Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi ndi mkhalidwe wotani umene uyenera kusonyezedwa pa maubatizo Achikristu?
Limenelo ndi funso lokondweretsa, pakuti ngakhale kuti oŵerenga athu ambiri ali obatizidwa kale, likuwakhudza, mofanana ndi amene akubatizidwa. Tiyeni choyamba tikambepo za awo amene amabatizidwa, kumizidwadi m’madzi. Kodi mkhalidwe wawo uyenera kukhala wotani?
Pa Mateyu 28:19, 20, Yesu anauza otsatira ake kupita ndi kukapanga ophunzira mwa anthu, kuwaphunzitsa ndi kuwabatiza. Iye sanasonyeze ubatizo kukhala chochitika chochititsa kutengeka maganizo, kachitidwe kosonkhezeredwa ndi nthumanzi ya kanthaŵi. Uli chochitika chachikulu, monga momwe timaonera m’chitsanzo cha Yesu. Luka 3:21 amati: “Ndipo Yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo.” Inde, Wopereka Chitsanzo wathu anaona ubatizo kukhala wofunika kwambiri, ndi kukhala nkhani ya pemphero. Sitingayerekezere kuti iye, atatuluka m’madzi, anapanga chizindikiro cha chipambano, kuliza nthungululu, kapena kukweza mikono yake m’mwamba, ngakhale kuti ena achita zonga zimenezo posachedwapa. Ayi, ali ndi Yohane Mbatizi yekha, Yesu anatembenukira kwa Atate wake m’pemphero.
Komabe, Baibulo silimapereka lingaliro lakuti ubatizo uyenera kukhala chochitika chachisoni kapena chowopsa, chofuna kakhalidwe kapadera kapena kubwereza kutchula mawu akutiakuti, monga momwe amafunira matchalitchi ena m’Dziko Lachikristu lerolino. Ndi iko komwe, talingalirani za tsiku la Pentekoste, pamene zikwizikwi za Ayuda ndi otembenuka analoŵa muubatizo Wachikristu. Anali ataphunzira kale Chilamulo cha Mulungu nakhala paunansi ndi iye. Chotero anangofunikira kuphunzira za Mesiya, Yesu, ndi kumlandira. Atachita zimenezo akabatizidwa.
Machitidwe 2:41 (NW) akusimba kuti: “Iwo amene analandira mawu ake mokondwera anabatizidwa.” Matembenuzidwe a Baibulo a Weymouth amati: “Chotero, awo amene analandira mawu ake mosangalala anabatizidwa.” Iwo anasangalala ndi uthenga wokondweretsa wonena za Mesiya, ndipo ndithudi chisangalalo chimenecho chinafika pa ubatizo weniweniwo, ubatizo umene unachitidwa pamaso pa openyerera osangalala mazanamazana. Ngakhale angelo kumwamba anali kupenyerera ndi kukondwera. Kumbukirani mawu a Yesu: “Ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.”—Luka 15:10.
Pali njira zosiyanasiyana zimene aliyense wa ife angasonyezere ponse paŵiri kulemera ndi kukondweretsa kwa ubatizo. M’matchalitchi ena anthu amene akubatizidwa amavala zovala zoyera kapena zakuda. Malemba samachirikiza konse chofunika chotero. Komabe, zovala zosambira zazifupi kwambiri kapena zoonetsa zamkati zili zosayenera, kwa amuna kapena akazi. Ndipo monga momwe taonera, atatuluka m’madzi, Mkristu watsopanoyo sayenera kupanga majesichala apadera kapena kuchita ngati kuti wapeza chilakiko chachikulu. Akristu ena onse ngachimwemwe kuti watsopanoyo wabatizidwa. Ayenera kuzindikira kuti kusonyeza chikhulupiriro kumeneku kuli chiyambi chabe pa njira yaitali ya umphumphu kuti apeze chiyanjo cha Mulungu.—Mateyu 16:24.
Openyererafe pa ubatizo wapoyera timakondwera nawo pachochitikacho, makamaka ngati wachibale kapena munthu amene tinaphunzira naye Baibulo ndiye amene akubatizidwa. Komabe, kuti tikondwere kwambiri, tiyenera kumvetsera nkhani yonse ndi oyembekezera ubatizowo, kuwamva akuyankha poyera mafunso ofunsidwa kwa iwo, ndi kugwirizana nawo m’pemphero. Kuchita zimenezo kudzatithandiza kusonyeza mzimu woyenera pa ubatizo weniweniwo; tidzauona monga momwe Mulungu amauonera. Pambuyo pa ubatizowo, chimwemwe chathu sichimafuna kuti tichite chikondwerero cha chipambano, kupereka maluŵa, kapena kuchita phwando lolemekeza wobatizidwayo. Koma tingapite kwa mbale kapena mlongo wathu watsopanoyo ndi kusonyeza kukondwa kwathu ndi njira yabwino koposa yomwe watenga ndi kumlandira ndi manja aŵiri mu ubale wathu Wachikristu.
Mwachidule, tonsefe, kuphatikizapo awo amene akumizidwa, tiyenera kupatsa ubatizo ulemu woyenera. Si nthaŵi ya kukuwa motengeka maganizo, ya phwando, kapena ya phokoso lachikondwerero. Koma siilinso nthaŵi yachisoni kapena yowopsa. Moyenera tiyenera kukondwera kuti atsopano agwirizana nafe panjira ya ku moyo wosatha. Ndipo tiyenera ndi mtima wonse kulandira abale ndi alongo athu atsopanowo.
[Chithunzi chachikulu patsamba 31]