Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • re mutu 3 tsamba 15-17
  • Zinthu Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zinthu Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa
  • Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Yotumizira Uthenga
  • Khalani Oŵerenga Achimwemwe a Buku la Chivumbulutso
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Dzina la Buku la M’Baibulo, Lakuti Chivumbulutso, Limatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mmene Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Akukukhudzirani
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Imvani Chimene Mzimu Unena ku Mipingo
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
re mutu 3 tsamba 15-17

Mutu 3

Zinthu Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa

1. Kodi mungatani kuti mudzapulumuke Mulungu akamaweruza dzikoli?

N’CHIFUKWA chiyani muyenera kuganizira kwambiri zinthu zimene zikuchitika m’dziko masiku ano? Chifukwa chakuti posachedwapa, Mulungu aweruza dzikoli koma inuyo mukhoza kupulumuka. Mungapulumuke ngati mutapewa kukhala “mbali ya dziko” limene liwonongedwe posachedwapa. Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti muzikhala moyo wodzimana monyanyira. Zikutanthauza kuti muzikhala ndi moyo wosangalala koma muzipewa kulowerera m’ndale, kuchita nawo malonda achinyengo ndiponso muzipewa zipembedzo zimene sizilemekeza Mulungu. Komanso muzipewa kuchita zachiwawa ndi zachiwerewere ndipo muzitsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino ndi kuyesetsa kuchita zimene iye amafuna. (Yohane 17:14-16; Zefaniya 2:2, 3; Chivumbulutso 21:8) Buku la Chivumbulutso limasonyeza kufunika kosintha moyo wathu kuti ugwirizane ndi mfundo zimenezi.

2. Polemba ulosi wofunika wa m’buku la Chivumbulutso, kodi mtumwi Yohane anayamba ndi mawu otani, ndipo kodi Mulungu ankapereka kwa ndani uthenga umenewu?

2 Polemba ulosi wofunika umenewu, mtumwi Yohane anayamba ndi mawu akuti: “Chivumbulutso choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa, kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.” (Chivumbulutso 1:1a) Yesu Khristu atabwerera kumwamba, analandira uthenga wamphamvu umenewu kuchokera kwa Mulungu. Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu amagonjera Mulungu, yemwe ndi Atate ake. Izi n’zosiyana ndi zinthu zovuta kumvetsa zimene ena amakhulupirira kuti iye ndi mmodzi mwa milungu itatu imene amati ndi mulungu mmodzi. Nawonso “akapolo” amene amapanga mpingo wachikhristu amagonjera Yesu Khristu moti ‘amamutsatira kulikonse kumene akupita.’ (Chivumbulutso 14:4; Aefeso 5:24) Kodi ndani amene alidi “akapolo” a Mulungu masiku ano, ndipo uthenga wa m’buku la Chivumbulutso umawapindulitsa bwanji?

3. (a) Kodi ndani amene ali “akapolo” amene amagonjera Yesu Khristu? (b) Kodi “akapolo” okhulupirika akugwira ntchito yotani motsogoleredwa ndi angelo?

3 Mtumwi Yohane, amene analemba buku la Chivumbulutso, ananena kuti iyeyo ndi mmodzi wa akapolo amenewo. Iye anali mtumwi amene anakhala ndi moyo nthawi yaitali ndipo anali m’gulu la “akapolo” odzozedwa ndi mzimu amene Mulungu anawasankha kuti akalandire moyo umene sungafe, kumwamba. Masiku ano pali anthu ochepa a m’gulu limeneli amene ali ndi moyo padziko lapansi. Koma pali mamiliyoni ambiri a atumiki enanso a Mulungu, omwe ndi khamu lalikulu la amuna, akazi ndi ana. Motsogoleredwa ndi angelo, iwowa limodzi ndi “akapolo” odzozedwa, akugwira ntchito yolengeza uthenga wabwino wosatha kwa anthu onse. “Akapolo” onsewa akugwira ntchito mwakhama pothandiza anthu ofatsa padziko lapansi kuti adzapulumuke. (Mateyu 24:14; Chivumbulutso 7:9, 14; 14:6) Buku la Chivumbulutso limasonyeza zimene muyenera kuchita kuti mupindule ndi uthenga wake wabwino komanso wosangalatsa.

4. (a) Popeza kuti tsopano patha zaka zoposa 1,900 Yohane atalemba buku la Chivumbulutso, n’chifukwa chiyani analemba kuti ‘zinthu zimenezi ziyenera kuchitika posachedwapa’? (b) Kodi umboni umene ulipo masiku ano ukusonyeza chiyani ponena za ulosi wa m’Baibulo?

4 Yohane anati “akapolo” amenewa adzasonyezedwa “zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.” Kodi iye ankatanthauza chiyani popeza kuti tsopano patha zaka zoposa 1,900 kuchokera nthawi imeneyo? Yehova amaona kuti zaka 1,000 zili ngati “dzulo lapitali.” Choncho zaka 1,900 ndi nthawi yaifupi tikaiyerekezera ndi zaka zosawerengeka zimene iye anakhala akulenga ndi kukonza dziko lapansi kuti anthu azikhalamo. (Salimo 90:4) Nayenso mtumwi Paulo analemba kuti, “ndikudikira mwachidwi, ndiponso ndili ndi chiyembekezo.” Analemba zimenezi chifukwa ankatsimikiza kuti nthawi yoti alandire mphoto yake ili pafupi. (Afilipi 1:20) Masiku anonso pali umboni wotsimikiza kuti zinthu zonse zimene zinaloseredwa zichitika pa nthawi yake. Kuposa nthawi ina iliyonse m’mbuyomu, panopa pali zinthu zambiri zimene zingalepheretse anthu kupulumuka. Koma Mulungu yekha ndi amene angawapulumutse.—Yesaya 45:21.

Njira Yotumizira Uthenga

5. Kodi uthenga wa m’buku la Chivumbulutso unaperekedwa bwanji kwa mtumwi Yohane ndiponso kumipingo?

5 Lemba la Chivumbulutso 1:1b, 2 limapitiriza kuti: “Yesuyo anatumiza mngelo wake kuti adzapereke Chivumbulutsocho mwa zizindikiro kwa kapolo wake Yohane. Yohaneyo anachitira umboni mawu a Mulungu, ndiponso umboni umene Yesu Khristu anapereka, kutanthauza zonse zimene anaona.” Apa zikusonyeza kuti Yohane analandira uthenga wouziridwa kudzera mwa mngelo. Yohane analemba uthengawo mumpukutu, n’kuutumiza kumipingo imene inalipo pa nthawiyo. Ndife oyamikira kuti Mulungu anaonetsetsa kuti uthenga umenewo usungidwe mpaka lero kuti uzilimbikitsa mipingo pafupifupi 100,000 ya atumiki ake ogwirizana padziko lonse lapansi.

6. Kodi Yesu anasonyeza kuti ndi njira iti imene adzagwiritse ntchito popereka chakudya chauzimu kwa ‘akapolo’ ake masiku ano?

6 M’nthawi ya Yohane, Mulungu anali ndi njira yotumizira uthenga wa m’buku la Chivumbulutso ndipo anagwiritsira ntchito Yohaneyo potumiza uthengawo padziko lapansi. Masiku anonso Mulungu ali ndi njira yoperekera chakudya chauzimu kwa ‘akapolo’ ake. Mu ulosi wake waukulu wonena za mapeto a nthawi ino, Yesu anasonyeza kuti njira imene adzagwiritse ntchito popereka chakudya padziko lapansi ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera.” (Mateyu 24:3, 45-47) Iye amagwiritsira ntchito kapolo ameneyu, yemwe ndi Akhristu odzozedwa, pofotokoza matanthauzo a ulosi.

7. (a) Kodi zizindikiro za m’buku la Chivumbulutso ziyenera kutikhudza bwanji? (b) Kodi ena mwa Akhristu odzozedwa agwira nawo kwa nthawi yaitali bwanji ntchito yokwaniritsa masomphenya a m’buku la Chivumbulutso?

7 Mtumwi Yohane analemba kuti Yesu anapereka uthenga wa m’buku la Chivumbulutso “mwa zizindikiro.” Zizindikiro zimenezi n’zochititsa chidwi komanso n’zosangalatsa kwambiri kuziphunzira. Zizindikirozi zikusonyeza zochitika zikuluzikulu zimene zingatithandize kukhala akhama polengeza ulosi ndiponso matanthauzo a ulosiwo. M’buku la Chivumbulutso muli masomphenya ambiri osangalatsa ndi ochititsa chidwi, ndipo Yohane ankachita nawo zinthu zimene ankaonazo koma nthawi zina ankangoonerera. Akhristu odzozedwa akusangalala kuti mzimu wa Mulungu wawaululira matanthauzo a masomphenyawa kuti iwonso afotokozere anthu ena. Ndipo ena mwa iwo agwira nawo kwa zaka zambiri ntchito yokwaniritsa masomphenya amenewa.

8. (a) Kodi masomphenya alionse a m’buku la Chivumbulutso akusiyana bwanji ndi anzake? (b) Kodi ulosi wa Danieli umatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la zilombo zotchulidwa m’buku la Chivumbulutso?

8 Masomphenya a m’buku la Chivumbulutso amenewa sanalembedwe mwa ndondomeko yotsatira nthawi imene adzakwaniritsidwe. Masomphenya alionse ali ndi nthawi yake imene adzakwaniritsidwe. Masomphenya ambiri akufanana ndi maulosi ena a m’mabuku ena a m’Baibulo amene amatithandiza kumvetsa tanthauzo la masomphenyawo. Mwachitsanzo, ulosi wa Danieli unatchula zilombo zinayi zoopsa, ndipo unafotokoza kuti zilombo zimenezi zikuimira maulamuliro amphamvu kwambiri padziko lonse lapansi. Zimenezi zatithandiza kumvetsa kuti zilombo zotchulidwa m’buku la Chivumbulutso zikuimira magulu andale, ndipo ena mwa iwo alipo mpaka pano.—Danieli 7:1-8, 17; Chivumbulutso 13:2, 11-13; 17:3.

9. (a) Kodi Akhristu odzozedwa asonyeza motani mtima wofanana ndi wa Yohane? (b) Kodi Yohane watisonyeza bwanji njira yotithandiza kukhala osangalala?

9 Yohane anali wokhulupirika polengeza uthenga umene Mulungu anam’patsa kudzera mwa Yesu Khristu. Iye anafotokoza mwatsatanetsatane zinthu “zonse zimene anaona.” Akhristu odzozedwa amapempha Mulungu ndi Yesu Khristu mwakhama kuti awathandize kumvetsa bwino ulosi, n’cholinga choti nawonso auze anthu a Mulungu mfundo zake mwatsatanetsatane. Pofuna kuthandiza mpingo wa Akhristu odzozedwa (ndiponso khamu lalikulu la padziko lonse limene Mulungu adzalipulumutse pa chisautso chachikulu) kupeza njira imene ingawathandize kukhala osangalala, Yohane analemba kuti: ‘Wodala ndi munthu amene amawerenga mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu, komanso amene akusunga zolembedwamo, pakuti nthawi yoikidwiratu ili pafupi.’—Chivumbulutso 1:3.

10. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti buku la Chivumbulutso likuthandizeni kukhala osangalala?

10 Mukamawerenga buku la Chivumbulutso ndi kutsatira zimene mukuwerengazo, mungapindule kwambiri. Yohane anafotokoza m’kalata yake ina kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa. Onse amene ali ana a Mulungu amagonjetsa dziko. Ndipo tagonjetsa dziko ndi chikhulupiriro chathu.” (1 Yohane 5:3, 4) Chikhulupiriro ngati chimenechi chingakuthandizeni kukhala osangalala kwambiri.

11. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera mwamsanga mawu a ulosi? (b) Kodi ndi nthawi iti imene tsopano yayandikira kwambiri?

11 M’pofunika kumvera mwamsanga mawu a ulosi, “pakuti nthawi yoikidwiratu ili pafupi.” Kodi imeneyi ndi nthawi yoikidwiratu ya chiyani? Ndi nthawi yoti maulosi a m’buku la Chivumbulutso akwaniritsidwe komanso nthawi yoti Mulungu apereke chiweruzo. Nthawi yoti Mulungu ndi Yesu Khristu aweruze komaliza dziko la Satanali yayandikira. Yesu ali padziko lapansi ananena kuti Atate ake okha ndi amene akudziwa “za tsikulo kapena ola lake.” Ponena za mavuto amene akuchulukirachulukirabe padzikoli masiku ano, Yesu ananenanso kuti: “M’badwo uwu sudzatha konse, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.” Choncho nthawi imene Mulungu anaikiratu kuti aweruze dzikoli yayandikira kwambiri. (Maliko 13:8, 30-32) Zimenezi zikugwirizana ndi lemba la Habakuku 2:3 lomwe limati: “Masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Iwo sadzachedwa.” Kuti tidzapulumuke pa chisautso chachikulu, tiyenera kumvera ulosi wa m’Mawu a Mulungu.—Mateyu 24:20-22.

[Bokosi patsamba 15]

Kuti timvetse bwino buku la Chivumbulutso tiyenera

● Kuthandizidwa ndi mzimu wa Yehova

● Kuzindikira nthawi imene tsiku la Ambuye linayamba

● Kuzindikira amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru masiku ano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena