Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi Yehova Mulungu analankhula kwa Adamu mwachindunji, kapena kodi analankhula kupyolera mwa Mawu, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu?
Baibulo silimatipatsa yankho lachindunji ku funso limeneli. Pamene kuli kwakuti Mulungu akanalankhula mwachindunji kwa mwana wake waumunthu wangwiro mu Edeni, mwachiwonekere Iye analankhula ndi Adamu kupyolera mwa Mawuyo.
Kaŵirikaŵiri Baibulo limalankhula za Mulungu kukhala akumachita zinthu pamene m’chenicheni iye anachita zinthuzo kupyolera mwa mngelo mmodzi kapena oposapo. Mwachitsanzo, Genesis 1:1 akutiuza kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Kukanakhala kuti zimenezo ndizo zokha zimene Baibulo linanena ponena za chiyambi cha chilengedwe chonse, tikadati Mulungu anachilenga mwachindunji, ndi manja ake enieni. Komabe, Malemba Achikristu Achigiriki, amakulitsa kumvetsetsa kwathu. Timaŵerenga kuti: “Mwa [Mwana wa Mulungu], zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko, zowoneka ndi zosawoneka . . . zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.” (Akolose 1:16, 17) Malemba ena amatsimikizira ntchito ya Mwanayo m’kulenga chilengedwe chonse. (Yohane 1:3, 10; Ahebri 1:1, 2) Chikhalirechobe, ntchito yake inali yokhala mmisiri wogonjera kwa Yehova, amene anayambitsa, kupereka mphamvu, ndi kutsogoza kulenga.—Salmo 19:1.
Mulungu anati kwa munthu woyamba: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko.” (Genesis 2:16, 17) Yehova sanafunikire chiŵiya cha makina kapena chamagetsi, chonga megafoni kapena wailesi ya shortwave. Monga mmene Nsanja ya Olonda ya August 1, 1989, inanenera kuti: “Mwamunayo sanawone aliyense akulankhula. Liwulo linachokera kosawoneka, m’bwalo losawoneka, ndipo linali kulankhula kwa iye. Linali liwu la Mpangi wa mwamunayo, Mlengi wake! . . . Mwamunayo sanafunikire cholandirira cha wailesi yamakono ya usayansi kuti amve liwu laumulungulo. Mulungu analankhula naye mwachindunji.”
Kodi Mulungu analankhulira mwa mngelo, mwinamwake Logosi, yemwe anadzakhala Yesu? Ichi nchothekera kwenikweni. Posakhala woumirira, C. T. Russell analemba kuti: “Mwinamwake Yesu anali Woimira wa Mulungu m’Munda wa Edeni ndi Adamu.” (The Watch Tower, February 1, 1915) Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu anatumikira kwa nthaŵi yaitali m’thayo lolemekezeka la kukhala “Mawu” a Atate wake, kapena Womlankhulira, kwa angelo ndi anthu. (Yohane 1:1; 12:49, 50; Chibvumbulutso 1:1, 2) Chotero ngakhale kuti cholembera cha Genesis chimapereka lingaliro lakuti Mulungu analankhula mwachindunji kwa Adamu wokhala yekha, chimenecho sichimachotsapo nsonga ya kulankhula Kwake kupyolera mwa mngelo, kuphatikizapo Mawuyo, Mwana wakumwamba wa Yehova. Izi ziyenera kukhala tero makamaka polingalira kuti Yehova anagwiritsira ntchito Logosi kulenga munthu poyamba, ndipo ameneyu ‘anakonda zinthu zochita ndi ana a anthu.’—Miyambo 8:22, 31; Yohane 1:3.
Mwachitsanzo, lingalirani chochitika cha Mose pamene anakwera ku Phiri la Sinai. Eksodo 19:21-24 amalongosola kuti: “Ndipo Yehova anati kwa Mose . . . Ndipo Mose anati kwa Yehova . . . Ndipo Yehova anati kwa iye.” Kenaka mbiri ya kupatsidwa kwa Malamulo Khumi ikuperekedwa mwanjira iyi: “Ndipo Mulungu ananena mawu onse amenewa, nati.” (Eksodo 20:1) Kodi zimenezo zimamveka ngati kuti Mulungu analankhula mawu a Chilamulo mwaumwini? Lingaliro loterolo lingapeze chilikizo m’chakuti tikuuzidwa kuti Mulungu analankhula kwa Mose “kopenyana maso.”—Eksodo 33:11.
Chikhalirechobe, tiri ndi vumbulutso lowonjezereka pa zimenezi. Mtumwi Paulo analemba ponena za Chilamulo kuti: “Chinakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe.” (Agalatiya 3:19) Pambuyo pake, Paulo mwachindunji anasiyanitsa malangizo amene Mulungu anapereka mu Chilamulo ndi zimene Akristu analandira kupyolera mwa Yesu kuti: “Pakuti ngati mawu adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chirichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera . . . , tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? chimene [chidayamba kulankhulidwa mwa, NW] Ambuye [Yesu] . . . , ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife.” (Ahebri 2:2, 3) Chotero Mulungu sanalankhule mawu a Chilamulo ndi liwu lake lenileni, sanagwiritsirenso ntchito Logosi. M’malo mwake, iye anasankha kugwiritsira ntchito angelo ena.
Ngakhale nditero, kodi nsonga yaikulu njotani? Kaŵirikaŵiri pamene timaŵerenga za Mulungu akulakhula kwa anthu, timawona kuti iye anatero kupyolera mwa zolengedwa zake zauzimu zomvera zimene zinamlankhulira. (Yerekezerani ndi Genesis 18:2, 3, 33; 19:1; Eksodo 3:2-4; Oweruza 6:11, 12, 20-22.) Kutchedwa kwa Yesu kukhala Mawu kumapereka lingaliro lakuti ali iye amene Mulungu anamgwiritsira ntchito kaŵirikaŵiri kulankhula ndi zolengedwa zake zina. Kodi zimenezo zinaphatikizapo mwana wa Mulungu wangwiro Adamu? Zikuwonekadi tero.—Luka 3:38.
Nzowona kuti pamene Logosi pambuyo pake anali pa dziko lapansi, Atateyo analankhula katatu momveka kotero kuti “Adamu wotsirizayo” anakhoza kumva. (1 Akorinto 15:45; Mateyu 3:16, 17; 17:1-5; Yohane 12:28-30) Pa zochitika zimenezi, kodi Mulungu akanalankhuliranji kwa kapena ponena za Mwana wake wamtengo wapatali kupyolera mwa mngelo wokhala pakati? Mwanzerudi, Yehova akalankhula mwachindunji; Mwana wake wangwiro, ndipo ngakhale anthu opanda ungwiro okhala pafupi, anamva liwu lenileni la Mulungu. Chotero pamene munthu wangwiro Adamu analengedwa, Atate wake wachikondi ayenera kukhala anachita mwachindunji ndi cholengedwa chatsopano chimenechi. Komabe, polingalira zapamwambazi, nkowonekeratu kuti iye anagwiritsira ntchito Mawuyo.