-
Olamulira Okhala m’Malo a MizimuNsanja ya Olonda—1995 | July 15
-
-
Atangobatizidwa, Yesu anayesedwa ndi cholengedwa chauzimu chosaoneka chotchedwa Satana Mdyerekezi. Posonyeza amodzi amayesowo, Baibulo limati: “Mdyerekezi anamuka [ndi Yesu] ku phiri lalitali, namuonetsa maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo.” (Mateyu 4:8) Ndiyeno Satana anauza Yesu: “Ndidzapatsa inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wawo: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna. Chifukwa chake ngati inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.”—Luka 4:6, 7.
Satana ananena kuti anali ndi ulamuliro pa maufumu onse, kapena maboma, a dzikoli. Kodi Yesu anatsutsa mawuwo? Ayi. Iye kwenikweni anawavomereza panthaŵi ina mwa kutchula Satana kukhala “mkulu wa dziko lapansi.”—Yohane 14:30.
Malinga ndi kunena kwa Baibulo, Satana ndi mngelo woipa wokhala ndi mphamvu yaikulu. Mtumwi Wachikristu Paulo amagwirizanitsa Satana ndi “magulu oipa amizimu” ndipo amalankhula za iwo monga “olamulira dziko a mdima uno.” (Aefeso 6:11, 12, NW) Ndiponso, mtumwi Yohane anati “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Buku la Baibulo la Chivumbulutso limati Satana ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9) Mophiphiritsira, Chivumbulutso chimasonyezanso Satana kukhala chinjoka chimene chimapatsa magulu andale a dziko “mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.”—Chivumbulutso 13:2.
Zochitika za dzikonso zimasonyeza kuti pali mphamvu ina yoipa imene ikugwira ntchito, ikumachititsa anthu kudzivulaza. Kodi chifukwa china nchiti chimene chimachititsa maboma a anthu kulephera kuchirikiza mtendere? Kodi nchiyaninso chimene chingachititse anthu kudana ndi kuphana? Atanyansidwa ndi kuphana ndi imfa mu nkhondo yachiŵeniŵeni, mboni ina yoona ndi maso inati: “Sindikumvetsetsa chifukwa chake zimenezi zinachitika. Si udani chabe. Ndi mizimu yoipa imene ikugwiritsira ntchito anthu ameneŵa kuwonongana.”
-
-
Olamulira Okhala m’Malo a MizimuNsanja ya Olonda—1995 | July 15
-
-
Chifukwa Chake Satana Waloledwa Kulamulira
Kodi mukukumbukira zimene Satana anauza Yesu ponena za ulamuliro wa pa dziko lonse lapansi? “Ndidzapatsa inu ulamuliro wonse umenewu . . . chifukwa unaperekedwa kwa ine,” anatero Satana. (Luka 4:6) Mawu amenewo akusonyeza kuti Satana Mdyerekezi amalamulira kokha chifukwa cha kuloledwa ndi Mulungu. Koma kodi nchifukwa ninji Mulungu amalekerera Satana?
-