-
Yesu Anapereka Malangizo pa Nkhani ya ChumaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Kodi ndi ndani amene ankafunika kufunafuna Ufumu wa Mulungu? Yesu ananena kuti amene azidzachita zimenezi ndi anthu ochepa okhulupirika a “kagulu ka nkhosa.” Ndipo patapita nthawi zinadzadziwika kuti chiwerengero cha anthuwo chinali 144,000. Kodi kagulu kameneka kankayembekezera chiyani? Yesu ananena kuti: “Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.” Anthu a mu kaguluka saganizira kwambiri zopeza chuma cha m’dzikoli, chomwe anthu akhoza kuba, koma amaganizira za “chuma chosatha kumwamba,” komwe akalamulire ndi Khristu.—Luka 12:32-34.
-
-
Woyang’anira Nyumba Wokhulupirika Ayenera Kukhala WokonzekaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Yesu anafotokoza kuti a “kagulu ka nkhosa” okha ndi amene ali ndi malo mu Ufumu wakumwamba. (Luka 12:32) Koma munthu amene wapatsidwa mwayi umenewu sayenera kuuona mopepuka. Ndipotu Yesu anafotokoza kufunika koti munthu amene wasankhidwa kuti akalamulire nawo mu Ufumu aziona zinthu moyenera.
-