Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 40 tsamba 100-tsamba 101 ndime 7
  • Anawaphunzitsa Kukhululukira Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anawaphunzitsa Kukhululukira Ena
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Phunziro m’Chifundo
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Phunziro M’chifundo
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2010
  • “Phunzirani kwa Ine”
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 40 tsamba 100-tsamba 101 ndime 7
Mzimayi wochimwa akugwada kumapazi a Yesu pamene Yesuyo akudya pa tebulo limodzi ndi alendo ena

MUTU 40

Anawaphunzitsa Kukhululukira Ena

LUKA 7:36-50

  • MZIMAYI WOCHIMWA ANATHIRA MAFUTA MAPAZI A YESU

  • ANAWAPHUNZITSA KUKHULULUKA POGWIRITSA NTCHITO FANIZO LA NGONGOLE

Zimene anthu ankachita akamva kapena kuona zimene Yesu wachita zinkadalira mtima wa munthu. Zimenezi zinaoneka bwino pamene Yesu anali kunyumba ya Mfarisi wina mumzinda wa Galileya. Mfarisiyu yemwe dzina lake anali Simoni anaitana Yesu kuti akadye kunyumba kwake ndipo mwina anachita zimenezi kuti akakhale ndi mwayi wocheza ndi Yesu, yemwe ankachita zinthu zamphamvu. Yesu anavomera kupita kunyumba ya Mfarisiyu poona kuti akakhala ndi mwayi wolalikira kwa anthu enanso amene anaitanidwa. Kameneka si kanali koyamba kuitanidwa chifukwa nthawi ina ataitanidwa anavomera ndipo anadya ndi anthu okhometsa msonkho komanso anthu ena ochimwa.

Yesu atafika, sanalandiridwe ngati mmene ankalandilira alendo ena onse nthawi imeneyo. Ku Palesitina kunali mwambo woti mlendo akafika pa khomo azimusambitsa mapazi ndi madzi ozizira chifukwa anthu ankayenda m’misewu ya fumbi atavala masandasi, zomwe zinkachititsa kuti azimva kutentha m’mapazi komanso azituwa kwambiri. Koma Yesu atafika sanamusambitse mapazi kapena kumupsompsona ngati mmene ankachitira akalandira mlendo. Mwambo wina umene ankachita unali wothira mafuta m’mutu mwa mlendoyo posonyeza kuti amulandira ndi manja awiri koma Yesu sanamuchitirenso zimenezi. Kodi pamenepa tinganenedi kuti anamulandira?

Alendo onse anakhala mozungulira tebulo n’kuyamba kudya. Ali mkati mwa kudya, mzimayi wina yemwe sanaitanidwe analowa m’chipindamo mwakachetechete. Mayiyu “anali wodziwika mumzindawo kuti ndi wochimwa.” (Luka 7:37) Anthu onse ndi ochimwa koma zikuoneka kuti mzimayiyu anali ndi makhalidwe oipa ndipo mwina anali hule. N’kutheka kuti mayiyu anamva zimene Yesu ankaphunzitsa komanso anamva akuitana anthu onse ‘ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, kuti awatsitsimule.’ (Mateyu 11:28, 29) Zimene Yesu ankaphunzitsa komanso zimene ankachita zinamufika pamtima mayiyu moti anayamba kumufunafuna ndipo anamupeza.

Mzimayiyo atalowa m’chipindamo anafika pamene panali Yesu kudzera kumbuyo kwake ndipo anagwada kumapazi ake. Kenako anayamba kulira moti misozi yake inkagwera pamapazi a Yesu ndipo ankaipukuta ndi tsitsi lake. Anapsompsonanso mapazi a Yesu mwachikondi n’kuwathira mafuta onunkhira amene anabweretsa. Simoni ankangoyang’anitsitsa zimene zinkachitikazo koma sanagwirizane nazo. Mumtima mwake ankanena kuti: “Munthu uyu akanakhala mneneri, akanadziwa kuti mkazi amene akumugwirayu ndi ndani, ndiponso kuti ndi wotani. Akanadziwa kuti ndi wochimwa.”—Luka 7:39.

Munthu yemwe anali ndi ngongole akuthokoza munthu amene anamukongoza kuti wamukhululukira ngongole yake, ndipo munthu wina yemwe wakhululukiridwanso ngongole yake akuchoka

Yesu atadziwa zimene Simoni ankaganiza, ananena kuti: “Simoni, ndikufuna ndikuuze kanthu kena.” Iye anati: “Ndiuzeni Mphunzitsi!” Yesu ananena kuti: “Amuna awiri anatenga ngongole kwa munthu wina wokongoza ndalama. Mmodzi anatenga ngongole ya madinari 500, koma winayo anatenga ngongole ya madinari 50. Atasowa chopereka kuti abweze ngongolezo, mwiniwake uja anakhululukira onsewo ndi mtima wonse. Kodi ndani mwa awiriwo amene angam’konde kwambiri?” Simoni anangoyankha monyinyirika kuti: “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira zochulukayo.”—Luka 7:40-43.

Yesu anavomereza zimene Simoni ananena. Kenako Yesu akuyang’ana mzimayi uja anauza Simoni kuti: “Ukumuona kodi mayi uyu? Ngakhale kuti ndalowa m’nyumba yako, sunandipatse madzi otsukira mapazi anga. Koma mayi uyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuipukuta ndi tsitsi lake. Iwe sunandipsompsone, koma chilowereni muno, mayiyu sanaleke kupsompsona mapazi anga mwachikondi. Iwe sunathire mafuta m’mutu mwanga, koma mayiyu wapaka mapazi anga mafuta onunkhira.” Yesu anaona kuti zimene mayiyu anachita zinali umboni wakuti walapa kuchokera pansi pa mtima ndipo wasiya khalidwe lake loipalo. Choncho Yesu ananena kuti: “Ndikukuuza kuti, machimo ake akhululukidwa, ngakhale kuti ndi ochuluka. N’chifukwa chake akusonyeza chikondi chochuluka. Koma amene wakhululukidwa machimo ochepa amasonyezanso chikondi chochepa.”—Luka 7:44-47.

Zimene zinachitikazi si zikusonyeza kuti Yesu amalekerera makhalidwe oipa. Koma zikusonyeza kuti amamvetsa ndiponso kuchitira chifundo anthu amene achita machimo akuluakulu koma kenako amva chisoni ndi zimene achitazo n’kutembenukira kwa Khristu kuti awathandize. Ndipotu mosakayikira mayiyu analimbikitsidwa Yesu atamuuza kuti: “Machimo ako akhululukidwa. . . . Chikhulupiriro chako chakupulumutsa. Pita mu mtendere.”—Luka 7:48, 50.

  • Kodi Yesu analandiridwa bwanji kunyumba kwa Simoni?

  • N’chifukwa chiyani mzimayi wina ankafunafuna Yesu?

  • Kodi Yesu ananena fanizo lotani ndipo ankatanthauza chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena