Aneneri Onyenga Lerolino
YEREMIYA anatumikira monga mneneri wa Mulungu m’Yerusalemu panthaŵi imene mzindawo unali wodzala ndi kulambira mafano, chisembwere, chiphuphu, ndi kukhetsa mwazi wopanda liŵongo. (Yeremiya 7:8-11) Iye sanali mneneri yekha wokangalika panthaŵiyo, koma ena ochuluka anali kudzitumikira okha ndipo anali oipa. Mwanjira yotani? Yehova akulengeza kuti: ‘Kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga. Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang’onopang’ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.’—Yeremiya 6:13, 14.
Aneneri onyengawo anayesa kupanga zinthu kuwonekera ngati kuti zinali bwino mosasamala kanthu za kuipa konse m’dzikolo, ndikuti anthuwo anali pamtendere ndi Mulungu; koma sizinali tero. Chiweruzo cha Mulungu chinali kuwayembekezera, monga momwe Yeremiya analengezera mopanda mantha. Mneneri wowonayo Yeremiya, osati aneneri onyenga, anatsimikiziridwa kukhala wowona pamene Yerusalemu anapasulidwa ndi asirikali a Babulo mu 607 B.C.E., kachisi anawonongedwa, ndipo anthuwo anaphedwa kapena kutengeredwa muukapolo ku Babulo wakutali. Anthu oŵerengeka omvetsa chifundo omwe anatsala m’dzikomo anathaŵira ku Igupto.—Yeremiya 39:6-9; 43:4-7.
Kodi aneneri onyengawo adachitanji? ‘Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene amaba mawu anga, yense kumbera mnansi wake.’ (Yeremiya 23:30) Aneneri onyengawo anaba mphamvu ndi zotulukapo zakumvetsera mawu a Mulungu mwakulimbikitsa anthuwo kumvetsera mabodza mmalo mwa chenjezo lowona lochokera kwa Mulungu. Iwo anali kunena, osati ‘zazikulu za Mulungu,’ koma malingaliro awoawo, zinthu zimene anthuwo anafuna kuzimva. Uthenga wa Yeremiya unalidi wochokera kwa Mulungu, ndipo ngati Aisrayeli akanachitapo kanthu pa mawu ake, akadapulumuka. Aneneri onyengawo ‘anaba mawu a Mulungu’ natsogolera anthuwo kutsoka. Zinalidi monga momwe Yesu ananenera ponena za atsogoleri achipembedzo osakhulupirika a m’tsiku lake kuti: ‘Ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse aŵiri adzagwa m’mbuna.’—Machitidwe 2:11; Mateyu 15:14.
Mofanana ndi m’tsiku la Yeremiya, lerolino palinso aneneri onyenga amene akudzinenera kuti amaimira Mulungu wa Baibulo; koma nawonso akuba mawu a Mulungu mwakulalikira zinthu zimene zikucheutsa anthu ku zimene Mulungu akunenadi kupyolera m’Baibulo. Mwanjira yotani? Tiyeni tiyankhe funsoli mwakugwiritsira ntchito chiphunzitso chachikulu cha Baibulo cha Ufumu monga fanizo.
Chowonadi Chonena za Ufumu
Ufumu wa Mulungu unali mutu waukulu wa kuphunzitsa kwa Kristu, ndipo umatchulidwa nthaŵi zoposa zana limodzi m’Mauthenga Abwino. Kumayambiriro kwa uminisitala wake, Yesu anati: “Ndiyenera kulalikira mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu, chifukwa ndinatumizidwa kudzachita ichi.” Anawaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze.”—Luka 4:43, NW; 11:2.
Pamenepo, kodi Ufumuwo nchiyani? Malinga ndi kunena kwa The New Thayer’s Greek English Lexicon, liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “ufumu” m’Baibulo poyamba limatanthauza “mphamvu zachifumu, ufumu, ukumu, ulamuliro” ndipo kachiŵiri, “gawo lokhala pansi pa ulamuliro wa mfumu.” Kuchokera ku matanthauzowa tingatsimikizire moyenerera kuti Ufumu wa Mulungu uli boma lenileni lolamuliridwa ndi Mfumu. Kodi ziridi choncho?
Inde, ziri choncho, ndipo Mfumuyo ndiye Yesu Kristu mwiniyo. Yesu asanabadwe mngelo Gabriyeli anamuuza Mariya kuti: ‘Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo [Yehova, NW] Mulungu adzampatsa iye mpando wachifumu wa Davide atate ŵake.’ (Luka 1:32) Kulandira mpando wachifumu kwa Yesu kumatsimikizira kuti alidi Mfumu, Wolamulira boma. Ndiponso ulosi uwu wa Yesaya ukutsimikizira kuti Ufumuwo uli boma lenileni: “Pakuti kwa ife mwana wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa: ndipo boma lidzakhala pa pheŵa lake . . . Sipadzakhala mapeto a kuwonjezeka kwa boma lake ndi mtendere.”—Yesaya 9:6, 7, King James Version.
Kodi Yesu akulamulira kuti? Ku Yerusalemu? Ayi. Mneneri Danieli anawona m’masomphenya Yesu akulandira Ufumu, ndipo masomphenya ake akusonyeza Yesu ali kumwamba. (Danieli 7:13, 14) Zimenezi zimagwirizana ndi njira imene Yesu analankhulira za Ufumuwo. Kaŵirikaŵiri Anautcha ‘ufumu wakumwamba.’ (Mateyu 10:7; 11:11, 12) Zimagwirizananso ndi mawu a Yesu aŵa kwa Pilato pamene Yesu anali kuzengedwa mlandu pamaso pake: ‘Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.’ (Yohane 18:36) Kodi minisitala wanu kapena wansembe wakuphunzitsani kuti Ufumu wa Yesu uli boma lenileni, lolamulira kuchokera kumwamba? Kapena kodi wakuphunzitsani kuti Ufumuwo uli kokha chinachake chimene chimakhala mumtima? Ngati ndichoncho, iye wakuberani mawu a Mulungu.
Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa boma la Ufumu ndi mitundu yonse yosiyanasiyana ya maboma aumunthu? Malinga ndi kunena kwa The Encyclopedia of Religion, yokonzedwa ndi Mircea Eliade, pamene Wokonzanso Martin Luther anali kufotokoza za Ufumu, anapereka lingaliro lakuti: “Boma ladziko . . . lingatchedwenso ufumu wa Mulungu.” Ena amaphunzitsa kuti mwa zoyesayesa zawo, anthu akhoza kupanga maboma aumunthu kukhala ngati Ufumu wa Mulungu. Mu 1983 Bungwe la Matchalitchi Lapadziko Lonse linatsimikizira kuti: “Pamene tikuwona chikhumbo chathu chenicheni cha mtendere ndi kuchitapo kanthu kwachindunji, Mzimu wa Mulungu ungagwiritsire ntchito zoyesayesa zathu zofooka kupangitsa maufumu adzikoli kukhala ngati ufumu wa Mulungu.”
Komabe, tawonani kuti m’Pemphero la Ambuye (“Atate Wathu”), Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze ndipo pambuyo pake mpamene anawauza kupemphera kuti: ‘Kufuna kwanu [kwa Mulungu] kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’ (Mateyu 6:10) M’mawu ŵena, anthu samadzetsa Ufumuwo mwakuchita chifuniro cha Mulungu. Kuli kudza kwa Ufumuwo kumene kumachititsa chifuniro cha Mulungu kuchitidwa padziko lapansi. Motani?
Tamvetserani zimene ulosi wa Danieli mutu 2, vesi 44 ukunena: ‘Masiku a mafumu aja [olamulira aumunthu m’nthaŵi yamapeto] Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.’ Nkosadabwitsa kuti Yesu ananena kuti Ufumu wake suli wa dziko lino! Mmalomwake, Ufumuwo udzawononga maufumu, maboma, adziko lino lapansi ndi kutenga malo awo m’kulamulira anthu. Monga boma la anthu lopatsidwa ndi Mulungu, lidzatsimikizira kuti chifuniro cha Mulungu chachitidwa padziko lapansi.
Chifukwa chimene Ufumuwo udzachitira mwamphamvu chotero chikuwonekera bwino pamene tilingalira amene akulamulira dziko lino. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) “Woipayo” ali Satana Mdyerekezi, amene Paulo anamutcha “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.” (2 Akorinto 4:4, NW) Palibe njira iriyonse imene ziungwe za m’dziko lomwe mulungu wake ali Satana Mdyerekezi zingakhalire zogwirizana ndi Ufumu wa Mulungu.
Ichi ndichifukwa chimodzi chimene Yesu sanafunire kudziloŵetsa m’ndale zadziko. Pamene Ayuda autundu anayesa kumpanga mfumu, iye anawathaŵa. (Yohane 6:15) Monga momwe tawonera, iye anamuuza Pilato momasuka kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.” Ndipo mogwirizana ndi chimenechi, iye anauza otsatira ake kuti: “Siali a dziko lapansi monga ine sindiri wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Chifukwa chake, atsogoleri achipembedzo amene amaphunzitsa kuti kudza kwa Ufumu wa Mulungu kumafulumizidwa ndi kuwongokera kwa dongosolo la zinthu ndi kulimbikitsa nkhosa zawo kugwirira ntchito chonulirapo chimenecho ali aneneri onyenga. Iwo amaba chisonkhezero ndi chotulukapo cha zimene Baibulo limanenadi.
Kodi Nchifukwa Ninji Uli Wofunika?
Kodi chimenechi ndichigomeko chaukatswiri chabe? Kutalitali. Ziphunzitso zolakwa zonena za Ufumu wa Mulungu zasokeretsa ambiri ndipo zafikira pakuyambukira zochitika m’mbiri. Mwachitsanzo, bukhu lakuti Théo, bukhu lanazonse la Roma Katolika limanena kuti: “Anthu a Mulungu akupita patsogolo ku Ufumu wa Mulungu womwe unayambitsidwa padziko lapansi ndi Kristu . . . Tchalitchi chiri mbewu ya Ufumuwo.” Kudzigwirizanitsa kwa Tchalitchi cha Katolika ndi Ufumu wa Mulungu kunapatsa tchalitchicho mphamvu zazikulu zolamulira mkati mwa Nyengo Zapakati zodzaza ndi malaulo. Ngakhale lerolino, akuluakulu a tchalitchi amayesayesa kusonkhezera zochitika za dziko, akumachita zinthu mokomera madongosolo ena andale ndi kumatsutsa ena.
Wothirira ndemanga wina anapereka lingaliro lina lomwe liri lofala lerolino pamene ananena kuti: “Njira yopandukira ndiyo ufumuwo chifukwa chakuti kupanduka ndiko kugwirizana kwa anthu m’kachitidwe katsopano, kosonkhezeredwa ndi chizindikiro chaumulungu choperekedwa mwa munthu wa chowonadi—Yesu . . . Gandhi . . . ndi anyamata aŵiri a Berrigan.” Chiphunzitso chakuti Ufumu wa Mulungu ungafulumizidwe ndi kukhala wokangalika m’zandale ndi kunyalanyaza zenizeni za Ufumu kwachititsa atsogoleri achipembedzo kulondola udindo wandale. Kwachititsa ena kuloŵa m’nkhondo yachiweniweni ndipo ngakhale kutenga mbali m’nkhondo yachizembera. Palibe chirichonse cha zimenezi chimene chimagwirizana ndi chowonadi chakuti Ufumuwo suli wa dziko lino. Ndipo atsogoleri achipembedzo amene amadziloŵetsa mozama m’ndale zadziko ali kutalitali nkusakhala a dziko lino, monga momwe Yesu ananenera kuti ophunzira ake owona akakhalira. Amene amaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu ungafikiridwe mwa kuchitapo kanthu mwandale ali aneneri onyenga. Iwo akubera anthu mawu a Mulungu.
Ngati atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko anaphunzitsadi zimene Baibulo limanena, nkhosa zawo zikanadziŵa kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsadi mavuto onga umphaŵi, matenda, kusagwirizana kwa mafuko, ndi kuponderezana. Koma zidzachitidwa panthaŵi ya Mulungu ndi m’njira ya Mulungu. Sizidzachitidwa mwa kusintha madongosolo andale zadziko, omwe adzatha pamene Ufumuwo udza. Ngati atsogoleri achipembedzo ameneŵa analidi aneneri owona, akanaphunzitsa nkhosa zawo kuti pamene akuyembekezera Ufumu wa Mulungu kuchitapo kanthu, angapeze chithandizo chenicheni choperekedwa ndi Mulungu chakusamalira mavuto amene amachititsidwa ndi kupanda chilungamo kwa dzikoli.
Pomalizira, akanaphunzitsa nkhosa zawo kuti mikhalidwe yomaipiraipira yadziko lapansi imene imachititsa nkhaŵa yaikulu inaloseredwa m’Baibulo ndipo iri chizindikiro chakuti Ufumu ukudzawo uli pafupi. Inde, posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzaloŵererapo ndi kutenga malo a madongosolo andale zadziko alipowa. Ha, limenelo lidzakhala dalitso lotani nanga!—Mateyu 24:21, 22, 36-39; 2 Petro 3:7; Chivumbulutso 19:11-21.
Anthu Pansi pa Ufumu wa Mulungu
Kodi kudza kwa Ufumu wa Mulungu kudzatanthauzanji kwa anthu? Eya, kodi mungadziyerekezere inumwini mukuuka m’maŵa uliwonse mukudzimva wanyonga? Palibe aliyense amene mumadziŵa amene akudwala kapena kufa. Ngakhale akufa anu okondedwa abwezeretsedwa kwa inu mwa chiukiriro. (Yesaya 35:5, 6; Yohane 5:28, 29) Palibenso nkhaŵa zachuma zochititsidwa ndi malonda adyera kapena madongosolo achuma osalingana. Muli ndi nyumba yanuyanu yabwino ndiponso malo okwanira kubzala zonse zomwe mukuzifunikira kudyetsa banja lanu. (Yesaya 65:21-23) Mukhoza kupita kulikonse panthaŵi iriyonse yausana kapena usiku popanda kuwopa kuukiridwa. Kulibenso nkhondo—palibiretu chirichonse chowopseza chisungiko chanu. Aliyense akufunirani zabwino koposa. Oipa apitiratu. Chikondi ndi chilungamo ndizo ziripo. Kodi mungayerekezere nthaŵi imeneyo? Limenelo ndilo dziko limene Ufumuwo udzabweretsa.—Salmo 37:10, 11; 85:10-13; Mika 4:3, 4.
Kodi limeneli ndiloto wamba? Ayi. Ŵerengani malemba olembedwa m’ndime yapitayo, ndipo mudzapeza kuti zonse zomwe zanenedwa m’menemo zimasonyeza malonjezo otsimikizirika a Mulungu. Ngati simunakhalebe ndi chithunzi chabwino cha zimene Ufumu wa Mulungu ungachite ndipo udzachitira anthu, pamenepo munthu wina wakuberani mawu a Mulungu.
Mwachimwemwe, zinthu sizifunikira kukhala motero. Yesu ananena kuti m’tsiku lathu “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Magazini omwe mukuŵerengawa ali mbali ya ntchito yolalikira imeneyo. Tikukulimbikitsani kupeŵa kunyengedwa ndi aneneri onyenga. Santhulani mozama Mawu a Mulungu kuti mupeze chowonadi chonena za Ufumu wa Mulungu. Ndiyeno, dzigonjetsereni ku Ufumuwo, womwe uli kakonzedwe ka Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu. Kunena zowona, ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu, ndipo sudzalephera.
[Chithunzi patsamba 5]
Luther anaphunzitsa kuti boma laumunthu lingawonedwe monga Ufumu wa Mulungu
[Mawu a Chithunzi]
Mwachilolezo cha Trustees of the British Museum
[Chithunzi patsamba 7]
Mofanana ndi Mbusa wachikondi, Yehova, kudzera mwa Ufumu wake, adzabweretsa mikhalidwe imene palibe munthu angaibweretse