Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 74 tsamba 174-tsamba 175 ndime 8
  • Zimene Tikuphunzira pa Nkhani Yochereza Alendo Komanso ya Pemphero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Tikuphunzira pa Nkhani Yochereza Alendo Komanso ya Pemphero
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Uphungu kwa Marita, ndi Chilangizo pa Pemphero
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Uphungu kwa Marita, ndi Malangizo pa Pemphero
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Ndimakhulupirira”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • “Ndimakhulupirira”
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 74 tsamba 174-tsamba 175 ndime 8
Mariya wakhala pafupi ndi Yesu pamene Yesuyo akulankhula ndi Marita

MUTU 74

Zimene Tikuphunzira pa Nkhani Yochereza Alendo Komanso ya Pemphero

LUKA 10:38–11:13

  • YESU ANAPITA KUNYUMBA KWA MARITA NDI MARIYA

  • CHIFUKWA CHAKE TIYENERA KUPEMPHERA MWAKHAMA

Mzinda wa Betaniya unali chakum’mawa kwa phiri la Maolivi ndipo unali pa mtunda wa makilomita atatu kuchokera ku Yerusalemu. (Yohane 11:18) Tsiku lina, Yesu anapita ku Betaniya ndipo anafikira kunyumba ya Marita ndi Mariya. Yesu ankagwirizana kwambiri ndi Marita ndi Mariya komanso mchimwene wawo, Lazaro. Atafika kumeneko anthuwa analandira Yesu ndi manja awiri.

Anthuwa anasangalala kwambiri kulandira Mesiya kunyumba kwawo. Choncho pofuna kusonyeza kuti amulandira bwino, Marita anayamba kukonzera Yesu chakudya chabwino kwambiri. Pamene Marita ankakonza chakudyachi n’kuti Mariya atakhala pansi n’kumamvetsera zimene Yesu ankalankhula. Patapita kanthawi Marita anauza Yesu kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekerera ndekha ntchito? Tamuuzani kuti andithandize.”—Luka 10:40.

Koma m’malo modzudzula Mariya, Yesu anapereka malangizo kwa Marita chifukwa choti ankadera nkhawa kwambiri zinthu zakuthupi. Anamuuza kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri. Komatu zinthu zofunika kwenikweni n’zochepa chabe, mwinanso n’chimodzi chokha basi. Kumbali yake, Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri, ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.” (Luka 10:41, 42) Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti zinali zosafunika kuti Marita atenge nthawi yaitali akukonza chakudya chambiri, chifukwa chakudya chosavuta kukonza chinali chokwanira.

Marita anali ndi maganizo abwino chifukwa ankafuna kusonyeza kuti walandira Yesu ndi manja awiri. Koma chifukwa chodera nkhawa kwambiri za chakudya, analephera kuphunzira zinthu zofunika kwambiri kuchokera kwa Mwana wa Mulungu. Yesu ananena kuti Mariya anasankha bwino kwambiri chifukwa anasankha zinthu zokhalitsa ndipotu limeneli ndi phunzironso kwa ife.

Pa nthawi ina Yesu ananenanso mfundo yofanana ndi imeneyi. Wophunzira wake wina anamupempha kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, ngati mmene Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.” (Luka 11:1) Pafupifupi chaka ndi hafu m’mbuyomo, pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anali ataphunzitsa ophunzira akewo mmene angamapempherere. (Mateyu 6:9-13) Zikuoneka kuti pa nthawi imene Yesu anaphunzitsa nkhani ya pempheroyi wophunzirayu panalibe. Choncho Yesu anabwereza mfundo zikuluzikulu zimene anaphunzitsa. Ndiyeno pofuna kuthandiza ophunzirawo kuti amvetse kufunika kochita khama popemphera, anawafotokozera fanizo.

Iye anati: “Ndani wa inu amene ali ndi bwenzi lake kumene angapite pakati pa usiku kukam’pempha kuti, ‘Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate, chifukwa mnzanga wangofika kumene kuchokera ku ulendo ndipo ndilibe chomupatsa’? Ndiyeno ali m’nyumbayo n’kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine. Takhoma kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona kale. Sindingadzukenso kuti ndikupatse kanthu.’ Ndithu ndikukuuzani, Adzadzuka ndi kum’patsa zonse zimene akufuna, osati chifukwa chakuti ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha kukakamira kwake.”—Luka 11:5-8.

Pamenepa Yesu sanatanthauze kuti Yehova amachita kukakamizika kuti ayankhe mapemphero ngati mmene anachitira munthu wa m’fanizoli. Koma iye ankatanthauza kuti ngati munthu wa m’fanizo lija anathandiza mnzakeyo chifukwa chomuchonderera mobwerezabwereza, ndiye kuti Atate wathu wakumwamba yemwe amatikonda adzayankha mapemphero ochokera pansi pamtima a atumiki ake okhulupirika. Yesu ananenanso kuti: “Choncho ndikukuuzani, Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. Pakuti aliyense wopempha amalandira, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzam’tsegulira.”—Luka 11:9, 10.

Kenako Yesu pofuna kuthandiza ophunzirawo kumvetsa mfundo yake anayerekezera Mulungu ndi zimene bambo amene ali ndi ana amachita. Iye anati: “Kodi kapena pakati panu alipo bambo amene mwana wake atam’pempha nsomba, angam’patse njoka m’malo mwa nsomba? Kapena atam’pempha dzira iye angam’patse chinkhanira? Choncho ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:11-13) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Atate wathu amamvetsera komanso kuti ndi wofunitsitsa kuyankha zimene tamupempha.

  • Fotokozani kuti maganizo a Marita ndi Mariya ankasiyana bwanji pa zinthu zomwe ankaona kuti ndi zofunika, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani?

  • N’chifukwa chiyani Yesu anabwereza nkhani ya pemphero?

  • Kodi Yesu anapereka fanizo lotani pofuna kusonyeza kufunika kochita khama popemphera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena