Mbiri Yabwino Kaamba ka Mtundu Wonse wa Anthu!
‘NDIPO ndinawona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nayo Mbiri Yabwino yosatha, ailalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu onse.’ (Chibvumbulutso 14:6) Ndi mawu amenewo, mtumwi Yohane wokalambayo analongosola masomphenya ouziridwa aulosi, masomphenya amene akukwaniritsidwa m’tsiku lathu. Ndi mpumulo wotani nanga kudziŵa kuti pali mbiri yabwino mu mbadwo uno wa upandu, kuipitsa, uchigaŵenga, nkhondo, ndi kufalikira komakwerakwera ndi kusatsimikizirika kwa zachuma! Koma kodi ndi mbiri yotani imene ingakhale yabwino koposa kotero kuti ikufunikira mngelo kuilengeza? Kodi ndi mbiri yotani imene ingakhale yosangalatsa mokwanira kotero kuti iyenerere kulalikidwa ku mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu onse?
Tingayankhe zimenezo titalingalira za chochitika china kumbuyoko pamene mngelo mwaumwini analengeza mbiri yabwino. Zimenezo zinali pamene zaka za zana loyamba B.C.E. zinali kufika kumapeto, chifupifupi zaka zana limodzi Yohane asanawone masomphenya ake. Abusa anali kunja ndi nkhosa zawo m’munda pafupi ndi Betelehemu, ndipo mngelo anawonekera nalengeza za kubadwa kwa Yesu, akumati: ‘Onani, ndikuuzani inu mbiri yabwino ya chikondwerero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse pakuti wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.’—Luka 2:10, 11.
Kubadwa kwa Yesu kunalidi ‘mbiri yabwino ya chikondwerero chachikulu.’ Iye anakula kukhala Kristu wolonjezedwa ndi Mpulumutsi, iye amene anapereka moyo wake waumunthu wangwiro kotero kuti akhulupiriri ake angwiro angakhale ndi moyo. Kuwonjezera pa zimenezo, iye anayenera kudzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, “Kalonga wa Mtendere,” amene mu ulamuliro wake chilungamo ndi mtendere pomalizira pake zidzakhala kwa mtundu wa anthu. (Yesaya 9:6; Luka 1:33) Zowonadi, kubadwa kwake kunali mbiri yabwino imene inayenerera kulengezedwa ndi mngelo!
Yesu Ali Mfumu
Kubwerera mu zaka za zana loyamba, Yesu anakwaniritsa zifuno zambiri za Mulungu kaamba ka iye, koma panthaŵiyo anali asadaikidwe kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Monga mmene magazine ano asonyezera kaŵirikaŵiri, zimenezo sizinachitike kufikira 1914. Monga mmene kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewo kukusonyezera mowonekera, m’chaka chimenecho Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba. (Chibvumbulutso 12:10, 12) Ngakhale kuti kunali mbiri yoipa kwambiri mu 1914—kuwulika kwa Nkhondo ya Dziko ya I—kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu kunali mbiri yabwino koposa. Chimenecho ndicho chifukwa chake Yesu analosera kaamba ka tsiku lathu kuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse.”—Mateyu 24:14, NW.
Kodi ulosi wa Yesu wakwaniritsidwa? Yankho ndi lakuti inde! Ndipo masomphenya aulosi a Yohane akukwaniritsidwanso. Zowonadi, sitingamuwone mngelo wosawoneka amene Yohane anawona. Koma Mboni za Yehova zakhala zikuwoneka kwambiri pamene zikulalikira mbiri yabwino ya mngeloyo “kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” M’maiko ndi zisumbu za m’nyanja 212, mawu awo amvedwa. Ndipo makamu akuvomereza. Zokumana nazo za ena a ameneŵa zidzasonyeza mmene mbiri imeneyi yonena za Ufumu wa Mulungu iriri yabwino.