Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 23 tsamba 60-tsamba 61 ndime 5
  • Yesu Anachita Zozizwitsa Ali ku Kaperenao

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anachita Zozizwitsa Ali ku Kaperenao
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Zozizwitsa Zowonjezereka m’Kapernao
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Sunagoge Anali Malo Amene Yesu ndi Ophunzira Ake Ankakonda Kulalikira
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yesu Analalikira M’madera Ambiri a ku Galileya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 23 tsamba 60-tsamba 61 ndime 5
Anthu odwala asonkhana kunyumba kwa Petulo ndipo Yesu akuwachiritsa

MUTU 23

Yesu Anachita Zozizwitsa Ali ku Kaperenao

MATEYU 8:14-17 MALIKO 1:21-34 LUKA 4:31-41

  • YESU ANATULUTSA CHIWANDA

  • YESU ANACHIRITSA APONGOZI AKE A PETULO

Yesu anali atangosankha kumene ophunzira 4, omwe mayina awo anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane kuti akhale asodzi a anthu. Tsiku la Sabata litafika, iwo anapita ku sunagoge wa ku Kaperenao ndipo Yesu anayamba kuphunzitsa m’sunagogemo. Anthu anadabwa ndi mmene ankaphunzitsira chifukwa ankaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro ndipo izi zinali zosiyana kwambiri ndi mmene alembi ankaphunzitsira.

Pa tsiku limeneli, m’sunagogemo munalinso munthu wina wogwidwa ndi mzimu woipa ndiyeno munthu uja anafuula mwamphamvu kuti: “Kodi tili nanu chiyani, Yesu Mnazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu.” Yesu anadzudzula mzimu umene unagwira munthuyo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!”—Maliko 1:24, 25.

Pamenepo mzimuwo unagwetsera munthu uja pansi moti anayamba kugubuduka komanso kukuwa kwambiri. Koma mzimuwo unatuluka mwa munthuyo “osamuvulaza.” (Luka 4:35) Anthu amene anali m’sunagogemo anadabwa kwambiri ndipo anafunsa kuti: “Kodi chimenechi n’chiyani? Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu, ndipo ikumumvera.” (Maliko 1:27) N’zosadabwitsa kuti nkhani yochititsa chidwiyi inafalikira ku Galileya konse.

Atachoka ku sunagogeko, Yesu ndi ophunzira ake anapita kwawo kwa Simoni amene ankadziwikanso kuti Petulo. Kumeneko apongozi ake a Petulo ankadwala malungo aakulu ndipo anapempha Yesu kuti akawachiritse. Atafika kumeneko, anagwira dzanja la mayiwo n’kuwadzutsa. Atangotero malungowo anatheratu ndipo sanalole kuti Yesu ndi ophunzirawo anyamuke nthawi yomweyo. Mwina anachita zimenezo kuti awaphikire kaye chakudya.

Dzuwa litatsala pang’ono kulowa, anthu ochokera m’madera osiyanasiyana anabwera ndi anthu odwala kunyumba kwa Petulo moti pakhomopo panadzaza anthu ambiri. Kodi anthuwo ankabwera kudzatani? Ankabwera kuti Yesu adzawathandize, chifukwa “onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweretsa kwa iye. Ndipo iye anawachiritsa mwa kuika manja ake pa aliyense.” (Luka 4:40) Yesu anachiritsa matenda a mtundu uliwonse mogwirizana ndi zimene Malemba ananena. (Yesaya 53:4) Iye anathandizanso anthu amene anagwidwa ndi mizimu yoipa. Pamene mizimuyo inkatuluka, inkafuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” (Luka 4:41) Koma Yesu anaidzudzula ndipo sanailolenso kuti ilankhule chilichonse. Mizimuyo inkadziwa kuti Yesu anali Khristu ndipo iye sankafuna kuti izidzionetsa ngati kuti nayonso inkatumikira Mulungu woona.

MUNTHU WOGWIDWA NDI MZIMU WOIPA

Mizimu yoipa ikalowa mwa munthu, inkamuzunza kwambiri. (Mateyu 17:14-18) Koma mizimuyo ikatulutsidwa, munthuyo ankakhalanso bwinobwino. Yesu anasonyeza mobwerezabwereza kuti anali ndi mphamvu zochotsera mizimu yoipa pogwiritsira ntchito mzimu woyera wa Mulungu.—Luka 8:39; 11:20.

  • Kodi chinachitika n’chiyani m’sunagoge wa ku Kaperenao pa tsiku la Sabata?

  • Kodi Yesu anapita kuti atachoka ku sunagoge, nanga anakachita chiyani kumeneko?

  • Kodi anthu a mumzindawo anatani ataona zimene Yesu anachita kumeneko?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena