Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 11/15 tsamba 8-9
  • Kukanidwa m’Bwalo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukanidwa m’Bwalo
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Kukanidwa m’Bwalo Lamilandu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Petulo Anakana Yesu Kunyumba kwa Kayafa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kukhululukira Ena
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 11/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kukanidwa m’Bwalo

ATAMSIYA Yesu m’munda wa Getsemane ndikuthaŵa pamodzi ndi atumwi ena onse pochita mantha, Petro ndi Yohane akuima m’kuthaŵa kwawo. Mwinamwake akumana ndi Yesu pamene akuperekedwa kunyumba kwa Anasi. Pamene Anasi akumtumiza kwa Mkulu wa Ansembe Kayafa, Petro ndi Yohane akutsatira chapatali, mwachiwonekere osweka maganizo chifukwa cha mantha kaamba ka miyoyo yawo ndi nkhaŵa yaikulu ya chimene chidzachitikira Mbuye wawo.

Atafika panyumba pa Kayafa pa malo aakulu, Yohane watha kuloŵa m’bwalo, popeza kuti ngwodziŵika kwa mkulu wa ansembeyo. Komabe, Petro, watsala ali chiimire pakhomo. Koma mwamsanga Yohane akubwerera ndikulankhula kwa wosunga pakhomo, mdzakazi, ndipo Petro aloledwa kuloŵa.

Tsopano kwazizira, ndipo akalinde amnyumbamo ndi asirikali a mkulu wansembe asonkha moto wamakala. Petro agwirizana nawo kuti afunde podikirira kuzengedwa mlandu kwa Yesu. Pamenepo, m’kuunika kwa moto wowala, wosunga pakhomo yemwe analola Petro kuloŵa akumyang’anitsitsa bwino. “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya,” akufuula motero.

Atakwiya chifukwa chomuulula pamaso pa onse, Petro akukana kuti sanamdziŵe konse Yesu. ‘Sindidziŵa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe,’ iye akutero.

Pamenepo, Petro akutuluka kunja nanka pafupi ndi chipata. Kumeneko, msungwana wina amuwona ndikunenanso kwa oimirira pafupi nati: ‘Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.’ Kachiŵirinso, Petro akukana, nalumbira: ‘Sindidziŵa munthuyo.’

Petro akadali m’bwalomo, akuyesayesa kudzibisa monga momwe angathere. Mwinamwake tsopano akudzidzimutsidwa ndi kulira kwa tambala mumdima wambandakucha. Pakali pano, kuzengedwa mlandu kwa Yesu kukadali mkati, mwachiwonekere kukuchitiridwa m’chipinda chapamwamba pa bwalolo. Mwinamwake Petro ndi ena odikirira pansipo akuwona mboni zosiyanasiyana zikumaloŵa ndikutuluka zimene zikubweretsedwa kudzapereka umboni.

Pafupifupi ola limodzi lapita kuchokera pamene Petro anazindikiridwa kwanthaŵi yapita monga mnzake wa Yesu. Tsopano ambiri oimirira mozungulira adza kwa iye ndikunena: ‘Zowonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.’ Mmodzi wa gululo ali wachibale wa Malko, amene Petro anamdula khutu lake. ‘Ine sindinakuwona iwe kodi m’munda pamodzi ndi iye?’ iye akutero.

‘Sindidziŵa munthuyo.’ Petro akukana mwamphamvu. Kwenikweni, iye akuyesayesa kuwakhutiritsa kuti onse ali olakwa mwakutemberera ndi kulumbirira nkhaniyo, mwakutero, akudziitanira tsoka pa iyemwini ngati sanena chowona.

Pamene Petro wangotha kukana kachitatu, tambala akulira. Ndipo pamphindi yomweyo, Yesu, amene mwachiwonekere watulukira kunja pakhonde lapamwamba pa bwalo, akutembenuka namuyang’ana. Mwamsanga, Petro akukumbukira zimene Yesu anali atamuuza maola angapo apitapo m’chipinda chosanja kuti: ‘Tambala asanalire kaŵiri, udzandikana ine katatu.’ Povutika ndi kukula kwa tchimo lake, Petro akutuluka kunja ndikulira mopwetekedwa.

Kodi zimenezi zingachitike motani? Kodi ndimotani mmene Petro angakanire Mbuye ŵake katatu motsatizana mofulumira choncho, pambuyo pokhala wotsimikiza motero za nyonga yake yauzimu? Mosakaikira zochitikazo zamgwira mosadziŵa Petro. Chowonadi chapotozedwa, ndipo Yesu akusonyezedwa kukhala wambanda woipa. Chimene chiri cholondola chikuchititsidwa kuwoneka cholakwika, wopanda liŵongo monga waliŵongo. Chotero chifukwa cha zipsinjo za chochitikacho, Petro akutekeseka. Mwadzidzidzi malingaliro ake a kukhulupirika asweka. Mwachisoni akutha mphamvu kaamba ka kuwopa munthu. Tisalole konse kuti zimenezo zichitike kwa ife! Mateyu 26:57, 58, 69-75; Marko 14:30, 53, 54, 66-72; Luka 22:54-62; Yohane 18:15-18, 25-27.

▪ Kodi ndimotani mmene Petro ndi Yohane akuloŵera m’bwalo la mkulu wa ansembe?

▪ Pamene Petro ndi Yohane ali m’bwalomo, kodi nchiyani chikuchitika m’nyumbamo?

▪ Kodi tambala akulira kangati, ndipo kodi Petro akukana kangati kuti sakumdziŵa Kristu?

▪ Kodi nchifukwa ninji Petro akutemberera ndi kulumbira?

▪ Kodi nchiyani chimene chipangitsa Petro kukana kuti sakumdziŵa Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena