Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 10/15 tsamba 8-9
  • Kuperekedwa ndi Kugwidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuperekedwa ndi Kugwidwa
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Kuperekedwa ndi Kugwidwa
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Khristu Anaperekedwa Kenako Anamangidwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu m’Munda
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yesu Anamangidwa
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 10/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kuperekedwa ndi Kugwidwa

PAKATI pausiku papita kale pamene Yudase akutsogoza khamu lalikulu la asilikali, akulu ansembe, Afarisi, ndi ena kunka m’munda wa Getsemane. Ansembewo avomereza kumlipira Yudase ndalama zasiliva 30 kuti ampereke Yesu.

Koyambirirako, pamene Yudase anachotsedwa pa chakudya cha Paskha, mwachiwonekere iye analunjika kunka kwa akulu ansembewo. Mosataya nthaŵi, awa anasonkhanitsa nduna zawo, limodzinso ndi gulu la asilikali. Mwinamwake Yudase poyamba anawatsogoza kumene Yesu ndi atumwi ake anachitira phwando la Paskha. Pamene apeza kuti iwo achokako kale, khamu lalikululo lokhala ndi zida ndi lonyamula nyali ndi miuni linatsatira Yudase kunja kwa Yerusalemu nadutsa Chigwa cha Kedroni.

Pamene Yudase akutsogolera gululo kukwera Phiri la Azitona, iye akukhala wotsimikiza kudziŵa kumene angampeze Yesu. M’mlungu wapita, pamene Yesu ndi atumwi ake ankadutsadutsa pakati pa Betaniya ndi Yerusalemu, iwo kaŵirikaŵiri ankaima m’munda wa Getsemane kuti apume ndikukambirana. Koma tsopano, pokhala kuti mwinamwake Yesu wabisika ndi mdima pansi pa mitengo ya azitona, kodi asilikaliwo adzamzindikira motani iye? Iwo mwinamwake sanamuwonepo konse. Yudase akupereka chizindikiro, akumati: ‘Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire.’

Yudase akutsogolera khamu lalikululo kunka m’mundamo, awona Yesu ali ndi atumwi ake, napita molunjika kwa iye. “Tikuoneni, Rabi,” iye atero nampsompsonetsa.

“Mnzanga, wafikiranji iwe?” Yesu akufunsa mokalipa. Kenaka, akumayankha funso lake lomwe, iye akuti: ‘Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi chimpsompsono kodi?’ Koma zakwanira kwa wompereka wakeyo! Yesu anka kutsogolo kwa muini ndi nyali zoyakazo nafunsa kuti: “Mufuna yani?”

“Yesu Mnazarayo,” ndilo yankho.

“Ndine,” Yesu akuyankha motero, pamene akuima molimba mtima pamaso pawo. Atazizwitsidwa ndi kulimbika mtima kwake nasowa choyembekezera, amunawo akubwerera m’mbuyo nagwa pansi.

“Ndati, Ndine,” Yesu akupitiriza mwabata. ‘Chifukwa chake ngati mufuna ine, lekani awa amuke.’ Nthaŵi yochepa yapitayo m’chipinda chosanja, Yesu anauza Atate ake m’pemphero kuti anasunga atumwi ake okhulupirika ndipo sanataike ngakhale mmodzi ‘koma mwana wa chitayiko.’ Chotero, kuti mawu ake akwaniritsidwe, iye akupempha kuti atsatiri ake aloledwe kumuka.

Pamene asilikaliwo akupezanso nyonga zawo, naimirira, nayamba kum’manga Yesu, atumwiwo akuzindikira chimene chiri pafupi kuchitika. “Ambuye, tidzakantha ndi lupanga kodi?” iwo akufunsa. Yesu asanayankhe, Petro, asolola limodzi la malupanga aŵiri amene atumwiwo abweretsa, nawukira Malko, kapolo wa mkulu wa ansembe. Nkhonya ya Petro iphonya mutu wa kapoloyo koma adula khutu lake lakumanja.

“Lolani kufikira kumene,” Yesu akutero pamene akuloŵereramo. Akumalikhudza khutulo, iye apoletsa chirondacho. Pamenepo aphunzitsa phunziro lofunika koposa, akumalamula Petro nati: ‘Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga. Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri?’

Yesu ngwofunitsitsa kuti agwidwe. Popeza iye akufotokoza kuti: ‘Malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?’ Ndipo akuwonjezera motere: ‘Chikho chimene Atate wandipatsa ine sindichimwere ichi kodi?’ Iye wavomerezana kotheratu ndi chifuniro cha Mulungu kwa iye!

Kenaka Yesu akulankhula ndi khamulo. ‘Kodi munatulukira kundigwira ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba?’ iye akuwafunsa tero. ‘Tsiku ndi tsiku ndimakhala m’kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira. Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe.’

Pamenepo gulu la asilikaliwo ndi mtsogoleri wa ankhondo ndi nduna za Ayuda amgwira Yesu nam’manga. Powona zimenezi, atumwiwo akumsiya Yesu nathaŵa. Komabe, mwamuna wachichepere​—mothekera kwenikweni ndiwophunzira Marko​—akutsalira pakati pa khamulo. Iye angakhale adali kunyumba kumene Yesu anachitira phwando la Paskha ndipo pambuyo pake anatsatira khamulo kuchokera kumeneko. Komabe, iye tsopano wazindikiridwa, ndipo akuyesera kumgwira. Koma akusiya malaya ake nathaŵa wosavala bwino. Mateyu 26:47-56; Marko 14:43-52; Luka 22:47-53; Yohane 17:12; 18:3-12.

◆ Kodi nchifukwa ninji Yudase anali wotsimikiza kuti akampeza Yesu m’munda wa Getsemane?

◆ Kodi Yesu anakusonyeza motani kudera nkhaŵa kaamba ka atumwi ake?

◆ Kodi Petro akuchitanji pochinjiriza Yesu, koma kodi Yesu akumuuzanji ponena za icho?

◆ Kodi Yesu akuvumbula motani kuti ngwovomerezana kotheratu ndi chifuniro cha Mulungu kwa iye?

◆ Pamene atumwiwo amsiya Yesu, ndani yemwe watsala, ndipo kodi nchiyani chikuchitika kwa iye?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena