Akufa Anu Okondedwa—Kodi Mudzaŵaonanso?
JOHN anali ndi zaka zisanu ndi zinayi zokha pamene amayi ake anafa. Pambuyo pake, iye anakumbukira zimene zinachitika pa nyumba yamaliroyo: “Ndinawajambulira chithunzithunzi ndi kulembapo kalata yaifupi kuwapempha kudikirira tonsefe kumwamba. Ndinachipereka kwa Atate kuti akachiike m’bokosi lamaliro pamodzi nawo, ndipo ngakhale kuti anali akufa, ndimakonda kuganiza kuti analandira uthenga womalizira umenewo wochokera kwa ine.”—How It Feels When a Parent Dies, lolembedwa ndi Jill Krementz.
Sipangakhale chikayikiro chilichonse kuti John anakonda kwambiri amayi ake. Pambuyo polongosola mikhalidwe yawo yabwino, iye anati: “Mwinamwake zangochitika kuti sindikufuna kukumbukira zinthu zoipa, koma sindingaganize za chilichonse choipa ponena za iwo. Iwo anali mkazi wokongola koposa amene ndinaonapo m’moyo wanga wonse.”
Mofanana ndi John, ambiri ali ndi zikumbukiro zachikondi ponena za akufa awo okondedwa ndipo amavomereza malingaliro ofuna kuŵaonanso. Edith, amene mwana wake wamwamuna wazaka 26 anafa ndi kansa, anati: “Ndimafuna kukhulupirira kuti mwana wanga ali ndi moyo kwinakwake koma sindikudziŵa kuti ndi kuti. Kodi ndidzamuonanso? Sindikudziŵa koma ndimayembekeza kuti ndidzatero.”
Ndithudi, Mlengi wachikondi wa munthu sali wosalingalira ponena za chikhumbo chachibadwa cha anthu chimenechi. Ndicho chifukwa chake walonjeza kuti idzafika nthaŵi imene mamiliyoni adzagwirizananso ndi akufa awo okondedwa. Mawu a Mulungu ali ndi maumboni ambirimbiri onena za lonjezo limeneli la kuuka kwa akufa kukudzako.—Yesaya 26:19; Danieli 12:2, 13; Hoseya 13:14; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:12, 13.
Kodi Ndani Amaukitsidwira Kumwamba?
Tiyeni tisinkhesinkhe za chiyembekezo cha John chakuti amayi ake okondedwa akumudikirira kumwamba. Opita kutchalitchi ambiri ali ndi chiyembekezo kapena chikhulupiriro chimenechi. Poyesayesa kuchirikiza malingaliro otero, atsogoleri achipembedzo ndi ena ogwira ntchito yothandiza anthu amagwiritsira ntchito molakwa malemba a m’Baibulo.
Mwachitsanzo, katswiri wothandiza oferedwa, Dr. Elisabeth Kübler-Ross, ananena m’buku lake lakuti On Children and Death: “Kufa kumangotanthauza kuti timataya thupi lathu monga momwe timatayira chovala chakale chong’ambika, kapena kutuluka m’chipinda chimodzi kuloŵa m’china. Mu Mlaliki 12:7, timaŵerenga kuti: ‘Fumbi ndi kubwerera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwerera kwa Mulungu amene anaupereka.’ Yesu anati: ‘Ndipita kukukonzerani inu malo kuti kumene kuli ineko mukakhale inunso.’ Ndipo kwa wakuba amene anali pamtanda anati: ‘Lerolino udzakhala ndine m’paradaiso.’”
Kodi malemba apamwambawa amatanthauzadi kuti akufa athu okondedwa ali ndi moyo tsopano ndipo akutidikirira kumwamba? Tiyeni tisinkhesinkhe malembawo mosamalitsa kwambiri, kuyamba ndi Mlaliki 12:7. Mwachionekere, munthu wanzeru amene analemba mawu amenewo sanali ndi cholinga chotsutsa zimene anali atanena kale m’buku la Baibulo limodzimodzilo: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Iye anali kulongosola imfa ya mtundu wa anthu mwachisawawa. Kodi nkwanzeru kukhulupirira kuti osakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu ouma mtima onse ndi apandu okakala amabwerera kwa Mulungu pamene afa? Kutalitali. Kwenikweni, zimenezo sizinganenedwe kwa aliyense wa ife, mosasamala kanthu kuti timadziona kukhala abwino kapena oipa motani. Popeza kuti palibe aliyense wa ife amene anakhala ndi Mulungu kumwamba, kodi zinganenedwe motani kuti timabwerera kwa iye?
Pamenepo, kodi wolemba Baibuloyo anatanthauzanji mwa kunena kuti pa imfa, ‘mzimu umabwerera kwa Mulungu’? Mwa kugwiritsira ntchito liwu Lachihebri lotembenuzidwa kuti “mzimu,” iye sanali kunena za chinachake chapadera chimene chimasiyanitsa munthu mmodzi kwa wina. Mmalo mwake, pa Mlaliki 3:19, wolemba Baibulo wouziridwa mmodzimodziyo akulongosola kuti munthu ndi zinyama “onsewo ali ndi [mzimu, NW] umodzi.” Mwachionekere anatanthauza kuti “mzimu” ndiwo mphamvu ya moyo imene ili m’maselo amene amapanga matupi a munthu ndi zinyama. Sitinalandire mzimu umenewu mwachindunji kuchokera kwa Mulungu. Unaperekedwa kwa ife ndi makolo athu aumunthu pamene tinaumbidwa m’mimba ndipo pambuyo pake kubadwa. Ndiponso, mzimu umenewu sumayendadi m’mlengalenga ndi kubwerera kwa Mulungu pa imfa. Mawu akuti, ‘mzimu umabwerera kwa Mulungu,’ ali mawu okuluwika otanthauza kuti ziyembekezo za moyo za mtsogolo za munthu wakufayo tsopano zili ndi Mulungu. Zili kwa iye kusankha amene adzakumbukira ndi kuukitsa pambuyo pake. Taonani nokha mmene Baibulo limasonyezera zimenezi momvekera bwino pa Salmo 104:29, 30.
Yehova Mulungu walinganiza kuti chiŵerengero chokhala ndi polekezera cha otsatira okhulupirika a Kristu, okwanira 144,000 okha, adzaukitsidwira ku moyo wakumwamba monga ana auzimu a Mulungu. (Chivumbulutso 14:1, 3) Ameneŵa amapanga boma lakumwamba ndi Kristu kaamba ka kudalitsa mtundu wa anthu padziko lapansi.
Oyambirira kuphunzira za zimenezi anali atumwi okhulupirika a Yesu, kwa amene iye anati: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.” (Yohane 14:2, 3) Atumwi amenewo ndi Akristu ena oyambirira anafa ndipo anayenera kudikirira osadziŵa kanthu mu imfa kufikira Yesu atabwera kudzawafupa ndi chiukiriro cha kumwamba. Ndicho chifukwa chake timaŵerenga kuti Mkristu wophedwera chikhulupiriro woyambirira, Stefano, “anagona tulo [mu imfa, NW].”—Machitidwe 7:60; 1 Atesalonika 4:13.
Kuukitsidwira ku Moyo Padziko Lapansi
Koma bwanji ponena za lonjezo la Yesu kwa mpandu amene anafa pambali pake? Mofanana ndi Ayuda ambiri a nthaŵi imeneyo, munthu ameneyu anakhulupirira kuti Mulungu akatumiza Mesiya amene akakhazikitsa ufumu ndi kubwezeretsa mtendere ndi chisungiko ku mtundu Wachiyuda padziko lapansi. (Yerekezerani 1 Mafumu 4:20-25 ndi Luka 19:11; 24:21 ndi Machitidwe 1:6.) Ndiponso, wochita zoipayo anasonyeza chikhulupiriro kuti Yesu anali Uyo amene anasankhidwadi ndi Mulungu kukhala Mfumu. Komabe, pa mphindi imeneyo, imfa yomayandikira ya Yesu monga munthu woweruzidwa inapangitsa zimenezi kuonekera kukhala zosatheka. Ndicho chifukwa chake Yesu anatsimikizira mpanduyo mwa kuyamba lonjezo Lake ndi mawu aŵa: “Ndithudi ndikukuuza lerolino, Udzakhala nane m’Paradaiso.”—Luka 23:42, 43, NW.
Matembenuzidwe a Baibulo amene amaika mpatuliro lisanalembedwe liwu lakuti “lerolino” amachititsa vuto kwa anthu amene akufuna kumvetsetsa mawu a Yesu. Yesu sanapite ku paradaiso aliyense tsiku limodzimodzilo. Mmalo mwake, iye anagona wosadziŵa kanthu mu imfa kwa masiku atatu kufikira Mulungu anamuukitsa iye. Ngakhale pambuyo pa kuuka kwa Yesu ndi kukwera kumwamba, iye anayenera kudikirira kudzanja lamanja la Atate wake kufikira itakwana nthaŵi yakuti iye alamulire monga Mfumu pa mtundu wa anthu. (Ahebri 10:12, 13) Posachedwapa, ulamuliro wa Ufumu wa Yesu udzadzetsa mpumulo ku mtundu wa anthu ndi kusanduliza dziko lonse lapansi kukhala paradaiso. (Luka 21:10, 11, 25-31) Pamenepo adzakwaniritsa lonjezo lake kwa mpandu ameneyo mwa kumuukitsira ku moyo padziko lapansi. Ndipo Yesu adzakhala ndi mwamuna ameneyo m’lingaliro lakuti Iye adzathandiza kupereka zofuna zonse za munthuyo, kuphatikizapo kufunika kwa kugwirizanitsa njira yake ya moyo ndi malamulo olungama a Mulungu.
Kuuka kwa Ambiri
Mofanana ndi mpandu wolapa ameneyo, kuuka kwa anthu ochuluka kudzachitika pano padziko lapansi. Zimenezi zili zogwirizana ndi chifuno cha Mulungu polenga munthu. Mwamuna ndi mkazi oyambirira anaikidwa m’munda wa paradaiso ndi kuuzidwa kugonjetsa dziko lapansi. Ngati iwo akanakhalabe omvera Mulungu, sakanakalamba ndi kufa. M’nthaŵi yake ya Mulungu, dziko lonse lapansi likadagonjetsedwa, kupangidwa kukhala mbulunga ya paradaiso ndi Adamu ndi mbadwa zake zangwiro.—Genesis 1:28; 2:8, 9.
Komabe, chifukwa chakuti Adamu ndi Hava anachimwa mwadala, iwo anadzetsa imfa pa iwo eni ndi ana awo a mtsogolo. (Genesis 2:16, 17; 3:17-19) Ndicho chifukwa chake Baibulo limati: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 5:12.
Pakhala munthu mmodzi yekha amene anabadwa wopanda uchimo wa choloŵa. Ameneyo anali Mwana wangwiro wa Mulungu, Yesu Kristu, amene moyo wake unasamutsidwa kumwamba kumka m’mimba mwa namwali Wachiyuda, Mariya. Yesu anakhala wopanda tchimo ndipo sanayenere kuphedwa. Chotero, imfa yake ili ndi mphamvu ya kuombola “tchimo lake la dziko lapansi.” (Yohane 1:29; Mateyu 20:28) Ndicho chifukwa chake Yesu anakhoza kunena kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.”—Yohane 11:25.
Chotero, inde, mungakhale ndi chiyembekezo cha kugwirizananso ndi akufa anu okondedwa, koma zimenezi zimafuna kuti mukhale ndi chikhulupiriro mwa Yesu monga Momboli wanu ndi kumvera iye monga Mfumu yoikidwa ya Mulungu. Posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzasesa kuipa konse pa dziko lapansili. Anthu onse amene amakana kugonjera ku ulamuliro wake adzawonongedwa. Komabe, nzika za Ufumu wa Mulungu zidzapulumuka ndi kukhala zotanganidwa m’ntchito yosanduliza dziko lapansili kukhala paradaiso.—Salmo 37:10, 11; Chivumbulutso 21:3-5.
Pamenepo idzafika nthaŵi yokondweretsa yakuti chiukiriro chiyambe. Kodi mudzakhalapo kudzachingamira akufa? Zonse zimadalira pa zimene mukuchita tsopano. Madalitso abwino koposa akudikirira awo amene tsopano akugonjera ku ulamuliro wa Ufumu wa Yehova mwa Mwana wake, Yesu Kristu.