-
‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’Nsanja ya Olonda—2008 | October 1
-
-
Mariya ndi Yosefe atafika anapeza kuti mzindawo wadzaza ndi anthu. Anzawo ena odzalembetsa anali atafika kale, moti malo onse ogona anali atatha.b Ndiye chifukwa chozingwa anakagona m’khola. Kodi mukuganiza kuti Yosefe anamva bwanji kuona mkazi wake akuyamba kubuula ndi ululu wobereka kwa nthawi yoyamba? Ndipotu tangoganizirani kuti zonsezi zinkachitikira m’khola.
Mayi aliyense angathe kumvetsa zimene zinam’chitikira Mariya. Panthawiyi n’kuti patapita zaka 4,000 kuchokera pamene Yehova analosera kuti akazi onse azidzamva ululu pobereka, chifukwa cha uchimo umene anthu anatengera kwa Adamu ndi Hava. (Genesis 3:16) Palibe umboni uliwonse woti Mariya yekha sanamve ululu. Luka sananene chilichonse pankhani imeneyi, m’malomwake anangoti: “Anabereka mwana wake woyamba wamwamuna.” (Luka 2:7) Uyu anali “mwana woyamba” wa Mariya, mwa ana osachepera 7 amene iye anabereka. (Maliko 6:3) Komabe mwana woyambayo anali wosiyana kwambiri ndi anzake onsewo. Iyeyu kwenikweni anali mwana wa Yehova “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” kapena kuti Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.—Akolose 1:15.
Apa Luka anatchulapo mfundo yodziwika kwambiri yakuti: “Anamukulunga ndi nsalu n’kumugoneka modyeramo ziweto.” (Luka 2:7) Padziko lonse, m’zithunzi ndiponso m’masewero ambiri a kubadwa kwa Ambuye Yesu, amaonetsa zimenezi m’njira yokometsera kwambiri. Koma kodi zenizeni zimene zinachitika zinali zotani? Malo odyera ziweto sakhala malo aukhondo ayi. Motero banjali linagona m’khola monunkha komanso mwauve, monga mmene makola ambiri amakhalira. Palibe makolo amene angasankhe kuti mwana wawo akabadwire m’malo amenewa ngati patakhala malo ena abwinopo. Makolo ambiri amayesetsa kusamalira kwambiri ana awo. Ndiye kodi mukuganiza kuti Mariya ndi Yosefe akanasankha dala kuti Mwana wa Mulungu abadwire malo osasamalika chonchi?
Ngakhale kuti sakanatha kupeza malo abwino, iwo sanakhumudwe koma anayesetsa kuchita zimene akanatha mogwirizana ndi kupeza kwawo. Mwachitsanzo taonani kuti Mariya anam’samalira yekha mwanayo, anamukulunga bwinobwino ndi nsalu. Kenaka anamugoneka modyera ziweto kuti azimva kutenthera n’kugona tulo tabwino. Mariya sanalole kuti kuganizira mavuto awo kumulepheretse kuchita zimene akanatha posamalira mwana wake. Iyeyu pamodzi ndi Yosefe ankadziwa kuti chinthu chofunika kwambiri ndicho kum’samalira mwanayo mwauzimu. (Deuteronomo 6:6-8) Masiku ano, makolo anzeru amaonanso kuti kusamalira ana awo mwauzimu m’dziko losakonda Mulunguli n’kofunika kwambiri kuposa zinthu zonse.
-
-
‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’Nsanja ya Olonda—2008 | October 1
-
-
b Masiku amenewo mzinda uliwonse unkakhala ndi malo ogona anthu apaulendo, kaya ndi oyenda pansi kapena paziweto.
-