Chikristu Choona Chikupambana!
“Mawu a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika.”—MACHITIDWE 19:20.
1. Fotokozani mmene Chikristu chinafalira m’zaka za zana loyamba.
ATADZAZIDWA ndi mphamvu ya mzimu woyera, Akristu oyambirira analengeza mawu a Mulungu ndi changu chosazirala. Katswiri wina wambiri yakale analemba kuti: “Chikristu chinafala mofulumira kwambiri m’mayiko onse achiroma. Podzafika m’chaka cha 100 zikuoneka kuti m’chigawo chilichonse cha m’mphepete mwa nyanja ya Mediterranean munali Akristu ambiri.
2. Kodi Satana anayesa motani kusukulutsa uthenga wabwino, ndipo kodi zimenezi zinali zitanenedweratu motani?
2 Satana Mdyerekezi sanathe kupondereza Akristu oyambirirawo. M’malo mwake, iye anayesa kusukulutsa mphamvu ya uthenga wabwino m’njira zina monga mpatuko. Yesu anali ataneneratu kuti zimenezi zidzachitika m’fanizo lake la tirigu ndi namsongole. (Mateyu 13:24-30, 36-43) Mtumwi Petro anali atachenjezanso kuti mumpingo mudzauka aphunzitsi onyenga, ndi kuyambitsa magulu ampatuko owononga. (2 Petro 2:1-3) Mofananamo, mtumwi Paulo anachenjeza mosapita m’mbali kuti mpatukowo udzakhalako lisanafike tsiku la Yehova.—2 Atesalonika 2:1-3.
3. Kodi chinachitika n’chiyani atumwi atamwalira?
3 Atumwi atatha kumwalira, ziphunzitso zachikunja ndi mafilosofe zinaphimba uthenga wabwino. Monga momwe ananeneratu, aphunzitsi onyenga anapotoza ndi kusukulutsa uthenga weniweni wa choonadi. Pang’ono ndi pang’ono, chinyengo cha Matchalitchi Achikristu chinaphimba Chikristu chenicheni. Kunabuka gulu la atsogoleri amatchalitchi achikristu limene linayesetsa kuti Baibulo lisamapezeke ndi anthu wamba. Ngakhale kuti chiŵerengero cha anthu odzitcha Akristu chinawonjezeka, koma kulambira kwawo sikunali koyera. Matchalitchi Achikristu anafalikira m’mayiko ambiri ndi kukhala amphamvu zedi ndiponso osonkhezera kwambiri m’chikhalidwe cha Azungu, koma Mulungu sanawadalitse ndipo analibe mzimu wake.
4. N’chifukwa chiyani zolinga za Satana zofuna kulepheretsa zifuno za Mulungu zinalephera?
4 Komabe, zolinga za Satana zofuna kulepheretsa zifuno za Yehova zinalephereka. Ngakhale m’nthaŵi zamdima zenizenizo za mpatuko, Chikristu choona chinali champhamvube kwa ena. Amuna omwe anakopa Baibulo anayesetsa kuchita zimenezo mosamala kwambiri. Chotero, Baibulo silinasinthe, ngakhale kuti ambiri odzinenera kuti ali ndi udindo wophunzitsa Baibulo, anatanthauzira uthenga wake molakwa. Zaka mazana angapo zapitazo, ophunzira monga Jerome ndi Tyndale anatembenuza Mawu a Mulungu mwaukatswiri ndi kuwafalitsa. Anthu mamiliyoni ambiri analidziŵa Baibulo ndipo anadziŵanso kuti kuli Chikristu, ngakhale kuti chinali chonyenga.
5. Kodi mneneri Danieli analosera kuti chiyani za ‘chidziŵitso cholondola.’?
5 Mkupita kwanthaŵi, monga momwe buku la Danieli linaloserera, ‘chidziŵitso cholondola chachuluka.’ Zimenezi zachitika ‘m’nthaŵi ya chimaliziro’—nthaŵi yomwe tikukhala ino. (Danieli 12:4) Mzimu woyera watsogolera anthu okonda choonadi padziko lonse kuti am’dziŵe bwino Mulungu woona ndi zifuno zake. Ngakhale kuti ampatuko aphunzitsa ziphunzitso zawo kwa zaka mazana ambiri, komabe mawu a Mulungu apambana! Lerolino, uthenga wabwino ukulengezedwa paliponse, kusonyeza anthu chiyembekezo cha dziko latsopano lokondweretsa. (Salmo 37:11) Tsono tiyeni tione mmene mawu a Mulungu akulira m’masiku athu ano.
Kukula kwa Mawu a Mulungu Lerolino
6. Kodi Ophunzira Baibulo anazindikira choonadi chotani podzafika m’chaka cha 1914?
6 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kagulu kakang’ono ka Ophunzira Baibulo, omwe lerolino akudziŵika kuti Mboni za Yehova, kanasonkhezereka ndi choonadi cha m’Baibulo. Pofika m’chaka cha 1914, Baibulo kwa iwo linali lamoyo. Anazindikira choonadi chochititsa chidwi chokhudza zifuno za Mulungu. Anachita chidwi kwambiri ndi chikondi cha Yehova potumiza Mwana wake kudziko lapansi, ndi kutsegula njira ya kumoyo wosatha. Anadziŵanso ndi kuzindikira dzina la Mulungu ndi umunthu wake. Komanso, anazindikira kuti “nthaŵi zawo za anthu akunja” zinali zitatha kale, kusonyeza kuti nthaŵi inali pafupi yakuti boma la Ufumu wa Mulungu lidzetse madalitso kumtundu wa anthu. (Luka 21:24) Unalitu uthenga wabwino wosangalatsa kwabasi! Aliyense anayenera kuuzidwa za choonadi champhamvu chimenechi kwina kulikonse, chifukwatu miyoyo inali pangozi!
7. Kodi choonadi cha Baibulo chakula motani m’nthaŵi yathu ino?
7 Yehova anadalitsa chiŵerengero chochepa kwambiricho cha Akristu odzozedwa ndi mzimu. Lerolino, chiŵerengero cha omwe apeza Chikristu choona chaposa mamiliyoni asanu ndi imodzi. Mawu a Mulungu afalikiranso m’mayiko ambiri, mwakuti Mboni za Yehova zikupezeka m’mayiko 235. Komanso, mphamvu za choonadi cha Baibulo zaŵirikiza ndi kugonjetsa zopinga zonse zachipembedzo ndi zina zotero. Ntchito yolalikira ya padziko lonse imeneyi ikupereka umboni wina wosatsutsika wakuti tsopano Yesu ndiye akulamulira monga Mfumu.—Mateyu 24:3, 14.
8. Kodi ena anenanji zokhudza kuwonjezeka kwa Mboni za Yehova?
8 Monga momwe akatswiri ambiri yakale anathirira ndemanga pa kufala kochititsa chidwi kwa Chikristu m’zaka za zana loyamba, akatswiri ambiri aperekanso ndemanga zokhudza kuwonjezeka kwa anthu a Yehova m’nthaŵi yamakono ino. Ku United States, akatswiri aŵiri analemba mogwirizana kuti: “M’zaka 75 zapitazi, Mboni za Yehova zawonjezeka modabwitsa zedi . . . ndipo kuwonjezeka kumeneku kwachitika padziko lonse.” Nyuzipepala ina ya Kum’maŵa kwa Africa inati Mboni ndi “chimodzi mwa zipembedzo zomwe zikukula mofulumira ndiponso kulemekezedwa kwambiri padziko lonse, ndipo n’zodziŵika m’mayiko ochuluka chifukwa chotsatira kwambiri ziphunzitso za m’Baibulo.” Komanso magazini ya Akatolika, yomwe imafalitsidwa ku Ulaya, inanenapo za “kuwonjezeka moŵirikiza kwa Mboni za Yehova.” Kodi n’chiyani chachititsa kuwonjezeka kotereku?
Mzimu Woyera Ukugwira Ntchito Lerolino
9. (a) Kodi pali chifukwa chachikulu chiti chomwe chachititsa kuti mawu a Mulungu apambane lerolino? (b) Kodi Yehova amakokera motani anthu kwa iye?
9 Chifukwa chachikulu chomwe mawu a Mulungu apambanira lerolino n’chakuti mzimu wa Yehova ukugwira ntchito mwamphamvu kwambiri, monga momwe unachitira m’zaka za zana loyamba. Yesu anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye.” (Yohane 6:44) Mawu ameneŵa akusonyeza kuti Mulungu amakoka pang’onopang’ono amene ali oyenerera, ndi kuwakhudza mitima yawo. Kudzera m’ntchito yolalikira ya Mboni zake, Yehova akukoka anthu ena kuti adzam’lambire. Ameneŵa ndiwo “zofunika za amitundu onse”—anthu odzichepetsa onga nkhosa a dziko lapansi.—Hagai 2:6, 7.
10. Ndi anthu otani amene alabadira mawu a Mulungu?
10 Mzimu woyera walimbitsa anthu a Mulungu kuti afikitse mawu a Mulungu kumalekezero a dziko lapansi; ndiponso wasonkhezera anthu amitundu yonse kuti alabadire uthenga wabwino. Kunena zoona, amene alabadira mawu a Mulungu achokera ku “mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse.” (Chivumbulutso 5:9; 7:9, 10) Achokera m’mabanja olemera ndi osauka omwe, ophunzira kwambiri ndi osaphunzira. Ena aphunzira choonadi m’nthaŵi ya nkhondo ndi chizunzo chankhanza, pamene ena achiphunzira m’nthaŵi yamtendere. Muulamuliro wamtundu uliwonse, m’chikhalidwe chilichonse, kuyambira kundende mpaka kunyumba zachifumu, amuna ndi akazi alabadira uthenga wabwino.
11. Kodi mzimu woyera umagwira ntchito motani m’moyo wa anthu a Mulungu, ndipo tikuona kusiyana kotani?
11 Ngakhale kuti anthu a Mulungu n’ngosiyana kwambiri, akukhalira limodzi mogwirizana. (Salmo 133:1-3) Umenewu ndi umboni winanso wosonyeza kuti mzimu woyera ukugwira ntchito m’moyo wa anthu amene akutumikira Mulungu. Mzimu wake ndi mphamvu zosaneneka zimene zimathandiza atumiki ake kusonyeza chikondi, chimwemwe, mtendere, chifundo, ndi mikhalidwe inanso yabwino. (Agalatiya 5:22, 23) Lerolino, tikuona bwino lomwe zimene mneneri Mika analosera kalelo kuti: ‘Mudzazindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.’—Malaki 3:18.
Mawu a Mulungu Akusonkhezera Antchito Achangu
12. Kodi Mboni za Yehova zimaiona motani ntchito yolalikira, ndipo zikamalalikira zimayembekezera zotani?
12 Mboni za Yehova lerolino sizimangopita kutchalitchi ngati mwambo chabe. Iwo amagwiranso ntchito yolalikira mwakhama. Mofanana ndi Akristu oyambirira, iwoŵa amadzipereka mofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu, amayesetsa kuthandiza ena kuti nawonso aphunzire za malonjezo a Ufumu wa Yehova. Iwo ndi antchito anzake a Mulungu amene, mogwirizana ndi mzimu wake woyera, amasonkhanitsa ena kuti atumikire Yehova. Mwakuchita zimenezi, amasonyeza chifundo cha Yehova ndi chikondi chake pa anthu osakhulupirira. Ndipotu amachita zimenezo ngakhale akumane ndi osamvetsera, onyoza, kapenanso ozunza. Yesu anauza ophunzira ake kukonzekera zinthu zosiyanasiyana zimene anthu adzachita pakumva uthenga wabwino. Iye anati: “Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mawu anga, adzasunga anunso.”—Yohane 15:20.
13. Ndi zinthu ziti zomwe Matchalitchi Achikristu amalephera kuchita koma zimene Mboni za Yehova zikuchita?
13 Timachita chidwi zedi ndi kufanana kwa Mboni za Yehova lerolino ndi aja amene anapeza Chikristu chenicheni m’zaka za zana loyamba. Chinanso choonekeratu ndicho kusiyana kwa Mboni za Yehova ndi Matchalitchi Achikristu lerolino. Atalemba za changu cha Akristu oyambirira pantchito yolalikira, katswiri wina wamaphunziro anati: “N’zokayikitsa kuti matchalitchi angapite patsogolo m’zochitika pokhapokha ngati atasintha njira zawo zamakono zochitira zinthu, kotero kuti monga momwe zinalili kale, ntchito yolalikira ikhalenso udindo wa Mkristu aliyense wobatizidwa, ndikuti izichirikizidwa ndi makhalidwe abwino kwambiri kuposa alionse amene osakhulupirira angasonyeze.” Zinthu zomwe Matchalitchi Achikristu amalephera kuchita, Mboni za Yehova zikuchita! Chikhulupiriro chawo n’chamoyo, chikhulupiriro chenicheni, ndipo n’chikhulupiriro chochokera m’choonadi cha Baibulo mwakuti amasonkhezereka kuuza onse ofuna kumvetsera.—1 Timoteo 2:3, 4.
14. Kodi Yesu anauona motani utumiki wake, nanga ophunzira ake amasonyeza mtima wotani lerolino?
14 Yesu anaona utumiki wake monga chinthu chofunika kwambiri, anauika pamalo oyamba. Iye anauza Pilato kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Anthu a Mulungu amamva monga momwe Yesu anamvera. Popeza kuti choonadi cha Baibulo chili m’mitima yawo, amayesetsa kupeza njira zakuti auze ochuluka monga momwe angathere za choonadicho. Zina mwa njira zimenezi n’zaukatswiri zedi.
15. Kodi ena asonyeza motani ukatswiri polalikira uthenga wabwino?
15 M’dziko lina ku South America, Mboni zinkapita kunsi kwa mtsinje umene umathirira m’mtsinje waukulu wa Amazon kuti akauze anthu choonadi. Komabe, nkhondo yapachiweniweni itabuka m’chaka cha 1995, anthu wamba anawaletsa kupalasa ngalawa zawo mumtsinjewo. Pofunitsitsa kugaŵira zofalitsa zofotokoza Baibulo kwa osonyeza chidwi, Mbonizo zinaganiza zoti madzi azitenga uthengawo ndi kukaufikitsa kunsi kwa mtsinjewo. Analemba makalata ndi kuwaika m’mabotolo apulasitiki opanda kanthu limodzi ndi makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kenako anaponya mabotolowo mumtsinjemo. Anapitirizabe kuchita zimenezi kwa zaka zinayi ndi theka kufikira pamene analolanso athu wamba kuyamba kugwiritsa ntchito mtsinjewo. Anthu okhala m’mphepete mwa mtsinjewo, anathokoza Mbonizo chifukwa cha magaziniwo. Mkazi wina yemwe anali wophunzira Baibulo anawakumbatira misozi itadzaza m’maso ndipo anati: “Ndinkaganiza kuti sitidzaonananso. Komabe, nditayamba kulandira magazini a m’mabotolo, ndinadziŵa kuti munali kundikumbukirabe!” Ena omwe ankakhala m’mphepete mwa mtsinjewo anati anaŵerenga magaziniwo mobwerezabwereza. Midzi yambiri inali ndi “positi ofesi,” kutanthauza malo amene zinthu zoyandama zimakochezapo kwakanthaŵi. Okondwerera ankapita pafupipafupi pamalo ameneŵa kukayang’ana ngati “mtokoma” wawo wafika kuchokera kumtunda kwa mtsinjewo.
16. Kodi kudzipereka nthaŵi zina kumatipatsa motani mwayi wopanga ophunzira?
16 Ntchito yolalikira uthenga wabwino akuitsogolera ndiponso kuichirikiza ndi Yehova Mulungu limodzi ndi angelo ake amphamvu. (Chivumbulutso 14:6) Tikangodzipereka, mwayi wosayembekezeka wopanga ophunzira nthaŵi zina umangobwera. Ku Nairobi m’dziko la Kenya, akazi aŵiri achikristu omwe anali muutumiki wakumunda anatsiriza kulalikira m’nyumba zomwe anauzidwa. Mwadzidzidzi mayi wina wachitsikana anawafikira ndi kunena mwansangala kuti: “Ndakhala ndikupemphera kuti ndikumane ndi anthu ngati inu.” Nthaŵi yomweyo anapempha Mbonizo kuti zipite kunyumba kwake kuti akakambirane, ndipo tsiku lomwelo anayamba kuphunzira naye Baibulo. N’chifukwa chiyani mayi ameneyu sanazengereze kukakumana ndi Akristu aŵiriwo? Pafupifupi milungu iŵiri mmbuyomo, mwana wake anali atamwalira. Choncho ataona kamnyamata kena katanyamula thirakiti lakuti “Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa?” anafunitsitsa litakhala lake ndipo anapempha mnyamatayo kuti amupatse. Mnyamatayo anakaniza, koma anamuuza kuti Mboni zina n’zimene zinam’patsa thirakitilo. Posakhalitsa mayi ameneyu anayamba kupita patsogolo mwauzimu ndipo anatha kupirira kupweteka kwa imfa ya mwana wake.
Chikondi cha Mulungu Chiyenera Kusefukira
17-19. Kodi Yehova wasonyeza chikondi chotani ku mtundu wa anthu kudzera mu dipo?
17 Kukula kwa mawu a Mulungu padziko lonse lapansi n’kogwirizana kwambiri ndi nsembe yadipo ya Kristu Yesu. Mofanana ndi dipo, ntchito yolalikira imasonyeza chikondi chimene Yehova alinacho pa anthu kwina kulikonse. Mtumwi Yohane anauziridwa kulemba kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi [la anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
18 Tangolingalirani chikondi chimene Yehova anasonyeza mwa kupereka dipo. Kwa zaka zosaŵerengeka, Mulungu anali paubwenzi ndi mwana wake wokondedwa, mwana wobadwa yekha, “woyamba wa chilengo cha Mulungu.” (Chivumbulutso 3:14) Yesu amakonda kwambiri atate wake, ndipo Yehova anakonda Mwana wake “lisanakhazikike dziko lapansi.” (Yohane 14:31; 17:24) Yehova analola kuti Mwana wokondedwa ameneyu afe kotero kuti anthu akalandire moyo wosatha. Kunalitu kusonyeza chikondi ku mtundu wa anthu mozizwitsa kwambiri!
19 Yohane 3:17 amati: “Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.” Choncho, Yehova anatumiza Mwana wake kudzagwira ntchito yachikondi yopulumutsa, osati kudzaweruza kapena kudzapereka chilango. Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a Petro akuti: “[Yehova] sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.”—2 Petro 3:9.
20. Kodi chipulumutso chikugwirizana motani ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino?
20 Atapereka njira yoyenerera ya chipulumutso yomwenso inam’khudza kwambiri, Yehova akufuna kuti anthu ochuluka apindule nayo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanam’khulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?”—Aroma 10:13, 14.
21. Kodi tiyenera kumva bwanji polingalira za mwayi wogwira nawo ntchito yolalikira?
21 Ndi mwayitu waukulu kwabasi kugwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa yapadziko lonse imeneyi! Si ntchito yophweka, komabe Yehova amakondwera akaona anthu ake akuuza ena uthenga wabwino mokhulupirika ngakhale kuti ntchitoyi n’njovuta. Chotero kaya zinthu zikukuyenderani motani, lolani mzimu wa Mulungu ndi chikondi chomwe chili mumtima mwanumo kukusonkhezerani kugwira nawo ntchito imeneyi. Ndipo kumbukirani kuti zomwe taona zikukwaniritsidwa padziko lonse zimapereka umboni wokhutiritsa wakuti posachedwapa Yehova Mulungu akwaniritsa lonjezo lake lodzetsa “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” laulemerero mmene “mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani mpatuko sunathe kuletsa alaliki a uthenga wabwino?
• Kodi Mawu a Mulungu akula motani m’tsiku lathu?
• Kodi mzimu wa Mulungu ukugwira ntchito m’njira ziti lerolino?
• Kodi dipo likugwirizana motani ndi kulalikidwa kwa uthenga wabwino?
[Chithunzi patsamba 16]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kuwonjezeka kwa olengeza Ufumu m’zaka za m’ma 1900
Avareji ya Ofalitsa (m’mamiliyoni)
6.0
5.5
5.0
4.5
4.0
3.5
3.0
2.5
2.0
1.5
1.0
0.5
1900 1910 1920 1930 1940 1950 1960 1970 1980 1990 2000
[Zithunzi patsamba 15]
JEROME
TYNDALE
GUTTENBERG
HUS
[Mawu a Chithunzi]
Gutenberg ndi Hus: Kuchokera m’buku lakuti The Story of Liberty, 1878
[Chithunzi patsamba 15]
Ophunzira Baibulo akulengeza uthenga wabwino m’zaka za m’ma 1920
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Padziko lonse, anthu akulabadira uthenga wabwino
[Chithunzi patsamba 18]
Mofanana ndi nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, ntchito yolalikira imasonyeza ukulu wa chikondi cha Mulungu