Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 25 tsamba 208-216
  • Kodi Mukuchirikiza Dziko la Satana, kapena Dongosolo Latsopano la Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukuchirikiza Dziko la Satana, kapena Dongosolo Latsopano la Mulungu?
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • DZIKO LA SATANA—KODI NCHIYANI?
  • MMENE MUNGAPEWERE KUKHALA MBALI YA DZIKO
  • Opulumuka Sayenera Kukhala “Mbali ya Dziko”
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Khalani Maso Satana Akufuna Kukumezani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mdyerekezi Ndani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 25 tsamba 208-216

Mutu 25

Kodi Mukuchirikiza Dziko la Satana, kapena Dongosolo Latsopano la Mulungu?

1. Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kwenikweni kuti mukuchirikiza dongosolo latsopano la Mulungu?

KODI MUKUCHIRIKIZA dongosolo latsopano lolungama la Mulungu, ndipo kodi mukufuna kuti lidze? Kodi mukutsutsa Satana, ndipo kodi mukufuna dziko lake kuti lithe? Munganene kuti, Inde, ku mafunso awiriwo. Koma kodi zimenezo nzokwanira? Pali mwambi wakale wakuti zochita zimalankhula mofuula koposa mawu. Ngati mukukhulupirira dongosolo latsopano la Mulungu, ndiko mmene mukukhalira moyo wanu kumene kudzakutsimikiziradi.—Mateyu 7:21-23; 15:7, 8.

2. (a) Kodi ambuye awiri amene tingatumikire ndani? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza amene ife tiri kapolo kapena mtumiki wake?

2 Chenicheni ndicho, kakhalidwe kanu kangakhale kokondweretsa kwa mmodzi yekha wa ambuye awiri. Mwina mukutumikira Yehova Mulungu kapena Satana Mdyerekezi. Chilangizo chopezeka m’Baibulo chimatithandiza kuzindikira zimenezi. Chimati: “Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye?” (Aroma 6:16) Kodi mumamvera yani? Kodi mumachita chifuniro chayani? Mosasamala kanthu za yankho lanu, ngati mutsatira njira zosalungama za dziko simungakhale mukutumikira Mulungu wowona, Yehova.

DZIKO LA SATANA—KODI NCHIYANI?

3. (a) Kodi Baibulo limasonyeza yani kukhala wolamulira wa dziko? (b) M’pemphero, kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kusiyana pakati pa dziko ndi ophunzira ake?

3 Yesu anatcha Satana “wolamulira wa dziko lino.” Ndipo mtumwi Yohane ananena kuti “dziko lonse likugona m’mphamvu ya woipayo.” (Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19, NW) Wonani kuti m’pemphero kwa Mulungu Yesu sanaphatikize ophunzira ake kukhala mbali ya dziko la Satana. Iye anati: “Ndikuwapemphera [ophunzira ake]; sindikupempherera dziko . . . Iwo sali mbali ya dziko, monga momwedi ine sindiri mbali ya dziko.” (Yohane 17:9, 16; 15:18, 19, NW) Nkowonekera kuchokera m’zimenezi kuti Akristu owona ayenera kukhala olekana ndi dziko.

4. (a) Pa Yohane 3:16, NW, kodi kanenedweko “dziko” kamatanthauza yani? (b) Kodi ndi“dziko” lotani limene atsatiri a Kristu ayenera kulekana nalo?

4 Koma kodi Yesu anali kutanthauzanji pamene anati “dziko”? M’Baibulo kanenedweko “dziko” nthawi zina kamangotanthauza anthu onse. Mulungu anatumiza Mwana wake kuti apereke moyo wake monga dipo kaamba ka dziko la anthu ili. (Yohane 3:16, NW) Komabe Satana walinganiza ochuluka a anthu motsutsana ndi Mulungu. Motero dziko la Satana ndilo chitaganya cha anthu cholinganizidwa chino chimene chikukhala molekana kapena kunja kwa gulu lowoneka la Mulungu. Ndilo dziko limeneli limene Akristu owona ayenera kulakana nalo.—Yakobe 1:27, NW.

5. Kodi mbali yaikulu ya dziko ndiyiti, ndipo kodi ikuphiphiritsiridwa motani m’Baibulo?

5 Dziko la Satana—chitaganya chake cha anthu olinganizidwa—lapangika ndi mbali zogwirizana kwambiri zosiyanasiyana. Mbali yaikulu ndiyo chipembedzo chonyenga. M’Baibulo chipembedzo chonyenga chikuphiphiritsiridwa kukhala “mkazi wachigololo wamkulu,” kapena wadama, ndi dzinalo “Babulo Wamkulu.” Ichi ndicho ufumu wadziko lonse, monga momwe kwasonyezedwera ndi chenicheni chakuti icho “chiri ndi ufumu pa mafumu a dziko lapansi.” (Chivumbulutso 17:1, 5, 18, NW) Koma kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Babulo Wamkulu ndiye ufumu wadziko wachipembedzo?

6, 7. (a) Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti Babulo Wamkulu ndiufumu wachipembedzo? (b) Kodi ndichigwirizano chotani chimene chipembedzo chonyenga chakhala nacho ndi maboma andale zadziko?

6 Popeza kuti “mafumu a dziko lapansi” akunenedwa kuti ‘akuchita chigololo’ naye, Babulo Wamkulu sangakhale ufumu wadziko wandale zadziko. Ndipo popeza kuti “amalonda oyendayenda” a dziko lapansi akuima patali ndi kulira maliro pa chiwonongeko chake, iye sali ufumu wadziko wamalonda. (Chivumbulutso 17:2; 18:15, NW) Komabe, chakuti iye alidi ufumu wachipembedzo chikusonyezedwa ndi mawu a Baibulo akuti mwa njira ya ‘machitidwe ake auchiwanda mitundu yonse inasochezedwa.’—Chivumbulutso 18:23.

7 Chosonyezanso kuti Babulo Wamkulu ali ufumu wachipembedzo ndicho unansi wake ndi “chirombo.” M’Baibulo zirombo zoterozo zimaphiphiritsira maboma andale zadziko. (Danieli 8:20, 21) Babulo Wamkulu akufotokozedwa kukhala “akukhala pa chirombo chofiira . . . chimene chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.” Iye motero wakhala akuyesayesa kuchita ulamuliro pa “chirombo” chimenechi, kapena boma ladziko. (Chivumbulutso 17:3) Ndipo nkotsimikizirika kuti mkati mwa mbiri yonse chipembedzo chaphatikizidwa ndi ndale zadziko, kawirikawiri chikumauza maboma chochita. Iye wachitadi “ufumu pa mafumu a dziko lapansi.”—Chivumbulutso 17:18, NW.

8. Kodi mbali ina yaikulu ya dziko la Satana ndiyiti, ndipo kodi iwo amaphiphiritsiridwa motani m’Baibulo?

8 Maboma andale zadziko amenewa amapanga mbali ina yaikulu ya dziko la Satana. Monga momwe tawonera kale, iwo akuphiphiritsiridwa m’Baibulo kukhala zirombo. (Danieli 7:1-8, 17, 23) Chakuti maboma onga zirombo amenewa akulandira ulamuliro wawo kuchokera kwa Satana chikusonyezedwa ndi masomphenya olembedwa ndi mtumwi Yohane: “Ndinawona chirombo chikutuluka m’nyanja, chokhala ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri . . . Ndipo chinjoka chinapereka ulamuliro wake kwa chirombo.” (Chivumbulutso 13:1, 2; 12:9) Umboni wowonjezereka wakuti maufumu amenewa, kapena maboma, ali mbali ya dziko la Satana ndiwo chenicheni chakuti Satana anayesa Yesu mwa kulonjeza maufumu amenewa kwa iye. Satana sakadachita zimenezi ngati iye sadali wolamulira wawo.—Mateyu 4:8, 9.

9. (a) Kodi mbali ina ya dziko la Satana ikufotokozedwa motani pa Chivumbulutso 18:11? (b) Kodi imachita ndi kuchirikiza chiyani, ikumatsimikizira kuti Satana ali kumbuyo kwake?

9 Komabe mbali ina yaikulu ya dziko la Satana ndiyo dongosolo laumbombo ndi lotsendereza lamalonda, limene likutchulidwa pa Chivumbulutso 18:11 kukhala “amalonda oyendayenda.” Dongosolo lamalonda limakulitsa chikhumbo chadyera mwa anthu kuti agule zinthu zimene limatulutsa, ngakhale kuli kwakuti iwo sangazifune ndipo angakhaledi bwinopo popanda izo. Pa nthawi imodzimodziyo dongosolo lamalonda laumbombo limakundika chakudya m’nkhokwe koma limalola mamiliyoni ambiri a anthu kufa ndi njala chifukwa chakuti iwo sangalipirire chakudyacho. Ndiponso, zida zankhondo zokhoza kuwononga banja lonse laanthu zimapangidwa ndi kugulitsidwa kaamba ka phindu. Motero dongosolo lamalonda la Satana, limodzi ndi chipembedzo chonyenga ndi maboma andale zadziko, limachirikiza dyera, upandu ndi nkhondo zowopsa.

10, 11. (a) Kodi mbali ina ya dziko la Satana ndiyiti? (b) Kodi pali machenjezo Abaibulo otani oletsa kudzilowetsa m’mbali imeneyi?

10 Chitaganya cha anthu cholinganizidwa chotsogozedwa ndi Satana chiridi choipa ndi chonyansa. Nchotsutsidwa ndi malamulo olungama a Mulungu, ndipo chadzaza mitundu yonse ya machitidwe oipa. Motero mbali ina ya dziko la Satana inganenedwe kukhala kakhalidwe kake kosadziletsa ndi njira zake zoipa. Kaamba ka chifukwa chimenechi mtumwi Paulo ndi Petro yemwe anachenjeza Akristu kuti apewe machitidwe oipa a anthu a mitundu.—Aefeso 2:1-3; 4:17-19; 1 Petro 4:3, 4.

11 Mtumwi Yohane, nayenso, anagogomezera kufunika kwakuti Akristu achechenjere zikhumbo zolakwa ndi njira zoipa zadziko. Iye analemba kuti: “Musakhale okonda dziko kapena zinthu za m’dziko. Ngati aliyense akonda dziko, chikondi cha Atate sichiri mwa iye; chifukwa chakuti chirichonse m’dziko—chikhumbo cha thupi ndi chikhumbo cha maso ndi kuwonetsera kakhalidwe kanu—sichimachokera kwa Atate, koma chimachokera kudziko.” (1 Yohane 2:15, 16, NW) Wophunzira Yakobo ananena kuti ‘ngati aliyense akufuna kukhala bwenzi la dziko, iye akudzipanga mdani wa Mulungu.’—Yakobo 4:4.

MMENE MUNGAPEWERE KUKHALA MBALI YA DZIKO

12, 13. (a) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti Akristu ayenera kukhala m’dziko? (b) Kodi nkotheka motani kukhala m’dziko koma kusakhala mbali yake?

12 Malinga ngati dziko la Satana liripobe, Akristu ayenera kukhalamo. Yesu anasonyeza zimenezi pamene anapemphera kwa Atate wake: “Sindikupemphani kuti muwachotse m’dziko.” Komano Yesu anatinso ponena za atsatiri ake: “Iwo sali mbali ya dziko.” (Yohane 17:15, 16, NW) Kodi kuli kotheka motani kukhala m’dziko la Satana komanso osakhala mbali yake?

13 Eya, mukukhala pakati pa anthu amene akupanga chitaganya chaanthu cholinganizidwa cha lerolino. Anthu amenewa akuphatikizapo adama, mbombo ndi ena amene amachita zinthu zoipa. Mungagwire nawo ntchito, kupita nawo kusukulu, kudya nawo, ndi kuchita nawo limodzi ntchito zina zotero. (1 Akorinto 5:9, 10) Muyeneranso kuwakonda, monga momwe amachitira Mulungu. (Yohane 3:16) Koma Mkristu wowona samakonda zinthu zoipa zimene anthuwo amachita. Iye samatengere malingaliro awo, machitidwe kapena zolinga m’moyo. Iye samakhala ndi mbali m’chipembedzo chawo choipa ndi ndale zadziko. Ndipo pamene kuli kwakuti iye kawirikawiri ayenera kugwira ntchito m’dziko lamalonda kuti apeze chakudya, iye samachita machitidwe amalonda osawona mtima; ndiponso kupeza zinthu zakuthupi sikumakhala cholinga chake chachikulu m’moyo. Popeza kuti iye amachirikiza dongosolo latsopano la Mulungu, iye amapewa utsamwali woipa wa awo okhalira moyo dziko la Satana. (1 Akorinto 15:33; Salmo 1:1; 26:3-6, 9, 10) Chifukwa cha chimenecho, iye ali m’dziko la Satana komanso sali mbali yake.

14. Ngati mukuchirikiza dongosolo latsopano la Mulungu, kodi mudzamvera lamulo Labaibulo lotani?

14 Bwanji ponena za inu? Kodi mukufuna kukhala mbali ya dziko la Satana? Kapena kodi mukuchirikiza dongosolo latsopano la Mulungu? Ngati mukuchirikiza dongosolo latsopano la Mulungu, mudzakhala olekana ndi dziko, kuphatikizapo chipembedzo chake chonyenga. Mudzamvera lamulolo: “Tulukani m’menemo [Babulo Wamkulu], anthu anga.” (Chivumbulutso 18:4) Komabe, kutuluka m’Babulo Wamkulu, ufumu wadziko wa chipembedzo chonyenga, kumaphatikizapo zambiri koposa chabe kudula zigwirizano ndi magulu achipembedzo chonyenga. Kumatanthauzanso kusakhala ndi chirichonse chochita ndi mapwando achipembedzo a dziko.—2 Akorinto 6:14-18.

15. (a) Koposa ndi kubadwa kwa Yesu, kodi Akristu analamulidwa kusunga chiyani? (b) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Yesu sakadabadwa m’kuzizira kwa nyengo yachisanu? (c) Kodi nchifukwa ninji detilo Disembala 25 linasankhidwa kukhala tsiku lokondwerera kubadwa kwa Yesu?

15 Krisimasi nditchuti chachipembedzo chotchuka lerolino. Koma mbiri imasonyeza kuti silinali phwando lochitidwa ndi Akristu oyambirira enieni. Yesu anauza omtsatira kusunga chikumbutso cha imfa yake, osati cha kubadwa kwake. (1 Akorinto 11:24-26) Chenicheni ndicho, Disembala 25 siliri deti la kubadwa kwa Yesu. Silikadatero, popeza kuti Baibulo limasonyeza kuti pa nthawi ya kubadwa kwake abusa anali chikhalirebe kubusa usiku. Iwo sakanakhala ali kumeneko m’nyengo ya chisanu yozizira ndi yamvula. (Luka 2:8-12) Kwenikweni Disembala 25 linasankhidwa kukhala deti lokumbukira kubadwa kwa Yesu chifukwa chakuti, monga momwe The World Book Encyclopedia limafotokozera: “Anthu a m’Roma analisunga ndikale monga Phwando la Saturn, kukondwerera tsiku la kubadwa kwa dzuwa.”

16. (a) Kodi nditchuti china chachipembedzo chotchuka chotani chimene chinali ndi ziyambi zosakhala Zachikristu? (b) Kodi Akristu owona samasunga Krisimasi ndi Isita kaamba ka zifukwa zabwino zotani?

16 Isita nditchuti china chachipembedzo chotchuka. Mlungu Woyera m’maiko ena a Latin-America ngwofanana. Koma Isita sinali kusungidwanso ndi Akristu oyambirira. Iyo, nayonso, inali ndi ziyambi zake m’mapwando osakhala Achikristu. The Encyclopædia Britannica imati: “Mulibe chisonyezero cha kusungidwa kwa phwando la Isita m’Chipangano Chatsopano.” Komabe kodi ziri nkanthu kuti Krisimasi ndi Isita siziri mapwando Achikristu koma kwenikweni anayambitsidwa ndi olambira milungu yonyenga? Mtumwi Paulo anachenjeza kusanganiza zowona ndi zonama, akumanena kuti ngakhale “chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse.” (Agalatiya 5:9) Iye anauza Akristu ena oyambirira kuti kunali kolakwa kwa iwo kusunga masiku amene adasungidwa m’chilamulo cha Mose koma amene Akristu adafafaniziridwira ndi Mulungu. (Agalatiya 4:10, 11) Nkofunika kwambiri chotani nanga mmene kuliri kuti Akristu owona lerolino alekane ndi matchuti amene Mulungu sananene kuti ayenera kusungidwa ndi amene anachokera m’chipembedzo chonyenga!

17. (a) Kodi cholakwika nchiyani ndi matchuti amene amalemekeza anthu otchuka kapena mitundu? (b) Kodi Baibulo limasonyeza motani njira imene Akristu ayenera kutsatira?

17 Matchuti ena adziko amalemekeza anthu ochuka. Enanso amalemekeza ndi kutamanda mitundu kapena magulu adziko. Koma Baibulo limatsutsa kupereka maulemu olambira kwa anthu, kapena kukhulupirira magulu aanthu kuti achite zimene Mulungu yekha angachite. (Machitidwe 10:25, 26; 12:21-23; Chivumbulutso 19:10; Yeremiya 17:5-7) Motero matchuti amene amayedzamira kutamanda munthu kapena gulu laanthu sali ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, ndipo Akristu owona sadzawachita.—Aroma 12:2.

18. (a) Kodi ndizinthu zotani zimene anthu apanga kuti alemekeze kapena kulambira?(b) Kodi lamulo la Mulungu limanenanji ponena za kupereka ulemu wolambira ku chinthu?

18 Zinthu zambiri zapangidwa ndi anthu zimene anthu akuuzidwa kuti azilemekeze kapena kulambira. Zina za zimenezi nzopangidwa ndi chitsulo kapena mtengo. Zina nzopangidwa ndi nsalu ndipo angakhale atasokerapo kapena kujambulapo chithunzithunzi cha kanthu kena ka kumwamba kapena padziko lapansi. Mtundu ungapereke lamulo limene likunena kuti munthu aliyense ayenera kupereka ulemu wolambira ku chinthu choterocho. Koma lamulo la Mulungu limanena kuti atumiki ake sayenera. (Eksodo 20:4, 5; Mateyu 4:10) Kodi anthu a Mulungu achitanji mu mkhalidwe woterowo?

19. (a) Kodi mfumu ya Babulo inalamula aliyense kuchitanji? (b) Kodi Akristu achita bwino kutsatira chitsanzo cha yani?

19 M’Babulo wakale Mfumu Nebukadinezala anawaka fano lalikulu lagolidi nalamulira kuti aliyense aligwadire. ‘Yense amene sakutero,’ iye anatero, ‘adzaponyedwa m’ng’anjo yotentha yamoto.’ Baibulo likutiuza kuti Ahebri atatu achichepere, Sadrake, Mesake ndi Abedinego, anakana kuchita zimene mfumu idalamula. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kunalowetsamo kulambira, ndipo kulambira kwawo kunali kokha kwa Yehova. Mulungu anavomereza zimene iwo anachita, ndipo anawapulumutsa ku mkwiyo wa mfumu. Kunena zowona, Nebukadinezala anafika pa kuwona kuti atumiki a Yehova amenewa sanali chiwopsezo ku Boma, chifukwa cha chimenecho iye anapereka lamulo lotetezera ufulu wawo. (Danieli 3:1-30) Kodi simukuchita kaso ndi kukhulupirika kwa anyamata amenewa? Kodi mudzasonyeza kuti inu mukuchirikizadi dongosolo latsopano la Mulungu mwa kumvera onse a malamulo a Mulungu.—Machitidwe 5:29.

20. Kodi ndinjira zosiyanasiyana zotani zimene Satana amagwiritsira ntchito kuyesa kutchititsa kuswa malamulo a Mulungu onena za kugonana koyenera?

20 Ndithudi, Satana samafuna kuti ife titumikire Yehova. Iye amafuna kuti ife timtumikire. Motero iye amayesayesa kutichititsa kuchita zimene akufuna, popeza kuti iye amadziwa kuti timakhala akapolo, kapena atumiki, a iye amene tikumvera. (Aroma 6:16) Mwa njira zosiyanasiyana, kuphatikizapo televizheni, akanema, mipangidwe ina ya kuvina ndi mabukhu oipa, Satana amasonkhezera kugonana pakati pa anthu osakwatirana, kuphatikizapo chigololo. Khalidwe loterolo limapangitsidwa kuwonekera kukhala lovomerekezeka, ngakhale loyenera. Komabe, limeneli nlotsutsidwa ndi malamulo a Mulungu. (Ahebri 13:4; Aefeso 5:3-5) Ndipo munthu amene amachita khalidwe loterolo akusonyezadi kuti iye akuchirikiza dziko la Satana.

21. Kodi ndimachitidwe ena otani amene, ngati munthu awachita, adzasonyeza kuti iye akuchirikiza dziko la Satana?

21 Pali machitidwe ena amene dziko la Satana lawapangitsa kutchuka koma amene ali otsutsidwa ndi malamulo a Mulungu. Kuledzera ndi zakumwa zoledzeretsa ndiko amodzi a iwo. (1 Akorinto 6:9, 10) Ena ndiwo kugwiritsiridwa ntchito kwa mankhwala onga ngati chamba ndi namgoneka kaamba ka chikondwerero, kuphatikizapo kugwiritsiridwa ntchito kwa fodya. Zinthu zimenezi nzovulaza thupi ndipo nzautchisi. Kugwiritsiridwa ntchito kwawo mwachiwonekere nkosemphana ndi chilangizo cha Mulungu cha ‘kudziyeretsa ku chodetsa chirichonse cha thupi ndi mzimu.’ (2 Akorinto 7:1) Kusuta fodya kumavulazanso thanzi la awo oyandikira amene ayenera kupuma utsiwo, motero wosutayo akuswa lamulo la Mulungu limene limanena kuti Mkristu ayenera kukonda mnansi wake.—Mateyu 22:39.

22. (a) Kodi Baibulo limanenanji ponena za mwazi? (b) Kodi nchifukwa ninji kulandira kuthiriridwa mwazi sikuli kwenikweni kosiyana ndi “kudya” mwazi? (c) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti ‘kusala mwazi’ kumatanthauza kusaulowetsa konse m’thupi lanu?

22 Kachitidwe kena kofala m’mbali zosiyanasiyana za dziko ndiko kudya mwazi. Motero nyama zosakhetsedwa mwazi moyenera zimadyedwa kapena mwazi ungakhetsedwe ndi kugwiritsiridwa ntchito monga chakudya m’zakudya. Komabe Mawu a Mulungu amaletsa kudya mwazi. (Genesis 9:3, 4; Levitiko 17:10) Pamenepa, bwanji ponena za kulandira kuthiriridwa mwazi? Anthu ena angalingalire kuti kulandira mwazi wothiriridwa sikuli kwenikweni “kudya.” Koma kodi sizowona kuti pamene wodwala ali wosakhoza kudya chakudya ndi pakamwa pake, dokotala kawirikawiri amalangiza kumdyetsa mwa njira imodzimodziyo mu imene mwazi wothiriridwa umaperekedwera? Baibulo limatiuza ‘kusala . . . mwazi.’ (Machitidwe 15:20, 29) Kodi kumeneku kukutanthauzanji? Ngati dokotala akanakuuzani kusala kachasu, kodi zimenezo zikangotanthauza kuti simuyenera kummwera pakamwa panu koma kuti mukatha kumthirira mwachindunji m’mitsempha mwanu? Ndithudi ayi! Chomwechonso, ‘kusala mwazi,’ kumatanthauza kusaulowetsa konse m’thupi lanu.

23. (a) Kodi mukufunikira kupanga chosankha chotani? (b) Kodi nchiyani chimene chidzasonyeza chosankha chimene mwapanga?

23 Mufunikra kusonyeza Yehova Mulungu kuti mukuchirikiza dongosolo lake latsopano ndipo simuli mbali ya dziko lino. Kumeneku kumafuna chosankha. Chosankha chimene mukufunikira kupanga ndicho kutumikira Yehova, kuchita chifuniro chake. Simungakhale wamitima iwiri, monga momwe analiri Aisrayeli ena m’nthawi zakale. (1 Mafumu 18:21) Pakuti kumbukirani, ngati simukutumikira Yehova, pamenepo mukutumikira Satana. Inu munganene kuti mukuchirikiza dongosolo latsopano la Mulungu, koma kodi khalidwe lanu likunenanji? Kukhala wochirikiza dongosolo latsopano la Mulungu kumaphatikizapo kupewa machitidwe onse amene Mulungu amatsutsa ndi amene sadzakhala m’dongosolo lake latsopano lolungama.

[Chithunzi patsamba 209]

Kodi nchiyani chimene chiri dziko limene Yesu sakanapempherera ndi limene ophunzira ake sali mbali yake?

[Zithunzi patsamba 211]

M’Baibulo, chipembedzo chonyenga chimaphiphiritsiridwa kukhala mkazi wachigololo woledzera, ndipo boma ladziko limene iye akukwera kukhala chirombo

Kakhalidwe kosadziletsa ndiko mbali ya dziko la Satana. Dongosolo lamalonda laumbombo lirinso mbali yaikulu

[Chithunzi patsamba 213]

Popeza kuti pa kubadwa kwa Yesu abusa anali chikhalirebe kubusa ndi magulu awo ankhosa usiku, iye sakanakhala atabadwa pa Disembala 25

[Chithunzi patsamba 214]

Atumiki a Mulungu anakana kulambira fano loimikidwa ndi mfumu. Kodi mudzachitanji mu mkhalidwe wofananawo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena