Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chakudya Chamadzulo cha Ambuye—Kodi Chiyenera Kuchitidwa Kangati?
    Nsanja ya Olonda—1994 | March 15
    • Phwando Limodzilo

      Kuchitidwa kwa phwando limeneli kunayambitsidwa ndi Yesu tsiku limene anafa. Iye anachita chikumbutso cha phwando Lachiyuda la Paskha ndi atumwi ake. Ndiyeno anapereka mkate wina wopanda chotupitsa wa Paskhayo kwa iwo, akumati: “Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu.” Kenako, Yesu anapereka chikho cha vinyo, nati: “Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.” Iye anatinso: “Chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.” (Luka 22:19, 20; 1 Akorinto 11:24-26) Kuchitidwa kwa phwando kumeneko ndiko Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, kapena Chikumbutso. Ndilophwando lokha limene Yesu analamulira otsatira ake kulisunga.

      Matchalitchi ambiri amanena kuti amasunga phwando limeneli pamodzi ndi mapwando awo ena onse, koma ambiri amalikumbukira m’njira yosiyana ndi imene Yesu analamula. Mwinamwake kusiyana kodziŵika kwambiri ndiko nthaŵi zimene phwandolo limachitidwa. Matchalitchi ena amalichita mwezi ndi mwezi, mlungu ndi mlungu, ngakhale tsiku ndi tsiku. Kodi zimenezi nzimene Yesu anafuna pamene anauza otsatira ake kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa”? The New English Bible imati: “Chitani ichi monga chikumbutso changa.” (1 Akorinto 11:24, 25) Kodi chikumbutso kapena chikondwerero chimasungidwa kangati? Kaŵirikaŵiri, kamodzi kokha pachaka.

      Kumbukiraninso kuti Yesu anayambitsa phwando limeneli ndiyeno anafa padeti la kalenda Yachiyuda la Nisani 14.a Limenelo linali tsiku la Paskha, phwando lokumbutsa Ayuda za chilanditso chawo chachikulu ku Igupto m’zaka za zana la 16 B.C.E. Pa nthawiyo, nsembe ya mwanawankhosa inachititsa chipulumutso kwa oyamba kubadwa Achiyuda, pamene mngelo wa Yehova anakantha oyamba kubadwa onse a Igupto.​—Eksodo 12:21, 24-27.

      Kodi zimenezi zimatithandiza motani kumvetsetsa kwathu? Eya, mtumwi Wachikristu Paulo analemba kuti: “Paskha wathu waphedwa, ndiye Kristu.” (1 Akorinto 5:7) Imfa ya Yesu inali nsembe ya Paskha yaikulu kwambiri, ikumapatsa anthu mwaŵi wa chipulumutso chachikulu koposa. Chotero, kwa Akristu, Chikumbutso cha imfa ya Kristu chinaloŵa mmalo Paskha Wachiyuda.​—Yohane 3:16.

      Paskha anali phwando lapachaka. Pamenepo, mwanzeru, Chikumbutsonso chili motero. Paskha​—tsiku limene Yesu anafa​—nthaŵi zonse anali kuchitika pa tsiku la 14 la mwezi Wachiyuda wa Nisani. Chifukwa chake, imfa ya Kristu iyenera kukumbukiridwa kamodzi pachaka patsiku la kalenda limene limagwirizana ndi Nisani 14. Mu 1994 tsiku limenelo ndi Loŵeruka, March 26, dzuŵa litaloŵa. Komabe, kodi nchifukwa ninji matchalitchi a Dziko Lachikristu sanapange tsikuli kukhala lokumbukiridwa mwapadera? Kupenda kwachidule kwa mbiri yake kudzayankha funso limenelo.

  • Chakudya Chamadzulo cha Ambuye—Kodi Chiyenera Kuchitidwa Kangati?
    Nsanja ya Olonda—1994 | March 15
    • a Mwezi woyamba wa chaka Wachiyuda wa Nisani, unayamba ndi kuonekera koyamba kwa mwezi watsopano. Motero nthaŵi zonse Nisani 14 inafika pamene mwezi unali wathunthu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena