Anali Kalambula Bwalo wa Mesiya
LAMBA lalikulu lachikopa linachititsa khungu lake lakuda chifukwa cha dzuŵa kuoneka lodera kwambiri. Atavala chovala cha ubweya wa ngamila, anaonekadi ngati mneneri. Ambiri anakonda kumka kwa iye kumtsinje wa Yordano. Kumeneko mwamuna wochititsa chidwi ameneyu analengeza molimba mtima kuti anali wokonzekera kubatiza ochimwa olapa.
Anthu anazizwa! Kodi mwamunayu anali yani? Kodi cholinga chake chinali chotani?
Yesu Kristu ponena za munthuyu anati: “Koma munatulukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri. . . . Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi.” (Mateyu 11:9-11) Kodi nchifukwa ninji Yohane anali munthu wapadera chotero? Chifukwa chakuti anali kalambula bwalo wa Mesiya
Ntchito Yake Inanenedweratu
Zaka zoposa 700 Yohane asanabadwe, Yehova analengeza kuti munthu ameneyu adzafuula m’chipululu: “Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m’dziko loti se khwalala la Mulungu wathu.” (Yesaya 40:3; Mateyu 3:3) Zaka zoposa 400 Yohane asanabadwe, Mulungu Wamphamvuyonse analengeza: “Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.” (Malaki 4:5) Kubadwa kwa Yohane Mbatizi pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabadwe sikunachitike mwangozi, ndiponso sikunachitike mwachibadwa. Mofanana ndi kubadwa kwa mwana wolonjezedwayo Isake, kubadwa kwa Yohane kunali chozizwitsa, pakuti makolo ake onse aŵiri, Zakariya ndi Elisabeti, anapyola usinkhu wa kubala ana.—Luka 1:18.
Ngakhale pamene mimba ya Yohane isanakhale, utumiki wake, ntchito, ndi moyo zinafotokozedwa ndi mngeloyo Gabrieli. Ndi mphamvu ndi mzimu wa Eliya, Yohane anali kudzabweza anthu osamvera panjira ya imfa ndipo kuwakonzekeretsa kulandira Yesu monga Mesiya. Kuyambira pakubadwa kwake, Yohane anali kudzakhala Mnaziri, wodzipatuliradi kwa Mulungu, ndipo sanali kudzakhudza vinyo kapena chakumwa chaukali. Ndithudi, chakudya chake m’chipululu chinali “dzombe ndi uchi wa kuthengo.” (Marko 1:6; Numeri 6:2, 3; Luka 1:13-17) Mofanana ndi Samueli, kuyambira pa ubwana Yohane anapatulidwa kaamba ka utumiki wolemekezeka wa Mulungu Wam’mwambamwamba.—1 Samueli 1:11, 24-28.
Ngakhale dzina lakuti Yohane linasankhidwa ndi Mulungu. Dzina Lachihebri lotembenuzidwa kuti “Yohane” limatanthauza kuti “Yehova Wasonyeza Chiyanjo; Yehova Wakhala Wokoma Mtima.”
Pamene mwanayo anadulidwa pa tsiku lachisanu ndi chitatu, atate wake, Zakariya, anauziridwa ndi Mulungu kulengeza kuti: “Ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu: pakuti udzatsogolera [Yehova, NW], kukonza njira zake; kuwapatsa anthu ake adziŵitse chipulumutso, ndi makhululukidwe a machimo awo, chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu. Mmenemo mbanda kucha wa kumwamba udzatichezera ife.” (Luka 1:76-78) Utumiki wapoyera wa Yohane unali kudzakhala wofunika koposa m’moyo wake. Zinthu zina zonse zinali zopanda pake poziyerekeza nawo. Chifukwa chake, Malemba amafotokoza za zaka 30 zoyamba za moyo wa Yohane m’vesi limodzi motere: “Mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m’mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israyeli.”—Luka 1:80.
Mawu m’Chipululu
M’chaka cha 15 cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pamene Pontiyo Pilato anali kazembe wa Yudeya, Yohane Mbatizi anaonekera m’chipululu ndi uthenga uwu wodabwitsa: “Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 3:2; Marko 1:4; Luka 3:1, 2) Anthu a m’chigawo chonsecho anagalamutsidwa. Chilengezo choperekedwa molimba mtima chimenecho chinakhudza mitima ya anthu olakalaka chiyembekezo chenicheni. Chilengezo cha Yohane chinatokosanso kudzichepetsa kwa munthu chifukwa chakuti chinafuna kulapa koona. Kuona mtima kwake ndi chidaliro zinasonkhezera makamu a anthu oona mtima kumuona kukhala munthu wotumidwa ndi Mulungu.
Mbiri ya Yohane inafalikira mofulumira. Monga mneneri wa Yehova, iye anadziŵidwa mosavuta chifukwa cha kavalidwe kake ndi kudzipereka. (Marko 1:6) Ngakhale ansembe ndi Alevi anayenda ulendo kuchokera ku Yerusalemu kuti akaone zimene zinasonkhezera chidwi cha anthu onsewo. Kulapa? Chifukwa, ndipo pa chiyani? Kodi munthuyu anali yani? Iwo anafuna kudziŵa. Yohane anafotokoza: “Sindine Kristu. Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iyayi. Chifukwa chake anati kwa iye, Ndiwe yani? kuti tibwezere mawu kwa iwo anatituma ife. Unena chiyani za iwe wekha? Anati, Ndine mawu a wofuula m’chipululu, Lungamitsani njira ya [Yehova, NW], monga anati Yesaya mneneriyo. Ndipo otumidwawo anali a kwa Afarisi. Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Kristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?”—Yohane 1:20-25.
Kulapa ndi ubatizo zinali masitepe oyenera kwa awo amene akaloŵa Ufumuwo. Chifukwa chake, Yohane anayankha: ‘Inetu ndibatiza ochimwa olapa ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; iyeyu adzakubatizani inu ndi mzimu woyera ndi moto: amene chouluzira chake chili m’dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m’chiruli chake; koma mankhusu adzatentha m’moto.’ (Luka 3:15-17; Machitidwe 1:5) Ndithudi, mzimu woyera unali kudzaikidwa pa otsatira Mesiya, koma adani ake anali kudzatenthedwa ndi moto wachiwonongeko.
“Anthu a Mtundu Uliwonse” Achenjezedwa
Mawu a Yohane analasa mitima ya Ayuda ambiri oona mtima ndipo analapa poyera machimo awo a kusakhulupirika ku pangano la Chilamulo. Anasonyeza poyera kulapa kwawo mwa kulola Yohane kuwabatiza mu mtsinje wa Yordano. (Mateyu 3:5, 6) Motero, mitima yawo inali mumkhalidwe woyenera kulandira Mesiya. Kuti athetse ludzu lawo la kufuna kudziŵa zofunika zolungama za Mulungu, Yohane mofunitsitsa anawaphunzitsa monga ophunzira ake, akumawaphunzitsa ngakhale mmene angapempherere.—Luka 11:1.
Ponena za wapatsogolo ameneyu wa Mesiya, mtumwi Yohane analemba kuti: “Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti [anthu a mtundu uliwonse, NW] akakhulupirire mwa iye.” (Yohane 1:7) Chotero anthu a mtundu uliwonse anadza kudzamva Yohane Mbatizi pamene ‘analalikira ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israyeli.’ (Machitidwe 13:24) Iye anachenjeza okhometsa msonkho za kulanda. Anachenjeza asilikali za kusavuta munthu aliyense kapena kunamizira munthu. Ndipo anauza Afarisi ndi Asaduki onyengawo, okhala ngati opembedza: “Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthaŵa mkwiyo ulinkudza? Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.”—Mateyu 3:7-9; Luka 3:7-14.
Monga gulu, atsogoleri achipembedzo a m’tsiku la Yohane anakana kumkhulupirira ndipo ananena monama kuti anali ndi chiŵanda. Anakana njira yachilungamo yotsogolera ku moyo wosatha. Komano, amisonkho ochimwa ndi akazi adama amene anakhulupirira umboni wa Yohane analapa nabatizidwa. Panthaŵi yake, iwo analandira Yesu Kristu monga Mesiya.—Mateyu 21:25-32; Luka 7:31-33.
Mesiya Adziŵikitsidwa
Kwa miyezi isanu ndi umodzi—kuyambira m’ngululu kukafika mu mphakasa ya 29 C.E.—Yohane mboni yokhulupirikayo ya Mulungu anasonyeza Ayuda Mesiya wakudzayo. Inali nthaŵi ya kuonekera kwa Mfumu Yaumesiya. Koma pamene anatero, iye anadza kumadzi amodzimodziwo a Yordano napempha kubatizidwa. Poyamba Yohane anakana, komano pambuyo pake anavomera. Tangolingalirani za chisangalalo chake pamene mzimu woyera unakhala pa Yesu ndipo liwu la Yehova losonyeza kuyanja Mwana Wake linamveka.—Mateyu 3:13-17; Marko 1:9-11.
Yohane anali woyamba kudziŵa kuti Yesu ndiye Mesiya, ndipo anasonyeza ophunzira ake Wodzozedwa ameneyu. “Onani,” Yohane anatero, “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!” Iye analengezanso: “Ndiye amene ndinati za iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine. Ndipo sindinamdziŵa iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israyeli, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi.”—Yohane 1:29-37.
Ntchito ya Yohane inapitiriza kuchitidwa mogwirizana ndi utumiki wa Yesu kwa miyezi isanu ndi umodzi. Aliyense wa iwowa anadziŵa bwino ntchito imene wina anali kuchita. Yohane anadziyesa mnzake wa Mkwatibwi ndipo anakondwera kuona Kristu akukula pamene iye ndi ntchito yake anali kuchepa.—Yohane 3:22-30.
Yesu anadziŵikitsa Yohane kukhala wapatsogolo wake, woimiridwa ndi Eliya. (Mateyu 11:12-15; 17:12) Panthaŵi ina, Yesu anati: “Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu, ndipo munthu [wa mtundu uliwonse, NW] akangamira kuloŵamo.”—Luka 16:16.
Wokhulupirika Kufikira Mapeto
Yohane anagwidwa ndi kuikidwa m’ndende chifukwa chakuti analengeza choonadi molimba mtima. Sanapeŵe thayo lake la kuvumbula ngakhale tchimo la Mfumu Herode. Moswa lamulo la Mulungu, mfumu imeneyi inali kukhala m’chigololo ndi Herodiya, mkazi wa mbale wake. Yohane analankhula molimba mtima kotero kuti mwina mwamunayo angalape ndi kulandira chifundo cha Mulungu.
Yohane anapereka chitsanzo chabwino chotani nanga cha chikhulupiriro ndi chikondi! Anasonyeza kukhulipirika kwake kwa Yehova Mulungu ndi kukonda anthu anzake modzimana ufulu. Atakhala m’ndende kwa chaka chimodzi, Yohane anadulidwa mutu chifukwa cha chiŵembu chosonkhezeredwa ndi Mdyerekezi chopangidwa ndi Herodiya woipayo, amene “anamuda.” (Marko 6:16-19; Mateyu 14:3-12) Koma kalambula bwalo wa Mesiyayo anasunga umphumphu wake kwa Yehova ndipo posachedwa adzaukitsidwa kwa akufa kudzakhala ndi moyo m’dziko latsopano lolungama la Mulungu.—Yohane 5:28, 29; 2 Petro 3:13.