Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 166
  • Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya ndalama?
  • N’chifukwa chiyani Baibulo limati kukonda ndalama n’koipa?
  • Kodi malangizo a m’Baibulo angatithandize bwanji pa nkhani ya ndalama?
  • Ndalama
    Galamukani!—2014
  • Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?
    Galamukani!—2015
  • Tiziona Ndalama Moyenera
    Galamukani!—2007
  • Kodi Ndalama Tingazione Motani M’njira Yoyenera?
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 166
Munthu wapeza ndalama zambirimbiri.

Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?

Yankho la m’Baibulo

Ayi. Baibulo silinena kuti ndalama ndi zoipa kapena kuti ndi zomwe zimabweretsa mavuto. Komabe, zimene anthu ambiri amakonda kunena zoti ndalama ndi muzu wa zoipa zonse, zimangosonyeza kuti samvetsa zimene Baibulo limafotokoza. Baibulo limanena kuti “muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama.”a—1 Timoteyo 6:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau A Mulungu.

  • Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya ndalama?

  • N’chifukwa chiyani Baibulo limati kukonda ndalama n’koipa?

  • Kodi malangizo a m’Baibulo angatithandize bwanji pa nkhani ya ndalama?

  • Malemba a m’Baibulo onena za ndalama

Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya ndalama?

Baibulo limanena kuti munthu akamagwiritsa ntchito ndalama mwanzeru, zikhoza kumuthandiza komanso ‘kumuteteza.’ (Mlaliki 7:12) Ndipotu limayamikira anthu owolowa manja omwe amathandiza anzawo, kuphatikizapo kuwapatsa ndalama.—Miyambo 11:25.

Ngakhale zili choncho, Baibulo limatichenjezanso kuti tisamakonde kwambiri ndalama. Limanena kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” (Aheberi 13:5) Apa mfundo ndi yakuti m’malo momangosakasaka chuma, tizigwiritsa ntchito ndalama zimene tili nazo mwanzeru ndipo tizikhala okhutira ndi zinthu zomwe tapeza monga chakudya, zovala ndi pogona.—1 Timoteyo 6:8.

N’chifukwa chiyani Baibulo limati kukonda ndalama n’koipa?

Anthu a umbombo sadzapeza moyo wosatha. (Aefeso 5:5) Tikutero chifukwa umbombo uli ngati kulambira mafano kapena kuti kulambira konyenga. (Akolose 3:5) Komanso anthu a umbombo akafuna kupeza chinthu, sagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Lemba la Miyambo 28:20 limanena kuti munthu “woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.” Anthu amene amafuna kuti apeze zinthu mofulumira, amachita zinthu mwachiphamaso, amalanda zinthu za ena, amaba, kusunga anthu ena mokakamiza ngakhalenso kupha anthu ena.

Ngakhale kuti anthu ena amaganiza kuti kukonda ndalama sikungawachititse kukhala ndi makhalidwe oipa, komabe kuli ndi mavuto ake. Baibulo limanena kuti: “Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa.”—1 Timoteyo 6:9.

Kodi malangizo a m’Baibulo angatithandize bwanji pa nkhani ya ndalama?

Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kutsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ndalama, Mulungu adzasangalala nafe ndipo sangatisiye. Ndipotu Mulungu akulonjeza anthu amene amayesetsa kumusangalatsa kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheberi 13:5, 6) Iye amatitsimikiziranso kuti “munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri.”—Miyambo 28:20.

Malemba a M’Baibulo Onena za Ndalama

Mlaliki 7:12: “Ndalama zimatetezera.”

Mfundo yake: Ndalama zikhoza kumuteteza munthu ngati akuzigwiritsa ntchito mwanzeru.

Luka 12:15: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”

Mfundo yake: Ndalama si zofunika kwambiri pa moyo wathu ndipo sizingatithandize kuti tidzapulumuke.

1 Timoteyo 6:10: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.”

Mfundo yake: Ndalama pazokha si zoipa. Koma amene amazikonda kwambiri ndiponso kumangokhalira kuziganizira, zimawabweretsera mavuto ambiri monga kusokonezeka kwa mabanja komanso sakhala ndi thanzi labwino chifukwa choti amangokhalira kugwira ntchito.

Aheberi 13:5: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”

Mfundo yake: M’malo momangokhalira kusakasaka chuma, tizikhutira ndi zimene tili nazo.

Mateyu 19:24: “N’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.”

Mfundo yake: Pa nthawiyi Yesu anauza mnyamata wina yemwe anali wachuma kuti akhale wotsatira wake. Mnyamatayo anakana chifukwa choti ankakonda kwambiri chuma chakecho. Ndiyeno Yesu anapereka chenjezo loti munthu amene amakonda kwambiri chuma kuposa Mulungu, sangadzapeze moyo wosatha.

a M’Mabaibulo ena vesili linamasuliridwanso kuti: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena