Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/03 tsamba 1
  • ‘Khalani Okonzekeratu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Khalani Okonzekeratu’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Tumikirani Yehova popanda Chochenjeneketsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Kodi Tikudikira—Tikumapeŵa Zochenjenetsa?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Khalani Okonzekeratu Tsiku la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 11/03 tsamba 1

‘Khalani Okonzekeratu’

1 Mu ulosi wake wapadera wonena za mapeto a dziko lapansi lino, Yesu anachenjeza kuti tizipeŵa kukondetsa zinthu zopanda pake pamoyo. (Mat. 24:36-39; Luka 21:34, 35) Popeza chisautso chachikulu chingayambe nthaŵi ina iliyonse, n’kofunika zedi kuti timvere langizo la Yesu lakuti: ‘Khalani okonzekeratu; chifukwa nthaŵi imene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.’ (Mat. 24:44) Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi?

2 Kuthana ndi Nkhaŵa Ndiponso Zopinga: Umodzi mwa misampha yauzimu imene tiyenera kupeŵa ndi “zosamalira za moyo uno.” (Luka 21:34) M’mayiko ena, umphaŵi, ulova, ndiponso kukwera mitengo kwa zinthu kumapangitsa kuti kupeza zinthu zofunika kwambiri pamoyo wa munthu kukhale kovuta. M’mayiko ena, anthu ambiri amafuna kupeza chuma. Ngati tidera nkhaŵa kwambiri zopeza chuma, sitingaike maganizo athu pa zinthu za Ufumu. (Mat. 6:19-24, 31-33) Misonkhano yachikristu imatithandiza kuikabe maganizo athu pa zinthu za Ufumu. Kodi chimakhala cholinga chanu kupezeka pa misonkhano yonse?—Aheb. 10:24, 25.

3 Dziko masiku ano lili ndi zopinga zambiri zimene zingatibere mosavuta nthaŵi yamtengo wapatali. Maola ambiri angathere pa wailesi ya kanema, mafilimu, pa zinthu zimene timakonda kuchita pa nthaŵi yongokhala, kuŵerenga mabuku a kudziko, kuyenda solo, bawo, ntchuwa, ndiponso kuchita maseŵero olimbitsa thupi, n’kutisiyira nthaŵi kapena mphamvu zochepa zochitira zinthu zauzimu. Ngakhale kuti kusangalala ndi kupuma zingatitsitsimule pang’ono, kuphunzira Baibulo patokha ndiponso ndi banja kuli ndi phindu losatha. (1 Tim. 4:7, 8) Kodi tsiku lililonse mumapatula nthaŵi yoti musinkhesinkhe Mawu a Mulungu?—Aef. 5:15-17.

4 Tiyenera kuyamikira kwambiri kuti gulu la Yehova lakonza pulogalamu ya malangizo auzimu kuti itithandize ‘kulimbika kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.’ (Luka 21:36) Tigwiritsetu ntchito mokwanira zinthu zimenezi ndipo ‘tikhale okonzekeratu’ kuti chikhulupiriro chathu chikhale ‘chochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Kristu.’—1 Pet. 1:7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena