Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/15 tsamba 9-14
  • Sonyezani Chikhulupiriro Chozikidwa pa Chowonadi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sonyezani Chikhulupiriro Chozikidwa pa Chowonadi
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chikhulupiriro Nchiyani?
  • Chozikidwa pa Zowona Zamaziko
  • Chipatso cha Mzimu Woyera
  • Kukwaniritsa Chikhulupiriro
  • Kodi Nkuchipenderanji Chikhulupiriro Chathu?
  • Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Malonjezo a Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Chikhulupiriro Chimatipatsa Mphamvu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kodi Mumakhulupiriradi Uthenga Wabwino?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Ndithandizeni M’mene Ndisoŵa Chikhulupiriro!”
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/15 tsamba 9-14

Sonyezani Chikhulupiriro Chozikidwa pa Chowonadi

‘Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.’​—AHEBRI 11:6.

1, 2. Kodi ndimotani mmene chikhulupiriro cha Adamu chinaikidwira pachiyeso, ndipo ndi chotulukapo chotani?

CHIKHULUPIRIRO chimafuna zoposa kungokhulupirira kuti Mulungu aliko. Mwamuna woyamba, Adamu, analibe chikaikiro chirichonse ponena za kukhalako kwa Yehova Mulungu. Mulungu analankhula ndi Adamu, mwachiwonekere kupyolera mwa Mwana Wake, Mawuyo. (Yohane 1:1-3; Akolose 1:15-17) Komabe, Adamu anataya chiyembekezo cha moyo wamuyaya chifukwa chakuti analephera kumvera Yehova ndi kusonyeza chikhulupiriro mwa iye.

2 Chimwemwe cha mtsogolo cha Adamu chinawonekera kuikidwa paupandu pamene mkazi wake, Hava, sanamvera Yehova. Eya, ngakhale lingaliro lenilenilo lakutaya mkazi wake linaika chikhulupiriro cha mwamuna woyambayo pachiyeso! Kodi Mulungu akatha kuthetsa vutoli mwanjira yakuti ikasungabe chimwemwe cha Adamu ndi mkhalidwe wake wabwino? Mwakugwirizana ndi Hava m’kuchimwa, Adamu anasonyeza kuti iye mwachiwonekere sanaganize motero. Iye anayesa kuthetsa vutolo mwa njira yakeyake, m’malo mofuna chitsogozo chaumulungu. Polephera kusonyeza chikhulupiriro mwa Yehova, Adamu anadzetsa imfa pa iyemwini ndi ana ake onse.​—Aroma 5:12.

Kodi Chikhulupiriro Nchiyani?

3. Kodi ndimotani mmene kumasulira kwa Baibulo kwa chikhulupiriro kumasiyanira ndi kwa dikishonale ina?

3 Dikishonale ina imamasulira chikhulupiriro kukhala “kukhulupirira zolimba chinthu chimene palibe umboni.” Komabe, posachirikiza lingaliro limeneli mpang’ono ponse, Baibulo limagogomezera zosiyana kotheratu. Chikhulupiriro chimazikidwa pa mfundo, pa zenizeni, pa chowonadi. Malemba amanena kuti: “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikiziridwa cha zinthu zoyembekezeredwa, chisonyezero chowonekera bwino cha zenizeni ngakhale sizinapenyeke.” (Ahebri 11:1, NW) Munthu wokhala ndi chikhulupiriro ali ndi chitsimikiziro chakuti chirichonse cholonjezedwa ndi Mulungu chimakhala ngati chokwaniritsidwa kale. Umboni wokhutiritsa wa zinthu zosapenyeka umakhala wamphamvu kwakuti chikhulupiriro chimanenedwa kukhala chofanana ndi umboniwo.

4. Kodi ndimotani mmene bukhu lina lazilozero limachirikizira kumasulira kwa Baibulo kwa chikhulupiriro?

4 Mu New World Translation, liwu lotanthauza kuchita la mneni Wachihebri ʼa·manʹ nthaŵi zina limamasuliridwa “kusonyeza chikhulupiriro.” Malinga ndi Theological Wordbook of the Old Testament, “tanthauzo lenileni la liwu loyambirira limapereka lingaliro la kutsimikizirika . . . mosiyana ndi malingaliro amakono a chikhulupiriro kukhala chinthu chothekera, choyembekezeredwa kukhala chowona, koma chosatsimikizirika.” Bukhu limodzimodzilo limati: “Tanthauzo la ʼāmēn ‘motsimikiza’ limapitirizidwa mu Chipangano Chatsopano ndi liwu lakuti amēn limene ndiliwu Lachingelezi lakuti ‘amen.’ Yesu analigwiritsira ntchito liwulo kaŵirikaŵiri (Mat 5:18, 26, ndi ena otero) kugogomezera kutsimikizirika kwa nkhani.” Liwu lomasuliridwa “chikhulupiriro” m’Malemba Achikristu Achigiriki limatanthauzanso kukhulupirira chinachake chozikidwa zolimba pa chenicheni kapena chowonadi.

5. Kodi ndimotani mmene liwu Lachigiriki lomasuliridwa “chiyembekezo chotsimikiziridwa” pa Ahebri 11:1 linagwiritsiridwira ntchito m’zikalata zamalonda zakale, ndipo kodi chimenechi chiri nkufunika kotani kwa Akristu?

5 Liwu Lachigiriki lakuti (hy·poʹsta·sis) lomasuliridwa “chiyembekezo chotsimikiziridwa” pa Ahebri 11:1, (NW) linagwiritsiridwa ntchito mofala m’zikalata zakale zagumbwa zamalonda kupereka lingaliro la chinachake chimene chimatsimikizira kutenga chinthu kukhala chako kwa mtsogolo. Akatswiri Moulton ndi Milligan akupereka kumasulira kwakuti: “Chikhulupiriro ndicho title deed [lamulo la umwini] ya zinthu zimene zikuyembekezeredwa.” (Vocabulary of the Greek Testament) Mwachiwonekere, ngati munthu ali ndi lamulo la umwini pa chinthu, iye akhoza kukhala ndi “chiyembekezo chotsimikiziridwa” chakuti tsiku lina chiyembekezo chake chakupeza chinthucho chidzakwaniritsidwa.

6. Kodi liwu Lachigiriki lomasuliridwa “chisonyezero chowonekera bwino” pa Ahebri 11:1, liri nkufunika kotani?

6 Pa Ahebri 11:1 (NW), liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “chisonyezero chowonekera bwino” (eʹleg·khos) limapereka lingaliro la kupereka umboni kuti musonyeze chinachake, makamaka chosiyana ndi mmene zinthu zikuwonekera. Umboni wowona kapena wamphamvu umamveketsa bwino lomwe zimene poyamba sizinawonedwe, mwakutero kutsutsa zimene zinali zachiphamaso. Chifukwa chake ponse paŵiri m’Malemba Achihebri ndi Achigiriki, chikhulupiriro sichiri konse “kukhulupirira zolimba chinthu chimene palibe umboni.” Mosiyana, chikhulupiriro chimazikidwa pa chowonadi.

Chozikidwa pa Zowona Zamaziko

7. Kodi ndimotani mmene Paulo ndi Davide amalongosolera anthu otsutsa kukhalako kwa Mulungu?

7 Mtumwi Paulo anatchula chowonadi chamaziko pamene analemba ponena za Mlengi kuti ‘zawoneka bwino zosawoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti [otsutsa chowonadi] adzakhale opanda mawu akuŵiringula.’ (Aroma 1:20) Inde, “zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu,” ndipo ‘dziko lapansi lidzala nacho chuma [chake].’ (Salmo 19:1; 104:24) Koma bwanji ngati munthu sakufuna kulingalira umboniwo? Wamasalmo Davide anati: ‘Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake [“chifukwa cha kudzitama kwake,” The New English Bible], akuti, sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.’ (Salmo 10:4; 14:1) Kumbali ina, chikhulupiriro chimazikidwa pa chowonadi chachikulu chakuti Mulungu aliko.

8. Kodi awo okhala ndi chikhulupiriro ali okhoza kukhala ndi chitsimikiziro ndi chidziŵitso chotani?

8 Sizimangothera pakuti Yehova aliko; iye alinso wokhulupirika, ndipo tikhoza kudalira malonjezo ake. Iye anati: ‘Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala.’ (Yesaya 14:24; 46:9, 10) Awa sali mawu opanda tanthauzo. Pali umboni wowonekera bwino lomwe wakuti mazanamazana amaulosi olembedwa m’Mawu a Mulungu akwaniritsidwa. Pokhala ndi kuunikiridwa kumeneku, awo osonyeza chikhulupiriro akhozanso kuzindikira kukwaniritsidwa kwa maulosi ena ambiri a Baibulo kumene kukuchitika tsopano. (Aefeso 1:18) Mwachitsanzo, iwo akuwona kukwaniritsidwa kwa ‘chizindikiro’ cha kukhalapo kwa Yesu, kuphatikizapo kufulumira kwa kulalikidwa kwa Ufumu wokhazikitsidwa, limodzinso ndi kufutukuka kwa kulambira kowona konenedweretuko. (Mateyu 24:3-14; Yesaya 2:2-4; 60:8, 22) Iwo amadziŵa kuti posachedwapa mitundu idzafuula “Mtendere ndi chisungiko!” ndikuti mwamsanga pambuyo pake Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ (1 Atesalonika 5:3, NW; Chibvumbulutso 11:18) Ha, ndalitso lotani nanga kukhala ndi chikhulupiriro chozikidwa pa zowona zaulosi!

Chipatso cha Mzimu Woyera

9. Kodi pali unansi wotani pakati pa chikhulupiriro ndi mzimu woyera?

9 Chowonadi chimene chikhulupiriro chazikidwapo chimapezedwa m’Baibulo, chotulukapo cha mzimu woyera wa Mulungu. (2 Samueli 23:2; Zekariya 7:12; Marko 12:36) Pamenepo, nkwanzeru kunena kuti chikhulupiriro sichingakhalepo popanda kugwira ntchito kwa mzimu woyera. Ndicho chifukwa chake Paulo analemba kuti: ‘Chipatso cha mzimu [chimaphatikizapo] . . . chikhulupiriro.’ (Agalatiya 5:22) Koma ambiri amakana chowonadi chaumulungu, namaipitsa miyoyo yawo ndi zilakolako zakuthupi ndi malingaliro amene amavutitsa mzimu wa Mulungu. Chifukwa chake, ‘sionse ali nacho chikhulupiriro,’ poti iwo alibe maziko ochimangirapo.​—2 Atesalonika 3:2; Agalatiya 5:16-21; Aefeso 4:30.

10. Kodi ndimotani mmene atumiki oyambirira ena a Yehova anasonyezera kuti anali nacho chikhulupiriro?

10 Komabe, mwa mbadwa za Adamu, anthu ena asonyeza chikhulupiriro. Ahebri mutu 11 amatchula Abeli, Enoke, Nowa, Abrahamu, Sara, Isake, Yakobo, Yosefe, Mose, Rahabi, Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide, ndi Samueli, pamodzi ndi atumiki ambiri a Yehova osatchulidwa maina, omwe ‘adachitidwa umboni mwa chikhulupiriro.’ Onani zimene zinachitidwa ‘mwa chikhulupiriro.’ Zinali ndi chikhulupiriro kuti Abeli “anapereka kwa Mulungu nsembe” ndipo Nowa ‘anamanga chingalawa.’ Ndi chikhulupiriro Abrahamu ‘anamvera kutuluka kunka ku malo amene adzalandira ngati choloŵa.’ Ndipo ndi chikhulupiriro, Mose ‘anasiya Igupto.’​—Ahebri 11:4, 7, 8, 27, 29, 39.

11. Kodi Machitidwe 5:32 amasonyezanji ponena za anthu omvera Mulungu?

11 Mwachiwonekere, atumiki a Yehova onsewo anachita zoposa kungokhulupirira kukhalapo kwa Mulungu. Posonyeza chikhulupiriro, iwo anamdalira kukhala Uyo amene ali ‘wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.’ (Ahebri 11:6) Iwo anachita zimene mzimu wa Mulungu unawatsogolera kuchita, mogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi chokhalako panthaŵiyo, ngakhale kuti chinali chochepa. Anali osiyana motani nanga ndi Adamu! Iye sanachite mwachikhulupiriro chozikidwa pa chowonadi kapena mogwirizana ndi chitsogozo cha mzimu woyera. Mulungu amapereka mzimu wake woyera kwa omumvera okha.​—Machitidwe 5:32.

12. (a) Kodi Abeli adali ndi chikhulupiriro m’chiyani, ndipo kodi anasonyeza motani chimenechi? (b) Mosasamala kanthu za chikhulupiriro chawo, kodi nchiyani chimene mboni za Yehova zokhalako Chikristu chisanadze sizinalandire?

12 Mosiyana ndi atate wake, Adamu, Abeli wopembedzayo anali ndi chikhulupiriro. Mwachiwonekere, iye anaphunzira kwa makolo ake ponena za ulosi woyambirira kuperekedwa wakuti: ‘[Ine Yehova Mulungu] ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.’ (Genesis 3:15) Chotero Mulungu analonjeza kuchotsapo kuipa ndi kubwezeretsa chilungamo. Ponena za mmene ulosiwu ukakwaniritsidwira, Abeli sanadziŵe. Koma chikhulupiriro chake chakuti Mulungu ndiye Wobwezera Mphotho kwa awo omfunafuna Iye chinali champhamvu mokwanira kumsonkhezera kupereka nsembe. Mwachiwonekere iye analingalira mwakuya ponena za ulosiwo nakhulupirira kuti kukhetsedwa kwa mwazi kukafunikira kuti lonjezolo likwaniritsidwe ndi kukwezera anthu kuungwiro. Chifukwa chake, nsembe yanyama ya Abeli inali yolandirika. Komabe, mosasamala kanthu za chikhulupiriro chawo, Abeli ndi mboni zina za Yehova zokhalako Chikristu chisanafike “sanalandira lonjezanolo.”​—Ahebri 11:39.

Kukwaniritsa Chikhulupiriro

13. (a) Kodi nchiyani chimene Abrahamu ndi Davide anadziŵa ponena za kukwaniritsidwa kwa lonjezanolo? (b) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti ‘chowonadi chinadza mwa Yesu Kristu’?

13 Pambuyo panyengo yakutiyakuti m’zaka mazana ambiri apitawo, Mulungu anakhala akuvumbula chowonadi chowonjezereka ponena za mmene lonjezo la ‘mbewu ya mkazi’ likakwaniritsidwira. Abrahamu anauzidwa kuti: ‘M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.’ (Genesis 22:18) Pambuyo pake, Mfumu Davide anauzidwa kuti Mbewu yolonjezedwayo ikabwera kupyolera mumzera wake wachifumu. Mu 29 C.E., Mbewuyo inafika monga munthu, Yesu Kristu. (Salmo 89:3, 4; Mateyu 1:1; 3:16, 17) Mosiyana ndi Adamu wosakhulupirira, “Adamu wotsirizayo,” Yesu Kristu, anapereka chitsanzo chabwino cha kusonyeza chikhulupiriro. (1 Akorinto 15:45) Iye anakhala ndi moyo wodzipereka ku utumiki wa Yehova ndi kukwaniritsa maulosi ambiri oneneratu za Mesiya. Chotero Yesu anapangitsa chowonadi cha Mbewu yolonjezedwa kumveka bwino lomwe ndi kuchititsa zinthu zochitiridwa chithunzi ndi Chilamulo cha Mose kukhala zenizeni. (Akolose 2:16, 17) Chotero tinganene kuti ‘chowonadi chinadza mwa Yesu Kristu.’​—Yohane 1:17.

14. Kodi ndimotani mmene Paulo anasonyezera Agalatiya kuti chikhulupiriro chinakhala ndi mfundo zatsopano?

14 Tsopano popeza kuti chowonadi chinadza mwa Yesu Kristu, panakhala maziko okulirapo ozikapo chikhulupiriro cha “lonjezanolo.” Chikhulupiriro chinalimbitsidwa, chinakhala ndi mfundo zatsopano, titero kunena kwake. Ponena za chimenechi Paulo anauza Akristu anzake odzozedwa kuti: ‘Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Kristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo. Koma chisanadze chikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira chikhulupiriro chimene chikavumbulutsidwa bwino bwino. Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro. Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi. Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Yesu Kristu.’​—Agalatiya 3:22-26.

15. Kodi chikhulupiriro chikakwaniritsidwa kokha mwanjira yanji?

15 Aisrayeli adasonyeza chikhulupiriro m’zochita za Mulungu ndi iwo kupyolera m’pangano la Chilamulo. Koma tsopano chikhulupirirochi chinafunikira kuwonjezeredwa. Motani? Mwakusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu wodzozedwa ndi mzimu kwa amene Chilamulocho chinalinganizidwira kuwatsogolera. Kokha mwa njirayo mpamene chikhulupiriro chokhalako Chikristu chisanadze chikakwaniritsidwira. Kunali kofunika chotani nanga kwa Akristu oyambirirawo ‘kuyang’anitsitsa dwii pa Mtsogoleri ndi Wokwaniritsa wa chikhulupiriro chawo’! (Ahebri 12:2, NW) Ndithudi, Akristu onse afunikira kuchita chimenecho.

16. Kodi ndimotani mmene mzimu woyera unabwerera mwa njira yowonjezereka, ndipo chifukwa ninji?

16 Polingalira za chidziŵitso chowonjezereka cha chowonadi chaumulungu ndi chikhulupiriro chotulukapo chokwaniritsidwa, kodi mzimu woyera nawonso unayenera kubwera mwanjira yowonjezeredwa? Inde. Pa Pentekoste wa 33 C.E., mzimu wa Mulungu, mthandizi wolonjezedwa amene Yesu adanenapo, unatsanuliridwa pa ophunzira ake. (Yohane 14:26; Machitidwe 2:1-4) Pamenepo mzimu woyera unayamba kugwira ntchito pa iwo mwa njira yatsopano kotheratu monga abale odzozedwa a Kristu. Chikhulupiriro chawo, chipatso cha mzimu woyera, chinalimbitsidwa. Icho chinawakonzekeretsa kaamba ka ntchito yaikulu yopanga ophunzira imene idali patsogolo pawo.​—Mateyu 28:19, 20.

17. (a) Kodi chowonadi chinabwera motani ndipo chikhulupiriro chakwaniritsidwa motani chiyambire 1914? (b) Kodi ndiumboni wotani umene tiri nawo wa kugwira ntchito kwa mzimu woyera chiyambire 1919?

17 Chikhulupiriro chinafika zaka 1,900 zapitazo, pamene Yesu anadzipereka monga Mfumu Yosankhidwiratu. Koma tsopano pokhala Mfumu yakumwamba yolamulira, maziko athu a chikhulupiriro​—chowonadi chovumbulidwa​—akula kwenikweni, motero kukwaniritsa chikhulupiriro chathu. Mofananamo, kugwira ntchito kwa mzimu woyera kwawonjezeredwa. Panali umboni wowonekera bwino wa chimenechi mu 1919, pamene mzimu woyera unapatsanso nyonga atumiki odzipereka a Mulungu kuwadzutsa ku mkhalidwe wa kutsala pang’ono kulekeratu kugwira ntchito. (Ezekieli 37:1-14; Chibvumbulutso 11:7-12) Pamenepo maziko a paradaiso wauzimu anayalidwa, amene m’zaka makumi otsatirapo wakhala wowonekera ndi waulemerero mowonjezerekawonjezereka chaka ndi chaka. Kodi pangakhale umboni wina woposapo wa kugwira ntchito kwa mzimu woyera wa Mulungu?

Kodi Nkuchipenderanji Chikhulupiriro Chathu?

18. Kodi ndimotani mmene azondi Achiisrayeli anasiyanirana m’chikhulupiriro?

18 Mwamsanga pambuyo pakumasulidwa kwa Aisrayeli kuukapolo m’Igupto, amuna 12 anatumidwa kukazonda dziko la Kanani. Komabe, khumi a iwo analibe chikhulupiriro, nakaikira kukhoza kwa Yehova kukwaniritsa lonjezo lake la kupatsa Aisrayeli dzikolo. Iwo anasonkhezeredwa ndi chiwonekedwe, ndi zinthu zakuthupi. Pakati pa 12, kokha Yoswa ndi Kalebu ndiwo anasonyeza kuti anayenda mwa chikhulupiriro, osati mwa chiwonekedwe. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 5:7.) Chifukwa chakusonyeza chikhulupiriro, iwo okha pakati pa amunawo anapulumuka kukaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.​—Numeri 13:1-33; 14:35-38.

19. Kodi ndimotani mmene maziko omangapo chikhulupiriro aliri akuya lerolino kuposa ndi kalelonse, komabe kodi tiyenera kuchitanji?

19 Lerolino, tikuima kumalire kwa dziko latsopano lolungama la Mulungu. Ngati titi tiloŵemo, chikhulupiriro nchofunika kwambiri. Mokondweretsa, maziko a chowonadi chozikapo chikhulupiriro chimenecho ngakuya kuposa ndi kale lonse. Tiri ndi Mawu athunthu a Mulungu, chitsanzo cha Yesu Kristu ndi otsatira ake odzozedwa, chichirikizo cha mamiliyoni a abale ndi alongo auzimu, ndi chichirikizo cha mzimu woyera wa Mulungu wosayerekezedwa ndi kale lonse. Komabe, tingachite bwino kupenda chikhulupiriro chathu ndi kutenga masitepe ochirimbitsira pamene tidakali okhoza kutero.

20. Kodi ndimafunso otani amene tiyenera kudzifunsa?

20 ‘Inde, ndikhulupirira kuti ichi ndicho chowonadi,’ inu mungatero. Koma kodi chikhulupiriro chanu ncholimba motani? Tadzifunsani kuti: ‘Kodi Ufumu wakumwamba wa Yehova ulidi weniweni kwa ine monga momwe boma laumunthu liriri? Kodi ndikulizindikira ndi kulichirikiza mokwanira gulu lowoneka la Yehova ndi Bungwe lake Lolamulira? Ndi maso a chikhulupiriro, kodi nditha kuwona kuti mitundu tsopano ikuikidwa m’malo a kaindeinde kaamba ka Armagedo? Kodi chikhulupiriro changa chimayerekezeka bwino ndi chija cha ‘mtambo waukulu wa mboni’ wotchulidwa mu Ahebri mutu 11?’​—Ahebri 12:1; Chibvumbulutso 16:14-16.

21. Kodi ndimotani mmene chikhulupiriro chimasonkhezerera amene ali nacho, ndipo kodi iwo amadalitsidwa motani? (Phatikizanipo ndemanga za m’bokosi la patsamba 13.)

21 Awo okhala nacho chikhulupiriro chozikidwa pa chowonadi amasonkhezeredwa kuchitapo kanthu. Mofanana ndi nsembe yolandirika yoperekedwa ndi Abeli, nsembe zawo za chitamando ziri zokondweretsa kwa Mulungu. (Ahebri 13:15, 16) Mofanana ndi Nowa, mlaliki wa chilungamo yemwe anamvera Mulungu, iwo amalondola njira ya chilungamo monga alaliki a Ufumu. (Ahebri 11:7; 2 Petro 2:5) Mofanana ndi Abrahamu, awo okhala ndi chikhulupiriro chozikidwa pa chowonadi amamvera Yehova mosasamala kanthu za kusawayendera bwino kwa zinthu ndipo ngakhale pansi pamikhalidwe yoipitsitsa. (Ahebri 11:17-19) Mofanana ndi atumiki okhulupirika a Yehova a nthaŵi zakale, awo okhala ndi chikhulupiriro lerolino amadalitsidwa molemera ndi kusamaliridwa ndi Atate wawo wachikondi wakumwamba.​—Mateyu 6:25-34; 1 Timoteo 6:6-10.

22. Kodi ndimotani mmene chikhulupiriro chingalimbitsidwire?

22 Ngati ndinu mtumiki wa Yehova koma mukupeza kuti chikhulupiriro chanu nchofooka mwa njira inayake, kodi mungachitenji? Chilimbitseni chikhulupiriro chanu mwakuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi kulola pakamwa panu kutulutsa madzi a chowonadi amene adzaza mtima wanu. (Miyambo 18:4) Ngati chikhulupiriro chanu sichimalimbitsidwa nthaŵi zonse, chikhoza kufooka, kusagwira ntchito, ngakhale kufa kumene. (1 Timoteo 1:19; Yakobo 2:20, 26) Khalani wotsimikiza mtima kuti ichi sichidzachitika konse ku chikhulupiriro chanu. Pemphani thandizo la Yehova, kupemphera kuti: “Ndithandizeni m’mene ndisoŵa chikhulupiriro!”​—Marko 9:24, NW.

Kodi Mayankho Anu Ngotani?

◻ Kodi chikhulupiriro nchiyani?

◻ Kodi nchifukwa ninji chikhulupiriro sichingakhalepo papanda chowonadi ndi mzimu woyera?

◻ Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu anakhalira Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupenda mmene chikhulupiriro chathu chiriri cholimba?

[Bokosi patsamba 13]

AWO AMENE ALI NDI CHIKHULUPIRIRO. . .

◻ Amalankhula ponena za Yehova.​—2 Akorinto 4:13.

◻ Amachita ntchito zofanana ndi za Yesu.​—Yohane 14:12.

◻ Ali magwero a chilimbikitso kwa ena.​—Aroma 1:8, 11, 12.

◻ Amalilaka dziko.​—1 Yohane 5:5.

◻ Samawopa kanthu.​—Yesaya 28:16.

◻ Ali pamzera wokalandira moyo wosatha.​—Yohane 3:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena