Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “New World Translation”—Yaukatswiri ndi Yowona
    Nsanja ya Olonda—1991 | March 1
    • Pa Luka 4:18, mogwirizana ndi New World Translation, Yesu anagwiritsira ntchito kwa iyemwini ulosi wa Yesaya, akumati: “Mzimu wa Yehova uli pa ine.” (Yesaya 61:1) Ambiri amatsutsa kugwiritsiridwa kwa dzina la Yehova panopa. Komabe, awa ndi amodzi okha a malo 200 pamene dzinalo limawonekera mu New World Translation ya Malemba Achikristu Achigiriki, otchedwa Chipangano Chatsopano. Zowonadi, palibe mamanyusikripiti oyambirira Achigiriki omwe adakalipo a “Chipangano Chatsopano” okhala ndi dzina laumwini la Mulungu. Koma dzinalo linaphatikizidwamo mu New World Translation kaamba ka zifukwa zabwino, osati mwalingaliro lansontho. Ndipo ena atsatira njira yofananayo. M’chinenero cha Chijeremani chokha, pafupifupi matembenuzidwe 11 amagwiritsira ntchito “Yehova” (kapena matchulidwe otsatira Chihebri akuti, “Yahweh”) m’malemba a “Chipangano Chatsopano,” pamene kuli kwakuti otembenuza anayi amaika dzinalo m’mabulaketi pambuyo pa “Ambuye.”c Matembenuzidwe Achijeremani oposa 70 amaligwiritsira ntchito m’mawu amtsinde kapena m’ndemanga.

  • “New World Translation”—Yaukatswiri ndi Yowona
    Nsanja ya Olonda—1991 | March 1
    • c Johann Babor, Karl F. Bahrdt, Petrus Dausch, Wilhelm M. L. De Wette, Georg F. Griesinger, Heinrich A. W. Meyer, Friedrich Muenter, Sebastian Mutschelle, Johann C. F. Schulz, Johann J. Stolz, ndi Dominikus von Brentano. August Dächsel, Friedrich Hauck, Johann P. Lange, ndi Ludwig Reinhardt anaika dzinalo m’mabulaketi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena