-
Mzimu wa Yehova Umatsogolera Anthu AkeNsanja ya Olonda—1992 | September 15
-
-
Mmene Mzimu Umathandizira
9. (a) Kodi mzimu woyera umagwira ntchito motani monga “mthandizi”? (b) Kodi timadziŵa motani kuti mzimu woyera simunthu? (Wonani mawu amtsinde.)
9 Yesu Kristu anatcha mzimu woyera “mthandizi.” Mwachitsanzo, anauza otsatira ake kuti: “Ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu [mthandizi, NW], kuti akhale ndi inu kunthaŵi yonse, ndiye mzimu wa chowonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuwona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.” Pakati pa zinthu zina, “mthandizi” ameneyo akakhala mphunzitsi, pakuti Kristu analonjeza kuti: “Koma [mthandiziyo, NW], mzimu woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.” Mzimuwo ukachitiranso umboni za Kristu, ndipo anatsimikiziritsa ophunzira ake kuti: “Kuyenera kwa inu kuti ndichoke ine. Pakuti ngati sindichoka, [mthandiziyo, NW] sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita, ndidzamtuma iye kwa inu.”—Yohane 14:16, 17, 26; 15:26; 16:7.a
10. Kodi ndimnjira zotani zimene mzimu woyera wakhalira mthandizi?
10 Kuchokera kumwamba, Yesu anatsanulira mzimu woyera wolonjezedwa pa otsatira ake pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E. (Machitidwe 1:4, 5; 2:1-11) Monga mthandizi, mzimu unawapatsa chidziŵitso chowonjezereka cha chifuno ndi cholinga cha Mulungu ndi kumasulira Mawu aulosi kwa iwo. (1 Akorinto 2:10-16; Akolose 1:9, 10; Ahebri 9:8-10) Mthandizi ameneyo anapatsanso mphamvu ophunzira a Yesu kukhala mboni m’dziko lonse lapansi. (Luka 24:49; Machitidwe 1:8; Aefeso 3:5, 6) Lerolino, mzimu woyera ungathandize Mkristu wodzipatulira kukula m’chidziŵitso ngati amagwiritsira ntchito zogaŵira zonse zauzimu zoperekedwa ndi Mulungu mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Mzimu wa Mulungu ungapereke chithandizo mwakugaŵira chilimbikitso ndi mphamvu zofunikira kuchitira umboni monga mmodzi wa atumiki a Yehova. (Mateyu 10:19, 20; Machitidwe 4:29-31) Komabe, mzimu woyera umathandizanso anthu a Mulungu m’njira zina.
-
-
Mzimu wa Yehova Umatsogolera Anthu AkeNsanja ya Olonda—1992 | September 15
-
-
a Ngakhale kuti mzimu woyera watchedwa “mthandizi” monga ngati kuti ndimunthu, uwo suli munthu, chifukwa mloŵa mmalo wa dzina Wachigiriki wosonya ku chinthu (womasuliridwa “iye”) wagwiritsiridwa ntchito pa mzimu. Aloŵa mmalo a dzina achikazi a Chihebri mofananamo amagwiritsiridwa ntchito kutchula nzeru monga munthu. (Miyambo 1:20-33; 8:1-36) Ndiponso, mzimu woyera “unatsanuliridwa,” zimene sizingachitidwe ndi munthu.—Machitidwe 2:33.
-