Kusodza Anthu m’Nyanja Yadziko Lonse
“Pakuti ngati ndilalikira [mbiri yabwino, “NW”] ndiribe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira [mbiri yabwino].”—1 AKORINTO 9:16.
1, 2. (a) Kodi ndani amene akwaniritsa chitokoso cha pa 1 Akorinto 9:16, ndipo nchifukwa ninji mukuyankha motero? (b) Kodi Mboni za Yehova zavomereza thayo lotani?
KODI ndani amene m’zaka za zana lino la 20 akhala ndi chitokoso choperekedwa ndi mawu a Paulo apamwambawo? Kodi ndani amene apita m’dziko kukasodza mamiliyoni a amuna ndi akazi ‘ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu’? (Mateyu 5:3) Kodi ndani amene adziika paupandu wa kuponyedwa m’ndende ndi kuphedwa, ndipo amene avutika ndi zotero m’maiko ambiri, chifukwa cha lamulo la Kristu la pa Mateyu 24:14?
2 Mbiri imapereka yankho: Mboni za Yehova. Chaka chatha chokha Mboni zoposa mamiliyoni anayi zinapita kunyumba ndi nyumba ‘zikumalalikira mbiri yabwino’ m’maiko 211 ndi magawo ndipo m’zinenero zoposa 200. Ameneŵa sanali kagulu ka osankhidwa okha ka amishonale ophunzitsidwa. Ayi, Mboni za Yehova zonse zimalingalira kukhala ziri ndi thayo lakulalikira ndi kuphunzitsa kunyumba ndi nyumba ndi pamwaŵi uliwonse woyenerera. Kodi nchifukwa ninji amakuwona kukhala kofunika kuuza ena zimene iwo amakhulupirira? Chifukwa chakuti amazindikira kuti chidziŵitso chimabweretsa thayo.—Ezekieli 33:8, 9; Aroma 10:14, 15; 1 Akorinto 9:16, 17.
Kusodza Anthu, Chitokoso Chapadziko Lonse
3. Kodi ntchito yosodza iyenera kufika kuukulu wotani?
3 Ntchito yaikulu yosodza imeneyi sinalekezere, kunena kwake titero, kumtsinje umodzi kapena ngakhale nyanja kapena nyanja yamchere. Ayi, monga momwe Yesu analamulira, iyenera kuchitidwa “kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Asanakwere kwa Atate wake, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mateyu 28:19, 20.
4. (a) Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chinadabwitsa otsatira a Yesu oyambirira Achiyuda? (b) Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zimawonera ukulu wa ntchito yawo yolalikira?
4 Kwa otsatira a Yesu Achiyuda, imeneyo inayenera kudzakhala ntchito yachilendo. Iye anali kuuza ophunzira ake Achiyudawo kuti tsopano akapita kwa Akunja “odetsedwa” a mitundu yonse ndi kuwaphunzitsa. Anafunikira kusintha maganizo awo akale kotero kuti alandire chitokoso cha ntchitoyo ndi kuikwaniritsa. (Machitidwe 10:9-35) Koma panalibe njira ina; Yesu anali atawauza m’fanizo kuti “munda ndiwo dziko lapansi.” Chifukwa chake, Mboni za Yehova lerolino zimawona dziko lonse monga malo oziyenera kusodzamo. Sipangakhale “malire a m’nyanja” oletsa ntchito yawo yochokera kwa Mulungu. Nthaŵi zina kuchenjera kumafunika kumadera kumene kulibe ufulu wachipembedzo. Komabe, iwo amasodza mwachangu. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho? Chifukwa chakuti zochitika zadziko ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo zimasonyeza kuti tiri m’mbali yomalizira ya ntchito yosodza yapadziko lonse.—Mateyu 13:38; Luka 21:28-33.
Kupita Patsogolo m’Ntchito Yakusodza Kwadziko Lonse
5. Kodi ndianthu amtundu wanji amene alabadira kuntchito yosodza yadziko lonse?
5 Ochuluka a oloŵa nyumba a Ufumu odzozedwa “anasodzedwa” m’mitundu isanafike 1935, chotero kwakukulukulu chiŵerengero chawo chonse chinakwanira. Chifukwa chake, makamaka kuyambira 1935, Mboni za Yehova zakhala zikufunafuna anthu odzichepetsa amene anganenedwe kukhala “ofatsa” amene “adzalandira dziko lapansi.” (Salmo 37:11, 29) Anthu ameneŵa “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa.” Iwo akuchitapo kanthu moyanja ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu ‘chisautso chachikulu’ chisanakanthe dongosolo la zinthu loluluzika ndi loipa la Satana ndi olambira ake amene aweruzira ku “ng’anjo ya moto” ya chiwonongeko chomalizira.—Ezekieli 9:4; Mateyu 13:47-50; 24:21.
6, 7. (a) Kodi ndimasitepe otani amene anatengedwa mu 1943 ponena za ntchito yolalikira? (b) Kodi zotulukapo zakhala zotani?
6 Kodi ntchito yosodza yapadziko lonse yakhaladi yachipambano? Lekani zochitika zipereke yankho. Kumbuyoko mu 1943, Nkhondo Yadziko ya II inali idakali mkati, komabe abale okhulupirika odzozedwa pamalikulu apadziko lonse a Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York, anawoneratu kuti ntchito yosodza yapadziko lonse ikayenera kuchitidwa. Chotero, kodi anachitaponji?a—Chivumbulutso 12:16, 17.
7 Mu 1943 Watchtower Society inakhazikitsa sukulu ya amishonale yotchedwa Gileadi (Chihebri “Mulu wa Umboni”; Genesis 31:47, 48) imene inayamba kuphunzitsa amishonale zana limodzi miyezi isanu ndi umodzi iriyonse kotero kuti akanatha kutumizidwa monga asodzi ophiphiritsira padziko lonse lapansi. Panthaŵiyo, panali Mboni 126,329 zokha zosodza anthu mokangalika m’maiko 54. M’zaka khumi ziŵerengero zimenezo zinawonjezereka kufika pa Mboni 519,982 m’maiko 143! Ndithudi, sukulu ya Gileadi inali kutulutsa asodzi olimba mtima amuna ndi akazi, ofunitsitsa kupita kumaiko atsopano ndi kukachita ndi mikhalidwe yachilendo kumene amasodza m’madera atsopano a nyanjayo. Monga chotulukapo, zikwi za anthu owona mtima zinalabadira. Amishonale amenewo, ndi Mboni zakumaloko zomwe anagwira nazo ntchito, anayala maziko a kuwonjezeka kodabwitsa komwe kukuchitika tsopano.
8, 9. (a) Kodi nzitsanzo zotani zimene zingatchulidwe za ntchito yaumishonale yapadera? (b) Kodi ndimotani mmene amishonale awonera kukula kwapadera m’minda yawo? (Onaninso 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses.)
8 Okhulupirika ambiri akale ochokera m’makalasi amenewo a Gileadi akutumikirabe m’magawo awo achilendo, ngakhale kuti tsopano ali oposa zaka 70 kapena ngakhale 80 zakubadwa. Chitsanzo chimodzi chimene chimasonyeza ambiri a ameneŵa nchija cha Eric Britten wa zaka zakubadwa 82 ndi mkazi wake, Christina, amene anamaliza maphunziro m’kalasi ya 15 ya Gileadi mu 1950 ndipo akutumikirabe ku Brazil. Pamene anapita kukatumikira ku Brazil, munali Mboni zosafika pa 3,000 m’dzikolo. Tsopano muli zoposa 300,000! Ndithudi, ‘wam’ng’ono wafikira kukhala mtundu wamphamvu’ m’Brazil, chifukwa chakuti ntchito yosodza yakhala ikubala zipatso zochuluka.—Yesaya 60:22.
9 Ndipo kodi tinganenenji ponena za amishonale mu Afirika? Ochuluka asinthira kumikhalidwe yosiyana kwambiri ndipo afikira pakuwakonda anthu a Afirika. Chitsanzo chapadera ndicho cha abale otchedwa John ndi Eric Cooke ndi akazi awo, Kathleen ndi Myrtle, omwe pakali pano akutumikira mu South Africa. John ndi Eric anamaliza maphunziro m’kalasi lachisanu ndi chitatu mu 1947. Maiko amene anatumikiramo ndiwo Angola, Zimbabwe, Mozambique, ndi South Africa. Amishonale ena anafera mu Afirika chifukwa cha matenda, ndipo ena chifukwa cha nkhondo ndi chizunzo, monga ngati Alan Battey ndi Arthur Lawson, omwe anafa m’nkhondo yachiŵeniŵeni yaposachedwapa mu Liberia. Komabe, gawo la nyanjayo la Afirika lakhaladi lobala zipatso kwambiri. Tsopano muli Mboni zoposa 400,000 zofalikira m’kontinenti yaikuluyo.
Onse Ali ndi Mbali
10. Kodi nchifukwa ninji ndipo ndim’njira yotani imene apainiya akuchitira ntchito yoyamikirika?
10 Komabe, tiyenera kuzindikira kuti pamene kuli kwakuti amishonale akumaiko ena afika zikwi, ofalitsa ndi apainiyab akumaloko afikira kukhala mamiliyoni. Iwo akuchita yochuluka ya ntchito yolalikira padziko lonse lapansi. Mu 1991 panali avareji ya apainiya 550,000 ndi aminisitala oyendayenda. Ha, chimenecho nchiŵerengero chosangalatsa motani nanga titaganiza za Mboni zokhulupirika zonsezi zimene zikupanga kuyesayesa kwapadera kukhala ndi phande m’ntchito yaikulu yosodza, zochita avareji ya maola 60 kufikira ku 140 a ulaliki mwezi uliwonse. Ambiri amachita zimenezi mwakudzimana kwakukulu ndi kutairapo ndalama zambiri. Koma nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti amakonda Yehova Mulungu wawo ndi mtima wawo wonse, nzeru zawo zonse, moyo wawo wonse, ndi nyonga zawo zonse, ndipo amakonda anansi awo monga eni okha.—Mateyu 22:37-39.
11. Kodi ndiumboni wotsimikizirika wotani umene ulipo wakuti mzimu wa Yehova ukugwira ntchito pakati pa anthu ake?
11 Kodi tinganenenji ponena za Mboni zinazo zoposa mamiliyoni atatu ndi theka zomwe siziri muutumiki wanthaŵi yonse komabe zikumatumikira Yehova ndi mtima wonse, molingana ndi mikhalidwe yawo? Ena ndiakazi okwatiwa, anakubala osamalira ana aang’ono, amene amaperekabe nthaŵi yawo yofunika kwambiri ku ntchito yosodza yapadziko lonse. Ambiri ndiamuna okwatira kapena atate okhala ndi ntchito zakudziko za nthaŵi zonse; komabe, amapatula nthaŵi kumapeto kwa mlungu ndi madzulo kukaphunzitsa chowonadi kwa anthu osawadziŵa. Ndiyeno pali khamu lalikulu la amuna ndi akazi amene ndimbeta ndi achichepere amene amakhala ndi phande m’kulalikira ndi omwe amavomereza chowonadi mwa khalidwe lawo. Kodi ndigulu lina lachipembedzo liti limene liri ndi antchito odzifunira osalipiridwa oposa mamiliyoni anayi amene amalalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu mwezi uliwonse? Ndithudi zimenezi zimachitira umboni wa kugwira ntchito kwa mzimu wa Yehova!—Salmo 68:11; Machitidwe 2:16-18; yerekezerani ndi Zekariya 4:6.
Zothandizira Kukulako
12. Kodi nchiyani chikupangitsa anthu kuchilandira chowonadi ndipo m’ziŵerengero zotani?
12 Ntchito yolalikira yaikulu imeneyi ikubweretsa zotulukapo zabwino koposa chaka chirichonse. Mu 1991 Mboni zatsopano zoposa 300,000 zinabatizidwa mwakumizidwa kotheratu m’madzi. Ndiko kuti mipingo yoposa 3,000 ya Mboni 100 uliwonse! Kodi zonsezi zikukwaniritsidwa motani? Kumbukirani zimene Yesu ananena: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye . . . Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi [Yehova, NW]. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa ine.” Chifukwa chake, kuvomereza kwa munthu kusodza kwapadziko lonse sikuli chabe kuyesayesa kwa anthu. Yehova amawona mkhalidwe wa mtima ndi kukokera oyenererawo kwa iye mwini.—Yohane 6:44, 45; Mateyu 10:11-13; Machitidwe 13:48.
13, 14. Kodi ndikaimidwe kamaganizo kabwino kotani kamene Mboni zambiri zasonyeza?
13 Komabe, osodza anthuwo ali nthumwi zimene Yehova akugwiritsira ntchito kukokera anthu kwa iye mwini. Chifukwa chake, kaimidwe kawo kamaganizo kulinga kwa anthu ndi gawo lomwe amasodzako nzofunika. Ha, nkolimbikitsa chotani nanga kuwona ochuluka akulabadira mawu a Paulo kwa Agalatiya: “Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti panyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”—Agalatiya 6:9.
14 Mboni zambiri zokhulupirika zakhala zikulalikira kwa zaka makumi ambiri, pamene zikupenyetsetsa zochitika zadziko. Iwo awona kubuka ndi kugwa kwa Chinazi, Chifasizimu, ndi madongosolo ena opondereza ufulu. Ena awona nkhondo zambiri zimene zachitika chiyambire 1914. Iwo awona atsogoleri adziko akuika chikhulupiriro chawo mu Chigwirizano cha Amitundu ndiyeno Mitundu Yogwirizana. Awona ntchito ya Yehova ikuletsedwa ndipo pambuyo pake kuvomerezedwa mwalamulo m’maiko ambiri. Mkati mwa zonsezi, Mboni za Yehova sizinaleme pakuchita zabwino, kuphatikizapo kutumikira monga asodzi a anthu. Ha, ndi cholembedwa chabwino chotani nanga cha kusunga umphumphu!—Mateyu 24:13.
15. (a) Kodi ndichithandizo chotani chimene anakhala nacho m’kusinthira kuzosoŵa za gawo lathu lapadziko lonse? (b) Kodi ndimotani mmene zofalitsidwa zimenezi zathandizira m’gawo lanu?
15 Pali zinthu zina zimene zathandizira kukula kwapadziko lonse kumeneku. Chimodzi cha izo ndicho kusintha kwa kaimidwe kamaganizo ka osodza anthuwo kulinga kuzosoŵa za gawo. Limodzi ndi kusamuka, miyambo yosiyanasiyana, zipembedzo, ndi zinenero, Mboni za Yehova zakulitsa kumvetsetsa kwawo malingaliro osiyanasiyana ameneŵa. Ndipo mpingo wapadziko lonse wathandiza mokulira mwakusindikiza Mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 200. New World Translation of the Holy Scriptures, yathunthu kapena mbali imodzi, tsopano iri m’zinenero 13, kuphatikizapo Chichek ndi Chislovak. Brosha la Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha! tsopano limapezeka m’zinenero 198, kuyambira Chialbania mpaka Chizulu, ndipo anasindikizidwa m’makope 72 miliyoni. Bukhu la The Greatest Man Who Ever Lived latembenuzidwa kale m’zinenero 69. Bukhu la Mankind’s Search for God, lofalitsidwa m’zinenero 29, limapereka chidziŵitso cha chiyambi ndi zikhulupiriro za zipembedzo zazikulu za dziko ndipo lakhaladi chithandizo chapadera m’kusodza kwapadziko lonse.
16. Kodi ena alabadira motani kuzosoŵa za m’maiko ena?
16 Kodi nchiyaninso chimene chapititsa patsogolo ntchito yosodza? Zikwi zakhala zofunitsitsa kulabadira ‘chiitano cha ku Makedoniya.’ Monga momwedi Paulo anali wofunitsitsa kusamuka ku Asia Minor kupita ku Makedoniya mu Yuropu, pachiitano cha Mulungucho Mboni zambiri zasamukira kumaiko ndi magawo kumene kuli kusoŵa kwakukulu kwa olalikira Ufumu, limodzinso ndi akulu ndi atumiki otumikira. Iwo akhala ngati asodzi enieni amene amapeza kuti dera lawo lasodzedwa kwambiri nasamukira ku dera lina limene liri ndi ngalaŵa zochepa ndi nsomba zambiri.—Machitidwe 16:9-12; Luka 5:4-10.
17. Kodi tiri ndi zitsanzo zotani za awo amene alabadira ku ‘chiitano cha ku Makedoniya’?
17 Makalasi aposachedwapa a sukulu ya amishonale ya Gileadi aphatikizapo ophunzira ochokera kumaiko osiyanasiyana a ku Yuropu amene aphunzira Chingelezi ndipo adzipereka kukatumikira kumaiko ena achilendo. Mofananamo, kupyolera mwa Sukulu ya Maphunziro Autumiki, abale ambiri omwe ndi mbeta amachita maphunziro osamalitsa kwa miyezi iŵiri ndiyeno amatumizidwa ku maiko ena kukalimbikitsa mipingo ndi madera. Malo ena osodzako apadera ali m’magawo amene akutseguka tsopano Kum’maŵa kwa Yuropu ndi maiko akale a Soviet Union.—Yerekezerani ndi Aroma 15:20, 21.
18. (a) Kodi nchifukwa ninji kaŵirikaŵiri apainiya amakhala aminisitala ogwira mtima? (b) Kodi angathandize motani ena mumpingo?
18 Chithandizo chowonjezereka m’ntchito yosodza yapadziko lonse ndicho Sukulu ya Utumiki Waupainiya imene apainiya okhazikika amapezekapo. Kupyolera m’milungu iŵiri ya kuphunzira kosamalitsa bukhu la Kuŵala Monga Zounikira m’Dziko, lokonzedwera apainiya, iwo amawongolera maluso awo auminisitala pamene alingalira mitu yonga yakuti “Kulondola Njira ya Chikondi,” “Tsatirani Yesu Monga Chitsanzo,” ndi “Kukulitsa Luso la Kuphunzitsa.” Mipingo yonse imakhala yoyamikira chotani nanga kukhala ndi timagulu ta asodzi akunyumba ndi nyumba toyeneretsedwa timeneti tingaphunzitse ambiri m’ntchito yaikulu yosodza imeneyi!—Mateyu 5:14-16; Afilipi 2:15; 2 Timoteo 2:1, 2.
Kodi Tingawongokere?
19. Mofanana ndi mtumwi Paulo, kodi tingawongolere motani uminisitala wathu?
19 Mofanana ndi Paulo, tikufuna kukhala ndi kaimidwe kamaganizo kabwino, koyang’ana kutsogolo. (Afilipi 3:13, 14) Iye anasinthira kumitundu yonse ya anthu ndi mikhalidwe. Anadziŵa kupeza maziko ofanana ndi kulingalira molingana ndi mikhalidwe ndi miyambo yakumaloko. Tingayambitse maphunziro Abaibulo mwakukhala maso kumayankhidwe a mwininyumba kuuthenga wa Ufumu ndiyeno kusinthira ulaliki wathu ku zosoŵa za munthuyo. Pokhala ndi zothandizira kuphunzira Baibulo zambiri, tingathe kugaŵira chimene chimayenerana ndi malingaliro a munthu payekha. Kukhala kwathu okhoza kusintha ndi amaso kulinso mbali zofunika m’kusodza kophula kanthu.—Machitidwe 17:1-4, 22-28, 34; 1 Akorinto 9:19-23.
20. (a) Kodi nchifukwa ninji ntchito yathu yosodza ili yofunika kwambiri tsopano? (b) Kodi nchiyani chomwe chiri thayo lathu la munthu payekha tsopano?
20 Kodi nchifukwa ninji ntchito yapadera yosodza yapadziko lonse imeneyi iri yofunika kwambiri tsopano? Chifukwa chakuti kuchokera m’maulosi a Baibulo osonyezedwa m’zinthu zomwe zachitika ndi zimene zikuchitika, kuli kowonekeratu kuti dongosolo ladziko la Satana likumka kumapeto a chiwonongeko. Chotero, kodi nchiyani chimene ifeyo, Mboni za Yehova, tiyenera kukhala tikuchita? Nkhani zitatu zophunziridwa m’magazini ano zagogomezera thayo lathu lakukhala okangalika ndi achangu m’ntchito yathu yosodza m’dera lathu la nyanja yadziko lonse. Tiri ndi chitsimikiziro champhamvu chochokera m’Baibulo chakuti Yehova sadzaiŵala ntchito yathu yakhama yosodza. Paulo anati: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachiwonetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe. Koma tikhumba kuti yense wa inu awonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro.”—Ahebri 6:10-12.
[Mawu a M’munsi]
a Onaninso Revelation—Its Grand Climax At Hand!, tsamba 185 ndi 186, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b “Mpainiya wofalitsa . . . Wantchito wanthaŵi yonse wa Mboni za Yehova.”—Webster’s Third New International Dictionary.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimawona dziko lonse kukhala malo a ntchito yawo yosodza?
◻ Kodi sukulu ya amishonale ya Gileadi yakhala dalitso lotani pantchito yosodza?
◻ Kodi ndizinthu zina zotani zimene zathandizira chipambano cha Mboni za Yehova?
◻ Kodi ndimotani mmene ife aliyense payekha tingawongolere uminisitala wathu Wachikristu?
[Tchati patsamba 24]
ZOTULUKAPO ZA KUSODZA KWAPADZIKO LONSE
Chaka Maiko Mboni
1939 61 71,509
1943 54 126,329
1953 143 519,982
1973 208 1,758,429
1983 205 2,652,323
1991 211 4,278,820
[Chithunzi patsamba 25]
Ntchito yochitira umboni ikuchitidwabe pakati pa asodzi a ku Galileya