herald Tribune inasimba mu September 1992 kuti: “Palibe amene akudziŵa za chiŵerengero cha anthu a ku Somalia amene afa, koma gulu la Red Cross linatchula chiŵerengerocho kukhala chopitirira 100,000. Anthu mazana ambiri, ndipo mwina zikwi zambiri, amafa tsiku ndi tsiku.”
Ziŵerengerozo sizimafotokoza kwenikweni nsautso ndi mavuto za anthu amene amaloŵetsedwamo. Yvette Pierpaoli, nthumwi ya ku Ulaya ya Refugees International, analemba m’magazini a Mitundu Yogwirizana otchedwa Refugees kuti: “Mu New York kapena m’Geneva, nkhani ya anthu othaŵa kwawo njodziŵika; ziŵerengero zimatchulidwa zokhala ndi mazero ovuta kudziŵa chiŵerengerocho. Komano kumaiko akutali mamailo zikwi zambiri, kumene zinthu zili zosalamulirika, munthuwe umachita kakasi ndipo ukulu wa mavuto ungakuchititse kufuna kulira.”
Pamene kuli kwakuti gulu la Red Cross likunena kuti zoyesayesa zake kuthandiza Somalia ndizo ntchito yaikulu koposa yothandiza anthu imene sinachitidwepo, openyerera ambiri akudandaula kuti mkhalidwe wake wa zinthu wonsewo ngwachithandizo chochepa ndiponso chochedwa kwambiri. Pierpaoli akudandaula kuti: “Maiko opereka chithandizo ngosafunitsitsa kupitiriza kutero, iwo atopa kuchilikiza Afirika amene akusweka. . . . Amaimba mlandu anthu a mu Afirika chifukwa cha kayendetsedwe kawo ka zinthu koipa, umbombo wa atsogoleri awo, mikangano yowonekera kukhala yosatha.”
Baibulo linaneneratu za nthaŵi pamene kudzakhala kupereŵera kwa chakudya “m’malo akutiakuti.” Kupereŵera kwa chakudya kumeneku, limodzi ndi zochitika zina zambiri, monga nkhondo, zivomezi, ndi miliri, zimasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. (Luka 21:11, 31) Baibulo limasonyezanso kuti pansi pa Ufumu wa Mulungu wabwino umenewu, padzakhala chakudya chochuluka kwa anthu onse. “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pamapiri,” analemba motero wamasalmo.—Salmo 72:16.