CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 6-7
Muzikhala Owolowa Manja
Munthu wowolowa manja amasangalala akamagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso zinthu zake pothandiza ndi kulimbikitsa ena.
Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “khalani opatsa” amasonyeza kukhala ndi chizolowezi chopatsa ena zinthu
Tikakhala opatsa, ena adzakhuthulira m’matumba athu “muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira.” Mawu a palembali angatanthauze zimene zinkachitika ogulitsa akamakhuthulira zinthu pamalaya akunja a munthu amene akugula