-
Kaisareya ndi Akristu OyambiriraNsanja ya Olonda—1989 | March 15
-
-
Ndiponso m’chipindachi muli ndalama ziŵiri zazing’ono za mkuwa zomwe ziri zokondweretsa mopambanitsa. Yoyambayo (kulamanja) iri ndi mawu ozokotedwa akuti: “Chaka chachiŵiri cha ufulu wa Ziyoni.” Pa yachiŵiri pali mawu akuti: “Chaka chachinayi ku chipulumutso cha Ziyoni.” Ophunzira amaika deti ndalama zimenezi kukhala 67 C.E. ndi 69 C.E. “Ufulu” wolozeredwakowo unali nyengo mkati mwa imene Ayuda anatenga Yerusalemu, pambuyo pakuti Cestius Gallus anachotsa magulu ake owukira Achiroma m’chaka cha 66 C.E.
Kubwerera kumeneko kunapangitsa kuthaŵa kuchoka m’Yerusalemu kukhala kothekera. Anthu omwe anakhulupirira mwa Yesu anathaŵa, popeza iye anali atanena mwachindunji kuti: “Koma pamene paliponse mudzawona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire ku mapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asaloŵemo.” (Luka 21:20, 21) Mwachiwonekere, opanga a ndalama “za chilakiko” zimenezi anali ndi lingaliro lochepera ponena za chiwonongeko chomwe chinawayembekezera iwo!
-
-
Kaisareya ndi Akristu OyambiriraNsanja ya Olonda—1989 | March 15
-
-
Courtesy of the Natural History Museum of Los Angeles County
-