Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu
    Nsanja ya Olonda—2003 | April 1
    • “Adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi [chitanthauza, NW] thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.”​—Luka 22:19.

      Pamene Yesu anatenga mkatewo nanena kuti “ichi chitanthauza thupi langa,” amasonyeza kuti mkate wopanda chotupitsawo unali kuimira, kapena unali chizindikiro, cha thupi lake lanyama lopanda uchimo, limene analipereka kuti “[li]khale moyo wa dziko lapansi.” (Yohane 6:51) Ngakhale kuti mabaibulo ena amanena kuti “ichi ndi [Chigiriki, es·tinʹ] thupi langa,” buku lolembedwa ndi Thayer lotchedwa Greek-English Lexicon of the New Testament limati verebu limeneli nthaŵi zambiri limatanthauza ‘kutanthauza kapena kuimira.’ Pa Chigiriki, munthu akamva liwu limeneli amaganiza za kuimira, kapena kuyerekezera.​—Mateyu 26:26, NW.

  • Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu
    Nsanja ya Olonda—2003 | April 1
    • [Bokosi/​Zithunzi patsamba 6]

      KODI TITI “ICHI NDI THUPI LANGA” KAPENA “ICHI CHITANTHAUZA THUPI LANGA?”

      Pamene Yesu ananena kuti “Ine ndine khomo” komanso, “Ine ndine mpesa weniweni,” palibe amene anaganiza kuti Yesu anali khomo lenileni kapena mpesa weniweni. (Yohane 10:7; 15:1) Momwemonso, pamene Baibulo limanena kuti Yesu anati: “Chikho ichi ndi pangano latsopano,” sitiganiza kuti chikhocho n’chimene chili pangano latsopanolo. N’chimodzimodzinso pamene ananena kuti mkate ‘unali’ thupi lake, m’posachita kufunsa kuti mkatewo umatanthauza, kapena umaimira, thupi lake. N’chifukwa chake Baibulo la Charles B. Williams limati: “Ichi chikuimira thupi langa.”​—Luka 22:19, 20.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena