Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Phunziro 31. Yesu Khristu ali pamaso pa Yehova ndipo akulamulira monga Mfumu kumwamba.

      PHUNZIRO 31

      Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

      Uthenga wofunika kwambiri m’Baibulo ndi wokhudza Ufumu wa Mulungu. Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu umenewu pokwaniritsa cholinga chimene anali nacho chokhudza dziko lapansili. Ndiye kodi Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? Timadziwa bwanji kuti Ufumuwu ukulamulira panopa? Ndi zinthu ziti zimene Ufumuwu wachita kale? Nanga udzachita zotani kutsogoloku? Mafunsowa ayankhidwa m’phunziroli komanso maphunziro awiri otsatira.

      1. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, nanga Mfumu yake ndi ndani?

      Ufumu wa Mulungu ndi boma limene linakhazikitsidwa ndi Yehova Mulungu. Mfumu yake ndi Yesu Khristu ndipo akulamulira kuchokera kumwamba. (Mateyu 4:17; Yohane 18:36) Ponena za Yesu, Baibulo limati: “Iye adzalamulira monga Mfumu . . . kwamuyaya.” (Luka 1:32, 33) Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzalamulira anthu onse padzikoli.

      2. Kodi ndi ndani akulamulira ndi Yesu?

      Yesu sakulamulira yekha. Anthu ochokera “mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse . . . adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Ndi anthu angati amene adzalamulire ndi Khristu? Kungoyambira pamene Yesu anabwera padziko lapansi, anthu ambiri akhala otsatira ake ndipo panopa alipo mamiliyoni ambiri. Koma ndi anthu okwana 144,000 okha amene adzapite kumwamba kukalamulira ndi Yesu. (Werengani Chivumbulutso 14:1-4.) Koma Akhristu ena onse adzakhala padziko lapansi ndipo azidzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu.​—Salimo 37:29.

      3. Kodi Ufumu wa Mulungu umaposa bwanji maboma a anthu?

      Ngakhale olamulira a dzikoli atayesetsa bwanji kuchita zinthu zabwino, iwo sangakwanitse kuchita zonse zimene akufuna. Pakapita nthawi amalowedwa m’malo ndi olamulira ena odzikonda kwambiri omwe safuna kuthandiza anthu. Mosiyana ndi olamulira amenewa, Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu sadzalowedwa m’malo ndi wina aliyense. Mulungu wakhazikitsa “ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.” (Danieli 2:44) Yesu adzalamulira dziko lonse lapansi ndipo sazidzakondera mtundu winawake wa anthu. Yesu ndi wachikondi, wachifundo komanso wachilungamo ndipo adzaphunzitsa anthu kuti azidzasonyezana makhalidwe amenewa.​—Werengani Yesaya 11:9.

      FUFUZANI MOZAMA

      Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake Ufumu wa Mulungu uli wabwino kwambiri kuposa maboma a anthu.

      Yesu Khristu ali pampando wachifumu kumwamba ndipo akulamulira dzikoli. Kumbuyo kwake kuli anthu omwe akulamulira naye. Ulemerero wa Yehova ukuonekera kumbuyo kwawo.

      4. Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi

      Yesu Khristu ali ndi mphamvu zolamulira dzikoli kuposa anthu onse amene akulamulira dzikoli. Werengani Mateyu 28:18, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi ulamuliro wa Yesu umaposa bwanji ulamuliro wa anthu?

      Maboma a anthu amasinthasintha ndipo dziko lililonse limakhala ndi wolamulira wake. Nanga bwanji Ufumu wa Mulungu? Werengani Danieli 7:14, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Popeza Ufumu wa Mulungu “sudzawonongedwa,” kodi zimenezi zili ndi ubwino wotani?

      • Kodi mukuganiza kuti tidzapindula bwanji Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dziko lonse?

      5. Maboma a anthu ayenera kuchotsedwa

      N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu uyenera kulowa m’malo mwa maboma a anthu? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali:

      VIDIYO: Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?​—Kachigawo Kake (1:41)

      • Kodi zotsatira za ulamuliro wa anthu ndi zotani?

      Werengani Mlaliki 8:9, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi mukuona kuti n’zoyenera kuti Ufumu wa Mulungu udzalowe m’malo mwa maboma a anthu? N’chifukwa chiyani mukutero?

      6. Ufumu wa Mulungu uli ndi olamulira amene amatimvetsa

      Popeza Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu anakhalapo munthu, iye ‘amatimvera chisoni pa zofooka zathu.’ (Aheberi 4:15) Yehova anasankha amuna ndi akazi okwana 144,000 omwe adzalamulire ndi Yesu kuchokera “mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse.”​—Chivumbulutso 5:9.

      • Popeza kuti Yesu komanso onse amene adzalamulire naye anakhalapo anthu, kodi mukuona kuti zimenezi n’zolimbikitsa? N’chifukwa chiyani mukutero?

      Amuna ndi akazi omwe ndi odzodzedwa ochokera m’mitundu yosiyanasiyana komanso a misinkhu yosiyanasiyana.

      Yehova wakhala akusankha amuna ndi akazi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana kuti adzalamulire ndi Yesu

      7. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri

      Maboma a anthu amapanga malamulo omwe amayenera kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Nawonso Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo amene nzika zake zimayenera kuwatsatira. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji padzikoli aliyense akamadzatsatira malamulo a Mulungu?a

      • Yehova amayembekezera kuti nzika za Ufumu wake zizitsatira malamulo ake, kodi mukuganiza kuti zimene Yehova amafunazi n’zoyenera? N’chifukwa chiyani mukutero?

      • Ndi mfundo iti imene ikusonyeza kuti anthu amene satsatira malamulo amenewa atha kusintha?​—Onani vesi 11.

      Wathirafiki akuimitsa magalimoto pamphambano ya msewu wodutsa anthu ambiri. Anthu amisinkhu yosiyanasiyana akuwoloka msewu.

      Maboma amakhazikitsa malamulo n’cholinga chofuna kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri omwe amathandiza ndi kuteteza nzika zake

      MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?”

      • Kodi mungamuyankhe bwanji?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Ufumu wa Mulungu ndi boma lomwe lili kumwamba ndipo udzalamulira dziko lonse lapansi.

      Kubwereza

      • Kodi ndi ndani amene adzalamulire mu Ufumu wa Mulungu?

      • Kodi Ufumu wa Mulungu umaposa bwanji maboma a anthu?

      • Kodi Yehova amayembekezera kuti nzika za Ufumu wake zizichita chiyani?

      Zolinga

      ONANI ZINANSO

      Onani zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza komwe Ufumu wa Mulungu uli.

      “Kodi Ufumu wa Mulungu Uli Mumtima Mwanu?” (Nkhani yapawebusaiti)

      N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amaona kuti kukhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala okhulupirika ku maulamuliro a anthu?

      Anthu Odzipereka ku Ufumu wa Mulungu 1:​43

      Onani zomwe Baibulo limafotokoza zokhudza anthu 144,000 omwe Yehova amawasankha kuti adzalamulire ndi Yesu.

      “Kodi Ndi Ndani Amene Amapita Kumwamba?” (Nkhani yapawebusaiti)

      N’chiyani chinathandiza mayi wina yemwe anali m’ndende kukhulupirira kuti Mulungu yekha ndi amene angabweretse chilungamo padzikoli?

      “Kumene Ndinadziwira Yemwe Adzathetse Kupanda Chilungamo” (Galamukani!, November 2011)

      a Ena mwa malamulo amenewa tidzawakambirana m’Gawo 3.

  • Kodi Kusakhala Mbali ya Dziko Kumatanthauza Chiyani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Phunziro 45. Mlongo wachitsikana waimirira pamene anthu akuimba nyimbo ya fuko koma iye sakuimba nawo kapena kuika dzanja kale pamtima ngati anzake ena.

      PHUNZIRO 45

      Kodi Kusakhala Mbali ya Dziko Kumatanthauza Chiyani?

      Yesu anaphunzitsa kuti otsatira ake sayenera ‘kukhala mbali ya dziko.’ (Yohane 15:19) Zimenezi zikutanthauza kusalowerera ndale kapena nkhondo zimene zimachitika m’dzikoli. Koma kuchita zimenezi si kophweka ndipo anthu angamatinyoze kapena kutiseka chifukwa chosachita nawo zinthu zam’dziko. Kodi tingatani kuti tisakhale mbali ya dziko ndi cholinga choti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova Mulungu?

      1. Kodi Akhristu oona amasonyeza bwanji kuti amalemekeza maboma a anthu?

      Akhristu amalemekeza maboma a anthu pomvera zimene Yesu ananena kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara.” Choncho, timamvera malamulo am’dziko lomwe tikukhala omwe amaphatikizapo kupereka misonkho. (Maliko 12:17) Baibulo limanena kuti maboma a anthu alipo chifukwa chakuti Yehova wawalola kuti alamulire. (Aroma 13:1) Choncho timazindikira kuti maboma a anthu ali ndi malire, kapena kuti mphamvu zochepa, powayerekezera ndi Mulungu. Timadziwa kuti Mulungu wathu yekha ndi amene adzathetse mavuto onse a anthu pogwiritsa ntchito Ufumu wake.

      2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitili mbali ya dziko?

      Mofanana ndi Yesu, nafenso sitichita nawo zandale. Pa nthawi ina anthu ataona zozizwitsa zimene Yesu anachita ankafuna kumuveka ufumu koma iye anakana. (Yohane 6:15) N’chifukwa chiyani Yesu anakana? Iye ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Popeza kuti ndife ophunzira a Yesu, nafenso timakana kukhala mbali ya dziko ndipo timachita zimenezi m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, sitimenya nawo nkhondo. (Werengani Mika 4:3.) Ngakhale kuti zizindikiro ngati mbendera timaziona kuti ndi zofunika, koma sitimazichitira sawatcha kapena kuzilambira chifukwa kuchita zimenezi kuli ngati kulambira mafano. (1 Yohane 5:21) Komanso sitiikira kumbuyo kapena kutsutsa chipani china chilichonse cha ndale ngakhalenso mtsogoleri wake. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti ndife okhulupirika ndi mtima wonse ku boma la Mulungu kapena kuti Ufumu wake.

      FUFUZANI MOZAMA

      Onani zinthu zimene zingachititse kuti zikhale zovuta kusakhala mbali ya dziko, kenako ganizirani mmene mungasankhire zinthu zomwe zingasangalatse Yehova.

      Munthu akusonyeza kuti sali mbali ya dziko. Sakusonyeza kuti ali mbali ya mtsogoleri wandale aliyense amene akuchititsa msonkhano wokopa anthu.

      3. Akhristu oona sakhala mbali ya dziko

      Yesu ndi otsatira ake anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Werengani Aroma 13:1, 5-7 ndi 1 Petulo 2:13, 14. Kenako onerani VIDIYO, ndi kukambirana mafunso awa:

      VIDIYO: Akhristu Oona Sakhala Mbali ya Dziko​—Gawo 1 (4:28)

      • N’chifukwa chiyani timafunika kulemekeza maboma a anthu?

      • Ndi zinthu ziti zomwe tingachite posonyeza kuti timawamvera?

      Pa nthawi ya nkhondo, mayiko ena amanena kuti sali mbali ya gulu lina lililonse la nkhondo, koma amapezeka kuti akuthandiza magulu awiri omwe akumenyanawo. Ndiye kodi kusakhala mbali ya dziko kumatanthauza chiyani? Werengani Yohane 17:16. Kenako, muonere VIDIYO ndi kukambirana funso ili:

      VIDIYO: Akhristu Oona Sakhala Mbali ya Dziko​—Gawo 2 (3:​11)

      • Kodi kusakhala mbali ya dziko kumatanthauza chiyani?

      Mungatani ngati akuluakulu a boma akufuna kuti muchite zinthu zotsutsana ndi malamulo a Mulungu? Werengani Machitidwe 5:28, 29. Kenako, muonere VIDIYO ndi kukambirana mafunso awa:

      VIDIYO: Akhristu Oona Sakhala Mbali ya Dziko​—Gawo 3 (1:18)

      • Ngati zimene malamulo a anthu amanena n’zotsutsana ndi zimene lamulo la Mulungu likunena, kodi tiyenera kumvera lamulo la ndani?

      • Kodi mukuganiza kuti Mkhristu sakuyenera kumvera olamulira a dziko pa zinthu ngati ziti?

      4. Muzipewa kuganiza ndi kuchita zinthu zosonyeza kuti muli mbali ya dziko

      Werengani 1 Yohane 5:21. Kenako, muonere VIDIYO ndi kukambirana mafunso awa:

      VIDIYO: N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Amafunika Kulimba Mtima Kuti Asalowerere Ndale? (2:49)

      • Muvidiyoyi, n’chifukwa chiyani Ayenge anakana kulowa chipani cha ndale kapena kuchita miyambo yosonyeza kukonda dziko lawo monga kuchitira sawatcha mbendera?

      • Kodi mukuganiza kuti iye anasankha zinthu mwanzeru?

      Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zingachititse kuti zikhale zovuta kusakhala mbali ya dziko? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      VIDIYO: Zimene Ndinaphunzira mu Nsanja ya Olonda​—Kusakhala Mbali ya Dzikoli (5:16)

      • Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitili mbali ya dziko pa nthawi imene pakuchitika mipikisano ya masewera a mayiko osiyanasiyana?

      • Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitili mbali ya dziko ngati andale asankha zinthu zabwino kapena zoipa zomwe zingathe kukhudza moyo wathu?

      • Kodi zimene timawerenga ndi kumvetsera kapenanso zimene timamva kwa anthu amene timacheza nawo zingatikhudze bwanji pa nkhani ya kusakhala mbali ya dziko?

      Zithunzi: 1. Gulu la anthu okwiya likuchita zionetsero ndipo ena anyamula zikwangwani. 2. Munthu ali kumpira ndipo akuchemerera timu yake atakweza mbendera m’mwamba. 3. Mwana wasukulu akuimba nyimbo ya fuko. 4. Msilikali wanyamula mfuti. 5. Atsogoleri awiri andale akuchita mtsutso. 6. Mzimayi akuvota.

      Kodi Mkhristu ayenera kupewa kuganizira ndiponso kuchita zinthu ziti zosonyeza kuti ali mbali ya dziko?

      MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “N’chifukwa chiyani simuchitira sawatcha mbendera kapena kuimba nyimbo ya fuko?”

      • Kodi mungamuyankhe bwanji?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Akhristu amayesetsa kupewa kuganiza, kulankhula ndi kuchita zinthu zomwe zingawachititse kukhala mbali ya dziko.

      Kubwereza

      • N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza maboma a anthu?

      • N’chifukwa chiyani sitichita nawo zandale?

      • Ndi zinthu ziti zomwe zingachititse kuti tikhale mbali ya dziko?

      Zolinga

      ONANI ZINANSO

      Kodi tingalolere kusiya zinthu ziti n’cholinga choti tisakhale mbali ya dziko?

      Yehova Sanatisiye (3:14)

      Kodi mabanja angakonzekere bwanji kupewa mayesero omwe angawachititse kuti akhale mbali ya dziko?

      Tisamachite Zinthu Zosonyeza Kuti Tili Mbali ya Dziko Tikakhala Pagulu (4:25)

      N’chifukwa chiyani kuteteza dziko lanu si kofunika kwambiri poyerekezera ndi kudzipereka kwa Mulungu?

      “Zinthu Zonse N’zotheka ndi Mulungu” (5:19)

      Onani zimene zingakuthandizeni kuti ‘musakhale mbali ya dziko’ mukamasankha ntchito yomwe mukufuna kugwira.

      “Yense Adzasenza Katundu Wake wa Iye Mwini” (Nsanja ya Olonda, March 15, 2006)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena